CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 1–3
“Ndikudziŵa Nchito Zako”
1:20; 2:1, 2
“Nyenyezi 7”: Akulu odzozedwa komanso akulu onse
“M’dzanja [la Yesu] lamanja”: Yesu ndiye ali na mphamvu, ulamulilo na citsogozo pa nyenyezi zimenezo. Ngati wina m’bungwe la akulu afunika kuwongoleledwa, Yesu amaonetsetsa kuti zimenezi zacitika pa nthawi yake komanso m’njila yoyenela
“Zoikapo Nyale 7 Zagolide”: Mipingo yacikhristu. Monga mmene coikapo nyale ca m’cihema cinali kuunikila, mipingo yacikhritsu imaunikila coonadi cocokela kwa Mulungu. (Mat. 5:14) Yesu ni “woyenda pakati” pa zoikapo nyale m’njila yakuti, ndiye amayang’anila zocitika za m’mipingo yonse