LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 August tsa. 7
  • Yesu Anafelanso M’bale Wako

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Anafelanso M’bale Wako
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Sungani Mgwilizano wa Mpingo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tizithetsa Mikangano Mwamtendele
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Musapunthwitse “Tianati”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 August tsa. 7
Yesu akuphunzitsa otsatila ake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yesu Anafelanso M’bale Wako

Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka anthu ocimwa. (Aroma 5:8) Mosakayikila, aliyense wa ise amayamikila kuti Yesu anationetsa cikondi mwa kutifela. Komabe, nthawi zina timaiŵala kuti Khristu anafelanso abale athu. Kodi abale na alongo amene ni opanda ungwilo ngati ise, tingawaonetse bwanji cikondi ngati cimene Khristu anationetsa? Ganizilani njila zitatu izi. Yoyamba, pa mabwenzi amene tili nawo kale tingawonjezelepo anthu a cikhalidwe cosiyana na cathu. (Aroma 15:7; 2 Akor. 6:12, 13) Yaciŵili, tiyenela kukhala osamala kuti tipewe kukamba kapena kucita zinthu zimene zingakhumudwitse ena. (Aroma 14:13-15) Yothela, ngati munthu wina watilakwila, tiyenela kumukhululukila mwamsanga. (Luka 17:3, 4; 23:34) Ngati tiyesetsa kutengela citsanzo ca Yesu m’njila zitatuzi, Yehova adzapitiliza kudalitsa mpingo kuti ukhale wamtendele komanso wogwilizana.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI KHALANI MUNTHU WABWINO KWAMBILI! NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Miki amulandila mu mpingo watsopano

    Kodi Miki poyamba anali kuuona bwanji mpingo wake?

  • Miki wakhumudwa na ena mumpingowo

    N’ciani cinamupangitsa kuyamba kukhala wokhumudwa?

  • Yesu akomela mtima atumwi ake olo kuti anali atagona

    Kodi citsanzo ca Yesu cinamuthandiza bwanji Miki kuyamba kuona zinthu moyenela? (Maliko 14:38)

  • Miki akuseka pamene kamwana kagunda kapu yake ya dilinki imene yamutaikila ku zovala zake

    Kodi Miyambo 19:11 ingatithandize bwanji kuyamba kuona Akhristu anzathu moyenela?

ZOTI MUSINKHESINKHE:

Kodi nimasungila cakukhosi munthu wina pa nkhani imene nifunika kungoinyalanyaza?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani