LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 October tsa. 3
  • Muziona Ubale Wanu na Yehova Kukhala Wamtengo Wapatali

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muziona Ubale Wanu na Yehova Kukhala Wamtengo Wapatali
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Muli pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Muzikhulupilila Yehova Nthawi Zonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Acinyamata—Kodi Yehova ni Bwenzi Lanu Lapamtima?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 October tsa. 3
Zithunzi: Munthu akulimbitsa ubale wake na Yehova. 1. Akupemphela. Ndipo cizindikilo cikuloza kumwamba. 2. Akuŵelenga Baibo. Ndipo cizindikilo cikuloza pansi.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Muziona Ubale Wanu na Yehova Kukhala Wamtengo Wapatali

Ife Mboni za Yehova tili na mwayi wapadela. Pokhala Akhristu odzipatulila komanso obatizika, timapitiliza kupanga ubale wolimba na Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Anatikokela kwa iye kupitila mwa Mwana wake. (Yoh. 6:44) Iye amamvetsela mapemphelo athu.—Sal. 34:15.

Kodi tingateteze bwanji ubale wathu wamtengo wapatali na Mulungu? Cimodzi cimene tiyenela kucita ni kupewa macimo ngati amene Aisiraeli anacita. Iwo atangocita pangano na Yehova, anapanga mwana wang’ombe wagolide n’kuyamba kumulambila. (Eks. 32:7, 8; 1 Akor. 10:7, 11, 14) Tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimacita bwanji nikakumana na mayeselo? Kodi zocita zanga zimaonetsa kuti nimaona ubale wanga na Yehova kukhala wamtengo wapatali?’ Kukonda kwambili Atate wathu wakumwamba kudzatithandiza kupewa kucita zinthu zimene iye amazonda. —Sal. 97:10.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI TETEZANI UBALE WANU NA YEHOVA (AKOL. 3:5), NDIPO PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi kusilila kwa nsanje n’ciani?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kupewa dyela na kulambila mafano?

  • Kodi cigololo na kulambila mafano n’zogwilizana bwanji?

  • N’cifukwa ciani maka-maka abale amene ali pa udindo afunika kuyesetsa kusamalila zosoŵa za mnzawo wa m’cikwati?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani