NYIMBO 37
Kutumikila Yehova na Moyo Wonse
Yopulinta
1. O Yehova Mfumu yathu,
Nimakukondani kwambili.
Ine nidzadzipeleka
Kutumikila imwe cabe.
Nikonda zikumbutso zonse
Zimene mumanipatsa!
(KOLASI)
Nadzipeleka Yehova
Kutumikila imwe cabe.
2. Zinthu zonse munapanga
Zimatamanda inu M’lungu.
Nipempha munithandize
Nikhale wokhulupilika.
Moyo wanga naupeleka,
Nidzatumikila inu.
(KOLASI)
Nadzipeleka Yehova
Kutumikila imwe cabe.
(Onaninso Deut. 6:15; Sal. 40:8; 113:1-3; Mlal. 5:4; Yoh. 4:34)