Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MARCH 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 16-17
“Yehova, ni Gwelo la Ubwino”
Acicepele, Mungakhale na Umoyo Wacimwemwe
PEZANI MABWENZI ABWINO
11 Ŵelengani Salimo 16:3. Davide anali kudziŵa cinsinsi copezela mabwenzi abwino. Iye anali kupeza cimwemwe coculuka mwa kukhala na anthu okonda Yehova. Anthu amenewo anali “oyela,” kutanthauza kuti anali na makhalidwe abwino. Wamasalimo wina anakamba mawu ofanana na amenewa ponena za mabwenzi ake. Anati: “Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani, ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.” (Sal. 119:63) Na imwe mungathe kupeza mabwenzi abwino ambili pakati pa anthu amene amaopa Yehova na kumumvela. Ndipo mabwenzi amenewo angakhale a misinkhu yosiyana-siyana.
‘Tiziona Ubwino wa Yehova’
Davide anaimba kuti: “Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa, komanso cikho canga. Inu mukundisungila bwino kwambili colowa canga. Zingwe zoyezela zandigwela m’malo abwino.” (Sal. 16:5, 6) Davide anali kuyamikila kwambili “gawo” lake, kapena kuti mwayi wokhala pa ubwenzi na Yehova komanso womutumikila. Mofanana na Davide, ife timakumana na mavuto ambili koma tadalitsidwanso m’njila zambili. Conco tiyeni tipitilize kusangalala potumikila Mulungu woona komanso ‘kuyang’ana moyamikila’ kacisi wauzimu wa Yehova.
w08 2/15 3 ¶2-3
Ikani Yehova Patsogolo Panu Nthawi Zonse
2 Tonsefe timaphunzila zambili pa nkhani za anthu odziŵika bwino a m’Baibo monga Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Davide, Esitere, mtumwi Paulo na ena. Komanso tingapindule na nkhani za anthu omwe si odziŵika kwambili. Kusinkhasinkha nkhani za m’Baibo kungatithandize kucita zimene wamasalimo anacita. Iye anati: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Sal. 16:8) Kodi mawuwa atanthauzanji?
3 Kale msilikali anali kugwilila lupanga kudzanja lake lamanja. Cifukwa ca zimenezi, mbali ya kumanjayo inali yosatetezeka na cishango comwe anali kunyamula ku dzanja lamanzele. Komabe, iye anali kukhala wotetezeka ngati msilikali mnzake akumenya nkhondo ataima capafupi kudzanja lake lamanja. Ifenso tikamakumbukila Yehova na kucita cifunilo cake nthawi zonse, adzatiteteza.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 714
Mwana wa Diso
Mu diso mukalowa kanthu, ngakhale kakang’ono-ng’ono monga kafumbi, limamva nthawi yomweyo. Conco, m’pofunika kusamala kuti m’diso musalowe ciliconse comwe cingawononge kakhungu ka mkati mwa diso komwe kamateteza mwana wa diso. Zili conco cifukwa mwana wa diso akawonongedwa, kapena kugwidwa na matenda, diso limaleka kuona bwino ngakhale kufelatu. Baibo imagwilitsa nchito citsanzo camphamvu ca “mwana wa diso” cimeneci ponena za cinthu cina cofunika kutetezedwa koposa ndico, cilamulo ca Yehova. (Miy. 7:2) Pokamba za mmene Mulungu anatetezela Aisiraeli, Deuteronomo 32:10 imati anawateteza “monga mwana wa diso lake.” Davide anapemphela kuti Mulungu amuteteze na kumusamalila “monga mwana wa diso.” (Sal. 17:8) Anali kufuna kuti Yehova acitepo kanthu mwamsanga pamene anaukilidwa na adani ake.—Yelekezelani na Zek. 2:8.
MARCH 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | SALIMO 18
“Yehova Ndiye . . . Wopeleka Cipulumutso Kwa Ine”
w09 5/1 14 ¶4-5
Kodi Mafanizo a M’Baibo Mumawamvetsa Bwino?
Baibo imayelekezelanso Yehova na zinthu zina zopanda moyo. Mwacitsanzo, imati iye ni “Thanthwe la Isiraeli,” “thanthwe,” ndiponso “malo acitetezo.” (2 Samueli 23:3; Salimo 18:2; Deuteronomo 32:4) Kodi zinthu zimenezi zikufanana bwanji na Yehova? Monga mmene thanthwe lilili lolimba komanso losasunthika, Yehova Mulungu ndiye citetezo cathu colimba ndiponso cosasunthika.
5 M’buku la Masalimo muli mafanizo ambili amene amafotokoza makhalidwe osiyanasiyana a Yehova. Mwacitsanzo, Salimo 84:11 limanena kuti Yehova ali ngati “dzuŵa ndiponso cishango,” cifukwa cakuti iye amatipatsa kuunika, moyo, mphamvu ndiponso amatiteteza. Komanso, Salimo 121:5 limati: “Yehova ndiye mthunzi wako wa ku dzanja lako lamanja.” Anthu amene amam’tumikila, Yehova amawateteza ku mavuto otentha kwambili ngati dzuŵa, mofanana na mmene mthunzi umatetezela munthu kuti asapse na dzuŵa. Amacita zimenezi powaphimba na mthunzi wa “dzanja” lake kapena wa “mapiko” ake.—Yesaya 51:16; Salimo 17:8; 36:7.
it-2 1161 ¶7
Mawu
Mulungu amamva mawu a atumiki ake. Amene amatumikila Mulungu mu mzimu na coonadi amapemphela kwa iye ali na cikhulupililo cakuti akumva, mosasamala kanthu za cilankhulo cawo. Ngakhale kuti nthawi zina sititulutsa mawu popemphela, Mulungu amadziŵa za mumtima wathu, ndipo ‘amamva’ mapemphelo athu. (Sal. 66:19; 86:6; 116:1; 1 Sam. 1:13; Neh. 2:4) Mulungu amamva kulila kwa anthu osautsika akamapempha thandizo. Amamvelanso zolankhula za anthu omutsutsa, ndipo amadziŵa anthuwo akamakonzela ciŵembu atumiki ake.—Gen. 21:17; Sal. 55:18, 19; 69:33; 94:9-11; Yer. 23:25.
Mmene Tingathanilane Nazo Nkhawa
2. Sinkhasinkhani. Mukakumbukila zimene mwapitamo pa umoyo, kodi mungaganizileko mayeso amene munakwanitsa kuwapilila cifukwa ca thandizo la Yehova? Tikaganizila mmene iye anatithandizila, komanso mmene anathandizila atumiki ake kumbuyoko, timakhala na mtendele wamaganizo, ndipo cidalilo cathu mwa iye cimalimbilako. (Sal. 18:17-19) Mkulu wina dzina lake Joshua anati: “Nili na mndandanda wa mayankho ku mapemphelo anga. Izi zimanithandiza kukumbukila nthawi pamene n’napempha Yehova cina cake mwacindunji, ndipo iye ananipatsa cinthuco.” Inde, tikamasinkhasinkha mmene Yehova wakhala akutithandizila, timapeza mphamvu yolimbana na nkhawa.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 432 ¶2
Kerubi
Akerubi anali kuimila kukhalapo kwa Yehova. Malemba amati: “Ine ndidzaonekela kwa iwe pamenepo ndi kulankhula nawe kucokela pamwamba pa civundikilo, pakati pa akerubi aŵiliwo amene ali pamwamba pa likasa la umboni.” (Eks. 25:22; Num. 7:89) Conco, zinali ngati Yehova “akukhala pa akerubi.” (1 Sam. 4:4; 2 Sam. 6:2; 2 Maf. 19:15; 1 Mbiri 13:6; Sal. 80:1; 99:1; Yes. 37:16) Mophiphilitsa, akerubi anali “cifanizilo ca galeta” limene Yehova ndiye amaliyendetsa (1 Mbiri 28:18), ndipo mapiko a akerubi anali kupeleka citetezo na kuthandiza kuti galeta liziyenda mofulumila. M’nyimbo yake ya ndakatulo, Davide anakamba kuti, Yehova anabwela kudzamuthandiza mofulumila ngati munthu amene wakwela “pakerubi wouluka” komanso “pamapiko a colengedwa cauzimu.”—2 Sam. 22:11; Sal. 18:10.
MARCH 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 19-21
“Zakumwamba Zikulengeza Ulemelelo wa Mulungu”
w04 1/1 8 ¶1-2
Anthu Onse Alengeze Ulemelelo wa Yehova
DAVIDE, mwana wa Jese, anakula monga m’busa ku dela la ku Betelehemu. Ayenela kuti nthawi zambili anali kuyang’anitsitsa kumwamba kodzaza na nyenyezi zambili-mbili usiku, kunja kuli zii, akuyang’anila ziweto za atate wake m’malo odyetselako nkhosa amene anali kukhala kwa okha. Mosakayikila, anakumbukila zinthu zosaiŵalika zimenezi pamene, motsogozedwa na mzimu woyela wa Mulungu, analemba na kuimba mawu ocititsa cidwi a mu Salimo 19, amene amati: “Zakumwamba zikulengeza ulemelelo wa Mulungu. Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza nchito ya manja ake. Zingwe zawo zoyezela zafika padziko lonse lapansi, mawu awo amveka kumalekezelo a dziko lapansi kumene kuli anthu.”—Salimo 19:1, 4.
2 Zakumwamba zocititsa cidwi zolengedwa na Yehova zimalengeza ulemelelo wa Yehova usana na usiku popanda kulankhula, popanda mawu, popanda liwu lawo kumveka. Cilengedwe sicisiya kulengeza ulemelelo wa Mulungu, ndipo tikaganizila kuti umboni wopanda mawu umenewu umapita “pa dziko lonse lapansi” kuti anthu onse okhalamo auone, zimaticititsa kuzindikila kuti ndife ocepa mphamvu kwambili. Komabe, umboni wopanda mawu wa cilengedwe si wokwanila. Anthu okhulupilika akulimbikitsidwa kulengeza nawo umboni umenewu na mawu awo. Wolemba salimo wina, amene dzina lake silinachulidwe, anauza olambila okhulupirlka kuti: “M’patseni Yehova ulemelelo ndi kuvomeleza kuti iye ndi wamphamvu. M’patseni Yehova ulemelelo woyenela dzina lake.” (Salimo 96:7, 8) Anthu amene ali pa ubwenzi wabwino na Yehova amasangalala kumvela langizo limeneli.
w04 6/1 11 ¶8-10
Cilengedwe Cimalengeza Ulemelelo wa Mulungu
8 Kenako, Davide anafotokoza cinthu cina codabwitsa m’cilengedwe ca Yehova. Anati: “Kumwambako Mulungu wamangila dzuŵa hema. Dzuŵalo limaoneka ngati mkwati amene akutuluka m’cipinda cake, limakondwa ngati mmene mwamuna wamphamvu amacitila akamathamanga m’njila. Limatuluka kucokela kumalekezelo ena a kumwamba, ndi kuzungulila mpaka kumalekezelo enanso. Palibe cinthu ciliconse cimene sicimva kutentha kwake.”—Salimo 19: 4-6.
9 Dzuŵa n’locepelapo poyelekezela na nyenyezi zina. Komabe, ni nyenyezi yaikulu, moti mapulaneti amene amazungulila dzuŵalo amaoneka aang’ono kwambili. Buku lina limanena kuti dzuŵa ni lolemela matani 2 biliyoni, biliyoni, biliyoni. Kulemela kumeneku kumaposelatu kutalitali kulemela kwa mapulaneti onse amene amazungulila dzuŵa kuwaphatikiza pamodzi. Mphamvu ya dzuŵa imacititsa kuti dziko lapansili lizizungulila dzuŵalo pa mtunda wa makilomita 150 miliyoni popanda kupatuka n’kupita kutali kapena kukokeka n’kuliyandikila kwambili. Ni mphamvu yocepa cabe ya dzuŵa imene imafika padziko lapansi koma ni yokwanila kuti zamoyo zikhalepobe padzikoli.
10 Wamasalimo anagwilitsa nchito mawu okuluŵika pofotokoza za dzuŵa pamene ananena kuti dzuŵa ni “mwamuna wamphamvu” amene amathamanga kucokela kumalekezelo ena kufika malekezelo ena masana, ndipo usiku amakagona mu “hema.” Nyenyezi yaikulu imeneyi ikamaloŵa kumadzulo, munthu akamaiona ali padziko lapansi imaoneka ngati imapita mu “hema,” ngati kuti ikukapuma. Kum’maŵa imaoneka ngati ikutumphuka, n’kuwala kwambili “ngati mkwati amene akutuluka m’cipinda cake.” Popeza anali mbusa, Davide anali kudziŵa kuti usiku kunali kuzizila kwambili. (Genesis 31:40) Anali kukumbukila kuti dzuŵa linali kumucititsa kumva kutenthela mofulumila komanso kutenthetsa malo amene iye anali. Mwacionekele, silinali kutopa pa “ulendo” wake wocoka kum’maŵa kufika kumadzulo koma linali ngati “mwamuna wamphamvu,” wokonzeka kubwelezanso ulendo wake.
g95 11/8 23 ¶1
Waluso Wonyalanyazidwa Koposa m’Nthawi Yathu
Kukulitsa ciyamikilo cathu kaamba ka luso m’cilengedwe kungatithandize kudziŵa Mlengi wathu, amene nchito zake zatizungulila. Nthawi ina Yesu anauza ophunzilla ake kuyang’anitsitsa maluŵa akuchile omela m’Galileya. Iye anati: “Phunzilani pa mmene maluwa akuchile amakulila, sagwila nchito, ndiponso sawomba nsalu. Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemelelo wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.” (Mateyu 6:28, 29) Kukongola kwa duŵa laling’ono kumatikumbutsa kuti Mulungu amasamalila zofunikila za mtundu wa anthu.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 1073
Ciheberi, II
Mu Ciheberi munali kalembedwe ka ndakatulo komwe mbali yaciŵili m’ciganizo siinali kungobweleza mfundo yomwe yakambidwa kale. Koma inali kumveketsa bwino ciganizoco kapena kuwonjezelapo mfundo ina yatsopano. Mwacitsanzo, onani ndakatulo lili pa Salimo 19:7-9:
Cilamulo ca Yehova ndi cangwilo,
cimabwezeletsa moyo.
Zikumbutso za Yehova ndi zodalilika,
zimapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu.
Malamulo ocokela kwa Yehova ndi olungama,
amasangalatsa mtima;
Cilamulo ca Yehova ndi coyela,
cimatsegula maso.
Kuopa Yehova n’koyela,
ndipo kudzakhalapo kwamuyaya.
Zigamulo za Yehova n’zolondola,
ndipo pa mbali iliyonse zasonyezadi kuti ndi zolungama.
Onani kuti mbali yaciŵili m’ciganizo ciliconse ikukwanilitsa bwino mfundo yonse. Conco vesi yonse ikugwilizanitsa bwino mbali ziŵili. Motelo, Munthu akaŵelenga mbali yaciŵili monga yakuti “cimabwezeletsa moyo,” komanso yakuti “zimapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu,” amatha kumvetse bwino mmene Cilamulo ca Yehova cilili cangwilo, komanso mmene zikumbutso za Yehova zilili zodalilika.
MARCH 25-31
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | SALIMO 22
Baibo Inakambilatu Zimene Zidzacitika pa Imfa ya Yesu
w11 8/15 15 ¶16
Anapeza Mesiya
16 Mesiya adzaoneka ngati wasiyidwa na Mulungu. (Ŵelengani Salimo 22:1.) Maliko ananena kuti ca m’ma 3 koloko, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “‘Eli, Eli lama sabachthani?’ Mawu amenewa akawamasulira amatanthauza kuti: ‘Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyilanji ine?’” (Maliko 15:34) Ponena zimenezi, sikuti Yesu anali atasiya kukhulupilila Atate wake wakumwamba. Iye anadziŵa kuti Mulungu sadzamuteteza kwa adani ake pa nthawi ya imfa yake. Unali mwayi woti Yesu asonyeze kuti adzakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu ngakhale pamene akuyesedwa. Kufuula kwa Yesu kumeneku kunakwanilitsa ulosi wa pa Salimo 22:1.
w11 8/15 15 ¶13
Anapeza Mesiya
13 Davide analosela kuti Mesiya adzanyozedwa. (Ŵelengani Salimo 22:7, 8.) Yesu atapacikidwa pamtengo wozunzikilapo ananyozedwa. Mateyu analemba kuti: “Tsopano anthu odutsa anayamba kunena mawu onyoza Yesu. Anali kupukusa mitu yawo n’kumanena kuti: ‘Iwe wogwetsa kacisi ndi kum’manga m’masiku atatu, dzipulumutse! Ngati ulidi mwana wa Mulungu, tsikatu pamtengo wozunzikilapowo!’” Nawonso ansembe aakulu, alembi komanso akulu anayamba kumucita cipongwe ndi kunena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ameneyutu ndi Mfumu ya Isiraeli, atsiketu pamtengo wozunzikilapowo kuti ife timukhulupilile. Suja amakhulupilila Mulungu? Mulunguyo am’pulumutse tsopano ngati akumufunadi. Ndi ujatu anali kunena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’” (Mat. 27:39-43) Yesu anapilila zonsezi popanda kupsa mtima kapena kubwezela. Iye ndiye citsanzo cabwino kwambili kwa ife.
w11 8/15 15 ¶14
Anapeza Mesiya
14 Adzacita maele pazovala za Mesiya. Wamasalimo analemba kuti: “Iwo akugawana zovala zanga pakati pawo, ndipo akucita maele pazovala zanga.” (Sal. 22:18) Zimenezi zinacitikadi. Baibo imanena kuti asilikali aciroma “atam’pacika [Yesu] anagawana malaya ake akunja mwa kucita maele.”—Mat. 27:35; ŵelengani Yohane 19:23, 24.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 11/1 29 ¶7
Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika
7 Pali njila zoonekelatu zimene tingalemekezele misonkhano yathu. Njila imodzi ndiyo kuimba nawo nyimbo za Ufumu. Zambili mwa nyimbo zimenezi zinalembedwa ngati mapemphelo, conco tiyenela kuziimba mwaulemu. Pogwila mawu Salimo 22, mtumwi Paulo analemba za Yesu kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga, pakati pa mpingo ndidzakutamandani ndi nyimbo.” (Aheberi 2:12) Conco tiziyesetsa kukhala pansi cheyamani asanachule nyimbo imene tiimbe kenaka n’kuimba moganizila kwambili tanthauzo la mawu a nyimboyo. Kuimba kwathu kuzisonyeza mmene wamasalimo ankamvera, amene analemba kuti: “Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse, pakati pa gulu la owongoka mtima ndi pamsonkhano wawo.” (Salimo 111:1) Zoonadi, kuimbila Yehova zitamando n’cifukwa cimodzi cabwino kwambili coti tizifikila mwamsanga pa misonkhano yathu n’kukhalapo mpaka pamapeto.
w03 9/1 20 ¶1
Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano”
Masiku ano, monga mmene zinthu zinalili kale, anthu okhulupilila amapatsidwa mwayi woti azitha kulankhula za cikhulupililo cawo “pakati pa msonkhano.” Aliyense ali na mwayi woyankha mafunso amene amafunsidwa kwa omvetsela pa misonkhano ya mpingo. Musamapeputse mphamvu ya ndemanga zimenezi. Mwacitsanzo, ndemanga zimene zimasonyeza zimene tingacite kuti tithane na mavuto kapena tiwapewe zimalimbikitsa abale kuti apitilizebe kutsatila mfundo za m’Baibo. Ndemanga zofotokoza malemba a m’Baibo amene achulidwa koma sanawagwile mawu pandimepo, kapena zofotokoza mfundo zimene munthu wapeza atachita kafukufuku payekha, zingalimbikitse ena kukulitsa cizolowezi cophunzila pa okha.
APRIL 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 23-25
“Yehova ni M’busa Wanga”
“Yehova Ndi M’busa Wanga”
Yehova amatsogolela nkhosa zake. Nkhosa zikakhala zopanda m’busa zimasocela. N’cimodzimodzinso anthufe, pa moyo wathu timafunika wotitsogolela. (Yeremiya 10:23) Davide anafotokoza kuti Yehova amatsogolela anthu ake “m’mabusa a msipu wambili,” na “m’malo opumila a madzi ambili.” Amawatsogolelanso “m’tinjila tacilungamo.” (Vesi 2 na 3) Zimene Yehova amacitazi zikufanana ni zimene m’busa amachita posamalila nkhosa zake ndipo zikutitsimikizila kuti tiyenela kumukhulupilila. Tikamatsatila malangizo a Mulungu opezeka m’Baibo, tingakhale na moyo wokhutila, wosangalala komanso tingakhale na tsogolo labwino.
“Yehova Ndi M’busa Wanga”
Yehova amateteza nkhosa zake. Nkhosa zikakhala zopanda m’busa zimacita mantha komanso zimasoŵa wozithandiza. Yehova amauza anthu ake kuti asacite mantha ngakhale ‘poyenda m’cigwa ca mdima wandiweyani.’ Imeneyi ingakhale nthawi imene munthu amaona kuti ali pa mavuto adzaoneni. (Vesi 4) Pa nthawi imeneyi Yehova amaona zimene zikucitikila atumiki ake ndipo amakhala wokonzeka kuŵathandiza. Iye amapatsa atumiki ake nzelu na mphamvu kuti athe kupilila mayeselo awo.—Afilipi 4:13; Yakobo 1:2-5.
“Yehova Ndi M’busa Wanga”
Yehova amadyetsa nkhosa zake. Nkhosa zimadalila m’busa wawo kuti azipezele cakudya. Anthufe tili na zosowa zauzimu zimene Mulungu yekha ni amene angatithandize kuti tizipeze. (Mateyu 5:3) Tikuyamikila kuti Yehova ni Wowolowa manja ndipo amapatsa atumiki ake cakudya cauzimu cambili. (Vesi 5) Tikamawelenga zinthu monga Baibo komanso mabuku othandiza anthu kuphunzila Baibo, ngati Nsanja ya Mlonda, timapeza cakudya cauzimu cimene cimatithandiza kudziŵa colinga ca moyo komanso zimene Mulungu akufuna kudzaticitila.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w11 2/15 24 ¶1-3
Muzikonda Cilungamo ndi Mtima Wanu Wonse
YEHOVA akutsogolela anthu ake “m’tinjila tacilungamo” kudzela m’Mawu ake ndiponso mwa mzimu wake woyela. (Sal. 23:3) Komabe popeza anthufe ndife opanda ungwiro, nthawi zina timacoka panjila yacilungamo. Zikatele pamafunika khama kuti tiyambilenso kucita zinthu zabwino. Kodi cingatithandize n’ciyani? Mofanana na Yesu, tiyenela kukonda kucita zinthu zolungama.—Ŵelengani Salimo 45:7.
2 Kodi palembali “tinjila tacilungamo” n’ciyani? “Tinjila” timeneti ni moyo umene munthu amakhala cifukwa cotsatila mfundo zolungama za Yehova. Mawu Aciheberi ndiponso Acigiriki amene amamasulidwa kuti “cilungamo” amatanthauza “kuwongoka” potsatila kwambili makhalidwe abwino. Popeza Yehova na “malo okhalamo cilungamo,” anthu amene amamulambila amadalila iyeyo kuti awauze njila za makhalidwe abwino zimene iwowo ayenela kutsatila.—Yer. 50:7.
3 Kuti tikondweletsedi Mulungu, tiyenela kuyesetsa na mtima wathu wonse kutsatila zimene iye amaona kuti ni zolungama. (Deut. 32:4) Kuti zimenezi zitheke, tiyenela kuphunzila zambili za Yehova Mulungu kucokela m’Mawu ake, Baibo. Tikamaphunzila zambili za Mulungu ndiponso kumuyandikila tsiku lililonse, m’pamenenso timakonda kwambili cilungamo cake. (Yak. 4:8) Komanso tikamasankha zinthu zofunika pa moyo wathu, tiyenela kulola kuti Mawu ouzilidwa a Mulungu azititsogolela.
APRIL 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 26-28
Zimene Davide Anacita Kuti Akhalebe Wokhulupilika
w04 12/1 14 ¶8-9
Yendani mu Umphumphu
8 Davide anapemphela kuti: “Ndisanthuleni, inu Yehova, ndi kundiyesa. Yengani impso zanga ndi mtima wanga.” (Salimo 26:2) Impso zili m’katikati mwa thupi lathu. Impsozo, mophiphilitsila zimaimila maganizo a munthu a pansi penipeni pa mtima. Ndipo mtima wophiphilitsila umaimila m’kati mwa munthu, kapena kuti zimene zimamusonkhezela kucita zinazake, mmene amamvela mumtima mwake, ndiponso nzelu zake. Popempha Yehova kuti amusanthule, Davide kwenikweni anali kupemphela kuti Yehova afufuze na kuyesa zoganiza zake za pansi pa mtima wake ndiponso mmene amamvela mumtima mwakemo.
9 Davide anapempha kuti impso na mtima wake ziyeletsedwe. Kodi Yehova amatiyeletsa motani m’kati mwathu? Davide anaimba kuti: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolela.” (Salimo 16:7) Kodi izi zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti malangizo a Mulungu anam’fika pamtima Davide n’kukhazikika mumtimamo, na kukonza maganizo am’katikati mwa mtima wake. Zimenezi zingaticitikilenso ifeyo ngati timasinkhasinkha na mtima woyamikila malangizo amene timalandila kudzela m’Mawu a Mulungu, anthu omuimila, ndiponso gulu lake, na kulola kuti malangizowo akhazikike mumtima mwathu. Kupemphela nthawi zonse kwa Yehova kuti atiyeletse motelemu kungatithandize kuti tiyende mu umphumphu.
w04 12/1 15 ¶12-13
Yendani mu Umphumphu
12 Pofotokoza cinthu cinanso comwe cinalimbitsa umphumphu wake, Davide anati: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu acinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo. Ndimadana ndi mpingo wa anthu ocita zoipa, Ndipo sindikhala pansi ndi anthu oipa.” (Salimo 26:4, 5) Davide sanakhale pansi na anthu oipa, ngakhale pang’ono cabe. Sanafune kugwilizana nawo.
13 Nanga bwanji ifeyo? Kodi timakana kukhala na anthu acabe, kudzela m’mapulogilamu a pa TV, m’mavidiyo, m’makanema, pa Intaneti, kapena m’njila zina? Kodi timapewa anthu amene amabisa umunthu wawo? Anthu ena kusukulu kapena kunchito kwathu anganamizile kuti ni anzathu pamene ali na zolinga zacinyengo. Ndithudi, sitingafune kugwilizana na anthu amene sayenda m’coonadi ca Mulungu. Ngakhale kuti ampatuko amati ni anthu oona mitima, nawonso angabise colinga cawo pofuna kuti atisiyitse kutumikila Yehova. Kodi tingatani ngati mumpingo wa Cikhristu muli ena amene ali na moyo waciphamaso? Nawonso ndiye kuti amabisa umunthu wawo weniweni. Jayson, yemwe tsopano ni mtumiki wothandiza, anali na anzake ngati amenewa ali wamng’ono. Pofotokoza za anthu amenewa, iye anati: “Tsiku lina mmodzi wa anzangawa ananiuza kuti: ‘Zimene timacita panopa zilibe nchito cifukwa dziko latsopano likamadzafika, tidzakhala titafa basi. Sitidzadziŵa kuti tikumanidwa ciliconse.’ Zimene ananenazi zinanigalamutsa. Ineyo sinikufuna kuti nidzakhale nitafa dziko latsopano likamadzabwela.” Jayson anacita zanzelu posiya kugwilizana na anthu amenewa. Mtumwi Paulo anacenjeza motele: “Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Motelo kupewa kugwilizana na anthu oipa n’kofunika kwambili.
w04 12/1 16 ¶17-18
Yendani mu Umphumphu
17 Cihema, pamodzi na nchito zake za nsembe, cinali likulu lolambililapo Yehova ku Isiraeli. Pofotokoza mmene anali kusangalalila na malo amenewo, Davide anapemphela kuti: “Yehova, ine ndimakonda nyumba imene inu mumakhala ndi malo amene kumakhala ulemelelo wanu.”—Salimo 26:8.
18 Kodi timakonda kusonkhana pamalo amene timaphunzila za Yehova? Nyumba ya Ufumu iliyonse, cifukwa ca maphunzilo auzimu amene amacitikilapo, imakhala likulu la kulambira koona m’dela limene muli nyumbayo. Ndipo, caka n’caka timakhala na misonkhano ya cigawo komanso ya dela. Pamisonkhanoyi pamafotokozedwa “zikumbutso” za Yehova. Tikaphunzila ‘kuzikonda kwambili’ zikumbutsozi, timakhala ofunitsitsa kupita kumisonkhano na kukachela khutu tikafika kumisonkhanoko. (Salimo 119:167) N’zotsitsimutsa kwambili kukhala na okhulupilila anzathu amene amadela nkhawa za moyo wathu komanso amene amatithandiza kupitiliza kuyenda mu umphumphu.—Aheberi 10:24, 25.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 7/15 28 ¶15
Yehova Amalanditsa Wovutika
15 Wamasalimo Davide anaimba kuti: “Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya, Yehova adzanditenga.” (Salimo 27:10) N’zolimbikitsa kudziŵa kuti cikondi ca Yehova cimaposa ca kholo lina lililonse. Ngakhale kuti kukanidwa komanso kuzunzidwa na makolo kungakhale koŵaŵa kwambili, sikungasinthe mmene Yehova amatisamalilila. (Aroma 8:38, 39) Kumbukilani kuti Yehova amakoka munthu yemwe wakonda. (Yohane 3:16; 6:44) Zilibe kanthu kuti anthu akhala akukucitilani zotani, Atate wanu wakumwamba amakukondani.
APRIL 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 29-31
Cilango ni Njila Imene Mulungu Amationetsela Cikondi
it-1 802 ¶3
Nkhope
Mawu akuti ‘kubisa nkhope’ ali na matanthauzo osiyanasiyana, malinga na zimene zikucitika. Yehova Mulungu akabisa nkhope yake, zimatanthauza kuti iye waleka kuwayanja anthuwo kapena kuwacilikiza. Izi zimacitika ngati munthu mmodzi kapena gulu la anthu, lalephela kumvela lamulo la Mulungu monga zinalili kwa Aisiraeli. (Yobu 34:29; Salimo 30:5-8; Yes. 54:8; 59:2) Nthawi zina, zimaonetsa kuti si nthawi yoti Yehova acitapo kanthu poyembekezela nthawi yake yoikika. (Sal. 13:1-3) Pamene Davide anapempha kuti, “Ndikhululukileni macimo anga,” zinali ngati akupempha Mulungu kuti abise nkhope yake ngati kuti sanaone macimo a Davide.—Sal. 51:9; yelekezelani na Sal. 10:11.
w07 3/1 19 ¶1
Osangalala Kudikila Yehova
Njila imene cilango ca Yehova cimatipindulila tingaiyelekezele na mmene zipatso zimakhwimila. Baibo imakamba mawu otsatilawa pankhani ya kulanga kwa Mulungu: “Kwa anthu amene aphunzilapo kanthu pa cilangoco, cimabala cipatso camtendele, comwe ni cilungamo.” (Aheberi 12:11) Zipatso zimatenga nthawi kuti zipse, motelo kusintha maganizo athu kuti agwilizane na zimene mawu a Mulungu amatiphunzitsa, kumatenganso nthawi. Mwacitsanzo, ngati khalidwe lathu linalake losayenela litacititsa kuti titaye mwayi winawake wotumikila mumpingo, mtima wodikila Mulungu ungatithandize kuti tisafooke kwambili n’kufika potayilatu mtima. Pamenepa, mawu ouzilidwa a Davide otsatilawa angatilimbikitse: “Mkwiyo wa Mulungu sukhalitsa pa munthu, koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse. Usiku kumakhala kulila, koma m’mawa kumakhala kufuula ndi cisangalalo.” (Salimo 30:5) Tikakhala woleza mtima na kutsatila malangizo a Mawu a Mulungu na gulu lake, nthawi yathu ya ‘kufuula na cisangalalo’ idzafika.
Kodi Kulapa Kwenikweni N’ciani?
18 Kuti munthu wocotsedwa aonetse kuti walapa zenizeni, ayenela kupezeka ku misonkhano nthawi zonse, komanso kucita zimene akulu anamulangiza kuti azipemphela nthawi zonse na kuŵelenga Baibo. Ayenelanso kucita khama kuti apewe zinthu zimene zinam’tsogolela ku chimolo. Ngati wayesetsa kukonza ubale wake na Yehova, iye ayenela kutsimikiza kuti Yehova adzamukhululukila, ndipo akulu adzamubwezeletsa mu mpingo. Posamalila nkhani ya munthu aliyense, akulu amapenda nkhaniyo malinga na zolowetsedwamo zake. Mwakutelo, amapewa kuweluza mlandu mopanda cilungamo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 5/15 19 ¶12
Mfundo Zazikulu za Cigawo Coyamba ca Masalimo
31:23—Kodi munthu wodzitama amabwezeledwa motani zoculuka? Zimene akuchula pano kuti adzabwezeledwa ni cilango. Munthu wolungama amabwezeledwa m’njila ya cilango cocokela kwa Yehova cifukwa ca zimene waphonyetsa mwangozi. Popeza munthu wodzitama sasiya kucita zoipa, amabwezeledwa zoculuka na cilango cokhwima.—Miyambo 11:31; 1 Petulo 4:18.
APRIL 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 32-33
N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kuulula Macimo Aakulu?
w93 3/15 9 ¶7
Cifundo ca Yehova Cimatipulumutsa Kukugwilitsidwa Mwala
7 Ngati tili na mlandu waukulu cifukwa tapwanya malamulo a Mulungu, zingakhale zovuta kuulula macimo athu, ngakhale kwa Yehova. Kodi cingacitike n’ciyani zinthu zikakhala conco? Mu Salimo 32, Davide anavomeleza kuti: ‘Pamene ndinakhala chete osaulula macimo anga, mafupa anga anafooka, cifukwa tsiku lonse ndinali kuvutika mumtima mwanga. Pakuti dzanja lanu [Yehova] linali kundilemela usana na usiku. Mphamvu zanga zinauma ngati madzi m’nyengo yotentha ya cilimwe.’ (Vesi 3, 4) Kuyesa kubisa chimo lake, kunaoangitsa Davide kufooka cifukwa cakuti cikumbumtima cake cinali kumuvutitsa. Nkhawa inathetsa nyonga yake kwambili moti anakhala ngati mtengo wopanda madzi m’thawi yacilala. Mwinanso, iye anali kuvutika maganizo, kudwala komanso kukhala wosasangalala. Ngati aliyense wa ife agwela mumkhalidwe wofananawo, kodi tiyenela kucitanji?
cl 262 ¶8
Mulungu “Wokhululukila”
8 Davide atalapa ananena mawu awa: “Pamapeto pake ndinaulula chimo langa kwa inu, ndipo sindinabise colakwa canga. . . . Ndipo inu munandikhululukila zolakwa zanga ndi macimo anga.” (Salimo 32:5) Mawu akuti “munandikhululukila” amasuliwa kucokela ku mawu Aciheberi amene makamaka amatanthauza kuti “kunyamula” kapena “kutenga.” Mmene agwilitsidwila nchito pa lembali akusonyeza kucotsa “colakwa, chimo, kapena coipa.” Motelo tingati Yehova ananyamula macimo a Davide n’kuwacotsa. Mosakayikila izi zinacepetsa malingalilo amene Davide anali nawo odziona kuti anali wolakwa. (Salimo 32:3) Ifenso tingakhale n’cidalilo conse mwa Mulungu yemwe amacotsa macimo a anthu ofuna kuti awakhululukile cifukwa ca kukhulupilila kwawo nsembe ya dipo ya Yesu.—Mateyu 20:28.
w01 6/1 30 ¶1
Kulapa Komwe Kumacilitsa
Davide atavomeleza macimo ake sanadzione monga wopanda pake. Mawu ake m’masalimo omwe analemba onena za kuulula macimo, aonetsa kuti anali womasuka komanso wotsimikiza kutumikila Mulungu mokhulupilika. Mwacitsanzo, onani Salimo 32. Vesi 1 imati: “Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene macimo ake aphimbidwa.” Ngakhale chimo litakhala lalikulu bwanji, zotsatila zake zimakhala zosangalatsa ngati munthu walapa moona mtima. Njila imodzi yoonetsa kuona mtima kumeneku, ndiyo kuvomeleza zomwe tacita monga anacitila Davide. (2 Samueli 12:13) Iye sanapeze zifukwa zopeputsila kucimwa kwake kwa Yehova kapena kuyesa kuloza ena cala. Vesi 5 ikuti: “Pamapeto pake ndinaulula chimo langa kwa inu, ndipo sindinabise colakwa canga. Ndinati: ‘Ndidzaulula kwa Yehova macimo anga.’ Ndipo inu munandikhululukila zolakwa zanga ndi macimo anga.” Kulapa kwenikweni kumakhazika mtima pansi, conco munthu savutikanso na cikumbumtima cake poganiza zomwe anacita kale.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 5/15 20 ¶1
Mfundo Zazikulu za Cigawo Coyamba ca Masalimo
33:6—Kodi “mpweya” wa m’kamwa mwa Yehova n’ciyani? Mpweya umenewu ni mphamvu yomwe Mulungu amagwilitsa nchito, kapena kuti mzimu woyela, imene anagwilitsa nchito polenga miyamba yomwe timaonayi. (Genesis 1:1, 2) Umachedwa mpweya wa m’kamwa mwake cifukwa cakuti, mofanana na kupuma mwamphamvu, mzimuwu ungathe kutumizidwa kukagwila nchito kutali kwambili.
APRIL 29–MAY 5
CUMA COPEZELA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 34-35
“Nidzatamanda Yehova Nthawi Zonse”
w07 3/1 22 ¶11
Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi
11 “ Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse. Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza.” (Salimo 34:1) Popeza Davide ankakhala mothawathawa, ayenera kuti ankada nkhawa kuti azipeza bwanji zosowa za moyo wake. Koma mawu amenewa aonetsa kuti Davide anapitilizabe kukhala na mtima wofuna kulemekeza Yehova, ngakhale kuti anali na nkhawa zimenezi. Iye alidi citsanzo cabwino kwa ife tikamakumana na mavuto. Kaya tili ku sukulu, ku nchito, tili limodzi na Akhristu anzathu, kapena tikulalikila, colinga cathu cacikulu cizikhala cofuna kulemekeza Yehova. Tangoganizilani zifukwa zambili-mbili zomwe tili nazo zocitila zimenezi. Mwacitsanzo, pali zinthu zambili zomwe tingaziphunzile na kusangalala nazo m’cilengedwe ca Yehova cocititsa cidwici. Ndipo taganizilani zimene Yehova wacita pogwilitsa nchito mbali ya padziko lapansi ya gulu lake. Yehova wakhala akuseŵenzetsa anthu okhulupilika kucita zinthu zazikulu, ngakhale kuti ni opanda ungwilo. Kodi nchito za Mulungu tingaziyelekezele ni za anthu amene dzikoli limawalambila? Kodi simukugwilizana na Davide, amene analemba kuti: “Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu. Ndipo palibe nchito zilizonse zofanana ndi nchito zanu.”?—Salimo 86:8.
w07 3/1 22 ¶13
Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi
13 “Ndidzadzitamandila mwa Yehova. Ofatsa adzamva ndi kukondwela.” (Salimo 34:2) Apa, Davide sanali kudzitama cifukwa ca zinthu zimene anacita bwino. Mwacitsanzo, sanadzitame cifukwa ca mmene ananamizila mfumu ya ku Gati. Anazindikila kuti Yehova anam’teteza ali ku Gati, na kuti anathaŵa cifukwa ca thandizo lake. (Miyambo 21:1) Conco Davide sanadzitame, koma anatamanda Yehova. Zimenezi zinacititsa anthu ofatsa kuyamba kukonda Yehova. Yesu nayenso anakweza dzina la Yehova, ndipo zimenezi zinacititsanso anthu odzicepetsa na ophunzitsika kuyamba kukonda Yehova. Masiku ano, anthu ofatsa a m’mayiko onse akuloŵa mu mpingo wa padziko lonse wa Akhristu odzozedwa, womwe Yesu ndiye Mutu wake. (Akolose 1:18) Anthu ofatsawa amakhudzidwa mtima akamva dzina la Mulungu likulemekezedwa na atumiki ake odzicepetsa ndiponso akamvetsetsa uthenga wa m’Baibo mothandizidwa na mzimu woyela wa Mulungu.—Yohane 6:44; Machitidwe 16:14.
w07 3/1 23 ¶15
Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi
15 “Ndinafunsa kwa Yehova ndipo iye anandiyankha, pakuthawathawa kwanga konse iye anandilanditsa.” (Salimo 34:4) Zinthu ngati zimenezi zinali zofunika kwambili kwa Davide. Conco anawonjezela kuti: “Wosautsikayu anaitana ndipo Yehova anamva. Anamupulumutsa m’masautso ake onse.” (Salimo 34:6) Tikakhala na okhulupilila anzathu, timakhala na mipata yambili yofotokoza zinthu zolimbikitsa zosonyeza mmene Yehova watithandizila kupilila mavuto. Zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo ca okhulupilila anzathu, monga momwe zimene Davide ananena zinalimbitsila cikhulupililo ca anthu omwe anali ku mbali yake. Anthu omwe anali na Davide “anamukhulupilila [Yehova] ndipo anasangalala ndipo nkhope zawo sizinacite manyazi.” (Salimo 34:5) Iwo sanacite manyazi ngakhale kuti anali kuthawa Mfumu Sauli. Anali na cikhulupililo coti Mulungu anali na Davide, ndipo nkhope zawo zinali zosangalala. Mofanana na zimenezi, anthu amene akungophunzila kumene coonadi komanso amene akhala Akhristu kwa nthawi yaitali amadalila Yehova kuti aŵathandize. Popeza adzionela okha kuti Yehova akuŵathandiza, nkhope zawo n’zosangalala ndipo zimaonetsa kuti ni otsimikiza mtima kukhalabe okhulupilika.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06 5/15 20 ¶2
Mfundo Zazikulu za Cigawo Coyamba ca Masalimo
35:19—Kodi pempho la Davide loti asalole adani ake kum’tsinzinila likutanthauza ciyani? Kutsinzina kukanasonyeza kuti adani a Davide akusangalala cifukwa ca kuyenda bwino kwa zolinga zawo zomucitila zoipa. Davide anapempha kuti zimenezi zisacitike.