Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
JANUARY 3-9
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 15-16
“Kusakhulupilika—Khalidwe Loipa Kwambili!”
w12 4/15 8 ¶4
Kusakhulupilika Ndi Cizindikilo ca Masiku Otsiliza
4Citsanzo coyamba ni ca Delila, mzimayi wacinyengo amene Woweluza Samisoni anali kumukonda. Samisoni anali kufunitsitsa kutsogolela anthu a Mulungu pa nkhondo yomenyana na Afilisiti. Olamulila asanu a Afilisiti ayenela kuti anali kudziŵa zoti Delila sanali kukonda kwenikweni Samisoni. Conco anamulonjeza kuti amupatsa ndalama zambili akawauza cinsinsi ca mphamvu zake zapadela. Iwo anacita zimenezi kuti aphe Samisoni. Cifukwa ca dyela, Delila anavomela koma analephela maulendo atatu kudziŵa cinsinsi ca mphamvu zake. Conco anapitiliza kumupanikiza “ndi mawu ake mosalekeza, ndi kum’condelela” mpaka Samisoni anafika “potopa nazo kwambili.” Ndiyeno anamuuza kuti sanametepo tsitsi lake moti atangometa, mphamvu zake zikhoza kuthela pomwepo. Delila atadziŵa zimenezi, anaitana munthu wina kuti amumete tsitsilo pamene anali kugona pamiyendo pake. Kenako anam’peleka kwa adani ake kuti athane naye. (Ower. 16:4, 5, 15-21) Zimene iye anacitazi zinali zoipa kwambili. Cifukwa ca dyela, Delila anapeleka Samisoni yemwe anali kumukonda.
w05 1/15 27 ¶4
Mfundo Zazikulu za M’buku la Oweruza
14:16, 17; 16:16. Kukonda kulila ndiponso kudandaula pofuna kuti munthu akucitileni zinazake kungathe kuwononga ubwenzi wanu na munthuyo.—Miyambo 19:13; 21:19.
w12 4/15 11-12 ¶15-16
Kusakhulupilika Ndi Cizindikilo ca Masiku Otsiliza
15Kodi anthu amene ali m’banja angatani kuti akhalebe okhulupilika? Mawu a Mulungu amati: “Usangalale ndi mkazi [kapena mwamuna] wapaunyamata wako.” Amanenanso kuti: “Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi [kapena mwamuna] wako amene umamukonda.” (Miy. 5:18; Mlal. 9:9) Pamene akukula, anthu okwatilana ayenela kucita zonse zimene angathe kuti azikondana ndiponso kusamalilana kwambili. Izi zikutanthauza kuti azidelana nkhawa, kukomelana mtima ndiponso azipeza nthawi yoceza limodzi. Ayenela kuganizila mmene angatetezele ukwati wawo ndiponso ubwenzi wawo na Yehova. Kuti izi zitheke, iwo ayenela kuphunzila Baibo limodzi, kuyendela limodzi mu utumiki ndiponso kupemphela limodzi kuti Yehova awadalitse.
KHALANIBE OKHULUPILIKA KWA YEHOVA
16Pali Akhristu ena amene anacita macimo akulu-akulu ndipo anadzudzulidwa “mwamphamvu, kuti akhale ndi cikhulupililo colimba.” (Tito 1:13) Koma anthu ena amacita zinthu zoyenela kucotsedwa nazo mu mpingo. “Anthu amene aphunzilapo kanthu pa cilango” coteleci amadzakhalanso olimba mwauzimu. (Aheb. 12:11) Bwanji ngati wacibale wathu kapena mnzathu wapamtima wacotsedwa? Apa tiyenela kukhala okhulupilika kwa Mulungu osati munthuyo. Yehova amacita nafe cidwi kuti aone ngati tikumvela lamulo lake lakuti tisamayanjane na munthu aliyense amene wacotsedwa.—Ŵelengani 1 Akorinto 5:11-13.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 3/15 27 ¶6
Samisoni Anapambana Cifukwa ca Mphamvu za Yehova
Samisoni anali wotsimikiza kukwanilitsa colinga cake, comenyana na Afilisti. Samisoni anakakhala kunyumba ya mkazi wadama ku Gaza na colinga comenyana na adani a Mulungu. Samisoni anafunikila malo ogona usiku mu mzinda wa adaniwo, ndipo malowo anapezeka m’nyumba ya mkazi wadama. Samisoni analibe colinga cocita dama. Iye anacoka kunyumba kwa mkaziyo pakati pa usiku, na kuzula mageti a pacipata ca mzindawo limodzi na vimitengo vake vam’mbali viŵili. Ndipo anazinyamula kupita nazo pamwamba pa phili pafupi na Heburoni, mtunda wa pafupifupi makilomita 60. Mulungu anavomeleza zomwe anacitazi ndipo anam’patsa mphamvu yocitila zimenezi.—Oweruza 16:1-3.
JANUARY 10-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 17-19
“Kusamvela Malamulo a Mulungu Kumabweletsa Mavuto”
it-2 390-391
Mika
1. Mwamuna wa ku Efuraimu. Mika anaphwanya lamulo la nambala 8 pa Malamulo Khumi (Eks. 20:15), mwa kuba ndalama zasiliva zokwana 1,100 za amayi ake. Mika atavomeleza kulakwa kwake na kubweza ndalamazo kwa amayi ake, amayi akewo anati: “Ndithudi ndipeleka ndalama zasilivazi kwa Yehova kuti zikhale zopatulika. Ndicita zimenezi kuti ndithandize mwana wanga, ndi kuti papangidwe cifanizilo cosema ndiponso cifanizilo copangidwa ndi citsulo cosungunula. Tsopano ndikubweza ndalamazi kwa iwe.” Kenako mayi akewo anatenga ndalama zasiliva zokwana 200 n’kukazipeleka kwa wosula siliva, ndipo wosula silivayo anapanga “cifanizilo cosema ndi cifanizilo copangidwa ndi citsulo cosungunula,” zimene pambuyo pake zinayamba kukhala m’nyumba ya Mika. Mika anali na “nyumba ya milungu,” ndipo anapanga efodi na aterafi. Komanso anapatsa mmodzi mwa ana ake mphamvu kuti azimutumikila monga wansembe wake. Cioneka kuti Mika anacita izi pofuna kulemekeza Yehova. Koma zimene anacitazo zinali zolakwika kwambili cifukwa kunali kuphwanya lamulo loletsa kulambila mafano (Eks. 20:4-6), ndiponso kunali kunyalanyaza cihema ca Yehova na ansembe ake. (Ower. 17:1-6; Deut. 12:1-14) Patapita nthawi, Mika anatenga mnyamata wina wa fuko la Levi, dzina lake Yonatani, mwana wa Gerisomu, mwana wa Mose n’kumakhala naye panyumba pake, ndipo anam’lemba nchito kuti azim’tumikila monga wansembe wake. (Ower. 18:4, 30) Poganiza kuti wacita zoyenela, Mika anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova andicitila zabwino.” (Ower. 17:7-13) Koma kumeneko kunali kudzinamiza cifukwa Yonatani sanali wa m’banja la Aroni, ndipo sanali woyenelela kutumikila monga wansembe. Izi zinangowonjezela kukula kwa chimo la Mika.—Num. 3:10.
it-2 391 ¶2
Mika
Patangopita nthawi yocepa, Mika pamodzi na amuna ena anathamangila amuna a fuko la Dani. Atawapeza anamufunsa cifukwa cake anali kuwathamangila. Mika anayankha kuti: “Mwatenga milungu yanga imene ndinapanga, ndipo mwatenganso wansembe n’kumapita naye. Nanga ine nditsala ndi ciani? Ndiye mungandifunse bwanji kuti, ‘Vuto lako n’ciani?’” Atamva izi, ana a Dani anamucenjeza Mika kuti amupha akapitiliza kuwalondola n’kumadandaula. Poona kuti amuna a fuko la Dani anali amphamvu kuposa iye, Mika anangobwelela kunyumba kwake. (Ower. 18:22-26) Pambuyo pake, amuna a fuko la Dani aja anapita kukapha anthu a ku Laisi, kutentha mzinda wawo, na kumangapo mzinda wa Dani pamalopo. Yonatani pamodzi na ana ake anakhala ansembe a fuko la Dani, ndipo ana a Dani “anadziimikila cifanizilo cosema . . . cimene Mika anapanga.” Ndipo cifaniziloco, “cinakhalabe coimilitsa masiku onse amene nyumba ya Mulungu woona inakhalabe ku Silo.”—Ower. 18:27-31.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Baibulo Lomasulidwa Bwino Kwambili
6Masiku ano tili na umboni wamphamvu woonetsa cifukwa cake tiyenela kugwilitsila nchito dzina la Yehova. Mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso la 2013, dzina la Mulungu limapezekamo nthawi zokwana 7,216. Ciŵelengelo cimeneci cikuonetsa kuti dzina la Mulungu lachulidwanso m’mavesi ena 6 kuwonjezela pa ciŵelengelo cakale. Mavesi 5 pa mavesi 6 amenewa, anawonjezeledwa cifukwa cakuti dzina la Mulungu linapezedwanso pa Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa imene inafalitsidwa posacedwapa. Mavesiwa akupezeka pa 1 Samueli 2:25; 6:3; 10:26; 23:14, 16. Vesi ina ya nambala 6 pamene pakupezekanso dzina la Mulungu ni pa Oweluza 19:18, ndipo linawonjezeledwa pambuyo popenda mosamalitsa mipukutu ina yakale ya Baibo.
JANUARY 17-23
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 20-21
“Pitilizani Kupempha Citsogozo ca Yehova”
w11 9/15 32 ¶2
Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi
Amuna a ku Gibeya, a fuko la Benjamini atagwilila na kupha mdzakazi wa Mlevi wina, mafuko ena ananyamuka kukamenyana na Abenjamini. (Ower. 20:1-11) Iwo anapemphela kwa Yehova asanakamenye nkhondo imeneyi koma anagonjetsedwa maulendo aŵili. (Ower. 20:14-25) Kodi umenewu unali umboni woti Mulungu sanamve mapemphelo awo? Kodi Yehova anasangalala kuona anthu amenewa akupita kukabwezela ciwembuco?
w05 1/15 27 ¶8
Mfundo Zazikulu za M’buku la Oweruza
20:17-48—N’cifukwa ciani Yehova analola kuti fuko la Benjamini ligonjetse mitundu inayo kaŵili, ngakhale kuti fuko limeneli linafunika kulangidwa? Polola kuti mafuko okhulupilikawo agonje kwambili poyambilila, Yehova anali kufuna kuwayesa mafukowo kuti aone ngati analidi otsimikiza mtima kucotselatu kuipa konse mu Isiraeli.
w11 9/15 32 ¶4
Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi
Kodi tikuphunzila ciani pa nkhaniyi? Mavuto ena mu mpingo amapitililabe ngakhale kuti akulu mu mpingo akucitapo kanthu komanso kupemphela kwa Mulungu kuti awathandize. Zimenezi zikacitika, akulu angacite bwino kukumbukila mawu a Yesu akuti: “Pitilizani kufunafuna [kapena kupemphela], ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulilani.” (Luka 11:9) Ngakhale kuti nthawi zina yankho la pemphelo lingachedwe, oyang’anila ayenela kudziŵa kuti Yehova adzawayankha pa nthawi yake.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Kodi Mudziŵa?
Mmene anthu anali kugwilitsila nchito gulaye pomenya nkhondo m’nthawi zakale
Davide anagwilitsila nchito gulaye kuti aphe cimphona cochedwa Goliyati. Mwacionekele, Davide anaphunzila kugwilitsila nchito cida cimeneci pamene anali m’busa wacicepele.—1 Samueli 17:40-50.
Gulaye imapezeka m’zolemba za Aiguputo na Asuri za m’nthawi za anthu ochulidwa m’Baibo. Cida cimeneci cinali kupangidwa na cikopa cimene cinali kumangidwa ku zingwe ziŵili. Munthu anali kuika m’gulaye mwala wosalala wolemela mwina magalamu 250. Ndiyeno anali kuzungulitsa gulaye na kuponya mwalawo mwamphamvu kwambili.
Pa zinthu zam’mabwinja zimene zinafukulidwa ku Middle East, panali miyala imene inali kugwilitsidwa nchito pomenya nkhondo na gulaye m’nthawi zakale. Asilikali aluso ayenela kuti anali kuponya miyalayi pa liŵilo la makilomita 160 mpaka 240 pa ola. Akatswili ofufuza zinthu amakayikila ngati gulaye anali m’gulu la uta. Komabe, gulaye anali cida cowononga.—Oweruza 20:16.
JANUARY 24-30
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | RUTE 1-2
“Pitilizani Kuonetsa Cikondi Cosasintha”
Tengelani Citsanzo ca Mabwenzi Apamtima a Yehova
5Acibale a Rute anali kukhala ku Mowabu. Rute akanafuna, akanabwelela, ndipo mwacionekele acibale akewo akanamusamalila. Iye anali kuwadziŵa bwino anthu a ku Mowabu. Anali kudziŵanso cinenelo na cikhalidwe cawo. Naomi anali kudziŵa kuti umoyo wa ku Betelehemu udzakhala wosiyana kwambili na umene Rute anazoloŵela. Ndipo Naomi anali kuda nkhawa kuti sadzapeza mwamuna woti akwatile Rute kapena nyumba yoti azikhalamo. Conco, Naomi anauza Rute kuti abwelele ku Mowabu. Monga mmene tafotokozela, Olipa ‘anabwelela kwa anthu a kwawo ndi kwa milungu yake.’ (Rute 1:9-15) Koma Rute sanabwelele kwawo kumene kunali milungu yonama.
Tengelani Citsanzo ca Mabwenzi Apamtima a Yehova
6Zioneka kuti Rute anaphunzila za Yehova Mulungu kucokela kwa mwamuna wake kapena kwa Naomi. Iye anaphunzila kuti Yehova sali monga milungu yonama ya ku Mowabu. Rute anali kukonda Yehova ndipo anadziŵa kuti iye ndiye Mulungu woyenela kum’konda na kum’lambila. Conco, Rute anasankha mwanzelu. Iye anauza Naomi kuti: “Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.” (Rute 1: 16) Timakhudzidwa mtima tikaganizila mmene Rute anali kukondela Naomi. Koma timacita cidwi kwambili tikaganizila mmene iye anali kukondela Yehova. Boazi nayenso anacita cidwi na zimenezi. Ndiye cifukwa cake anayamikila Rute cifukwa ‘cothawila m’mapiko mwa Yehova ndi kupezamo citetezo.’ (Ŵelengani Rute 2:12.) Mawu amene Boazi anakamba angatikumbutse za citetezo cimene mwana wa mbalame amapeza akakhala m’mapiko a mayi ake. (Salimo 36:7; 91:1-4) Mofananamo, Yehova anateteza Rute ndipo anamudalitsa cifukwa ca cikhulupililo cake. Rute sanadziimbepo mlandu cifukwa ca cosankha cimene anapanga.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 3/1 27 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Rute
1:13, 21—Kodi Yehova ndiye anacititsa kuti Naomi aumve kuŵaŵa moyo pomupatsa mavuto? Ayi, ndipo Naomi sanaimbe mlandu Mulungu kuti wamulakwila m’njila inayake. Komabe, poona zonse zimene zinam’citikila, iye anaganiza kuti Yehova sakumuyanja. Motelo anaŵaŵidwa mtima ndiponso anakhumudwa. Komanso masiku amenewo anthu anali kuona kuti kubeleka ni dalitso locokela kwa Mulungu, ndipo kusabeleka anali kukuona ngati tembelelo. Popeza kuti analibe zidzukulu ndiponso ana ake aamuna aŵili anali atafa, Naomi ayenela kuti anali kuona kuti akulondola poganiza kuti Yehova wamunyozetsa.
JANUARY 31–FEBRUARY 6
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | RUTE 3-4
“Pangani Mbili Yabwino Ndipo Isungeni”
Anali “Mkazi Wabwino Kwambili”
N’zosakayikitsa kuti zimene Boazi analankhula zinamukhazika mtima pansi Rute. Iye anauza Rute kuti: “Yehova akudalitse, mwana wanga. Kukoma mtima kosatha kumene wasonyeza panopa kukuposa koyamba kuja, popeza sunafune anyamata, kaya osauka kapena olemela.” (Rute 3:10) Rute anasonyeza kukoma mtima “koyamba” pamene anacoka ku Mowabu na apongozi ake kupita ku Isiraeli n’kumakawasamalila. Kukoma mtima kwaciŵili kunaonekela pa zimene Rute anacita, kuti sanafune anyamata, kaya osauka kapena olemela. Boazi anali kudziŵa kuti popeza Rute anali akadali mtsikana, akanatha kukwatiwa na mnyamata wa msinkhu wake. Koma iye anasankha kucitila zabwino Naomi komanso mwamuna wa Naomi amene anamwalila, n’colinga coti dzina la mwamuna wa Naomiyo, lisafe. N’cifukwa cake Boazi anacita cidwi kwambili na Rute.
Anali “Mkazi Wabwino Kwambili”
Rute ayenela kuti anali kusangalala kwambili akaganizila zimene Boazi ananena zoti anthu onse anali kumudziŵa kuti iyeyo ni “mkazi wabwino kwambili.” Zinali zoyeneladi kuti iye azidziŵika na mbili imeneyi cifukwa anali na colinga codziŵa Yehova komanso kumutumikila. Iye anasonyezanso kuti anali kudela nkhawa ndiponso kukomela mtima Naomi na anthu a mtundu wake, ndipo anali wofunitsitsa kutsatila miyambo yawo, yomwe mosakayikila inali yosiyana kwambili na yakwawo. Kutsanzila cikhulupililo ca Rute kungatithandize kuti nafenso tizilemekeza kwambili anthu ena komanso miyambo ya cikhalidwe cawo. Tikamacita zimenezi, ifenso tidzakhala na mbili yoti ndife anthu abwino kwambili.
w12 10/1 24 ¶3
Anali “Mkazi Wabwino Kwambili”
Zitatele, Boazi anakwatila Rute. Baibo imati: “Yehova anam’dalitsa [Rute] ndipo anatenga pakati n’kubeleka mwana wamwamuna.” Akazi a ku Betelehemu anayamba kudalitsa Naomi komanso kutamanda Rute kuti anacita zazikulu kwa Naomi zoposa zimene ana aamuna oposa 7 akanacita. Baibo limasonyeza kuti mwana wa Rute anadzakhala kholo la Mfumu Davide. (Rute 4:11-22) Ndiyeno Davideyo anadzakhala kholo la Yesu Khristu.—Mateyu 1:1.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 3/1 29 ¶3
Mfundo Zazikulu za M’buku la Rute
4:6—Kodi munthu wowombola ‘akanawononga’ bwanji colowa cake powombola mkazi? Cifukwa coyamba n’cakuti, ngati munthu amene analoŵa muumphawi uja anagulitsa colowa cake ca malo, wowombolayo anayenela kuwombolanso malowo pamtengo wogwilizana na zaka zimene zatsala kuti Caka Coliza Lipenga cifike. (Levitiko 25:25-27) Potelo ndiye kuti wowombolayo anali kuika paciswe katundu wake yemwe. Cifukwa cinanso n’cakuti mwana wamwamuna amene Rute akanabeleka ndiye anali woyenelela kuloŵa malo owomboledwawo, osati acibale apafupi a wowombolayo ayi.
FEBRUARY 7-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 1-2
“Mukhuthulileni za Mumtima Mwanu Yehova M’pemphelo”
ia 55 ¶12
Anapemphela Kucokela Pansi pa Mtima
Pamenepa Hana anapeleka citsanzo cabwino kwa atumiki onse a Mulungu pa nkhani ya pemphelo. Yehova amafuna kuti atumiki ake azipemphela kwa iye momasuka, osakayikila ciliconse. Iye amafuna kuti anthu azimuuza mavuto awo onse monga mmene mwana amacitila popempha cinthu kwa kholo lake limene limamukonda. (Ŵelengani Salimo 62:8; 1 Atesalonika 5:17.) Mtumwi Petulo analemba kuti popemphela kwa Yehova ‘tizimutulila nkhawa zathu zonse, pakuti amatidela nkhawa.’—1 Pet. 5:7.
w07 3/15 16 ¶4
Mmene Hana Anapezela Mtendele
Kodi tingaphunzile ciani pankhani imeneyi? Tikamapemphela kwa Yehova cifukwa coti tili na nkhawa, tizimuuza mmene tikumvela ndipo tizim’pempha mokhudzidwa mtima. Tikayesetsa kucita zonse zomwe tingathe poyesa kuthetsa vutolo, tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Palibe njila ina yabwino kuposa imeneyi.—Miyambo 3:5, 6.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 3/15 21 ¶5
Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba
2:10—N’cifukwa ciani Hana anapemphela kuti Yehova “adzapatsa mphamvu mfumu yake” pamene mu Isiraeli munalibe mfumu? Cilamulo ca Mose cinali citanenelatu kuti Aisiraeli adzakhala na mfumu. (Deuteronomo 17:14-18) Muulosi umene anaunena ali pafupi kumwalila, Yakobo anati: “Ndodo yacifumu [cizindikilo ca ulamulilo wa mfumu] sidzacoka kwa Yuda.” (Genesis 49:10) Komanso, ponena za Sara, mayi wa fuko la Isiraeli, Yehova anati: “Adzakhala mayi wa mitundu yambili ya anthu ndi wa mafumu a mitundu yambili ya anthu.” (Genesis 17:16) Conco, m’pemphelo lakeli, Hana anali kunena za mfumu ya m’tsogolo.
FEBRUARY 14-20
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 3-5
“Yehova Ni Mulungu Woganizila Ena”
Wamphamvuzonse Koma Woganizila Ena
3Samueli anayamba “kutumikila Yehova” pa cihema ali wamng’ono kwambili. (1 Sam. 3:1) Tsiku lina usiku, iye atagona, panacitika zinthu zina zimene sizinali kucitika kaŵili-kaŵili. (Ŵelengani 1 Samueli 3:2-10.) Anamva winawake akumuitana. Poganiza kuti Mkulu wa Ansembe Eli ndiye anali kumuitana, Samueli anathamangila kumene kunali iye nokamba kuti: “Ndabwela mbuyanga, ndamva kuitana.” Eli anakamba kuti sindiye anali kumuitana. Zaconco zitacitikanso kaŵili, Eli anazindikila kuti Mulungu ndiye anali kuitana Samueli. Conco anauza mnyamatayo mmene angayankhile akamvanso kuitana, ndipo Samueli anamvela. N’cifukwa ciani Yehova, kupitila mwa mngelo, sanadziulule kuti ndiye anali kuitana Samueli? Baibo siikamba cifukwa cake. Koma tikaganizila mmene zinthu zinayendela pambuyo pake, timatha kuona kuti Yehova anacita izi cifukwa comuganizila Samueli wacicepeleyo. Kodi anaonetsa bwanji kumuganizila?
Wamphamvuzonse Koma Woganizila Ena
4Ŵelengani 1 Samueli 3:11-18. M’Cilamulo ca Yehova, munali lamulo lakuti ana afunika kumalemekeza acikulile, makamaka atsogoleli. (Eks. 22:28; Lev. 19:32) Kodi muganiza kuti Samueli akanalimba mtima kupita kwa Eli m’maŵa kukamuuza uthenga woŵaŵa waciweluzo wocokela kwa Mulungu? Mwacionekele, yankho ni yakuti iyai. Ndipo Baibo imakamba kuti Samueli “anaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona.” Komabe, Mulungu anapangitsa Eli kuzindikila kuti Iye ndiye anali kuitana Samueli. Izi zinasonkhezela Eli kulamula Samueli kuti amufotokozele za masomphenyawo. Anati: “Usandibisile . . . ngakhale mawu amodzi pa mawu onse amene iye wakuuza.” Samueli anamvela, ndipo “anamuuza mawu onse.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 3/15 21 ¶6
Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba
3:3—Kodi Samueli anagonadi m’Malo Opatulikitsa? Ayi, sanagonemo. Samueli anali Mlevi wa fuko la Kohati lomwe silinali fuko la ansembe. (1 Mbiri 6:33-38) Pa cifukwa cimeneci, iye sanali wololedwa ‘kulowa kuti akaone zopatulikazo.’ (Numeri 4:17-20) Mbali yokha ya malo opatulikawo kumene Samueli anali waufulu kufikako inali bwalo la cihemaco. Ayenela kuti iye anagona kumeneko. Zikuoneka kuti Eli nayenso anali atagona penapake m’bwalo lomweli. Mawu akuti “mmene munali likasa la Mulungu,” ayenela kuti akunena malo amene panali cihemaco.
FEBRUARY 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 6-8
“Kodi Mfumu Yanu N’ndani?”
it-2 163 ¶1
Ufumu wa Mulungu
Anapempha Mfumu Yaumunthu. Patapita zaka pafupifupi 400 kucokela pamene Aisiraeli anatuluka mu Iguputo, komanso zaka zoposa 800 Mulungu atacita pangano na Abulahamu, Aisiraeli anapempha kuti akhale na mfumu yaumunthu yowatsogolela, monga zinalili na mitundu ina. Mwa kucita zimenezi, iwo anakana Yehova kuti asakhale mfumu yawo. (1 Sam. 8:4-8) N’zoona kuti Aisiraeli anali kuyembekezela ufumu wokhazikitsidwa na Mulungu, cifukwa monga takambila kale n’zimene iye anali atalonjeza kwa Abulahamu na Yakobo. Komanso anali kuyembekezela zimenezi cifukwa ca ulosi wokhudza Yuda umene Yakobo anakamba atatsala pang’ono kumwalila (Gen. 49:8-10), cifukwa ca mawu amene Yehova anauza Aisiraeli atatuluka mu Iguputo (Eks. 19:3-6), cifukwa ca mfundo za m’pangano la Cilamulo (Deut. 17:14, 15), komanso cifukwa ca mawu ena amene Mulungu anacititsa mneneli Balamu kukamba (Nu 24:2-7, 17). Ndipo Hana, mayi wokhulupilika wa Samueli anakamba za ciyembekezo cimeneci m’pemphelo lake. (1 Sam. 2:7-10) Komabe, Yehova anali asanaulule mokwanila “cinsinsi copatulika” cokhudza ufumuwo. Ndipo anali asanafotokoze nthawi imene Ufumuwo unali kudzakhazikitsidwa, mmene udzapangidwila, komanso kuti kaya udzakhala wa padziko lapansi kapena wakumwamba. Conco zimene Aisiraeli anacita, zoumilila kukhala na mfumu yaumunthu, kunali kusadzicepetsa.
Anakhalabe Wokhulupilika Ngakhale Anakumana ndi Mavuto
Koma tamvani zimene Yehova anayankha Samueli atamuuza nkhaniyi m’pemphelo. Yehova anati: “Mvela zonse zimene anthuwo akunena kwa iwe, pakuti sanakane iweyo koma akana ine kuti ndisakhale mfumu yawo.” Mawu a Yehova amenewa ayenela kuti anamulimbikitsa kwambili Samueli. Komabe mawuwa anasonyeza kuti anthuwo anacitila Mulungu Wamphamvuzonse cipongwe cacikulu. Yehova anauza mneneli Samueli kuti acenjeze Aisiraeli za kuipa kokhala na munthu woti aziwalamulila ngati mfumu yawo. Koma Samueli atawacenjeza, iwo anaumililabe kuti: “Ife tikufuna kuti mfumu izitilamulila.” Popeza nthawi zonse Samueli anali kumvela Mulungu, iye anapita kukadzoza mfumu imene Yehova anasankha.—1 Samueli 8:7-19.
w10 1/15 30 ¶9
Yehova Ndiye Woyeneladi Kulamulila
9Zimene zakhala zikucitika zasonyeza kuti zimene Yehova anacenjezazi zinali zoona. Aisiraeli anali kuvutika kwambili cifukwa colamulidwa na anthu makamaka olamulilawo akakhala osakhulupilika. Tikaganizila citsanzo ca Aisiraeli cimeneci, timamvetsa cifukwa cake maboma a anthu alephela kuthetsa mavuto. N’zoona kuti atsogoleli ena amapempha Mulungu kuti awadalitse n’colinga cakuti abweletse bata ndi mtendele. Komabe kodi Mulungu angadalitse bwanji anthu amene sagonjela ulamulilo wake?—Sal. 2:10-12.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w02 4/1 12 ¶13
N’cifukwa Ciani Tifunika Kubatizidwa?
13Tiyenela kutembenuka tisanabatizidwe kukhala Mboni za Yehova. Munthu amafuna yekha kutembenuka akasankha na mtima wonse kuti atsatile Khristu Yesu. Munthu wotelo amasiya zocita zake zoipa zakale, ndipo amatsimikiza mtima kucita zinthu zimene Mulungu amaziona kuti n’zabwino. M’Malemba, aneni a Ciheberi na Cigiriki otanthauza kutembenuka ali na ganizo la kubwelela, kusiya. Kumasonyeza kusiya zoipa na kutembenukila kwa Mulungu. (1 Mafumu 8:33, 34) Kutembenuka kumafuna kucita “nchito zoyenela kutembenuka mtima.” (Machitidwe 26:20) Kumafuna kuti tisiye kulambila konyenga, titsatile malamulo a Mulungu, na kulambila Yehova yekha basi. (Deuteronomo 30:2, 8-10; 1 Samueli 7:3) Kutembenuka kumaticititsa kusintha mmene tinali kuganizila, zolinga zathu, ndiponso mtima wathu. (Ezekieli 18:31) ‘Timabwelela’ pamene umunthu watsopano uloŵa m’malo mwa makhalidwe oipa.—Machitidwe 3:19; Aefeso 4:20-24; Akolose 3:5-14.
FEBRUARY 28–MARCH 6
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 SAMUELI 9-11
“Poyamba Sauli Anali Wodzicepetsa”
Muziyenda Modzicepetsa na Mulungu Wanu
11Ganizilani zimene zinacitikila Mfumu Sauli. Poyamba iye anali mnyamata wodzicepetsa. Iye anadziŵa kuti panali zinthu zina zimene sakanakwanitsa kucita, ndipo anayopa kulandila udindo wokhala mfumu. (1 Sam. 9:21; 10:20-22) Koma m’kupita kwa nthawi, Sauli anayamba kudzikuza. Khalidwe la kudzikuza limeneli linaonekela atangokhala mfumu. Mwacitsanzo, pa nthawi ina iye analephela kuugwila mtima pamene anali kuyembekezela mneneli Samueli. M’malo modalila Yehova kuti adzateteza anthu ake, Sauli anapeleka nsembe yopseleza olo kuti sunali udindo wake kucita zimenezo. Zotulukapo zake zinali zakuti Yehova analeka kumuyanja Sauli, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’kana kuti asakhale mfumu. (1 Sam. 13:8-14) Tingacite bwino kuphunzilapo kanthu pa citsanzo coticenjeza cimeneci mwa kupewa kucita zinthu modzikuza.
Khalanibe ndi Mzimu Wodzimana
8Citsanzo ca Mfumu Sauli cionetsa mmene kudzikonda kungawonongele mzimu wodzimana. Pamene Sauli anayamba kulamulila, anali wofatsa ndi wodzicepetsa. (1 Sam. 9:21) Iye anakana kulanga Aisiraeli amene ananyoza ulamulilo wake, ngakhale kuti kunali koyenela kucita zimenezo kuti ateteze udindo wopatsidwa na Mulungu. (1 Sam. 10:27) Mfumu Sauli analola mzimu wa Mulungu kuti umutsogolele na kuthandiza Aisiraeli kugonjetsa Aamoni. Kenako, iye modzicepetsa anatamanda Yehova kaamba ka cipambano.—1 Sam. 11:6, 11-13.
w95 12/15 10 ¶1
Aamoni—Anthu Amene Anabwezela Udani pa Kukoma Mtima
Aamoni kaciŵilinso anabwezela udani pa kukoma mtima kwa Yehova. Yehova sananyalanyaze ciwopsezo cankhanza cimeneci. “Sauli atamva mawu amenewa [a Nahasi] mzimu wa Mulungu unayamba kugwila nchito pa iye, ndipo anapsa mtima kwambili.” Motsogoleledwa na mzimu wa Mulungu, Sauli anasonkhanitsa amuna ankhondo 330,000 amene anakanthilatu Aamoni “moti sipanatsale anthu awili ali limodzi.”—1 Samueli 11:6, 11.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05 3/15 22 ¶8
Mfundo Zazikulu za M’buku la Samueli Woyamba
9:9—Kodi cocititsa cidwi n’ciani na mawu akuti “amene amachedwa mneneli masiku ano, kalekalelo anali kuchedwa kuti wamasomphenya”? Mawu amenewa akusonyeza kuti pamene aneneli anali kuculuka m’masiku a Samueli komanso m’nthawi imene Isiraeli anayamba kulamulilidwa na mafumu, anthu analeka kugwilitsa nchito liwu lakuti “wamasomphenya” m’malo mwake anayamba kugwilitsa nchito liwu lakuti “mneneli.” Samueli anali mneneli woyamba mwa aneneli amenewo.—Machitidwe 3:24.