Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
OCTOBER 5-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 31–32
“Pewani Kupembedza Mafano”
w09 5/15 11 ¶11
Yesetsani Kukula Mwauzimu Cifukwa “Tsiku Lalikulu la Yehova Lili Pafupi”
11 Kugwilitsa nchito zimene taphunzila m’Malemba kungakhale kovuta nthawi zina maka-maka pamene zinthu zavuta. Mwacitsanzo, Yehova atangopulumutsa kumene Aisiraeli ku Iguputo komwe anali akapolo, iwo “anayamba kukangana ndi Mose” ndipo anapitiliza “kuyesa Yehova.” Iwo anacita zimenezi pa nthawi imene anasoŵa madzi akumwa. (Eks. 17:1-4) Pasanathe miyezi iŵili iwo atacita pangano na Mulungu n’kuvomeleza kuti azicita ‘mawu onse amene Yehova ananena,’ iwo anaphwanya lamulo loletsa kulambila mafano. (Eks. 24:3, 12-18; 32:1, 2, 7-9) Kodi Aisiraeli anacita zimenezi cifukwa ca mantha ataona kuti Mose akucedwa ku Phili la Horebe kumene anapita kukalandila malangizo? Kapena kodi anali kuopa kuti Aamaleki akawaukilanso Mose kulibe asoŵa cocita? Pajatu Mose ndi amene anawathandiza kuti apambane pa nkhondo ina cifukwa cokweza manja ake. (Eks. 17:8-16) Kaya cinawacititsa n’ciani, koma mfundo ni yakuti Aisiraeli “anakana kumumvela.” (Mac. 7:39-41) Paulo analimbikitsa Akhristu kuti ‘acite ciliconse cotheka’ kuti apewe ‘kugwa ndi kutengela citsanzo ca kusamvela’ kumene Aisiraeli anasonyeza pocita mantha kuloŵa m’dziko lolonjezedwa.—Aheb. 4:3, 11.
w12 10/15 25 ¶12
Mvelani Mulungu Kuti Mupindule ndi Malumbilo Ake
12 Nthawi yomweyo, Yehova anayamba kukwanilitsa mbali yake yokhudza pangano la Cilamulo. Iye anauza anthu kukonza cihema kuti Aisiraeli azikamulambila kumeneko. Mulungu anakhazikitsanso ansembe kuti azigwilizanitsa anthu ocimwa na iye. Koma Aisiraeli sanacedwe kuiŵala zakuti anadzipatulila kwa Mulungu. Iwo “anali kumvetsa cisoni Woyela wa Isiraeli.” (Sal. 78:41) Mwacitsanzo, pamene Mose anali kulandila malangizo ena ku Phili la Sinai, Aisiraeli anaona kuti iye akucedwa ndipo cikhulupililo cawo cinayamba kucepa. Iwo anaganiza kuti Mose wawathaŵa. Conco anapanga fano la mwana wa ng’ombe n’kuuza anthu onse kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.” (Eks. 32:1, 4) Kenako anacita cikondwelelo cimene anacichula kuti “cikondwelelo ca Yehova” n’kuyamba kupeleka nsembe ndi kugwadila fano lawolo. Yehova ataona zimenezi, anauza Mose kuti: “Apatuka mofulumila panjila imene ndawalamula kuyendamo.” (Eks. 32:5, 6, 8) Comvetsa cisoni n’cakuti kuyambila nthawi imeneyo, Aisiraeli anali kungolumbila koma osacita.—Num. 30:2.
