LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr19 August masa. 1-6
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
  • Tumitu
  • AUGUST 5-11
  • AUGUST 12-18
  • AUGUST 19-25
  • AUGUST 26–SEPTEMBER 1
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
mwbr19 August masa. 1-6

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

AUGUST 5-11

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 TIMOTEYO 1-4

“Mulungu Sanatipatse Mzimu Wamantha”

w09 5/15 15 ¶9

Acinyamata, Yesetsani Kuti Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekele

9 Pofuna kuthandiza Timoteyo, Paulo anam’kumbutsa kuti, “Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha, koma wamphamvu, wacikondi, ndi wa kuganiza bwino.” (2 Tim. 1:7) “Kuganiza bwino” kumatanthauza kuganizila zinthu mwakuya komanso mwanzelu. Izi zimaphatikizapo kuona zinthu mmene zilili ndiponso kusakhumudwa msanga ngati zinthuzo sizinacitike mmene ife tinali kufunila. Acinyamata ena amasonyeza kuti ali na mzimu wamantha. Iwo akakumana na mavuto amayesa kuyathaŵa mwina poonela TV nthawi yaitali, kumwa kwambili moŵa na mankhwala osokoneza bongo, kugona kwambili, kukonda kupita m’maphwando kapena kucita zaciwelewele. Baibo imalangiza Akhristu kuti ayenela “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, ndi kukhala a maganizo abwino ndi a cilungamo ndi odzipeleka kwa Mulungu m’dongosolo lino la zinthu.”—Tito 2:12.

w03 3/1 9 ¶7

‘Khalani Amphamvu Ndipo Limbikani Mtima’

7 Paulo polembela Timoteyo anati: “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu . . . Potelo usacite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu.” (2 Timoteyo 1:7, 8; Maliko 8:38) Pamene taŵelenga mawu amenewa, tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimacita manyazi na cikhulupililo canga, kapena ndine wolimba mtima? Kodi kumene nimagwila nchito (kapena kusukulu), nimauzako anthu kuti ndine Mboni ya Yehova, kapena kodi nimabisa? Kodi nimacita manyazi kukhala wosiyana na anthu ena, kapena nimanyadila kuoneka wosiyana ni anthuwo cifukwa ca ubale wanga na Yehova?’ Ngati munthu akucita mantha kulalikila uthenga wabwino kapena kucita mantha kukhala na cikhulupililo cimene ena akuona ngati n’cotsalila, ayenela kukumbukila langizo la Yehova kwa Yoswa lakuti: “Khala wamphamvu, nulimbike mtima.” Osaiŵala kuti cofunika kwambili si mmene anthu amene timagwila nawo nchito kapena anzathu a kusukulu amatiganizila, koma mmene Yehova na Yesu Khristu amaonela zinthu.—Agalatiya 1:10.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w17.07 10 ¶13

Kufunafuna Cuma Ceni-ceni

13 Timoteyo anali na cikhulupililo colimba. Paulo anachula Timoteyo kuti ni “msilikali wabwino wa Khristu Yesu.” Pambuyo pake anamuuza kuti: “Msilikali amene ali pa nkhondo sacita nawo zamalonda zimene anthu wamba amacita, pofuna kukondweletsa amene anamulemba usilikali.” (2 Tim. 2:3, 4) Lelolinonso, otsatila a Yesu, kuphatikizapo khamu la atumiki a nthawi zonse oposa 1,000,000, amamvela malangizo a Paulo amenewa malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wawo. Iwo satengeka na zokamba za otsatsa malonda kapena zokopa zina za dzikoli. Ndipo amakumbukila mfundo yakuti: “Wobweleka amakhala kapolo wa wobweleketsayo.” (Miy. 22:7) Satana amafuna kuti tiziwononga nthawi yathu na mphamvu zathu zonse pocilikiza dongosolo la zamalonda la dzikoli. Zosankha zina zimene tingapange zingatipangitse kukhala akapolo ku nkhongole kwa zaka zambili. Mwacitsanzo, ena amatenga loni ya ndalama zambili kuti agulile nyumba, kulipilila ana a sukulu, kugulila galimoto yodula, kapena kuti acitile cikwati capamwamba. Tingaonetse kuti ndise anzelu mwa kukhala na umoyo wosalila zambili, kupewa nkhongole zazikulu, kapena kugula zinthu zodula. Tikatelo, tidzatumikila Mulungu momasuka, m’malo mokhala akapolo kwa anthu amalonda a dzikoli.—1 Tim. 6:10.

w14 7/15 14 ¶10

Anthu a Yehova “Aleke Kucita Zosalungama”

10 Masiku ano, anthu a Yehova sakumana na ampatuko mumpingo. Komabe, tisazengeleze kukana ziphunzitso zilizonse zosagwilizana na malemba. Ni kupanda nzelu kukangana na ampatuko kaya pamaso m’pamaso, pa mawebusaiti awo, kapena mwanjila ina iliyonse. Ngakhale pamene colinga cili kuthandiza winawake, kukambitsilana kotelo n’kosafunika malinga n’zimene takambilana. M’malo mwake, monga anthu a Yehova tiyenela kuwapewelatu ampatuko.

AUGUST 12-18

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | TITO 1–FILIMONI

“Kuika Akulu”

w14 11/15 28-29

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Ngakhale kuti Malemba safotokoza mwatsatane-tsatane mmene anali kuikila abale pa udindo, tingathe kuona mmene zimenezi zinali kucitikila. Timauzidwa kuti pamene Paulo na Baranaba anamaliza ulendo wawo woyamba wa umishonale, “anawaikila akulu mumpingo uliwonse, ndipo atapemphela ndi kusala kudya, anawapeleka kwa Yehova yemwe anamukhulupilila.” (Mac 14:23) M’kupita kwa zaka, Paulo analembela Tito amene anali kuyenda naye kuti: “Ndinakusiya ku Kerete kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike akulu mumzinda uliwonse, malinga ndi malangizo amene ndinakupatsa.” (Tito 1:5) Mofananamo, Timoteyo, amene anali kuyenda na mtumwi Paulo pa maulendo aatali, ayenela kuti anapatsidwa udindo umodzimodziwo. (1 Tim. 5:22) Conco, n’zoonekelatu kuti oyang’anila oyendela ni amene anali kuika abale pa maudindo, osati atumwi kapena akulu ku Yerusalemu.

Potengela citsanzo ca m’Baibo cimeneci, Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova lapanga masinthidwe okhudza kuika akulu na atumiki othandiza pa udindo. Kuyambila pa September 1, 2014, kuika abale pa udindo kumacitika motele: Woyang’anila dela aliyense amapenda mosamalitsa ziyamikilo za abale a m’dela lake. Pamene iye acezela mpingo amayesetsa kuwadziŵa bwino abale amene asankhidwa kuti aikidwe pa udindo, na kuseŵenza nawo mu ulaliki ngati n’kotheka. Pambuyo pokambilana ziyamikilo za abalewo na bungwe la akulu, woyang’anila dela ndiye amaika akulu na atumiki othandiza mu mpingo. Makonzedwe amenewa ni ofanana ndi a m’nthawi ya atumwi.

Nanga ndani amene amagwila nchito yaikulu imeneyi? Monga mwa nthawi zonse, “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” ndiye ali na udindo waukulu wopeleka cakudya kwa anchito apakhomo. (Mat. 24:45-47) Motsogoleledwa na mzimu woyela, amafufuza Malemba kuti apeleke malangizo oyenela a mmene gulu lifunika kuyendela pogwilitsila nchito mfundo za m’Baibo. Ndiponso, kapolo wokhulupilika amaika oyang’anila dela na abale a m’Komiti ya Nthambi. Ndipo ofesi ya nthambi imatithandiza kugwilitsila nchito malangizo ocokela kwa kapolo wokhulupilika. Bungwe la akulu lililonse lili na udindo wopenda mosamalitsa ziyenelezo za m’Malemba za abale amene asankhidwa kuti aikidwe pa udindo mu mpingo. Nayenso woyang’anila dela ali na udindo waukulu wopenda mosamalitsa komanso mwapemphelo ziyamikilo zocokela kwa akulu, na kuika pa udindo abale amene akwanilitsa ziyenelezo.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w89 5/15 31 ¶5

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Iye motsimikizilika sanali kuvomeleza malankhulidwe odzala, komanso ufuko kapena utundu motsutsana na Akerete. Tingakhale otsimikiza za cimeneco, popeza kuti Paulo anadziŵa kuti ku Kerete kunali Akhristu abwino omwe Mulungu anawavomeleza na kuwadzoza na mzimu Wake woyela. (Machitidwe 2:5, 11, 33) Panali Akhristu odzipeleka okwanila kupanga mipingo “m’midzi yonse.” Pamene kuli kwakuti Akhristu otelowo sanali anthu angwilo, tingakhale otsimikiza kuti sanali onyenga ndi aumbombo aulesi; kupanda apo iwo sakanapitiliza kukhala na civomelezo ca Yehova. (Afilipi 3:18, 19; Chivumbulutso 21:8) Ndipo monga mmene ife lelolino tikupezela m’mitundu yonse, mwacionekele analipo mu Kerete anthu a mitima yoona omwe anaipidwa makhalidwe oipa owazungulila, ndipo anali okonzekela kuvomeleza uthenga Wacikhristu.—Ezekieli 9:4; yelekezani na Machitidwe 13:48.

w08 10/15 31 ¶5

Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Tito, Filimoni na Aheberi

15, 16—Kodi n’cifukwa ciani Paulo sanapemphe Filimoni kuti amasule Onesimo mu ukapolo? Paulo anali kufuna kungogwila nchito yake ‘yolalikila za ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu’ basi. Motelo, sanafune kuloŵelela m’nkhani zina, monga zokhudza ukapolo.—Mac. 28:31.

AUGUST 19-25

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 1-3

“Kondani Cilungamo, Danani Nako Kusamvela Malamulo”

w14 2/15 5 ¶8

Tamandani Khristu, Mfumu Yaulemelelo!

8 Yehova anaika Mwana wake monga Mfumu Mesiya kumwamba mu 1914. ‘Ndodo yake yacifumu ndiyo ndodo yacilungamo.’ Conco, ulamulilo wake udzakhala wosakondela ndiponso wacilungamo. Iye ni woyenela kukhala mfumu cifukwa cakuti Mulungu ‘ndiye mpando wake wacifumu.’ Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova ni amene anamuika kukhala Mfumu. Kuwonjezela apo, ulamulilo wa Yesu udzakhalapo “mpaka kalekale, ndithu mpakila muyaya.” Timanyadila kutumikila Yehova motsogoleledwa na Mfumu yamphamvu imene Mulungu anaika.

w14 2/15 4-5 ¶7

Tamandani Khristu, Mfumu Yaulemelelo!

7 Ŵelengani Salimo 45:6, 7. Cifukwa cakuti Yesu amakonda ngako cilungamo, ndipo amadana na ciliconse cotonzetsa dzina la Atate wake, Yehova anam’dzoza kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. Mulungu anadzoza Yesu na “mafuta acikondwelelo cacikulu” kuposa “ca mafumu ena,” kutanthauza mafumu aciyuda omwe anali mu mzele wa Davide. Kodi Mulungu anadzoza Yesu kuposa mafumu ena m’njila zotani? Coyamba, Yesu anadzozedwa mwacindunji na Yehova. Caciŵili, Yehova anam’dzoza monga Mfumu ndiponso monga Mkulu wa Ansembe. (Sal. 2:2; Aheb. 5:5, 6) Cacitatu, Yesu anadzozedwa na mzimu woyela osati na mafuta, ndipo ufumu wake si wa pa dziko lapansi koma ni wakumwamba.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-1 1185 ¶1

Cifanizilo

Kodi Yesu wakhala akuonetsa bwanji cifanizilo ca Atate ŵake ndendende?

Yesu, Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu amene pambuyo pake anadzakhala munthu pa dziko, ali cifanizilo ca Atate ŵake. (2 Akor. 4:4) Popeza kuti n’zoonekelatu kuti Mulungu anali kukamba na Mwanayo pamene anati, “Tiyeni tipange munthu m’cifanizilo cathu,” ndiye kuti kufanana kumene kulipo pakati pa Mwana na Atate ŵake, amene ni Mlengi, kunayamba pamene Mwanayo analengedwa. (Gen. 1:26; Yoh. 1:1-3; Akol. 1:15, 16) Pamene anali pa dziko lapansi monga munthu wangwilo, iye anaonetsa bwino makhalidwe na umunthu wa Atate ŵake kulingana na zimene munthu angakwanitse, cakuti anakamba mawu akuti “amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9; 5:17, 19, 30, 36; 8:28, 38, 42) Komabe, kufanana kumeneku kunaonekela kwambili pamene Atate ŵake, Yehova Mulungu, anaukitsa Yesuyo kuti akhale na moyo wauzimu na kumupatsa “ulamulilo wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” (1 Pet. 3:18; Mat. 28:18) Popeza kuti Mulungu anakweza Yesu n’kumuika “pamalo apamwamba,” Mwana wa Mulungu lomba anaonetsa ulemelelo wa Atate ŵake pa mlingo wokulilapo, kuposa pamene asanacoke kumwamba kubwela pano pa dziko lapansi. (Afil. 2:9; Aheb. 2:9) Pali pano, iye ni “cithunzi ceni-ceni ca Mulungu weni-weniyo.”—Aheb. 1:2-4.

it-1 1063 ¶7

Kumwamba

Mawu a pa Salimo 102:25, 26 amakamba za Yehova Mulungu, koma mtumwi Paulo anagwila mawuwa pokamba za Yesu Khristu. Zili conco cifukwa Mwana wobadwa yekha wa Mulungu ameneyu, ndiye anali kutumikila pamene Mulungu anali kupanga cilengedwe. Paulo anasiyanitsa pakati pa kukhalapo kwamuyaya kwa Mwanayo na cilengedwe cimene Mulungu pocipanga, ‘akanangocipinda-pinda ngati mkanjo’ n’kucileka.—Aheb. 1:1, 2, 8, 10-12; yelekezelani na 1 Pet. 2:3.

AUGUST 26–SEPTEMBER 1

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 4-6

“Limbikilani Kuti Mukaloŵe mu Mpumulo wa Mulungu”

w11 7/15 24-25 ¶3-5

Kodi Mpumulo wa Mulungu N’ciani?

3 Pali mfundo ziŵili zotithandiza kudziŵa kuti tsiku la 7 linali kupitililabe m’nthawi ya Yesu nkomanso ya Akhristu oyambilila. Coyamba, taganizilani zimene Yesu anauza adani ake amene anamutsutsa cifukwa cocilitsa munthu pa Sabata. Adaniwo anaona kuti iye analakwa pogwila nchito pa Sabata. Yesu anawauza kuti: “Atate wanga akugwilabe nchito mpaka pano, inenso ndikugwilabe nchito.” (Yoh. 5:16, 17) Kodi pamenepa anatanthauza ciani? Mawu a Yesu akuti: “Atate wanga akugwilabe nchito” anayankha mlandu wakuti anagwila nchito pa Sabata. Ponena zimenezi, Yesu anatanthauza kuti: ‘Ine ndi Atate wanga tikugwila nchito yofanana. Popeza Atate wanga akhala akugwila nchito pa Sabata lawo la zaka masauzande ambili, inenso ndikhoza kugwila nchito pa Sabata.’ Conco mawu a Yesu akusonyeza kuti tsiku la 7, limene Mulungu anali kupuma pa nchito yake yolenga zinthu padziko, linali kupitililabe m’nthawi ya Yesu. Koma Mulungu anali kugwilabe nchito kuti akwanilitse colinga cake cokhudza anthu ndiponso dziko lapansi.

4 Mtumwi Paulo ananena mfundo yaciŵili. Asanagwile mawu a pa Genesis 2:2 onena za mpumulo wa Mulungu, iye analemba kuti: “Ife amene tasonyeza cikhulupililo tikuloŵadi mu mpumulowo.” (Aheb. 4:3, 4, 6, 9) Izi zikusonyeza kuti tsiku la 7 linali kupitililabe m’nthawi ya Paulo. Koma kodi tsiku limeneli likupitililabe?

5 Kuti tiyankhe funsoli tiyenela kukumbukila colinga ca tsiku la 7. Lemba la Genesis 2:3 limafotokoza colingaci kuti: “Mulungu anadalitsa tsiku la 7. Analipatula kuti likhale lopatulika.” Yehova ‘anapatula’ tsikuli pofuna kuti akwanilitse colinga cake. Colinga cimeneci n’cakuti padziko lapansi pakhale anthu omvela amene angalisamalile komanso kusamalila zamoyo zonse. (Gen. 1:28) Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu, yemwe ndi “Mbuye wa sabata,” “akugwilabe nchito mpaka pano” kuti akwanilitse colinga cimeneci. (Mat. 12:8) Tsiku la mpumulo wa Mulungu lipitililabe mpaka pamene colinga cimeneci cidzakwanilitsidwa pa mapeto pa ulamulilo wa Khristu wa zaka 1,000.

w11 7/15 25 ¶6

Kodi Mpumulo wa Mulungu N’ciani?

6 Mulungu anafotokoza colinga cake momveka bwino kwa Adamu na Hava, koma iwo anacita zosemphana na colingaco. Adamu na Hava anali anthu oyambilila kusamvela Mulungu. Kucokela nthawi imeneyo, anthu mamiliyoni ambili akhala osamvela. Ngakhale Aisiraeli, omwe anali anthu osankhika a Mulungu, anali na cizolowezi cosamvela Mulungu. N’cifukwa cake Paulo anacenjeza Akhristu m’nthawi yake kuti ngakhale iwowo akhoza kuyamba cizolowezi cosamvela ca Aisiraeli akale. Iye analemba kuti: “Cotelo, tiyeni ticite ciliconse cotheka kuti tiloŵe mu mpumulo umenewo, kuwopela kuti wina angagwe ndi kutengela citsanzo ca kusamvela ca makolo athuwo.” (Aheb. 4:11) Paulo anagwilizanitsa kusamvela na kulephela kuloŵa mu mpumulo wa Mulungu. Kodi ife tikuphunzilapo ciani pamenepa? Kodi zitanthauza kuti tikacita zinthu zinazake zosemphana na colinga ca Mulungu, tikhoza kulephela kuloŵa nawo mu mpumulo wa Mulungu? Tikambilana yankho la funso limeneli m’nkhani ino cifukwa ni lofunika kwambili kwa ife. Koma pali pano, tiyeni tikambilane za citsanzo coipa ca Aisiraeli kuti tione zinthu zina zokhudza kuloŵa mu mpumulo wa Mulungu.

w11 7/15 28 ¶16-17

Kodi Mpumulo wa Mulungu N’ciani?

16 Masiku ano, ife sitikhulupilila zoti Akhristu ayenela kutsatila Cilamulo ca Mose kuti akapulumutsidwe. Mawu a Paulo kwa Aefeso ni omveka bwino. Iye anati: “Mwa kukoma mtima kwakukulu kumeneku, ndithudi mwapulumutsidwa kudzela m’cikhulupililo, osati mwa inu nokha, koma monga mphatso ya Mulungu. Si cifukwanso ca nchito ayi, kuti munthu asakhale ndi cifukwa codzitamandila.” (Aef. 2:8, 9) Ndiyeno kodi Akhristu angaloŵe bwanji mu mpumulo wa Mulungu masiku ano? Yehova anapatula tsiku la 7 monga tsiku lake lopumula kuti akwanilitse colinga cake cokhudza dziko lapansi. Kudzela m’gulu lake, Yehova amatiuza za colinga cake komanso zimene akufuna kuti tizicita. Tikhoza kuloŵa mu mpumulo wa Yehova ngati timamumvela ndiponso kugwila nchito mogwilizana na gulu lake.

17 Koma ngati sitimvela malangizo ocokela m’Baibo amene kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amatipatsa n’kumafuna kucita zinthu zathu-zathu, ndiye kuti tikusemphana na colinga ca Mulungu. Izi zikhoza kusokoneza ubale wathu na Yehova. M’nkhani yotsatila tidzakambilana zinthu zina zimene anthu a Mulungu angakumane nazo zomwe zingatipatse mwayi wosonyeza kuti ndife anthu omvela. Zimene timacita tikakumana na zinthu zimenezi zimasonyeza ngati tinaloŵa mu mpumulo wa Mulungu kapena ayi.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w16.09 13

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Kodi “mawu a Mulungu” amene lemba la Aheberi 4:12 limakamba kuti ni “amoyo ndi amphamvu” n’ciani?

▪ Mavesi ozungulila lemba limeneli, aonetsa kuti Paulo anali kukamba za uthenga kapena kuti colinga ca Mulungu cochulidwa m’Baibo.

Nthawi zambili, lemba la Aheberi 4:12 limalembedwa m’zofalitsa zathu pofuna kuonetsa kuti Baibo ili na mphamvu yosintha anthu. M’pake kuti lembali limagwilitsidwa nchito motele. Ngakhale zili conco, tiyeni tipende lembali mozamilapo. Paulo anali kulimbikitsa Akhristu aciheberi kucita zinthu mogwilizana ni colinga ca Mulungu. Colinga cimeneci cinalembedwa m’malemba oyela. Pofuna kufotokoza colingaco, Paulo anagwilitsila nchito citsanzo ca Aisiraeli amene anapulumutsidwa kwa Aiguputo. Iwo anali kuyembekezela dziko lolonjezedwa “loyenda mkaka ndi uci.” M’dzikolo akanapeza mpumulo weni-weni.—Eks. 3:8; Deut. 12:9, 10.

Ici cinali colinga ca Mulungu. Koma m’kupita kwa nthawi, Aisiraeli anaumitsa mitima yawo ndi kutaya cikhulupililo cawo. Conco, ambili analephela kuloŵa mu mpumulo umenewo. (Num. 14:30; Yos. 14:6-10) Komabe, Paulo anakamba kuti “lonjezo loloŵa mu mpumulo [wa Mulungu] lidakalipo.” (Aheb. 3:16-19; 4:1) Mwacionekele, “lonjezo” limeneli ni mbali ya colinga ca Mulungu. Monga mmene Akhristu aciheberi anacitila, ifenso tingaŵelenge na kucita zinthu mogwilizana na colinga ca Mulungu cimeneci. Pofuna kuonetsa kuti lonjezo limeneli ndi la m’Malemba, Paulo anagwila mawu ena a pa Genesis 2:2 na Salimo 95:11.

N’zolimbikitsa kudziŵa kuti “lonjezo loloŵa mu mpumulo [wa Mulungu] lidakalipo.” Ndipo tikhulupilila kuti n’zotheka kuloŵa mu mpumulo wa Mulungu umenewu. Tayamba kale kucita zoyenela kuti tiloŵemo. Koma sitinacite zimenezo mwa kumamatila Cilamulo ca Mose, kapena mwa kucita zinthu zina kuti Yehova atiyanje iyai. M’malomwake, timaloŵa mu mpumulowo mwa kupitiliza kucita zinthu mwa cikhulupililo mogwilizana ni cifunilo ca Mulungu. Ndipo monga mmene takambila poyamba, anthu masauzande ambili padziko lonse akuphunzila Baibulo na colinga ca Mulungu. Zimenezi zathandiza ambili kusintha umoyo wawo, kukhala na cikhulupililo colimba, na kubatizika. Kusintha kumene acita ni umboni wakuti “mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” Uthenga wa Mulungu wochulidwa m’Baibo wakhudza kwambili umoyo wathu, ndipo udzapitilizabe kukhala wamphamvu pa ife.

it-1 1139 ¶2

Ciyembekezo

Ciyembekezo ca moyo wosatha komanso moyo wosakhoza kuwonongeka kwa aja ‘amene ali m’gulu la oitanidwa kumwamba’ (Aheb. 3:1), n’cozikika molimba, ndipo ni cinthu cimene sitingacikayikile. Ciyembekezoci cimacilikizidwa na zinthu ziŵili zoonetsa kuti n’zosatheka Mulungu kunama. Zinthuzo ni lonjezo na lumbilo lake, ndipo ciyembekezo cili mwa Khristu, amene pali pano ali na moyo wosafa kumwamba. Conco ciyembekezo cimeneci cimakambiwa kuti cili ngati “nangula wa miyoyo yathu ndipo n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika. Ciyembekezo cimeneci cimatiloŵetsa mkati, kuseli kwa nsalu yocinga, [monga mmene mkulu wa ansembe anali kuloŵela ku malo Opatulikitsa pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo], kumene Yesu, yemwe ni kalambulabwalo anakaloŵa cifukwa ca ife. Iyeyu wakhala mkulu wa ansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”—Aheb. 6:17-20.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani