Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
JULY 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AKOLOSE 1-4
“Vulani Umunthu Wakale, Muvale Watsopano”
w11 3/15 10 ¶12-13
Landilani Mzimu wa Mulungu Osati wa Dziko
12 Kodi khalidwe langa limaonetsa mzimu uti? (Ŵelengani Akolose 3:8-10, 13.) Mzimu wa dziko umalimbikitsa nchito za thupi. (Agal. 5:19-21) Kunena zoona, mzimu umene timayendela umaonekela pamene zinthu zavuta, osati pamene zili bwino-bwino. Mwacitsanzo, mzimuwo umaonekela pamene m’bale kapena mlongo watinyalanyaza, kutikhumudwitsa kapena kutilakwila. Ungaonekelenso pamene tili kwatekha m’nyumba. Tingacite bwino kudzifufuza pa nkhani imeneyi. Dzifunseni kuti, ‘Kodi pa miyezi 6 yapitayi naonetsa makhalidwe a Khristu, kapena nayambanso kulankhula na kucita zinthu zina zoipa?’
13 Mzimu wa Mulungu ukhoza kutithandiza ‘kuvula umunthu wakale pamodzi na nchito zake’ n’kuvala “umunthu watsopano.” Izi zingatithandize kukhala acikondi ndiponso okoma mtima kwambili. Tidzakonda kukhululukila ena na mtima wonse ngakhale pamene tili na cifukwa ceni-ceni codandaulila za iwo. Ngati taona kuti mwina pacitika zopanda cilungamo sitidzacita zinthu monga, ‘kuwawidwa mtima kwa njilu, kupsa mtima, kukwiya, kulalata ndiponso kulankhula mawu acipongwe.’ M’malomwake tidzayesetsa kukhala “acifundo cacikulu.”—Aef. 4:31, 32.
Kodi Mwasandulika?
18 Kuŵelenga na kuphunzila Baibo ni ciyambi cabe kuti Mawu a Mulungu atisandulize. Anthu ambili amaŵelenga Baibo nthawi na nthawi, ndipo amadziŵa zimene imanena. Mwina inuyo munakumanapo ndi anthu otelo mu ulaliki. Ena amakwanitsa kuchula pamtima zimene mavesi ena a m’Baibo amakamba. Koma zimenezi sizisintha kweni-kweni maganizo na khalidwe lawo. N’cifukwa ciani zili conco? Kuti Mawu a Mulungu asandulize munthu, iye ayenela kuwalola kumufika pamtima. (Agal. 6:6) Conco, tifunika kupatula nthawi kuti tisinkhe-sinkhe zimene timaphunzila. Tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakhulupililadi kuti zimene ndimaphunzila ni Mawu a Mulungu? Kodi ndimakhulupilila kuti ici ni coonadi? Kodi nimayesetsa kugwilitsila nchito zimene nimaphunzila osati kungouzako ena cabe? Nikamaphunzila, kodi nimamva kuti Yehova akamba na ine mwacindunji?’ Kuganizila na kusinkha-sinkha mafunso ngati amenewa kungathandize kukulitsa cikondi cathu pa Yehova. Ngati timakonda Mulungu kucokela pansi pa mtima, tidzapanga masinthidwe oyenela pa umoyo wathu.—Miy.4:23; Luka 6:45.
19 Kuŵelenga na kusinkha-sinkha Mawu a Mulungu nthawi zonse kudzatithandiza kupitiliza ‘kuvula umunthu wakale pamodzi na nchito zake, na kuvala umunthu watsopano umene Mulungu amapeleka, kutanthauza kuti mwa kudziŵa zinthu molondola, tidzacititsa umunthu wathu kukhala watsopano.’ (Akol. 3:9, 10) Ndithudi, tidzapindula kwamuyaya ngati timvetsetsa Mawu a Mulungu na kucita zimene amanena. Kuvala umunthu watsopano kudzatithandiza kupewa misampha ya Satana.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 169 ¶3-5
Ufumu wa Mulungu
“Ufumu wa Mwana Wake Wokondedwa.” Pambuyo pa masiku 10 Yesu atapita kumwamba, “anakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu.” Ophunzila ake anaona umboni wa cocitika cimeneci pa Pentekosite wa mu 33 C.E., pamene Yesu anatsanulila mzimu woyela pa iwo. (Mac. 1:8, 9; 2:1-4, 29-33) Pamenepo “pangano latsopano” linayamba kugwila nchito pa iwo, ndipo anali oyamba kudzozedwa mu “mtundu woyela” watsopano, umene ni Isiraeli wauzimu.—Aheb. 12:22-24; 1 Pet. 2:9, 10; Agal. 6:16.
Apa lomba, Khristu anakhala kudzanja lamanja la Atate ŵake, ndipo anali Mutu wa mpingowu. (Aef. 5:23; Aheb. 1:3; Afil. 2:9-11) Malemba amaonetsa kuti kucokela pa Pentekosite wa mu 33 C.E. kupita m’tsogolo, ufumu wauzimu unakhazikitsidwa pa ophunzila ake. Polembela kalata Akhristu a ku Kolose a m’zaka 100 zoyambilila, Paulo anasonyeza kuti Yesu Khristu anali kale na ufumu. Anati: “[Mulungu] anatilanditsa ku ulamulilo wa mdima, n’kutisamutsila mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa.”—Akol. 1:13; yelekezelani na Mac. 17:6, 7.
Kucokela pa Pentekosite wa mu 33 C.E. kupita m’tsogolo, ufumu wauzimuwo wa Khristu wakhala ukulamulila pa Isiraeli wauzimu, amene ni Akhristu obadwa mwa mzimu wa Mulungu kuti akhale ana ake auzimu. (Yoh. 3:3, 5, 6) Akhristu obadwa mwa mzimu amenewa akadzalandila mphoto yawo ya kumwamba, sadzakhalanso nzika za ufumu wauzimu wa Khristu pa dziko lapansi. M’malo mwake, adzakhala mafumu pamodzi na Khristu kumwamba.—Chiv. 5:9, 10.
w08 8/15 28 ¶8
Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Agalatiya, Aefeso, Afilipi, na Akolose
2:8—Kodi “mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli” zimene Paulo anacenjezapo n’ciani? Zimenezi ni zinthu za m’dziko la Satanali, kapena kuti mfundo zimene anthu m’dzikoli amayendela. (1 Yoh. 2:16) Zimenezi zimaphatikizapo zinthu monga nzelu za anthu, kukonda cuma, komanso zipembedzo zonyenga za dzikoli.
JULY 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 ATESALONIKA 1-5
“Pitilizani Kutonthozana ndi Kulimbikitsana”
w11 6/15 26 ¶12
“Muzilemekeza Anthu Amene Akugwila Nchito Mwakhama Pakati Panu”
12 Koma ‘kutsogolela’ mpingo sikungotanthauza kuphunzitsa. Mawu amene anawamasulila kuti ‘kutsogolela’ ndi ofanana ndi amene anawamasulila kuti ‘kuyang’anila’ pa lemba la 1 Timoteyo 3:4. Paulo ananena kuti woyang’anila mu mpingo ayenela kukhala “mwamuna woyang’anila bwino banja lake. Wa ana omumvela ndi mtima wonse.” Mawu amene anawamasulila kuti ‘kuyang’anila’ pa lembali sangotanthauza kuphunzitsa ana ake, komanso kuwatsogolela m’njila zina ndiponso kuti anawo ‘azimumvela.’ Nawonso akulu amatsogolela mpingo akamathandiza anthu mu mpingomo kuti azimvela Yehova.—1 Tim. 3:5.
w11 6/15 28 ¶19
“Muzilemekeza Anthu Amene Akugwila Nchito Mwakhama Pakati Panu”
19 Kodi mungacite ciani ngati munthu wina wakukonzelani mphatso inayake n’kukupatsani? Kodi mungaonetse kuti mukuiyamikila poigwilitsa nchito? Yehova wakupatsani “mphatso za amuna” kudzela mwa Yesu Khristu. Njila imodzi imene mungasonyezele kuyamikila mphatso zimenezi ndiyo kumvetsela mwachelu nkhani zimene akulu amakamba, ndiponso kugwilitsa nchito mfundo zimene mwamva m’nkhanizo. Kupeleka ndemanga zogwila mtima pa misonkhano ni njila inanso imene mungasonyezele kuti mumayamikila mphatsozi. Muzithandizanso pa nchito zimene akulu amatsogolela, monga utumiki wakumunda. Ngati mwapindula kwambili na malangizo amene mkulu wina anapeleka, bwanji osamuyamikila? Ni bwinonso kumayamikila anthu a m’banja la akulu. Kumbukilani kuti nthawi imene akulu amagwila nchito mwakhama mu mpingo ni nthawi imene akanakhala na banja lawo, koma banjalo limalolela zimenezi.
“Tizisonyezana Cikondi Ceni-ceni m’Zocita Zathu”
13 Muzithandiza ofooka. Tingaonetse kuti tilidi na cikondi ceni-ceni ngati titsatila lamulo la m’Baibo lakuti “thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Ates. 5:14) Ngakhale kuti abale na alongo ambili ofooka pambuyo pake amalimba m’cikhulupililo, ena timafunika kupitilizabe kuwathandiza moleza mtima. Tingacite zimenezo mwa kuwauzako mfundo zolimbikitsa za m’Malemba, kuwapempha kuti tiyende nawo mu ulaliki, kapena kuwamvetsela pamene afotokoza mavuto awo. Cinanso, si bwino kumangoganizila za kuti m’bale cite ni “wolimba” kapena mlongo cite ni “wofooka.” Tifunika kukumbukila kuti tonse tili na zofooka, ndi kuti pali zinthu zina zimene timacita bwino. Ngakhale mtumwi Paulo anavomeleza zofooka zake. (2 Akor. 12:9, 10) Conco, tonse timafunikila thandizo la Akhristu anzathu.
Khalani Wodzicepetsa ndi Wacifundo Monga Yesu
16 Mawu athu acifundo. Kumvelela ena cifundo kudzaticititsa ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wacisoni.’ (1 Ates. 5:14) N’ciani cimene tingakambe polimbikitsa anthu otelo? Tingawalimbikitse mwa kuwauza kuti timawakonda kwambili. Tingawayamikile mocokela pansi pamtima pa makhalidwe abwino na maluso amene ali nawo. Tingawakumbutse kuti Yehova anawakokela kwa Mwana wake, ndipo ni amtengo wapatali kwa iye. (Yoh. 6:44) Ndipo tingawatsimikizile kuti Yehova amawakonda kwambili atumiki ake a “mtima wosweka” kapena “odzimvela cisoni mumtima mwawo.” (Sal. 34:18) Kulankhula mwa njila imeneyi kungalimbikitse aja amene akufunikila citonthozo.—Miy. 16:24.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 863-864
Dama
Dama ni chimo limene munthu akalicita, angacotsedwe nalo mu mpingo wacikhristu. (1 Akor. 5:9-13; Aheb. 12:15, 16) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Mkhristu akacita dama amacimwila thupi lake, cifukwa amaseŵenzetsa ziwalo zake zobelekela kucita zinthu zonyansa. Munthu akacita zimenezi uzimu wake umakhudzidwa moipa, cifukwa amapangitsa mpingo wa Mulungu kukhala wodetsedwa, ndipo nayenso amakhala pa ngozi yotenga matenda akupha obwela kaamba ka kugonana. (1 Akor. 6:18, 19) Iye amaphela ufulu abale ake acikhristu (1 Ates. 4:3-7) (1) mwa kubweletsa cidetso, citonzo, na kunyozetsa mpingo (Aheb. 12:15, 16), (2) mwa kulepheletsa munthu amene wacita naye dama kukhala na khalidwe loyela, ndipo ngati munthuyo ni mbeta, amamuphela ufulu wokhala woyela poloŵa m’cikwati, (3) mwa kulepheletsa banja lake kukhala na mbili ya khalidwe loyela, komanso (4) mwa kucimwila makolo, mwamuna, kapena cibwenzi ca munthu amene wacita naye dama. Iye sanyalanyaza cabe malamulo a munthu, amene angalole kapena kuletsa dama, koma amanyalanyazanso Mulungu, amene adzamulanga cifukwa ca chimo lake.—1 Ates. 4:8.
“Cipulumutso Canu Cikuyandikila”
14 Kodi cidzacitika n’ciani Gogi wa Magogi akadzayamba kuukila anthu a Mulungu? Mabuku a Mateyo na Maliko amanena kuti: “[Mwana wa munthu] adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhidwa ake kucokela kumphepo zinayi, kucokela kumalekezelo ake a dziko lapansi kukafika kumalekezelo a m’mlengalenga.” (Maliko 13:27; Mat. 24:31) Kusonkhanitsa kumeneku sikutanthauza kusonkhanitsidwa koyamba kwa Akristu odzozedwa iyai, ndipo sikutanthauzanso kuwadinda cidindo comaliza. (Mat. 13:37, 38) Iwo adzadindidwa cidindo comaliza cisautso cacikulu cisanayambe. (Chiv. 7:1-4) Nanga Yesu anali kukamba za kusonkhanitsidwa kuti? Kusonkhanitsidwa kumeneku kudzacitika panthawi imene otsalila a 144,000 adzalandila mphoto yawo yakumwamba. (1 Ates. 4:15-17; Chiv. 14:1) Zimenezi zidzacitika pa nthawi inayake Gogi wa Magogi atayamba kale kuukila anthu a Mulungu. (Ezek. 38:11) Apa m’pamene mawu a Yesu adzakwanilitsika, akuti: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambili ngati dzuŵa mu ufumu wa Atate wawo.”—Mat. 13:43.
15 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti odzozedwa ‘adzakwatulidwa’ kupita kumwamba na thupi la nyama? Anthu ambili a m’Machalichi Acikhristu amakhulupilila kuti, Akhristu adzatengedwa na matupi awo. Ndiponso amaganiza kuti Yesu adzabwela ndipo adzamuona ndi maso awo akulamulila. Koma Baibo imanena momveka bwino kuti “cizindikilo ca Mwana wa munthu” cidzaonekela kumwamba ndipo Yesu adzabwela “pamitambo ya kumwamba.” (Mat. 24:30) Mawu amenewa akusonyeza kuti kubwela kwake kudzakhala kosaonekela ndi maso. Kuonjezela apo, “mnofu ndi magazi sizingaloŵe ufumu wa Mulungu.” Motelo odzozedwa akalibe kutengedwa kupita kumwamba, coyamba ‘adzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethila kwa diso, pa kulila kwa lipenga lomaliza.’ (Ŵelengani 1 Akorinto 15:50-53.) Conco, sitimanena kuti Akhristu odzozedwa ‘adzakwatulidwa’ cifukwa cakuti anthu amalimva molakwika liwuli. Koma adzatengedwa m’kanthawi kocepa.
JULY 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 ATESALONIKA 1-3
“Wosamvela Malamulo Aonekela”
it-1 972-973
Kudzipeleka kwa Mulungu
Pali cinsinsi cina cotsutsana kwambili na “cinsinsi copatulika” ca Yehova. Cinsinsico ni “cinsinsi ca kusamvela malamulo.” Cimeneci cinali cinsinsi kwa Akhristu oona, cifukwa m’nthawi ya mtumwi Paulo, “munthu wosamvela malamulo” anali asanayambe kuonetsa nchito zake, ndipo sanali kudziŵika bwino-bwino. Ngakhale pamene ‘munthuyo’ adzaonetsa nchito zake, zidzakhala zovuta kwa anthu ambili kumudziŵa, cifukwa zocita zake zoipa adzayamba kuzicitila mseli komanso m’dzina la mulungu. Kukamba zoona, iye adzakhala wampatuko, wocoka pa kudzipeleka kwa Mulungu. Paulo anakamba kuti “cinsinsi ca kusamvela malamulo” cinalipo kale m’nthawi yake, cifukwa mumpingo wacikhristu munali anthu osamvela malamulo amene anapangitsa kuti pakhale gulu la mpatuko. Pothela pake, wosamvela malamuloyu adzawonongedwa na Yesu Khristu pamene kukhalapo kwake kudzaonekela. Wampatuko ameneyu, amene Satana amamuseŵenzetsa ‘adzadzikweza pamwamba pa aliyense wochedwa ‘mulungu’ kapena ciliconse copembedzedwa’ (M’cigiriki, seʹba·sma). Conco, munthu wotsutsana na Mulungu ameneyu, amene Satana amamuseŵenzetsa, adzasoceletsa kwambili anthu ndipo adzacititsa kuti onse otsatila zocita zake awonongedwe. “Munthu wosamvela malamulo” ameneyo adzasoceletsadi ambili, cifukwa zocita zake zoipa zidzakhala zobisika pakuti adzadzionetsa monga wodzipeleka kwa Mulungu.—2 Ates. 2:3-12; yelekezelani na Mat. 7:15, 21-23.
it-2 245 ¶7
Bodza
Yehova Mulungu walola kuti anthu amene amakhulupilila bodza “anyengedwe ndipo azikhulupilila bodza,” m’malo mokhulupilila uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu. (2 Ates. 2:9-12) Mfundo imeneyi, ionekela bwino pa zimene zinacitikila Ahabu, Mfumu ya Aisiraeli zaka mahandiledi angapo kumbuyoko. Aneneli onama anatsimikizila Ahabu kuti adzapambana pa nkhondo yolimbana ndi Ramoti-giliyadi. Koma mneneli wa Yehova Mikaya, analosela kuti Ahabu adzaona tsoka. M’masomphenya amene Mikaya anaona, Yehova analola mngelo wina kukhala “mzimu wabodza” m’kamwa mwa aneneli a Ahabu. Kutanthauza kuti mngeloyo anaseŵenzetsa mphamvu zake pa aneneliwo, kuti akambe zabodza zocokela m’maganizo mwawo, komanso zimene Ahabu anali kufuna kumva. Ngakhale kuti Ahabu anali atacenjezedwa, iye anasankha kukhulupilila mabodza a aneneliwo, zimene zinam’tayitsa moyo wake.—1 Maf. 22:1-38; 2 Mbiri 18.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 834 ¶5
Moto
Petulo analemba kuti, “kumwamba kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi, azisungila moto.” Pa lembali ndiponso pa malemba ena, n’zoonekelatu kuti motowo si moto weni-weni ayi, koma umangoimilako ciwonongeko camuyaya. Cigumula ca m’nthawi ya Nowa sicinawononge kumwamba kweni-kweni na dziko lapansi leni-lenili ayi, koma cinawononga anthu osamvela Mulungu. Mofananamo, kubwela kwa Yesu Khristu pamodzi na angelo amphamvu m’moto walawi-lawi, kudzabweletsa ciwonongeko cothelatu kwa anthu osaopa Mulungu ndiponso ku dongosolo lawo loipa la zinthu.—2 Pet. 3:5-7, 10-13; 2 Ates. 1:6-10; yelekezelani na Yes. 66:15, 16, 22, 24.
it-1 1206 ¶4
Kuuzilidwa
“Mawu ouzilidwa”—Oona ndi Abodza. Liwu la Cigiriki lakuti pneuʹma (mzimu) amaliseŵenzetsa mwapadela m’zolemba za atumwi. Mwacitsanzo, pa 2 Atesalonika 2:2, mtumwi Paulo analimbikitsa abale ake a ku Tesalonika kukhala osagwedezeka pa maganizo awo, “kapena kutengeka-tengeka ndi mawu ouzilidwa [mawu ake eni-eni ndi “mzimu”] onena kuti tsiku la Yehova lafika. Musatelo ayi, ngakhale utakhala uthenga wapakamwa, kapena kalata yooneka ngati yacokela kwa ife.” N’zoonekelatu kuti Paulo anaseŵenzetsa liwu lakuti pneuʹma (mzimu) mogwilizana na njila zokambilana, monga “uthenga wapakamwa” kapena “kalata.” Pa cifukwa cimeneci buku la Lange lochedwa Commentary on the Holy Scriptures (peji 126) pa mawu awa inati: “Pokamba zimenezi, Mtumwiyu anali kutanthauza mawu auzimu, kulosela cocitika, mawu a mneneli.” (Yomasulidwa komanso kukonzedwa na P. Schaff, mu 1976) Buku ya Vincent yochedwa Word Studies in the New Testament inati: “Mwa mzimu. Mawu aulosi amene Akhristu ena anali kukamba pa misonkhano, oonetsa monga kuti avumbulutsidwa na Mulungu.” (1957, Vol. IV, peji 63) Conco, ngakhale kuti omasulila ena anamasulila liwu lakuti pneuʹma pa lembali na pa zocitika monga izi kuti “mzimu,” mabaibo ena analimasulila kuti “uthenga wa Mzimu” (AT), “kuyelekezela” (JB), “kuuzilidwa” (D’Ostervald; Segond [French]), “mawu ouzilidwa” (NW).
JULY 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 TIMOTEYO 1-3
“Kalamilani Nchito Yabwino”
Kodi Mumaona Kufunika Kopita Patsogolo Kuuzimu?
3 Ŵelengani 1 Timoteyo 3:1. M’Cigiriki, liwu lakuti ‘kuyesetsa’ kapena kuti kukalamila, limatanthauza kunyenyemphela kuti utenge cinacake pa malo amene sufikilapo. Pamene Paulo anakamba mawu amenewa, anaonetsa kuti kupita patsogolo kuuzimu kumafuna khama. Tiyelekeze kuti m’bale akuganizila mmene angapitile patsogolo mumpingo. Mwina si mtumiki wothandiza, koma adziŵa kuti afunika kukhala na makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa. Coyambilila, akuyesa-yesa kuti ayenelele kukhala mtumiki wothandiza. M’kupita kwa nthawi, akuganizilanso zimene angacite kuti ayenelele kukhala woyang’anila. Iye akucita khama kuti ayenelele kusenza maudindo mumpingo.
km 9/78 4 ¶7
Amene Akupanga “Mbili Yabwino”
7 N’cosavuta kuona cifukwa cake Paulo anakamba kuti amuna otelo amadzipangila “mbili yabwino.” Izi ni zosiyana na zimene anthu ena amaganiza, kukhala na udindo wapamwamba mu chechi. M’malo mwake, atumiki othandiza “otumikila bwino” adzalandila madalitso kwa Yehova na Yesu. Ndipo mpingo wonse umawalemekeza na kuwacilikiza. Ndipo m’pomveka kuti iwo amakhala na “ufulu waukulu wa kulankhula za cikhulupililo, mwa Khristu Yesu.” Cifukwa ca kaimidwe kawo kabwino, timawayamikila kaamba ka utumiki wabwino umene amacita. Iwo ali na cikhulupililo colimba ndipo amalengeza cikhulupililoco mopanda mantha kapena kuopa kuti adzanyozedwa.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 914-915
Mnzele Wobadwila
Kuphunzila na kukambilana nkhani zotelo kunalibe phindu lililonse, maka-maka pa nthawi imene Paulo anali kulembela kalata Timoteyo. Kusunga mabuku a mzele wobadwila kuti munthu azidziŵa makolo ake sikunali kofunika. Zili conco cifukwa Mulungu panthawiyi anali ataleka kuona kuti Myuda ni wosiyana na anthu amitundu ina mu mpingo wacikhristu. (Agal. 3:28) Ndipo mzele wobadwila wa makolo a Khristu mpaka kufika pa Davide unali utalembedwa kale. Kuwonjezela apo, sipanapite nthawi yaitali kucokela pamene Paulo anapeleka malangizo aya, kuti Yerusalemu awonongedwe pamodzi na zolemba za Ayuda. Mulungu sanaziteteze. Pa cifukwa cimeneci, Paulo anada nkhawa kuti mwina Timoteyo pamodzi na mipingo, angatengeke n’kuyamba kutaya nthawi yawo pa kufufuza na kukangana pa nkhani zokhudza mbawo wa makolo awo, zinthu zimene sizikanawathandiza pa cikhulupililo cawo monga Akhristu. Mbili ya mbadwo imene ipezeka m’Baibo ni umboni wokwanila woonetsa kuti Khristu analidi Mesiya. Ndipo mbadwo uwu ni umene uli wofunika kwambili kwa Akhristu. Mibadwo ina yolembedwa m’Baibo ni maumboni ena oonetsa poyela kuti Malemba ali na mbili yodalilika.
cl 12 ¶15
“Taonani, Uyu Ndiye Mulungu Wathu”
15 Dzina lina la udindo limene Yehova yekha ndiye amachulidwa nalo n’lakuti “Mfumu yosatha.” (1 Timoteyo 1:17; Chivumbulutso 15:3) Kodi limatanthauzanji? N’kovuta kuti timvetsetse popeza ndife anthu a maganizo opeleŵela, koma Yehova ndi wosatha kaya tibwelele m’mbuyo ku nthawi zakale ngakhalenso pamene tipita m’tsogolo. Salmo 90:2 limati: “Inde, kuyambila nthawi yosayamba kufikila nthawi yosatha, inu ndinu Mulungu.” Motelo Yehova alibe ciyambi; iye wakhalako nthawi zonse. Amachedwa molondola kuti “Nkhalamba ya kale lomwe;” iye analipo kwa nthawi yosadziŵika munthu wina aliyense kapena cinthu cina ciliconse m’cilengedwe conse cisanakhalepo! (Danieli 7:9, 13, 22) Kodi ndani angakayikile kuti iye ali ndi ufulu wokhala Ambuye Mfumu?
JULY 29–AUGUST 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 TIMOTEYO 4-6
“Kudzipeleka kwa Mulungu Kapena ku Cuma”
w03 6/1 9 ¶1-2
Kuphunzila Cinsinsi Cokwanitsidwa ndi Zimene Tili Nazo
Cinthu cacikulu cimene cinathandiza Paulo kusangalala ndico kukwanitsidwa ndi zimene anali nazo. Komabe, kodi kukwanitsidwa kumatanthauza ciani? Kunena mwacidule, kumatanthauza kukhutila ndi zinthu zofunika kwambili. Pankhani imeneyi, Paulo anauza Timoteyo, yemwe anali kuyenda naye mu utumiki kuti: “Koma cipembedzo pamodzi ndi kudekha [“kudzipeleka kwa Mulungu pamodzi ndi kukwanitsidwa,” NW] cipindulitsa kwakukulu; pakuti sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pocoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanile.”—1 Timoteyo 6:6-8.
Onani kuti Paulo anagwilizanitsa kukwanitsidwa ndi kudzipeleka kwa Mulungu. Anazindikila kuti munthu umapeza cimwemwe ceni-ceni osati cifukwa ca katundu kapena cuma koma cifukwa codzipeleka kwa Mulungu, kutanthauza kuti, kuika patsogolo kutumikila Mulungu. “Zakudya ndi zofunda” zinali zongom’thandizila kupitiliza kudzipeleka kwa Mulungu. Conco, cinsinsi cimene cinam’thandiza Paulo kuona zimene anali nazo kukhala zokwanila cinali kudalila Yehova, zivute zitani.
g 6/07 6 ¶2
Kodi Moyo Wofunitsitsa Kulemela Ungakusokonezeni Motani?
N’zoonadi, sikuti anthu ambili amafa cifukwa cofunitsitsa cuma. Komabe, ambili amatanganidwa kwambili ndi kufuna-funa cuma moti amakhala ndi moyo wosakhutila. Komanso sakhala ndi moyo wabwino ngati mavuto akunchito kapena mavuto a zacuma akuwacititsa kudela nkhawa kwambili, kusoŵa tulo, kumva mutu, kapena kudwala zilonda za m’mimba. Matenda onsewa angapangitse munthu kuti asakhale ndi moyo wautali. Ngakhale munthu ataganiza zosintha moyo umenewu, madzi amakhala atafika kale m’khosi. Mwina mwamuna kapena mkazi wake anasiya kale kumukhulupilila, ana ake anasokonekela kale maganizo, ndipo thanzi lake linawonongeka kale. Mavuto enawa atha kukonzedwanso, koma pangafunike kucita khama kwabasi. Ndithudi, anthu otele “adzibweletsela zopweteka zambili pa thupi pawo.”—1 Timoteyo 6:10.
g 11/08 6 ¶4-6
Mfundo 6 Zokuthandizani Kuti Zinthu Zizikuyendelani Bwino
Monga taonela m’nkhani yoyamba ija, anthu amene amafuna-funa cuma poganiza kuti cingawathandize kukhala ndi moyo wabwino, akulimbikila mtunda wopanda madzi. Iwo amakhumudwa komanso amadzibweletsela zopweteka zambili. Mwacitsanzo, pofuna cuma nthawi zambili anthu amanyalanyaza mabanja awo komanso mabwenzi awo. Ena sagona n’komwe cifukwa ca nchito, nkhawa kapenanso maganizo. Lemba la Mlaliki 5:12 limati: “Tulo ta munthu wogwila nchito n’tabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambili; koma kukhuta kwa wolemela sikum’gonetsa tulo.”
Ndalama zingatibweletsele zopweteka komanso n’zonyenga zedi. Ndipo Yesu Khristu ananena za “cinyengo camphamvu ca cuma.” (Maliko 4:19) M’mawu ena, tinganene kuti cuma cimaoneka ngati cingatipatse cimwemwe koma si mmene zimakhalila. Cimangopangitsa munthu kukhala ndi mtima wofuna cuma cambili. Lemba la Mlaliki 5:10 limati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva.”
Mwacidule, tingati munthu wokonda ndalama amadzipweteka yekha ndipo mapeto ake amakhumudwa ngakhale kucita zaciwembu kumene. (Miyambo 28:20) Kupatsa, kukhululukila ena, makhalidwe abwino, cikondi ndiponso ubwenzi wabwino ndi Mulungu n’zimene zimathandiza munthu kukhala wosangalala komanso ndi moyo wabwino.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Khalani na Cikumbumtima Cabwino kwa Mulungu
17 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khalani ndi cikumbumtima cabwino.” (1 Petulo 3:16) Koma ngati anthu apitiliza kunyalanyaza mfundo za Yehova, m’kupita kwa nthawi cikumbumtima cawo cimaleka kuwacenjeza ciliconse. Paulo anakamba kuti cikumbumtima cimeneco cimakhala monga ‘copseleza na citsulo camoto.’ (1 Timoteyo 4:2) Kodi munapyapo kwambili na moto? Mukapya kwambili, pamatsala cipsela moti sipamveka mukakhudzapo. N’cimodzi-modzi na cikumbumtima. Ngati munthu apitiliza kucita voipa, cikumbumtima cake cimakhala “copseleza.” Potsilizila pake, cimalekelatu kuseŵenza.
it-2 714 ¶1-2
Kuŵelenga Pamaso pa Anthu
Mu Mpingo Wacikhristu. M’zaka 100 C.E zoyambilila, ni anthu ocepa cabe amene anali na mipukutu yambili ya Baibo. Izi zinacititsa kuti kuŵelenga pamaso pa anthu kukhale kofunika. Mtumwi Paulo analimbikitsa mipingo kuti iziŵelenga makalata ake pamaso a anthu pa misonkhano yacikhristu. Ndipo anawalamula kuti azisinthana-sinthana makalata amenewo n’colinga cakuti mipingo inayo iŵelengeko. (Akol. 4:16; 1 Ates. 5:27) Paulo anapeleka malangizo kwa Mkhristu wacicepele Timoteyo, amene anali woyang’anila, kuti adzipeleke “powelenga pamaso pa anthu, powadandaulila, ndi powaphunzitsa.”—1 Tim. 4:13.
Kuŵelenga pamaso pa anthu kuyenela kucitika mosadodoma. (Hab. 2:2) Popeza kuti kuŵelenga pamaso pa anthu ni kuphunzitsa ena, munthu woŵelengayo afunika kumvetsa bwino zimene akuŵelenga. Afunikanso kudziŵa bwino colinga ca amene analemba nkhaniyo. Pa kaŵelengedwe kake, ayenela kusamala n’colinga cakuti asapeleke lingalilo lolakwika kwa omumvetsela. Malinga na Chivumbulutso 1:3, amene amaŵelenga ulosi umenewo mokweza, ndiponso amene amamvetsela mawu ake na kuwatsatila, adzakhala okondwa.