“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”
14 Aisiraeli anali kudziŵa kuti kulambila mafano ni chimo lalikulu pamaso pa Yehova. (Eks. 20:3-5) Ngakhale n’conco, iwo anayamba kulambila mwana wa ng’ombe. Olo kuti anali atacita chimo, Aisiraeli ayenela kuti anali kuganiza kuti akali ku mbali ya Yehova. Izi zionekela bwino pa zimene Aroni anakamba. Iye ananena kuti kulambila mwana wa ng’ombeko cinali “cikondwelelo ca Yehova.” Kodi Yehova anamvela bwanji? Anaona kuti anthuwo am’pandukila. Yehova anauza Mose kuti iwo ‘anacita zinthu zowawonongetsa’ komanso kuti ‘anapatuka mofulumila panjila imene iye anawalamula kuyendamo.’ Yehova anakwiya kwambili cakuti anafuna kufafaniza mtundu wonse wa Isiraeli.—Eks. 32:5-10.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
“Pali Nthawi” Yogwila Nchito Komanso Yopumula
4 Monga taonela, Yehova na Yesu amatipatsa citsanzo cabwino ca kugwila nchito molimbika. Kodi izi zitanthauza kuti kupumula n’kosafunikila kwa ife? Iyai. Yehova salema. Conco, safunikila kupumula akagwila nchito. Baibo imakamba kuti pambuyo polenga kumwamba na dziko lapansi, Yehova “anapuma pa nchito yake.” (Eks. 31:17) Yehova anayamba walekeza nchito yake yolenga zinthu, ndipo anakhutila na zimene anali atalenga. Olo kuti Yesu anali kugwila nchito molimbika pamene anali pa dziko lapansi, anali kupatula nthawi yopumula komanso kusangalala na cakudya pamodzi na mabwenzi ake.—Mat. 14:13; Luka 7:34.
w87 9/1 29
Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Munthu akadziŵika kwa Mulungu na kukhala woyanjidwa na iye (ndipo dzina lake lalembedwa “m’buku la moyo”), sizitanthauza kuti basi iye wayenelezedwa kukalandila moyo wosatha monga kuti zinakonzedwelatu kapena sizingasinthe. Ponena za Aisiraeli, Mose anafunsa Yehova kuti: “Komano ngati mukufuna kuwakhululukila chimo lawo,—koma ngati simukufuna, ndifafanizeni conde, m’buku lanu limene mwalemba.” Mulungu anayankha kuti: “Amene wandicimwilayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.” (Ekisodo 32:32, 33) Inde, ngakhale pambuyo pakuti Mulungu walemba dzina la munthu “m’buku” lake, munthuyo angaleke kukhala womvela kapena angataye cikhulupililo. Ngati iye wacita zimenezo, Mulungu ‘adzafafaniza dzina lake m’buku la moyo.’—Chivumbulutso 3:5.
OCTOBER 12-18
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 33-34
“Makhalidwe Abwino Kwambili a Yehova”
it-2 466-467
Dzina
Zinthu za m’cilengedwe zimene timaona zimacitila umboni kuti Mulungu aliko, koma sizitiuza dzina lake. (Sal. 19:1; Aroma 1:20) Kudziŵa dzina la Mulungu sikutanthauza kudziŵa cabe liwu lakuti Yehova. (2 Mbiri 6:33) Kumatanthauza kum’dziŵa bwino Mulungu. Kudziŵa zolinga zake, zocita zake, komanso makhalidwe ake mogwilizana na zimene Mawu ake amakamba. (Yelekezelani na 1 Maf. 8:41-43; 9:3, 7; Neh. 9:10.) Mfundo imeneyi ionekela bwino m’nkhani ya Mose, munthu amene Yehova anali ‘kumudziŵa bwino, ndi dzina lake lomwe,’ kapena kuti kum’dziŵa bwino kwambili. (Eks. 33:12) Mose anali na mwayi woona ulemelelo wa Yehova, komanso kumumva ‘akulengeza dzina lake lakuti Yehova.’ (Eks. 34:5) Kulengeza dzina kumeneko sikunatanthauze kungochula mobweleza-bweleza dzina lakuti Yehova, koma kunatanthauza kukamba mawu ofotokoza makhalidwe a Mulungu na zocita zake. Mawuwo anali akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi. Wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukila zolakwa ndi macimo, koma wosalekelela konse wolakwa osam’langa. Wolanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo cifukwa ca zolakwa za abambo awo.” (Eks. 34:6, 7) Mofanana na zimenezi, nyimbo ya Mose, imene ili na mawu akuti “pakuti ndidzalengeza dzina la Yehova,” imafotokoza zimene Mulungu anacitila Aisiraeli komanso makhalidwe ake.—Deut. 32:3-44.
w09 5/1 18 ¶3-5
Yehova Anafotokoza Makhalidwe Ake
Coyamba, Yehova anauza Mose kuti iye ndi “Mulungu wacifundo ndi wacisomo.” (Vesi 6) Katswili wina wa maphunzilo a Baibo ananena kuti mawu a Ciheberi amene anawamasulila kuti “wacifundo,” amanena za “cifundo cacikulu ca [Mulungu] ngati cimene bambo amacitila ana ake.” Ndipo mawu amene anawamasulila kuti “wacisomo,” amafanana ndi mawu amene “amanena za munthu amene ali ndi mtima wofunitsitsa kuthandiza munthu amene wakumana na mavuto.” N’zoonekelatu kuti Yehova amafuna kuti tidziŵe kuti iye amasamalila atumiki ake mofanana ndi mmene makolo amasamalila ana awo mwacikondi ndiponso kuwapezela zofunika paumoyo.—Salimo 103:8, 13.
Kenako Yehova anauza Mose kuti iye ndi “wosakwiya msanga.” (Vesi 6) Izi zitanthauza kuti Atumiki ake a padziko lapansi akalakwitsa zinthu, Mulungu amaleza nawo mtima ndipo amawapatsa nthawi yakuti alape.—2 Petulo 3:9.
Mulungu ananenanso kuti iye ndi “wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi.” (Vesi 6) Kukoma mtima kosatha kapena kuti cikondi cosatha, ni khalidwe la Yehova lapamwamba kwambili limene limacititsa kuti iye azigwilizana kwambili ndi anthu ake, ndipo cikondi cimeneci sicilephela. (Deuteronomo 7:9) Ndiponso Yehova ndiye cimake ca coonadi. Conco, iye sanganame kapenanso kunamizidwa. Popeza kuti iye ni “Mulungu wa coonadi,” timakhulupilila na mtima wonse zimene amakamba, kuphatikizapo zimene watilonjeza zokhudza m’tsogolo.—Salimo 31:5.
w09 5/1 18 ¶6
Yehova Anafotokoza Makhalidwe Ake
Mfundo inanso yofunika kwambili imene Yehova amafuna kuti tidziŵe ni yakuti iye ‘amakhululukila zolakwa ndi macimo.’ (Vesi 7) Iye ni ‘wokonzeka kukhululukila’ anthu ocimwa omwe alapa. (Salimo 86:5) Komabe Yehova sasangalala na ucimo. N’cifukwa cake iye anati ‘salekelela konse wolakwa osam’langa.’ (Vesi 7) Mulungu amene ni woyela ndiponso wacilungamo, sadzalekelela mpaka kalekale anthu amene amacimwa mwadala. Tsiku lina adzawalanga.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w04 3/15 27 ¶5
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ekisodo
33:11, 20—Kodi Mulungu anakambilana motani na Mose “pamasom’pamaso”? Mawu amenewa aonetsa kukambilana kwa anthu aŵili okondana kwambili. Mose anakamba na nthumwi ya Mulungu, ndipo anamuuza pakamwa malangizo a Yehova kudzela mwa iye. Koma Mose sanaone Yehova, popeza ‘palibe munthu angaone Mulungu n’kukhalabe ndi moyo.’ Ndipo Yehova sanalankhule naye mwacindunji Mose. Lemba la Agalatiya 3:19 limati Cilamulo “cinapelekedwa kudzela mwa angelo, kudzelanso m’dzanja la mkhalapakati.”
w98 9/1 20 ¶5
Tsimikizani Kuika Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba!
Mwamuna aliyense waciisiraeli ndiponso mwamuna aliyense wotembenukila kuciyuda m’dzikomo, analamulidwa kukaonekela pamaso pa Yehova katatu pacaka. Pozindikila kuti banja lonse linafunikila kupindula mwauzimu panthaŵi zimenezi, mitu yambili ya mabanja inali kupitila pamodzi ndi akazi ndi ana awo. Koma kodi ndani amene anali kuteteza nyumba na minda yawo kwa adani mabanjawo akacokapo? Yehova anawalonjeza kuti: “Palibe aliyense adzasilila dziko lanu pamene mwacoka kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu katatu pa caka.” (Ekisodo 34:24) Aisiraeliwo anafunika kukhala na cikhulupililo kuti azindikile kuti ngati aika zinthu zauzimu pamalo oyamba, iwo sadzataya zinthu zawo zakuthupi. Kodi Yehova anakwanilitsa mawu ake? Inde anakwanilitsadi!
OCTOBER 19-25
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 35-36
“Anapatsidwa Nzelu Kuti Agwile Nchito ya Yehova”
Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka
Cimene cinakondweletsa kwambili Yehova ndi mzimu wopeleka mofunitsitsa wa anthu amene anacilikiza kulambila koona osati zinthu zimene anapelekazo. Anthuwo anagwilitsilanso nchito nthawi yawo na mphamvu zawo pa nchitoyo. Nkhaniyi imanena kuti, “akazi onse aluso anawomba nsalu ndi manja awo.” Ndipo imanenanso kuti, “akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi.” Komanso, Yehova anapatsa Bezaleli mtima ‘wanzelu, wozindikila, wodziŵa zinthu, kuti akhale mmisili waluso pa nchito ina iliyonse.’ Zoonadi, Mulungu anacititsa Bezaleli ndi Oholiabu kukhala na luso lofunika kuti akwanitse kugwila nchito yonse imene anawapatsa.—Eks. 35:25, 26, 30-35.
w11 12/15 19 ¶6
Anthu Okhulupilika Akale Amene Anatsogoleledwa ndi Mzimu wa Mulungu
6 Bezaleli anali mtumiki wa Yehova amene analipo m’nthawi ya Mose. Zimene zinacitikila mtumiki ameneyu zingatithandize kumvetsa bwino mmene mzimu wa Mulungu ungatithandizile. (Ŵelengani Ekisodo 35:30-35.) Bezaleli anasankhidwa kuti atsogolele pa nchito yokonza cihema. Kodi iye anali na luso lokhudza nchitoyi asanasankhidwe? Mwina anali nalo, koma zikuoneka kuti nchito imene anali kugwila asanayambe zimenezi inali youmba njerwa za Aiguputo. (Eks. 1:13, 14) Nanga kodi Bezaleli anakwanitsa bwanji nchito yovuta imeneyi? Yehova ‘anam’patsa mzimu wake kuti akhale wanzelu, wozindikila, wodziŵa zinthu, ndi kuti akhale mmisili waluso pa nchito ina iliyonse. Anam’patsa mzimuwo kutinso akhale wotha kulinganiza kapangidwe ka zinthu . . . ndiponso wodziŵa kupanga mwaluso zinthu zina zilizonse.’ Kaya Bezaleli anali na luso lotani poyamba, mfundo ni yakuti mzimu woyela unam’thandiza. N’cimodzi-modzinso na Oholiabu. Bezaleli na Oholiabu ayenela kuti anamvetsa bwino zimene Mulungu anali kufuna pa nchito yawo cifukwa cakuti anaigwila bwino komanso anali kuphunzitsa anthu ena zoyenela kucita.
w11 12/15 19 ¶7
Anthu Okhulupilika Akale Amene Anatsogoleledwa ndi Mzimu wa Mulungu
7 Umboni wina wosonyeza kuti Bezaleli ndi Oholiabu anali kutsogoleledwa na mzimu wa Mulungu ni wakuti zimene anapanga zinali zolimba kwambili moti zinakagwilitsidwabe nchito patapita zaka 500. (2 Mbiri 1:2-6) Masiku ano, anthu amene amapanga zinthu amasaina maina awo kuti achuke koma Bezaleli ndi Oholiabu sanacite zimenezo. Iwo anafuna kuti ulemelelo wonse wa zimene anapangazo upite kwa Yehova.—Eks. 36:1, 2.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w05 5/15 23 ¶14
Phunzilani Njila za Yehova
14 Ikani zinthu zauzimu patsogolo. Mtundu wa Isiraeli sunayenele kulola zinthu zakuthupi kuwacotsela cidwi cawo pa zinthu zauzimu. Aisiraeli sanafunikile kutangwanika na zinthu wamba pa moyo wawo. Yehova anapatula nthawi wiki iliyonse kuti ikhale yopatulika, nthawi imene anafunikila kuigwilitsa nchito pa zinthu zokhazo zokhudzana ndi kupembedza Mulungu woona. (Ekisodo 35:1-3; Numeri 15:32-36) Caka ciliconse, anali kupatulanso nthawi ina yocita misonkhano inanso yopatulika. (Levitiko 23:4-44) Misonkhano imeneyi inali kuwapatsa mpata wokambilana nchito zodabwitsa za Yehova, kukumbutsidwa njila zake, na kuonetsa kuyamikila kwawo Mulungu cifukwa ca zabwino zonse zimene wawacitila. Anthu akasonyeza kudzipeleka kwawo kwa Yehova, anali kukulitsa mantha ndi cikondi cawo pa Mulungu, ndipo zinali kuwathandiza kuyenda m’njila zake. (Deuteronomo 10:12, 13) Mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’malangizo amenewo zimapindulitsa atumiki a Yehova lelolino.—Aheberi 10:24, 25.
w00 11/1 29 ¶1
Mtima Wamataya Umadzetsa Cimwemwe
Ndiyeno tangoganizani mmene Aisiraeliwo anamvelela. Mibadwo inali itavutika mu ukapolo wadzaoneni ndi umphaŵi wosaneneka. Tsopano anali omasuka ndipo anali naco cuma cambili. Kodi akanamva motani poganizila zocotsanso cina mwa cuma cimeneco? Iwo akanatha kulingalila kuti anali malipilo awo ndipo anayenela kucisunga. Komabe, atawapempha kuti apeleke cuma pocilikiza kulambila koyela, anapelekadi—ndipo osati mokakamizika kapena monyinyilika! Sanaiŵale kuti Yehova ndi amene anatheketsa kuti iwo akhale na cuma cimeneco. Conco, anapeleka siliva ndi golide wawo na zoŵeta zawo mowolowa manja. Anali ndi “mtima wofunitsitsa.” ‘Mitima yawo inali yofunitsitsa.’ ‘Mzimu wawo unawapangitsa kukhala ofunitsitsa.’ Ndithudi, inali “nsembe yaufulu kwa Yehova.’—Ekisodo 25:1-9; 35:4-9, 20-29; 36:3-7.
OCTOBER 26–NOVEMBER 1
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 37-38
“Maguwa Ansembe a pa Cihema Komanso Nchito Yawo pa Kulambila Koona”
it-1 82 ¶3
Guwa la Nsembe
Guwa la nsembe zofukiza. Guwa la nsembe zofukiza (lochedwanso “guwa la nsembe lagolide” [Eks. 39:38]) linalinso lopangidwa na matabwa a mthethe, ndipo linali lokutidwa na golide pamwamba komanso m’mbali mwake. Linalinso na mkombelo wagolide wozungulila m’mwamba mwake. Guwalo linali la masentimita 44.5 m’litali na m’lifupi mwake. Mbali zake zonse zinayi zinali zofanana, ndipo msinkhu wake unali masentimita 89. Linalinso na “nyanga” pamwamba, zotuluka m’makona onse anayi. Panapangidwanso mphete ziŵili zagolide zoloŵetsamo mitengo yonyamulila guwalo ya mtengo wa mthethe, imene inali yokuta na golide. Mphetezo zinaikidwa m’munsi mwa mkombelo wagolide uja, ina kumbali iyi ya guwa la nsembe, ina kumbali ina. (Eks. 30:1-5; 37:25-28) Paguwali anali kufukizilapo zofukiza zapadela, kaŵili patsiku, m’maŵa komanso madzulo. (Eks. 30:7-9, 34-38) Malemba ena amakamba kuti cofukizila, kapena kuti ciwaya cofukizila cinali kugwilitsidwa nchito pofukiza zofukiza. Ndipo mwacionekele umu ni mmenenso zinali kukhalila pa guwa la nsembe zofukiza. (Lev 16:12, 13; Aheb. 9:4; Chiv. 8:5; yelekezelani na 2 Mbiri 26:16, 19.) Guwa la nsembe zofukiza linali kukhala m’cihema, pafupi na nsalu yochinga ku Malo Oyela Koposa, moti Baibo imati linali kukhala “patsogolo pa likasa la umboni.”—Eks. 30:1, 6; 40:5, 26, 27.
it-1 1195
Zofukiza
Zofukiza zopatulika zimene zinali kugwilitsidwa nchito pa cihema m’cipululu zinali zopangidwa na zinthu zamtengo wapatali zimene Aisiraeli anapeleka monga zopeleka. (Eks. 25:1, 2, 6; 35:4, 5, 8, 27-29) Zofukizazo zinapangidwa mwa kusakaniza zinthu zinayi zonunkhilitsa. Pouza Mose mopangila msakanizowo, Yehova anati: “Tenga zonunkhila izi: madontho a sitakate, onika, mafuta onunkhila a galibanamu ndi lubani weni-weni. Zonsezi zikhale za muyezo wofanana. Zinthu zimenezi upangile zofukiza, msanganizo wa zonunkhilitsa zosakaniza mwaluso, wothila mchele, msanganizo weni-weni wopatulika. Kenako upele wina mwa msanganizo umenewu kuti ukhale ufa wosalala kwambili. Uike wina mwa ufawo patsogolo pa Umboni m’cihema cokumanako, kumene ndidzaonekela kwa iwe. Msanganizo umenewu ukhale wopatulika koposa kwa inu.” Ndiyeno pofuna kuthandiza Aisiraeli kuona kuti zofukiza zimenezi n’zopatulika komanso zoyela, Yehova anati: “Aliyense wopanga zofukiza zofanana ndi zimenezi pofuna kudzisangalatsa ndi kununkhila kwake, adzaphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.”—Eks. 30:34-38; 37:29.
it-1 82 ¶1
Guwa la Nsembe
Maguwa ansembe a pa Cihema. Cihema citamangidwa, panapangidwa maguwa aŵili ansembe mogwilizana na malangizo a kamangidwe amene Mulungu anapeleka. Guwa la nsembe zopseleza (lochedwanso “guwa la nsembe lamkuwa” [Eks. 39:39]) linali lopangidwa na matabwa a mthethe. Linali ngati bokosi lopanda kanthu mkati, mwacionekele losatseka pamwamba na pansi pomwe. Guwalo linali la mamita 2.2 m’mbali zake zonse zinayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 1.3. Linalinso na “nyanga” pamwamba pake zotuluka m’makona ake anayi. Mbali zonse za guwalo zinali zokutidwa na mkuwa. Panalinso sefa wa zitsulo zamkuwa zolukana-lukana umene unaikidwa mkati “capakati” pa guwalo, “m’munsi” mwa mkombelo. Mphete zinayi zinaikidwa ku mbali zonse zinayi za guwalo pafupi na sefa wa zitsulo zamkuwayo. Cioneka kuti mphete zimenezi ni zomwe zija zimene anali kuloŵetsamo mitengo iŵili yonyamulila guwa, ya mtengo wa mthethe, imene inali yokutidwa na mkuwa. Izi zingatanthauze kuti mbali ziŵili za guwalo zinabooledwako pang’ono kuti aziloŵetsamo sefayo, ndipo mphetezo zinaikidwa mbali zonse ziŵili kumapeto kwa sefayo. Akatswili ali na maganizo osiyana kwambili pankhaniyi. Koma ambili amakhulupilila kuti panali mphete zinayi. Amati mphete zina ziŵili, zomwe anali kuloŵetsamo mitengo yonyamulila guwalo, zinali zolumikizidwa mwacindunji kunja kwa guwalo. Panapangidwanso ziwiya zamkuwa monga ndowa na mafosholo ocotsela phulusa, mbale zolandilila magazi a nyama, mafoloko aakulu onyamulila nyama, komanso zopalila moto.—Eks. 27:1-8; 38:1-7, 30; Num. 4:14.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 36
Mtengo wa Mthethe
Mtengo wa mthethe umakhala na minga zitali-zitali, komanso nthambi zotambasuka kwambili. Kaŵili-kaŵili nthambi zimenezi zimakolana-kolana na nthambi za mitengo ina ya mthethe imene ili pafupi, n’kupanga gulu la mitengo yoŵilila. Mosakayikila, ici ndiye cifukwa cake pafupi-fupi nthawi zonse olemba Baibo anagwilitsila nchito liwu loculukitsa lakuti sitimu pokamba za mtengowu. Mtengo wa mthethe ungatalike kufika mamita 6 mpaka 8, koma kambili umakhala waufupi komanso woŵilila. Masamba ake amakhala ofeŵa ndiponso aubweya, ndipo umacita maluŵa acikasu a fungo labwino. Umabalanso tuzipatso tooneka ngati nyemba. Mtengowu umakhala na khungwa lakuda lokakala, koma ni wolimba kwambili, wansale zolukana bwino komanso wolema, ndipo sudyewa ciwamba-wamba na tulombo todya mitengo. Pa zifukwa zimenezi komanso cifukwa cakuti unali kupezeka mosavuta m’cipululu, mtengo wa mthethe ndiwo unali woyenelela kwambili kuuseŵenzetsa pomanga cihema na zokongoletsela zake. Ni umenenso anauseŵenzetsa popanga likasa la pangano (Eks. 25:10; 37:1), tebulo loikapo mkate wacionetselo (Eks. 25:23; 37:10), maguwa ansembe (Eks. 27:1; 37:25; 38:1), mitengo yonyamulila zinthu zimenezi (Eks. 25:13, 28; 27:6; 30:5; 37:4, 15, 28; 38:6), mizati ya nsalu yochinga na mizati ya nsalu yochinga khomo la cihema (Eks. 26:32, 37; 36:36), komanso mafelemu oimika (Eks. 26:15; 36:20) na mipilingidzo yake (Eks. 26:26; 36:31).
Kodi Mukudziŵa?
Magalasi odziyang’anila akale anali osiyana kwambili ndi a masiku ano. Magalasi akalewa nthawi zambili anali kupangidwa na buronzi. Koma nthawi zina anali kuwapanga na mkuwa, siliva, golide kapena golide wosakaniza ndi siliva. Baibo imachula koyamba za magalasi odziyang’anila otelewa pamene imanena za zinthu zimene anagwilitsa nchito pomanga cihema, malo amene Aisiraeli anali kukalambililako. Azimayi anapeleka magalasi awo kuti awasungunule n’kupangila beseni losambila la mkuwa ndi coikapo cake.—Ekisodo 38:8.