LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr18 July masa. 1-6
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
  • Tumitu
  • JULY 2-8
  • JULY 9-15
  • JULY 16-22
  • JULY 23-29
  • JULY 30–AUGUST 5
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
mwbr18 July masa. 1-6

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

JULY 2-8

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 6-7

“Tizipimila Ena Mowolowa Manja”

nwtsty mfundo younikila pa Luka 6:37

Pitilizani kukhululukila anthu macimo awo ndipo macimo anunso adzakhululukidwa: Kapena kuti “Pitilizani kumasula ena, ndipo na imwe mudzamasulidwa.” Liu la Cigiriki limene analimasulila kuti “kukhululuka,” tanthauzo lake leni-leni ni “kulekelela; kutumiza kutali; kumasula (mwacitsanzo, mkaidi).” Koma pa lembali, liuli tikalisiyanitsa na mau akuti kuweluza na kutsutsa, limapeleka lingalilo la kulekelela ndi kukhululuka, ngakhale kuti panali poyenela kuti cilango cipelekedwe.

nwtsty mfundo younikila pa Luka 6:38

Khalani opatsa: Kapena kuti “Pitilizani kupatsa.” Liu la Cigiriki limene anaseŵenzetsa pa lembali lingamasulidwe kuti “kupatsa,” ndipo lipeleka lingalilo lopitiliza kucita cinthu.

nwtsty mfundo younikila pa Luka 6:38

m’matumba anu: Mau ake eni-eni m’Cigiriki ni “pacifuwa canu,” koma pa lembali zioneka kuti mauwa atanthauza funga imene munthu amapanga pa malaya ake aakulu akunja. Mau akuti ‘Kukhuthulila m’matumba’ akamba za cizolowezi ca ogulitsa malonda amene anali kuikapo mbasela pa zinthu zimene munthu wagula.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Luka 7:35

zotsatila zake: kapena kuti “ana ake.” Pa lembali nzelu aikamba monga ni munthu amene ali ndi ana. Pa Mat. 11:19, nzelu anaikamba kuti imagwila “nchito.” Ana kapena kuti nchito za nzelu, kutanthauza umboni umene Yohane M’batizi na Yesu anapeleka, zinaonetsa kuti milandu imene iwo anapatsiwa inali yabodza. Kweni-kweni Yesu anali kukamba kuti: ‘Onani nchito zathu zolungama na khalidwe lathu labwino, kuti mudziŵe kuti milanduyi ni yabodza.’

JULY 9-15

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 8-9

“Khala Wotsatila Wanga—Motani?”

it-2 494

Cisa

Pamene m’modzi wa alembi anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatilani kulikonse kumene mungapite,” Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiletu poti n’kutsamila mutu wake.” (Mat. 8:19, 20; Luka 9:57, 58) Apa Yesu anaonetsa mfundo yakuti, kuti munthu akhale wotsatila wake safunika kuganizila zokhala na umoyo wawofu-wofu umene ena ali nawo, koma afunika kudalila Yehova kothelatu. Mfundo imeneyi ionekelanso m’pemphelo lacitsanzo limene anaphunzitsa ophunzila ake: “Mutipatse ife lelo cakudya cathu calelo,” komanso m’mau ake akuti: “Ndithu palibe aliyense wolephela kulekana ndi cuma cake conse amene angathe kukhala wophunzila wanga.”—Mat. 6:11; Luka 14:33.

nwtsty mfundo zounikila pa Luka 9:59, 60

kukaika malilo a bambo anga: Cioneka kuti mau amenewa satanthauza kuti atate a munthuyo anali atangomwalila kumene, na kuti munthuyo anali kupempha kuti apange makonzedwe a malilo. Ngati iwo anali atamwaliladi, iye sakanakwanitsa kupeza mpata wokamba na Yesu. Kale ku Middle East, munthu akamwalila m’banja anali kumuika m’manda mwamsanga, mwina tsiku lomwelo. Conco, atate a munthuyo sanali akufa, koma ayenela kuti anali odwala kapena okalamba. Ndipo Yesu sakanauza munthuyo kuti asiye kholo lake lodwalila kapena lofunikila thandizo. Conco payenela kuti panali acibale ena a munthuyo amene akanawasamalila. (Maliko 7:9-13) M’mau ena, munthuyo anali kukamba kuti, ‘Ndidzakutsatilani, koma kokha ngati atate amwalila. Muniyembekeze nikawaikiletu m’manda.’ Komabe, kwa Yesu munthuyo anali kutaya mwayi woika zinthu za Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wake.—Luka 9:60, 62.

Aleke akufa aike akufa awo: Monga mmene mfundo younikila ya pa Luka 9:59 yaonetsela, atate a munthu amene Yesu anali kukamba naye, sanali akufa koma anali odwala kapena okalamba. Apa mwacionekele Yesu anali kukamba kuti: ‘Aleke akufa mwauzimu aike akufa awo,’ kutanthauza kuti munthuyo anafunika kusiila abululu ake kuti asamalile atate ake mpaka pamene adzamwalila na kuikiwa m’manda. Mwa kutsatila Yesu, munthuyo akanaloŵa pa njila ya ku moyo wamuyaya, na kucoka pakati pa anthu amene Mulungu anali kuwaona kuti ni akufa mwauzimu. Mu yankho lake, Yesu anaonetsa kuti kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo na kuulengeza kulikonse, n’zofunika kuti munthu akhale wogalamuka mwauzimu.

nwtsty zithunzi

Kugaula

Nthawi zambili anthu anali kuyamba kugaula m’minda kuciyambi kwa dzinja, cifukwa cakuti mvula ikayamba, inali kufewetsako nthaka imene inali itauma gwa m’nyengo yotentha. (Onani Gawo 19 mu Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu.) Mapulawo ena anali na mlomo wa mtengo kapena wacitsulo, wogwilana na msana wapulawo, umene unali kudonsewa na nyama imodzi kapena kuposelapo. Akagaula nthaka, anali kubzala mbewu. M’Malemba Aciheberi, nchito yogaula na pulawo imeneyi anali kuiseŵenzetsa m’mafanizo. (Ower. 14:18; Yes. 2:4; Yer. 4:3; Mika 4:3) Kambili Yesu anali kuseŵenzetsa nchito za ulimi pofuna kupeleka mafanizo pophunzitsa mfundo zofunika. Mwacitsanzo, anakamba zimene zimacitika pogaula na pulawo n’colinga cakuti aonetse kufunika kokhala wophunzila wodzipeleka na mtima wonse. (Luka 9:62) Ngati wogwila pulawo akuyang’ana kumbuyo, akhoza kupanga mizele yobenda. Mofananamo, wophunzila wa Khristu amene amatengeka na zinthu zina kapena kuti kuyang’ana kumbuyo pamene akutumikila, amakhala wosayenela Ufumu wa Mulungu.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Luka 8:3

anali kutumikila Yesu ndi atumwiwo: Kapena kuti, “anali kuwacilikiza (kuwapezela zofunikila).” Liu la Cigiriki lakuti di·a·ko·neʹo lingatanthauze kuwathandiza mwakuthupi mwa kuwapezela cakudya, kuwaphikila, kuwapatsa cakudya, na nchito zina zaconco. Liuli laseŵenzetsedwa m’lingalilo lofanana pa Luka 10:40 (“nchito”), Luka 12:37 (“adzawatumikila”), Luka 17:8, (“kunditumikila”), Mac. 6:2 (“kugaŵa cakudya”). Koma liuli lingaseŵenzetsedwe ngakhale pa nchito zonse zimene munthu angacitile winawake. Palembali, liuli likufotokoza mmene azimayi ochulidwa pa vesi 2 na 3 anacilikizila Yesu na ophunzila ake, kuwathandiza kuti acite bwino nchito imene Mulungu anawapatsa. Mwa kucita izi, azimayiwo analemekeza Mulungu. Ndipo Mulungu anawayamikila mwa kusunga m’Baibo nchito zawo zacifundo zimene anacita na kuceleza kwawo, kuti mibadwo ya m’tsogolo izikaŵelenga za iwo. (Miy. 19:17; Aheb. 6:10) Liu la Cigiriki limeneli analiseŵenzetsa pokamba za azimayi pa Mat. 27:55; na pa Maliko 15:41.

JULY 16-22

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 10-11

“Fanizo la Msamariya Wacifundo”

nwtsty zithunzi

Mseu Wocoka ku Yerusalemu Kupita ku Yeriko

Mseu (1) umene ukuonekela m’kavidiyo aka mwacionekele ni mseu wolingana na uja wakale umene unali kucoka ku Yerusalemu kupita ku Yeriko. Mseuwo unali wautali kuposa makilomita 20, ndipo unali wosondomoka kwambili mukamacokela ku Yerusalemu kupita ku Yeriko. Kambili mu mseu umenewu munali kupezeka acifwamba cakuti anali kuikamo asilikali kuti aziteteza anthu opita mumsewu umenewu. Yeriko wa m’nthawi ya Aroma (2) unali kupezeka pa malo amene panayambila mseu umenewu, m’cipululu ca Yudeya. Koma mzinda wakale wa Yeriko (3) unali pamtunda wa makilomita pafupi-fupi aŵili kucokela pamene panali Yeriko wa m’nthawi ya Aroma.

nwtsty mfundo zounikila pa Luka 10:33, 34

Msamariya wina: Ayuda anali kuipidwa na Asamariya ndipo sanali kuyanjana nawo. (Yoh. 4:9) Ayuda ena anali kuseŵenzetsa liu lakuti “Msamariya” pofuna kunyoza kapena kutonza munthu. (Yoh. 8:48) M’Rabi wina anagwidwa mau m’buku yopatulika yochedwa Mishna. Iye anati: “Munthu amene amadya mkate wa Asamariya amafanana na munthu wakudya nyama ya nkhumba.” (Shebith 8:10) Ayuda ambili sanali kukhulupilila umboni wopelekewa na Msamariya ngakhale kulandila thandizo locoka kwa Msamariya. Yesu podziŵa khalidwe loipa la Ayuda, anaphunzitsa mfundo yamphamvu mu fanizo limene limadziŵika kuti fanizo la Msamariya wabwino kapena wacifundo.

kumanga mabala ake, [kuthila] mafuta ndi vinyo m’mabalamo: Luka, amene anali dokota, analemba fanizo la Yesu limeneli mosamala, mwa kufotokoza mankhwala a zilonda amene anthu anali kuseŵenzetsa pa nthawiyo. Kambili, anthu panyumba anali kuseŵenzetsa mafuta na vinyo monga mankhwala azilonda. Anali kuseŵenzetsa Mafuta kuti afewetse cilonda (Yelekezani na Yes. 1:6), ndipo anali kuseŵenzetsa vinyo cifukwa uli na mphamvu yopha tumabakitiliya. Luka anakambanso kuti pa cilonda anali kumangapo kuti pasatupe kwambili.

Kunyumba ya alendo: Liu lake la Cigiriki litanthauza “malo olandililako anthu onse.” Apaulendo na ziŵeto zawo anali kupeza pogona m’malo ngati amenewa. Woyang’anila malo amenewa anali kupeleka zofunikila kwa alendowo, ndipo akamusiila zakuti asamalile, anali kumupatsa malipilo.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Luka 10:18

Ndinayamba kuona Satana atagwa kale ngati mphezi kucokela kumwamba: Mwacionekele Yesu anali kukamba mwaulosi. Anali kukamba kuti anali ataona Satana akugwetsedwa kucoka kumwamba monga kuti zacitika kale. Pa Chiv. 12:7-9 pakamba za nkhondo imene inacitika kumwamba, na kugwetsedwa kwa Satana kumene kunacitika pamene Ufumu wa Mesiya unabadwa. Apa Yesu anali kutsindika mfundo yakuti Satana ndi ziwanda zake adzagonjetsedwa m’tsogolo, cifukwa panthawiyo, Mulungu anali atapeleka mphamvu yotulutsa ziwanda kwa ophunzila ake 70, omwe anali anthu wamba opanda ungwilo.—Luka 10:17.   

nwtsty mfundo zounikila pa Luka 11:5-9

Bwanawe, ndibwelekeko mitanda itatu ya mkate: Pa cikhalidwe ca ku Middle East, anthu anali kuona kuti ni udindo wawo kuceleza alendo, ndipo amakonda kucita zimenezo. Izi zionekela bwino m’fanizo ili. Olo kuti mlendoyo anabwela mosayembekezela pakati pa usiku, mwininyumbayo anaona kuti ni bwino kumupatsa cakudya, cifukwa anazindikila kuti ayenela kuti anakumana na zovuta zinazake pa ulendo wake. Iye anaona kuti panalibe vuto ngakhale kukadzutsa mnansi wake pa ola limenelo kuti apempheko cakudya.

Usandivutitse ine: Mnansi wa m’fanizo limeneli sanafune kuthandiza mnzake, osati cifukwa cakuti sanali waubwenzi, koma cifukwa cakuti iye anali atagona kale. Nyumba za m’nthawi imeneyo, makamaka za anthu osauka, zinali kukhala cabe na cipinda cimodzi cacikulu. Conco, ngati mwamuna wa m’nyumbayo wauka, mwacionekele anali kusokoneza banja lonse, ngakhale ana amene anali gone.

kukakamila: Liu la Cigiriki limene anaseŵenzetsa apa litanthauza “kusadzicepetsa” kapena “kusacita manyazi.” Koma pa lembali, liuli lipeleka lingalilo la kukakamila kapena kulimbikila. Munthu wa m’fanizo la Yesu sanacite manyazi kapena kugwa ulesi na kuleka kupempha zimene anali kufuna. Ndipo Yesu anauza ophunzila ake kuti ayenelanso kupemphela mwakhama, mosalekeza.—Luka 11:9, 10.

JULY 23-29

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 12-13

“Ndinu Ofunika Kwambili Kuposa Mpheta Zambili”

nwtsty mfundo younikila pa Luka 12:6

mpheta: Liu la Cigiriki lakuti strou·thiʹon limatanthauza mbalame iliyonse yaing’ono, koma nthawi zambili limatanthauza mpheta, mbalame yochipa kwambili pa mbalame zonse zimene anthu anali kugula monga cakudya panthawiyo.

nwtsty mfundo younikila pa Luka 12:7

ngakhale tsitsi lonse la m’mutu mwanu analiŵelenga: Tsitsi la m’mutu wa munthu nthawi zambili limaposa pa 100,000. Nzelu zozama za Yehova zofika pa kudziŵa tunthu twatung’ono conco, zionetsa kuti amacita cidwi ngako na wotsatila aliyense wa Khristu.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Luka 13:24

Yesetsani mwamphamvu: Kapena kuti “Pitilizani kulimbikila.” Malangizo a Yesu akutsindika pa kufunika kocitapo kanthu na mtima wonse kuti munthu aloŵe pakhomo lopapatiza. Pa lemba limeneli, Mabaibo ena anamasulila mauwa kuti: “Yesetsani na mphamvu zonse; Yesetsani kucita khama.” Velebu ya Cigiriki yakuti a·go·niʹzo·mai ifanana na dzina la Cigiriki lakuti a·gonʹ, limene nthawi zambili anali kuliseŵenzetsa pokamba za mpikisano wothamanga. Pa Aheb. 12:1, liuli analiseŵenzetsa mophiphilitsa pokamba za “mpikisano” wacikhristu wokapeza moyo. Amaliseŵenzetsanso pokamba za kulimbana na mavuto (Afil. 1:30; Akol. 2:1) kapena ‘kumenya nkhondo’ (1 Tim. 6:12; 2 Tim. 4:7). Koma mau a Cigiriki amene anaseŵenzetsa pa Luka 13:24, anawamasulila kuti ‘kucita nawo mpikisano’ (1 Akor. 9:25), “[kuyesetsa] mwakhama” (Akol. 1:29; 4:12; 1 Tim. 4:10), komanso ‘kumenyela’ (1 Tim. 6:12). Cifukwa cakuti liuli anali kuliseŵenzetsa pa mpikisano wa maseŵela othamanga, anthu ena akambapo kuti khama limene Yesu anatilimbikitsa kukhala nalo tingaliyelekezele na khama limene wothamanga amakhala nalo pothamanga na mphamvu zake zonse kuti awine mphoto.

nwtsty mfundo younikila pa Luka 13:33

n’kosayenela: Kapena kuti “n’kosafunika (sizingakhale bwino).” Olo kuti palibe ulosi wa m’Baibo umene umakamba mwacindunji kuti Mesiya anali kudzafela ku Yerusalemu, lingalilo limeneli liyenela kuti linatengewa pa Dan. 9:24-26. Kuwonjezela apo, cinali coyembekezeka kuti ngati Ayuda anali kudzapha mneneli, maka-maka Mesiya, iwo adzamuphela mu mzinda umenewo. Mamemba 71 a Sanihedirini, khoti lalikulu la Ayuda, anasonkhana ku Yerusalemu, kuti ayese onse amene anali kuganizilidwa kuti anali aneneli onama. Yesu ayenelanso kuti anali kudziŵa kuti ku Yerusalemu ndiye kumene anthu anali kupelekela nsembe kwa Mulungu nthawi zonse na kuti n’kumene anali kuphela nkhosa ya mwambo wa Pasika. Mau amene Yesu anakamba anakwanilitsika. Iye anapelekedwa ku khoti la Sanihedirini, ku Yerusalemu na kuweluzidwa. Ndipo ku Yerusalemu kumeneko, kunja kwa mpanda wa mzinda, n’kumene iye anafela monga “nsembe . . . ya Pasika.”—1 Akor. 5:7.

JULY 30–AUGUST 5

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 14-16

“Fanizo la Mwana Woloŵelela”

nwtsty mfundo zounikila pa Luka 15:11-16

Munthu wina anali ndi ana aamuna aŵili: Mbali zina za m’fanizo la mwana woloŵelela (lodziŵikanso kuti “mwana wotayika”) n’zapadela. Fanizoli ni limodzi mwa mafanizo aatali amene Yesu anapeleka. Cocititsa cidwi kwambili ni mgwilizano umene iye anafotokoza wokhudza banjalo. M’mafanizo ena, Yesu kambili anali kuseŵenzetsa zinthu zopanda moyo, monga mbewu zosiyana-siyana na nthaka, kapena mgwilizano wapadela wa pakati mbuye ndi akapolo ake. (Mat. 13:18-30; 25:14-30; Luka 19:12-27) Komabe, m’fanizo ili Yesu anaunika mgwilizano wapadela pakati pa tate ndi ana ake. Ambili mwa amene anamvela fanizoli ayenela kuti sanakhalepo na tate wacikondi ngati ameneyu. Fanizo limeneli limaonetsanso cifundo na cikondi cacikulu cimene Atate wathu wakumwamba ali naco kwa ana ake a padziko, ponse paŵili, kwa amene sanamusiye na aja amene amabwelela kwa iye pambuyo posocela.

Wamng’ono pa aŵiliwo: Malinga na Cilamulo ca Mose, mwana woyamba anali kupatsiwa magawo aŵili. (Deut. 21:17) Conco, ngati mwana wamkulu wa m’fanizoli anali woyamba kubadwa, ndiye kuti colowa ca mwana wang’ono cinali hafu ya colowa ca mwana wamkulu.

anasakaza: Liu la Cigiriki limene anaseŵenzetsa pa lembali limatanthauza “kumwaza (m’njila zosiyana-siyana).” (Luka 1:51; Mac. 5:37) Pa Mat. 25:24, 26, liuli analimasulila kuti ‘kupepeta.’ Koma palembali, analiseŵenzetsa m’lingalilo la kuwononga kapena kuseŵenzetsa mosasamala.

m’makhalidwe oipa: kapena kuti “umoyo wotayilila (wolekelela; waucinyama).” Liu lolinganako la Cigiriki lokhala na tanthauzo lofanana analiseŵenzetsa pa Aef. 5:18; Tito 1:6; na pa 1 Pet. 4:4. Ma Baibo ena amaonetsa kuti liu la Cigiriki limenelo lingatanthauzenso kusakaza cuma, kapena kuciwononga.

kuti azikaŵeta nkhumba: Nyama zimenezi zinali zodetsedwa malinga na Cilamulo. Conco, nchitoyi inali yotsika komanso yonyozeka kwa Ayuda.—Lev. 11:7, 8.

cakudya ca nkhumbazo: Kuvutika kwa mwana ameneyo kukuonekela bwino pa kufunitsitsa kwake kudya ngakhale cakudya ca nkhumba.—Onani mfundo younikila pa Luka 15:15.

nwtsty mfundo zounikila pa Luka 15:17-24

aganyu: Pamene mwana wamng’ono anabwelela kunyumba, anaganiza zakuti apemphe atate ake kuti amulandile, osati monga mwana wawo, koma monga waganyu. Aganyu analibe colowa panyumbapo, monga mmene analili akapolo, ndipo anali anthu akunja ongopatsidwa nchito ya tsiku limodzi.—Mat. 20:1, 2, 8.

anamupsompsona mwacikondi: Kapena kuti “anamupsompsona mokoma mtima.” Liu la Cigiriki limene analimasulila kuti “anamupsompsona mwacikondi” anthu amalimvetsa kuti ni liu lotsindika velebu yakuti phi·leʹo, imene nthawi zina amaimasulila kuti “kupsompsona” (Mat. 26:48; Maliko 14:44; Luka 22:47) koma nthawi zambili imapeleka tanthauzo la “kuonetsa cikondi” (Yoh. 5:20; 11:3; 16:27). Mwa kumupatsa moni mwacikondi komanso mwaubwenzi, tate wa m’fanizoli anaonetsa kuti anali wofunitsitsa kulandila mwana wake wolapayo.

kuchedwa mwana wanu: M’mipukutu ina anawonjezelamo mau akuti: “Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.” Koma zimene zili m’Baibo yokonzewanso zigwilizana na mipukutu yoyambilila yodalilika. Akatswili ena amaona kuti mau owonjezela amenewo anaikiwamo n’colinga cakuti vesiyi igwilizane na Luka 15:19.

mkanjo . . . mphete . . . nsapato: Mkanjo umenewu sunali mkanjo wamba, koma unali wabwino koposa—mwina wokonzedwa mwaluso umene anali kupatsa mlendo wolemekezeka. Kumuveka mphete mwanayo kumanja, kumene tate anacita, kunaonetsa kuti wamukomela mtima, wamukonda ndiponso wamulemekeza. Kunaonetsanso kuti wamulandila monga mwana wake. Nthawi zambili, akapolo sanali kuvala mphete na nsapato. Conco, tateyo anali kufuna kumutsimikizila mwanayo kuti wamulandila na manja aŵili monga mwana wa m’banja.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Luka 14:26

osadana: M’Baibo liu lakuti “kudana” lili na matanthauzo osiyana-siyana. Lingatanthauze kukhala na mkwiyo umene umayamba cifukwa ca cizondi. Mkwiyowo umasonkhezela munthu kuvulaza ena. Pena, lingatanthauze kuzonda kapena kuipidwa kwambili na munthu kapena cinthu cinacake, zimene zingapangitse kuti uleke kucita ciliconse na munthuyo kapena cinthuco. Penanso, liuli lingatanthauze kusam’konda kweni-kweni munthu poyelekezela na wina. Mwacitsanzo, pamene Baibo imakamba kuti Yakobo “anamuda” Leya na kukonda Rakele, limatanthauza kuti anakonda Rakele kuposa Leya. (Ge 29:31; De 21:15, Buku Lopatulika.) Ndipo m’zolemba zina zakale za Ayuda, liuli analiseŵenzetsa m’lingalilo limeneli. Conco, Yesu sanali kutanthauza kuti otsatila ake afunika kudzizonda kapena kudana na acibale awo ayi, cifukwa kucita zimenezi kumatsutsana na Malemba. (Yelekezelani na Maliko 12:29-31; Aef. 5:28, 29, 33.) Pa lembali, mau akuti ‘kudana’ tingawakambenso kuti “kusakonda kweni-kweni poyelekezela ndi” wina wake kapena cinacake.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani