LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Ziphunzitso za m’Baibo N’zothandiza Nthawi Zonse
    Nsanja ya Mlonda (Yogawila)—2018 | No. 1
    • yovuta imeneyi. Inamuthandiza maningi. Monga mmene tionele m’nkhani zitatu zotsatila, ambili apeza kuti kuseŵenzetsa malangizo a m’Baibo kwaŵathandiza kwambili kulimbana na mavuto mu umoyo. Iwo afika poona Baibo monga coumba cija cimene cafotokozedwa kuciyambi. Baibo ni yosiyana na mabuku ambili amene amatha nchito. Kodi kungakhale kuti Baibo inapangiwa mosiyana na mabuku ena? Kodi n’kuthekadi kuti maganizo ali m’Baibo ni a Mulungu, osati a anthu?—1 Atesalonika 2:13.

      Mwina na imwe mwafika povomeleza kuti moyo ni waufupi, wodzala na mavuto. Nanga mavuto akakukulilani msinkhu, kodi mumapeza kuti citonthozo, cilimbikitso, na malangizo odalilika?

      Tiyeni tione njila zitatu zikulu-zikulu za mmene Baibo ingakhalile yothandiza mu umoyo wanu. Ingakuthandizeni kudziŵa mmene

      1. mungapewele mavuto ngati n’kotheka.

      2. mungathetsele mavuto akabuka.

      3. mungapililile mukakumana na mavuto amene simungawathetse.

      Nkhani zotsatila zidzafotokoza mbali zitatu zimenezi.

  • Kodi Inatha Nchito Kapena Imakambilatu Zinthu Zimene Anthu Akalibe Kuzitulukila?
    Nsanja ya Mlonda (Yogawila)—2018 | No. 1
    • Kupatula anthu odwala matenda oyambukila.

      Cilamulo ca Mose cinakamba kuti anthu odwala matenda a khate ayenela kukhala kwaokha. Madokota anadziŵa kufunika koseŵenzetsa mfundo imeneyi pambuyo pa milili ya matenda a m’zaka za pakati pa 500 C.E. na 1500 C.E. Mpaka pano mfundo imeneyi yakhala yothandiza.—Levitiko, caputa 13 na 14.

      Kusamba m’manja pambuyo pogwila mtembo.

      Mpaka kumapeto kwa zaka za m’ma 1800, madokota nthawi zambili anali kusamalila mitembo kenako n’kusamalila anthu odwala, cosasamba m’manja. Mcitidwe umenewo unabweletsa imfa zambili. Koma Cilamulo ca Mose cinakamba kuti aliyense wogwila mtembo anali wodetsedwa. Cinapeleka malangizo akuti zimenezi zikacitika, munthu anali kufunika kuyeletsedwa na madzi, motsatila mwambo wa m’cilamulo. Zimenezi zinalinso ndi maubwino pa nkhani ya umoyo na thanzi.—Numeri 19:11, 19.

      Kutaya zonyansa za munthu.

      Caka ciliconse, ana opitilila 500,000 amafa cifukwa ca matenda othulula. Nthawi zambili zimakhala cifukwa ca kusataya moyenelela zonyansa za anthu. Cilamulo ca Mose cinakamba kuti zonyansa za munthu ziyenela kufoceledwa kutali na malo okhala anthu.—Deuteronomo 23:13.

      Nthawi yabwino yocita mdulidwe.

      Malinga ni Cilamulo ca Mulungu, mwana wa mwamuna anali kudulidwa pa tsiku la namba 8 kucokela pamene anabadwa. (Levitiko 12:3) Capezeka kuti magazi a makanda amatha kuundana mosavuta pakapita wiki imodzi kucokela pamene anabadwa. M’nthawi za m’Baibo kunalibe njila zamakono zotsogola zacipatala. Koma kucita mdulidwe pambuyo pa wiki imodzi kunali citetezo cabwino.

      Mgwilizano umene ulipo pakati pa maganizo na thanzi la munthu.

      Ofufuza za mankhwala ndi asayansi amakamba kuti kusangalala, kukhala na ciyembekezo, kuyamikila, na kukhululukila ena ndi mtima wonse, kuli na maubwino ake pa thanzi la munthu. Baibo imati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—Miyambo 17:22.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani