LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr20 January
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
  • Tumitu
  • JANUARY 6-​12
  • JANUARY 13-​19
  • JANUARY 20-​26
  • JANUARY 27–FEBRUARY 2
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
mwbr20 January

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

JANUARY 6-​12

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 1-2

“Yehova Analenga Zamoyo pa Dziko Lapansi”

it-1 527-​528

Cilengedwe

Pa Tsiku Loyamba pamene Mulungu anati “Pakhale kuwala,” mwacionekele kuwalako kunadutsa m’mitambo, ngakhale kuti pa nthawiyo zounikazo sizinali kuonekela pa dziko lapansi. Zioneka kuti kuwalako kunali kubwela pang’ono pang’ono, monga mmene womasulila wina dzina lake J. W. Watts anakambila. Anati: “Pang’ono n’pang’ono kuwala kunayamba kuonekela.”(Gen. 1:​3, A Distinctive Translation of Genesis) Mulungu analekanitsa pakati pa kuwala na mdima, ndipo anacha kuwalako Masana, mdimawo anaucha Usiku. Izi zionetsa kuti dziko lapansi linali kuzungulila ilo lokha kwinaku likuyenda mozungulila dzuŵa, kuti pamene kumbali ina kuli mdima, kwina kuzikhala usana.​—Gen. 1:​3, 4.

Pa Tsiku Laciŵili, Mulungu anapanga mlengalenga mwa kuika colekanitsa “pakati pa madzi ndi madzi.” Madzi ena anakhala pa dziko lapansi, koma oculuka anaikidwa pamwamba pa dziko lapansi, ndipo pakati pamadzi amenewo panakhala mlengalenga. Mulungu anacha mlengalengawo, Kumwamba. Koma uku n’kumwamba kwa padziko lapansi, cifukwa madzi amene anaikidwa mu mlengalengawo sanamize nyenyezi kapena zinthu zina za kuthambo.​—Gen. 1:​6-8.

Pa Tsiku Lacitatu, mwa mphamvu zake zozizwitsa, Mulungu anasonkhanitsa madzi, ndipo mtunda unaonekela. Anacha mtundawo Dziko Lapansi. Panali pa tsiku limeneli pamene Mulungu anaika mphamvu ya moyo m’zinthu zopanda moyo cakuti udzu, zomela zina, na mitengo yobala zipatso zinakhalako. Zinthu zimenezi sizinacitike mwangozi kapena mocita kusandulika. Ndipo magulu atatu a zinthu zimenezi anayamba kubala monga mwa “mtundu wake.”​—Gen. 1:​9-​13.

it-1 528 ¶5-8

Cilengedwe

Dziŵaninso kuti mu Ciheberi, pa Genesis 1:​16, sanaseŵenzetse liwu lakuti ba·raʼʹ, lotanthauza “kulenga.” M’malo mwake anaseŵenzetsa liwu lakuti ʽa·sahʹ, lotanthauza “kupanga.” Popeza kuti dzuŵa, mwezi, na nyenyezi zikuphatikizidwa kukhala “kumwamba” kochulidwa pa Genesis 1:​1, ndiye kuti zinali zitalengedwa kale Tsiku Lacinayi lisanafike. Ndiye zimene Mulungu anapitiliza kucita pa tsiku lacinayi, ni “kupanga” zinthu zakumwamba zimenezi, mwa kuziika pa malo ake oyenelela ku thambo pakati pa dziko lapansi na kumwamba. Pamene Baibo ikamba kuti, Mulungu “anaziika kuthambo kuti ziunikile dziko lapansi,” zionetsa kuti panthawiyi zinayamba kuonekela pa dziko lapansi, monga kuti zili mu mlengalenga. Cinanso, zounikila zimenezi zinali ‘kudzakhala zizindikilo, komanso kudzasonyeza nyengo, masiku, na zaka,’ ndipo izi zinali kudzathandiza anthu m’njila zosiyana-siyana.​—Gen. 1:​14.

Tsiku Lacisanu linali lolenga zamoyo zina pa dziko lapansi. Mulungu sanalenge camoyo cimodzi cabe kuti mwa kusandulika pakhale zamoyo za mitundu inanso ayi. Mwa mphamvu zake, analenga “zamoyo zambili-mbili.” Baibo imati: “Mulungu analenga zilombo zikulu-zikulu za m’nyanja ndi camoyo ciliconse cokhala mmenemo. Nyanja inatulutsa zimenezi zambili-mbili monga mwa mitundu yake.” Mulungu anakondwela na zimene analenga, ndipo anazidalitsa, pokamba kuti “muculuke.” Izi zinali zotheka cifukwa mitundu yambili ya zamoyo zimenezi, Mulungu anazilenga kuti zizikwanitsa kubelekana “monga mwa mtundu wake.”​—Gen. 1:​20-​23.

Pa Tsiku la 6 “Mulungu anapanga nyama zakuchile monga mwa mitundu yake. Anapanganso nyama zoweta monga mwa mitundu yake, komanso nyama iliyonse yokwawa panthaka monga mwa mtundu wake.” Zinthu zimenezi zinali zabwino, mofanana na zimene analenga poyamba.​—Gen. 1:​24, 25.

Cakumapeto kwa tsiku la kulenga la namba 6, Mulungu analenga camoyo cina capadela kwambili, capamwamba kuposa nyama koma cotsika pali angelo. Colengedwaco cinali munthu. Iye analengedwa m’cifanizilo ca Mulungu. Ngakhale kuti Genesis 1:​27 imakambako mwacidule za anthu kuti “[Mulungu] anawalenga mwamuna ndi mkazi,” nkhani yolingana na imeneyi yopezeka pa Genesis 2:​7-9 ionetsa kuti Yehova Mulungu anaumba munthu kucokela kufumbi lapansi, ndipo anauzila mpweya wa moyo m’phuno mwake, ndipo munthuyo anakhala na moyo. Mulungu anaika munthuyo m’paladaiso mmene munali zakudya. Apa Yehova anaseŵenzetsa zinthu za padziko lapansi pa nchito yake yolenga. Atalenga mwamuna, anapanganso mkazi mwakugwilitsila nchito nthithi ya Adamu. (Gen. 2:​18-​25) Mkazi atalengedwa, munthu anakhala wokwanila monga mwa “mtundu wake.”​—Gen. 5:​1, 2.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w15 6/1 5

Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?

Kutalika kwa nthawi imene dziko lapansi komanso cilengedwe conse cakhalako

Asayansi amakamba kuti dziko lapansi lakhalako zaka pafupi-fupi 4 biliyoni ndiponso cilengedwe conse cakhalapo zaka 13 kapena 14 biliyoni. Baibo siikamba zakuti cilengedwe conse cinakhalako liti. Komanso Baibo siionetsa paliponse kuti dziko lapansili langokhalapo zaka masauzande ocepa cabe. Vesi yoyambilila ya m’Baibo inangokamba kuti: “Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:⁠1) Mawu a m’Baibo ongonena kuti “pa ciyambi” popanda kuchula nthawi yeni-yeni, amalola asayansi kugwilitsila nchito maluso awo othandiza, kuyelekezela nthawiyi.

it-2 52

Yesu Khristu

Sanali Mlengi. Kutengako mbali pa nchito ya kulenga imene Atate ake anali kugwila, sikunapangitse Mwanayu nayenso kukhala Mlengi. Mphamvu za kulenga zinali kucokela kwa Mulungu mwa mzimu wake woyela, kapena kuti mphamvu yake yogwila nchito. (Gen. 1:2; Sal. 33:6) Ndipo popeza kuti Yehova ndiye Kasupe wa moyo uliwonse, cilengedwe conse, zinthu zooneka komanso zosaoneka, zonse zilipo cifukwa ca iye. (Sal. 36:⁠9) Mwanayo sanali Mlengi ayi, koma Yehova Mlengi anamuseŵenzetsa monga wotumikila, kapena monga cida cake polenga zinthu. Yesu anakamba kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse, mmenenso Malemba onse amakambila.​—Mat. 19:​4-6; onani CILENGEDWE.

JANUARY 13-​19

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 3-5

“Zotulukapo Zoipa za Bodza Loyamba”

w17.02 5 ¶9

Colinga ca Yehova Cidzakwanilitsika

Satana Mdyelekezi anaseŵenzetsa njoka kunyenga Hava kuti asamvele Atate wake, Yehova. (Ŵelengani Genesis 3:​1-5; Chiv. 12:⁠9) Satana anayambitsa nkhani yaikulu mwa kukamba kuti ana aumunthu a Mulungu analetsedwa kudya “zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu.” Zinali ngati akukamba kuti: ‘Kodi n’zoona kuti simungacite zimene mufuna?’ Cotsatila, anakamba bodza lamkunkhuniza kuti: “Kufa simudzafa ayi.” Ndiyeno, anapangitsa Hava kukhulupilila kuti safunika kumvela Mulungu mwa pokamba kuti: ‘Mulungu akudziŵa kuti tsiku limene mudzadya cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu.’ Mwamacenjela, Satana anapeleka cithunzi cakuti Yehova sanali kufuna kuti iwo adyeko cipatsoco kuopela kuti angatseguke mutu. Kuwonjezela apo, Satana anapeleka lonjezo labodza lakuti: “Mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.”

w00 11/15 25-​26

Titengelepo Phunzilo ku Banja Loyamba la Anthu

Kodi chimo la Hava linali losapeweka? Ndithudi ayi! Ganizilani izi: Tinene kuti inu ndinu Hava. Zimene njoka inanena zinasinthilatu zimene Mulungu na Adamu anakamba. Kodi imwe mungamvele bwanji ngati munthu amene simum’dziŵa akunamizila munthu amene mumam’konda na kum’khulupilila kuti ni wabodza? Hava anafunikila kutsutsa zimenezo, poonetsa kuipidwa na kukwiya nazo, ngakhalenso kukana kumvetsela. Akanaganiza kuti njokayo n’ndani kuti izikayikila cilungamo ca mawu a Mulungu na mawu a mwamuna wake? Polemekeza mfundo ya umutu, Hava akanayamba wafunsila kwa mwamuna wake asanacite ciliconse. N’zimene ifenso tiyenela kucita ngati tauzidwa zinthu zosiyana na malangizo ocokela kwa Mulungu. Hava anakhulupilila mawu a Womuyesayo pofuna kudzisankhila yekha cabwino na coipa. Ndipo cifukwa cosumika maganizo pa mfundoyo, inaoneka yabwino m’maganizo mwake. M’pamene Hava analakwila, kusangalatsidwa na colakwa, m’malo mocicotsa m’maganizo mwake, kapena kukakambilana nkhaniyo na mutu wa banja lake.​—1 Akorinto 11:3; Yakobo 1:​14, 15.

Adamu Amvela Mawu a Mkazi Wake

Posakhalitsa, Hava ananyengelela Adamu kuti nayenso acimwe. Kodi n’cifukwa ciani Adamu anangogonja mwakacete-cete? (Genesis 3:​6, 17) Mwacionekele, Adamu anali atagwila njakata. Amvelele Mlengi wake, amene anam’patsa zinthu zonse, kuphatikizapo mkazi wake wokondedwa, Hava kapena amvelele mkazi wake? Afunsile kwa Mulungu kuti adziŵe zofunika kucita? Kapena angogwela kwa mkazi wake cicitike-cicitike? Adamu anadziŵa bwino kuti zimene Hava anali kuyembekezela kupeza pakudya cipatso coletsedwa, zinali zogwilitsa mwala. Mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba kuti: “Adamu sananyengedwe, koma mkaziyo ndiye amene ananyengedwa ndipo anacimwa.” (1 Timoteyo 2:​14) Conco Adamu anacita kusankha dala kuti asamvele Yehova. Cinakula mwa iye ni kuwopa kulekana na mkazi wake, m’malo mokhulupilila kuti Mulungu anali na mphamvu yokonza zinthu.

w12 9/1 4 ¶2

Kodi Mulungu Amaona Kuti Akazi Ni Otsika?

Kodi Mulungu anatembelela akazi?

Ayi. Koma “njoka yakale ija, iye wochedwa Mdyelekezi,” ni imene Mulungu ‘anaitembelela.’ (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:​14) Pamene Mulungu anakamba kuti Adamu ‘adzalamulila’ mkazi wake, sanatanthauze kuti mwamuna ayenela kuona mkazi wake ngati kapolo. (Genesis 3:​16) Mulungu anangokambilatu za mavuto amene Adamu na Hava adzakumana nawo cifukwa ca ucimo.

w04 1/1 29 ¶2

Mfundo Zazikulu za m’Buku la Genesis​—Cigawo Coyamba

3:​17​—Kodi nthaka inatembeleledwa motani, ndipo kwa nthaŵi yaitali bwanji? Kutembeleledwa kwa nthaka kunatanthauza kuti kulima nthaka tsopano kudzakhala kovuta kwambili. Mbadwa za Adamu zinamvetsa bwino zotsatila za kutembeleledwa kwa nthaka, imene inabala minga na zitsamba zobaya. Lameki, atate ake a Nowa, anakambapo za “nchito . . . yopweteketsa manja, cifukwa colima nthaka imene Yehova anaitembelela.” (Genesis 5:​29) Cigumula citatha, Yehova anadalitsa Nowa na ana ake, ndipo anafotokoza colinga cake coti adzaze dziko lapansi. (Genesis 9:⁠1) Mwacionekele, tembelelo la Mulungu pa nthaka linatha panthawiyo.​—Genesis 13:⁠10.

it-2 186

Zoŵaŵa za Pobeleka

Zitanthauza kusautsika kumene kumakhalapo panthawi yobeleka. Mkazi woyamba Hava atacimwa, Mulungu anamuuza kuti adzayamba kumva zoŵaŵa pobeleka. Akanakhala womvela, sembe Mulungu anapitiliza kum’dalitsa, ndipo kubeleka kukanakhala cocitika cokondweletsa, cifukwa “madalitso a Yehova na amene amalemeletsa, ndipo sawonjezelapo ululu.” (Miy. 10:22) Koma m’malo mwake, cifukwa ca ucimo, kugwila nchito kwa thupi kumabweletsa zoŵaŵa. Ndiye cifukwa cake, Mulungu anakamba kuti (kungoti anthu ambili amaganiza kuti Mulungu akalola zinthu kucitika amati ndiye wazicita): “Nidzawonjezela kuvutika kwako pamene uli na pakati. Pobeleka ana udzamva zoŵaŵa.”​—Gen. 3:​16.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-2 192 ¶5

Lameki

Ndakatulo imene Lameki anapekela akazi ake, (Gen. 4:​23, 24) ionetsa kuti panthawiyo ciwawa cinali cofala. Ndakatulo yake inali motele: “Tamvelani mawu anga inu akazi a Lameki. Chelani khutu ku zonena zanga: Ndapha munthu cifukwa condipweteka, ndaphadi, mnyamata cifukwa condimenya. Ngati wopha Kaini ati adzalangidwe maulendo 7, ndiyetu wopha ine Lameki, adzalangidwa maulendo 77.” Cioneka kuti colinga ca Lameki cinali kudziteteza ku mlanduwo pocondelela kuti sanaphe munthu mwadala, mmene Kaini anacitila. Mfundo ya Lameki inali yakuti pofuna kudzicinjiliza, anapha munthu amene anamuvulaza. Conco, ndakatulo yake inali pempho lodziteteza kwa aliyense wofuna kubwezela cifukwa cakupha amene anamuvulazayo.

it-1 338 ¶2

Kunyoza Mulungu

Cioneka kuti “kuitanila pa dzina la Yehova” kumene kunayamba m’nthawi ya Enosi cigumula cisanacitike, sikunali na colinga cabwino. Tikamba conco cifukwa, Abele anali kuchula dzina la Mulungu popemphela. (Gen. 4:​26; Aheb. 11:⁠4) Malinga na zimene akatswili ena amakamba, ngati kuitanila pa dzina la Mulungu kumene kunadzayamba kumbuyoko kunali kogwilitsila nchito dzinalo molakwika, monga kuchula anthu kapena mafano kuti Yehova, ndiye kuti kumeneko kunali kunyoza Mulungu.

JANUARY 20-​26

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 6-8

“Anacitadi Momwemo”

w18.02 4 ¶4

Tengelani Cikhulupililo na Kumvela kwa Nowa, Danieli, komanso Yobu

Mavuto amene Nowa anakumana nawo. Pofika m’nthawi ya Inoki, amene anali ambuye awo a atate ake a Nowa, anthu anali kucita zinthu zoipa kwambili. Iwo anali kunenela Yehova zinthu “zonyoza koopsa.” (Yuda 14, 15) Ciwawa cinali ponse-ponse. Ndipo m’nthawi ya Nowa, Baibo imati, “dziko lapansi . . . linadzaza ndi ciwawa.” Angelo oipa anavala matupi a anthu na kudzitengela akazi, ndipo anabala viphona vankhanza. (Gen. 6:​2-4, 11, 12) Koma Nowa anali munthu wolungama. Baibo imati: “Nowa anayanjidwa ndi Yehova. . . . Iye anali wopanda colakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.”​—Gen. 6:​8, 9.

w13 4/1 14 ¶1

“Nowa Anayenda na Mulungu Woona”

Nchitoyi inatenga zaka zambili mwina 40 kapena 50. Iwo anafunika kugwetsa mitengo, kuinyamula komanso kuidula moyenelela na kuilumikiza. Cingalawaco cinafunika kukhala ca nsanjika zitatu, zipinda komanso khomo. Ciyenelanso kuti cinali na mawindo m’mwamba komanso ca mtenje wotukuka pakati kuti madzi azikunkhulikila m’mbali.​—Genesis 6:​14-​16.

w11 9/15 18 ¶13

Tiyeni Tithamange Mpikisano Mopilila

13 Kodi n’ciani cimene cinathandiza atumiki a Yehova amenewa kupilila n’kupambana pa mpikisanowu? Taonani zimene Paulo analemba zokhudza Nowa. (Ŵelengani Aheberi 11:⁠7.) Nowa anali asanaone ‘cigumula camadzi padziko lapansi cikuwononga camoyo ciliconse.’ (Gen. 6:​17) Zimenezi zinali zisanacitikepo ndipo panalibe amene anaganiza kuti zingacitike. Ngakhale zinali conco, Nowa sanaganize kuti n’zosatheka. Iye anatelo cifukwa cakuti anali kukhulupilila kuti ciliconse cimene Yehova wanena cidzacitika. Nowa sanaone kuti Mulungu wamupempha kucita zinthu zosatheka. Iye anatsatila zimene Mulungu analamula ndipo “anacitadi momwemo.” (Gen. 6:​22) Ganizilani cabe zimene Nowa anauzidwa kucita. Iye anayenela kumanga cingalawa, kusonkhanitsamo zinyama, kusunga cakudya coti azikadya na banja lake komanso ca zinyama. Anayenelanso kulalikila uthenga wocenjeza anthu ndiponso kuyesetsa kuti banja lake likhale lolimba mwauzimu. Imeneyi sinali nchito yamaseŵela. Koma cikhulupililo ndiponso kupilila kwa Nowa zinathandiza kuti iye na banja lake apulumuke ndiponso adalitsidwe.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w04 1/1 29 ¶7

Mfundo Zazikulu za m’Buku la Genesis​—Cigawo Coyamba

7:2​—Kodi cosiyanitsila pakati pa nyama zodetsedwa na zosadetsedwa maka-maka cinali ciani? Maziko amene anagwilitsidwa nchito posiyanitsa nyamazo mwacionekele anali okhudza kupeleka nsembe polambila, osati mfundo yakuti nyamayo ni yakuti anthu angadye kapena ayi. Cigumula cisanacitike, anthu sanali kudya nyama. Mawu akuti “zodetsedwa” kapena “zosadetsedwa” pankhani ya cakudya anali kugwila nchito pa nthawi ya Cilamulo ca Mose cabe, ndipo zimenezi zinaleka kugwila nchito pamene Cilamuloco cinatha. (Machitidwe 10:​9-​16; Aefeso 2:​15) Mwacionekele, Nowa anali kudziŵa nyama zimene zinali zoyenela kupeleka nsembe polambila Yehova. Atangotuluka m’cingalawa, iye “anamangila Yehova guwa lansembe. Atatelo, anatenga zina mwa nyama zonse zoyela, ndi zina mwa zouluka zonse zoyela, n’kuzipeleka nsembe yopseleza paguwapo.”​—Genesis 8:​20.

w04 1/1 30 ¶1

Mfundo Zazikulu za m’Buku la Genesis​—Cigawo Coyamba

7:​11​—Kodi madzi amene anacititsa Cigumula padziko lonse anacokela kuti? Mkati mwa nyengo yaciŵili yolenga kapena kuti “tsiku,” la kulenga pamene “mlengalenga” wa pa dziko lapansi unapangidwa, panali madzi ‘pansi pa mlengalengawo’ komanso ‘pamwamba pa mlengalengawo.’ (Genesis 1:​6, 7) Madzi amene anali ‘pansiwo’ ni amene anali kale padziko lapansi. Madzi amene anali “pamwamba,” anali cime coculuka cimene cinali mu mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi, cimene cinapanga “madzi akuya.” Madzi amenewa ni amene anagwa padziko lapansi m’masiku a Nowa.

JANUARY 27–FEBRUARY 2

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 9-​11

“Padziko Lonse Lapansi Panali Cilankhulo Cimodzi”

it-1 239

Babulo Wamkulu

Zocitika za ku Babulo Wamakedzana. Mzinda wa Babulo unamangidwa m’Cigwa ca “Sinara” pa nthawi imene anthu anaganiza zomanga Nsanja ya Babele. (Gen. 11:​2-9) Colinga codziŵika bwino cimene anthuwo anafuna kumangila nsanjayo na mzinda wake, cinali ‘kudzipangila dzina’ kuti achuke, osati kukweza dzina la Mulungu. Nsanja zimene anatulukila m’matongwe a Babulo wamakedzana, komanso ku madela ena ku Mesopotamiya, zitsimikizila kuti colinga cacikulu comangila Nsanja ya Babele cinali kulambila, mosasamala kanthu za mamangidwe ake. Yehova Mulungu anacitapo kanthu mwamsanga kuti cimango cimeneco cisapitilize. Izi zionetselatu kuti iye sanagwilizane nazo, cifukwa ndico cinali ciyambi ca cipembedzo conama. Kumbali ina, dzina laciheberi la mzinda umenewu lakuti Babele, limatanthauza ‘cisokonezo,’ dzina la cisumeria lakuti (Ka-dingir-ra) komanso la ciakadiya lakuti (Bab-ilu) amatanthauza “Cipata ca Mulungu.” Anthu amene anakhalila pa mzindawo anasintha dzina lake pofuna kupewa mfundo yakuti mzindawo sunayanjidwe na Mulungu. Ngakhale n’conco, dzina latsopano la mzindawo linaonetsabe kuti unali wokhudzana na zacipembedzo.

it-2 202 ¶2

Citundu

Nkhani ya m’buku la Genesis imafotokoza zakuti pambuyo pa Cigumula, anthu anagwilizana kuti amange nsanja. Zimene anthuwo anagwilizana, zinali zotsutsana na cifunilo ca Mulungu cifukwa zinali zosiyana na zimene Mulunguyo anauza Nowa na ana ake. (Gen. 9:⁠1) M’malo mwakuti iwo afalikile na ‘kudzaza dziko lapansi,’ anafuna kukhala pa malo amodzi, na kumanga malo awo okhala amene anadzadziŵika na dzina lakuti Zigwa za Sinara ku Mesopotamiya. Mwacionekele malo amenewa anali kudzakhalanso likulu la cipembedzo, lokhala na nsanja ya cipempembedzo.​—Gen. 11:​2-4.

it-2 202 ¶3

Citundu

Mulungu wamphamvuzonse analepheletsa nchito yawo yomanga mwa kusokoneza mgwilizano wawo. Anacita izi mwa kusokoneza citundu cimodzi cimene onse anali kukamba. Izi zinawalepheletsa kugwila nchito yawo mogwilizana, cakuti anabalalikila ku malo osiyana-siyana pa dziko lonse. Kusokoneza citundu cawo kunalepheletsa kuti m’tsogolo akagwilizanenso pa njila yawo yolakwika, yocita zinthu zosemphana na cifunilo ca Mulungu. Kunakhala kosatheka kuti anthuwo akaikenso pamodzi maluso na nzelu, osati zocokela kwa Mulungu, koma zawo-zawo. (Yelekezelani na Mlal. 7:​29; Deut. 32:⁠5.) Ngakhale kuti kusokoneza citundu kunabweletsa magaŵano aakulu pakati pa anthu, kunathandiza kuti anthu onse asagwilizanenso pa zolinga zoopsa komanso zoipa. (Gen. 11:​5-9; yelekezelani na Yes. 8:​9, 10) Tikaona masiku ano zimene anthu akukwanitsa kucita kapena kupanga mwa nzelu zawo, zimene akuzigwilitsila nchito molakwa, tikhoza kumvetsa cifukwa cake Mulungu poonelatu patali, sanalole kuti nchito yomanga nsanja ya Babele ipitilize.

it-2 472

Mitundu

Tsopano anthu anagaŵikana mwa vitundu, zikhalidwe, zopanga-panga zamaluso, miyambo, na cipembedzo. Mtundu uliwonse unali kucita zinthu mwa njila yawo-yawo. (Lev. 18:⁠3) Polekana na Mulungu, anthu ambili lomba anayamba kupanga mafano yambili ya milungu yawo.​—Deut. 12:30; 2 Maf. 17:​29, 33.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-1 1023 ¶4

Hamu

N’kutheka kuti Kanani ndiye anayamba kusokoneza zinthu, ndipo Hamu atate ake analephela kumuwongolela. N’kuthekanso kuti Nowa anakamba mwaulosi mouzilidwa, poona kuti khalidwe loipa la Hamu limene mwina linali litayamba kuonekela mwa mwana wake Kanani, lidzayambukilanso mbadwa za Kanani. Mbali ya tembelelo lake limeneli linakwanilitsikako pamene mbadwa za Semu zinagonjetsa Akanani. Ndipo amene sanawonongedwe (mwacitsanzo, Agibiyoni [Yos. 9]) anakhala akapolo a Aisiraeli. Patapita zaka zambili, tembelelo limeneli linapitiliza kukwanilitsika pamene mbadwa za Kanani mwana wa Hamu, zinakhala pansi pa ulamulilo wa padziko lonse wa mbadwa za Yafeti, ulamulilo wa Mediya na Perisiya, Girisi, na Roma.

it-2 503

Nimurodi

Ufumu wa Nimurodi unaphatikizapo mizinda ya Babele, Ereke, Akadi komanso Kaline, yonse m’dziko la Sinara. (Gen. 10:10) Conco, ayenela kuti ndiye analamula anthu kuti ayambe kumanga Babele na nsanja yake. Mfundo imeneyi igwilizananso na umboni wa Ayuda. Josephus analemba kuti: “Pang’ono na pang’ono, Nimurodi anayamba kusintha zinthu m’dziko kuti ayambe kupodeleza anthu. Iye anaganiza kuti njila yokha imene angaletsele anthu kuopa Mulungu ni mwa kuwapangitsa kuti azidalila ulamulilo wake nthawi zonse. Anakamba moopseza kuti adzabwezela Mulungu ngati adzafunanso kuwononga dziko lapansi na cigumula, cifukwa adzamanga cinsanja cacitali cimene madzi sangafikeko. Anatinso adzabwezela Mulungu cifukwa cowononga makolo awo akale-kale. Anthu anali okonzeka kutsatila maganizo a [Nimurodi], na kuyamba kuganiza kuti kugonjela Mulungu ni ukapolo. Conco anayamba kumanga nsanja . . . cakuti nchitoyo inathamanga modabwitsa kwambili.”​—Jewish Antiquities, I, 114, 115 (iv, 2, 3).

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani