Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAY 6-12
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 36-37
“Musapse Mtima Cifukwa ca Anthu Oipa”
Kodi Cidzacokapo N’ciani Ufumu wa Mulungu Ukadzabwela?
4 Kodi zocita za anthu oipa zimatikhudza bwanji masiku ano? Mtumwi Paulo atakamba kuti masiku otsiliza ano adzakhala “nthawi yapadela komanso yovuta,” anauzilidwanso kulemba kuti: “Anthu oipa ndi acinyengo adzaipilaipilabe.” (2 Tim. 3:1-5, 13) Kodi mwaona kukwanilitsidwa kwa mawu amenewa? Ambili a ife tinacitilidwapo nkhanza na anthu oipa monga aciwawa, odana na anzawo, komanso zigaŵenga zoopsa. Ena mwa anthu amenewa amacita zoipa moonetsela. Koma ena ni aciphamaso, amabisa zoipa zimene amacita n’kumadzionetsa monga anthu acilungamo. Ngakhale kuti mwina ife sitinacitilidwepo nkhanza za conco, zocita za anthu oipa zimatikhudza ndithu. Cimatiŵaŵa kwambili tikamvela nkhanza zimene anthuwo amacitila ana, okalamba, na anthu ena ovutika. Masiku ano, anthu oipa amangocita zinthu monga vilombo kapena viŵanda. (Yak. 3:15) Koma cokondweletsa n’cakuti Mawu a Yehova amatipatsa ciyembekezo cabwino.
Yehova Amadalitsa Amene Amakhululukila Anzawo
10 Kusunga cakukhosi kumavulaza. Yehova amafuna kuti tipeze mpumulo umene umabwela tikapewa kusunga cakukhosi, kumene kuli ngati kunyamula cikatundu colema. (Ŵelengani Aefeso 4:31, 32.) Iye amatilimbikitsa kuti: “Usapse mtima ndipo uzipewa kukwiya.” (Sal. 37:8) Timapindula tikatsatila ulangizi umenewu. Kusunga cakukhosi kungativulaze kuthupi, na kutibweletsela matenda a maganizo. (Miy. 14:30) Mwacitsanzo, tikamwa poizoni, thanzi lathu n’limene limawonongeka, osati la wina. Mofananamo, tikasunga cakukhosi timadzivulaza ife eni, osati anthu amene anatikhumudwitsa. Conco, tikamakhululukila ena, timapindulitsa moyo wathu. (Miy. 11:17) Timakhala na mtendele wa maganizo, ndipo timapitiliza kutumikila Yehova.
w03 12/1 14 ¶20
‘Kondwelani mwa Yehova’
20 Ndiyeno, “ofatsa adzalandila dziko lapansi.” (Salimo 37:11a) Koma kodi “ofatsa” amenewa ndani? Liwu limene analimasulila kuti “ofatsa” licokela ku liwu limene limatanthauza “kuzunza, kucepetsa, kunyozetsa.” Inde, “ofatsa” ni anthu amene amayembekezela Yehova modzicepetsa kuti adzakonza kupanda cilungamo kumene anthu ena akuŵacitila. “Adzasangalala ndi mtendele woculuka.” (Salimo 37:11b) Ngakhale pali pano, tikupeza mtendele woculuka m’paradaiso wauzimu amene ni mpingo woona wa Cikhristu.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 445
Phili
Okhazikika, amuyaya, kapena akulu. Baibo imaonetsa kuti mapili ni okhazikika komanso amakhalapo kwamuyaya. (Yes. 54:10; Hab. 3:6; yelekezelani na Salimo 46:2.) Conco, pamene wamasalimo anakamba kuti cilungamo ca Yehova cili ngati “mapili a Mulungu” (Sal. 36:6) ayenela anali kutanthauza kuti cilungamo ca Yehova sicisintha. Kapena, popeza kuti mapili ni aakulu, mwina anali kutanthauza kuti cilungamo ca Mulungu, n’capamwamba kwambili kuposa cilungamo ca anthu. (Yelekezelani na Yesaya 55:8, 9.) Pokamba za kuthila mbale ya 7 ya mkwiyo wa Mulungu, Chivumbulutso 16:20 imati: “Mapili sanapezeke.” Izi zionetsa kuti ngakhale zinthu zazikulu ngati mapili sizingapulumuke mkwiyo wa Mulungu.—Yelekezelani na Yeremiya 4:23-26.
MAY 13-19
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 38-39
Musamadziimbe Mlandu Mopitilila Malile
Yang’anani Kutsogolo
12 Ŵelengani 1 Yohane 3:19, 20. Tonsefe timadziimba mlandu nthawi zina. Mwacitsanzo, ena amadziimba mlandu pa zoipa zimene anacita asanaphunzile coonadi. Enanso amadziimba mlandu pa zoipa zimene anacita pambuyo pa ubatizo. (Aroma 3:23) Timafuna kucita zoyenela, koma “tonsefe timapunthwa nthawi zambili.” (Yak. 3:2; Aroma 7:21-23) Koma ngakhale kuti kudziimba mlandu si cinthu cokondweletsa, kungakhaleko na ubwino wake. Cifukwa ciyani? Kungatilimbikitse kuwongolela njila zathu, na kusafuna kudzabwelezanso zolakwazo.—Aheb. 12:12, 13.
13 Komabe, zingatheke kudziimba mlandu mopitilila malile—kutanthauza kumadziimbabe mlandu ngakhale pambuyo pakuti talapa ndipo Yehova waonetsa kuti watikhululukila. Kudziimba mlandu koteloko n’kovulaza. (Sal. 31:10; 38:3, 4) Motani? Ganizilani za mlongo wina amene anapitiliza kudziimba mlandu pa macimo ake akumbuyo. Iye anati: “N’nali kuona kuti kudzipeleka kwambili potumikila Yehova kunalibe phindu, cifukwa mwina ananiweluza kale.” Ambili a ife mwina tinamvelapo monga anamvelela mlongoyu. Tifunika kudziteteza ku msampha wodziimba mlandu mopitilila malile. Tangoganizani mmene Satana angakondwele ngati tingayambe kuganiza kuti ndine wolephela ndipo Yehova ananifulatila kale, pamene iye Yehova anatikhululukila.—Yelekezelani na 2 Akorinto 2:5-7, 11.
w02 11/15 20 ¶1-2
Kodi Tingatani Kuti Masiku a Moyo Wathu Asangalatse Yehova?
MASIKU a moyo wathu amaoneka kuti ni ocepa ndiponso amatha mofulumila. Wamasalimo Davide anasinkhasinkha kufupika kwa moyo wa munthu ndipo zimenezi zinamucititsa kupemphela kuti: “Inu Yehova, ndithandizeni kuzindikila kuti moyo wanga ndi waufupi, komanso kudziŵa ciŵelengelo ca masiku anga, kuti ndidziŵe kuti moyo wanga ndi waufupi bwanji. Ndithudi, mwacepetsa masiku a moyo wanga, ndipo masiku a moyo wanga si kanthu pamaso panu.” Nkhawa ya Davide inali kuti akhale na moyo umene ungasangalatse Mulungu, mwa zokamba na zocita zake. Pokamba za kudalila kwake Mulungu, iye anati: “Chiyembekezo changa [chili mwa] inu nokha.” (Sal. 39:4, 5, 7) Yehova anamumvela. Anaonadi zimene Davide anacita ndipo anam’patsa mphoto malinga na zocita zakezo.
N’zosavuta kukhala wotanganidwa nthawi zonse na kukhala na moyo wodzala na zocita. Zimenezi zingatibweletsele nkhawa, maka-maka cifukwa cokhala na zocita zambili pamene nthawi yakuti ticite zimenezo ni yocepa kwambili. Kodi nkhawa yathu ili ngati ya Davide, yakuti tikhale na moyo umene ungasangalatse Mulungu? Kunena zoona, Yehova amationa ndipo amatipenda mosamala tonsefe. Yobu, mwamuna amene anali kuopa Mulungu anazindikila zaka pafupifupi 3,600 zapitazo kuti Yehova anaona zonse zimene anali kucita. Yobu anafunsa kuti: “Kodi ndingamuyankhe ciyani atandifunsa?” (Yobu 31:4-6, 14) Tingacititse masiku a moyo wathu kusangalatsa Mulungu ngati tiika zinthu zauzimu patsogolo, kumvela malamulo ake, na kugwilitsa nchito nthawi yathu mwanzelu.
Konzaninso Ubwenzi Wanu na Yehova
Muzipemphela kwa Yehova nthawi zonse. Atate wanu adziŵa kuti mukamapitiliza kudziimba mlandu, cingakuvuteni kupemphela kwa iye. (Aroma 8:26) Ngakhale n’conco, “muzilimbikila kupemphela,” muuzeni Yehova kuti mufunitsitsa kukhala naye paubwenzi wolimba. (Aroma 12:12) Andrej anati: “N’nali kudziimba mlandu kwambili, komanso n’nali kucita manyazi. Koma pambuyo pa pemphelo lililonse n’nali kumvelako bwino. N’nali kukhala na mtendele wamaganizo.” Ngati simudziŵa zimene mungachule m’pemphelo, phunzilani pa mapemphelo amene Mfumu Davide yolapa inapeleka, olembedwa pa Salimo 51 na 65.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Onetsani Kuti Ndinu Wodalilika
16 Kudziletsa nakonso n’kofunika kwambili kuti anthu ena azitidalila. Khalidwe limeneli limatithandiza kukhala cete pamene mtima wathu walakalaka kukamba nkhani zimene n’zacisinsi. (Ŵelengani Miyambo 10:19.) Tikamagwilitsa nchito soshomidiya, kudziletsa kwathu kungayesedwe. Tikapanda kusamala, tingafalitse nkhani zacisinsi kwa anthu oculuka pa Intaneti. Tikatelo, sitingakwanitse kuletsa anthu kuzigwilitsa nchito molakwika nkhanizo, kapena kuvulaza nazo anthu ena. Cina, kudziletsa kudzatithandiza kukhala cete anthu otsutsa akafuna kutipusitsa kuti tiulule zinthu zimene zingaike moyo wa abale na alongo athu pa ciwopsezo. Izi zingacitike pamene apolisi akutifunsa mafunso m’dziko limene nchito yathu ni yoletsedwa. Pa zocitika zimenezi komanso zina, tingatsatile mfundo ya m’Baibo yakuti: “Ndidzaphimba pakamwa panga kuti ndisalankhule.” (Sal. 39:1) Pocita zinthu na a m’banja mwathu, mabwenzi athu, abale na alongo athu, kapena wina aliyense, tiyenela kukhala odalilika. Ndipo kudalilika kumeneku kumafuna kudziletsa.
MAY 20-26
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 40-41
N’cifukwa Ciyani Ni Cinthu Canzelu Kuthandiza Anthu Ena?
Anthu Opatsa Amakhala Osangalala
16 Anthu owolowa manja sapatsa ena zinthu n’colinga cakuti anthuwo adzawabwezele zinazake m’tsogolo. Yesu anali kuganizila mfundo imeneyi pamene anati: “Ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi osaona. Ukatelo udzakhala wosangalala cifukwa alibe coti adzakubwezele.” (Luka 14:13, 14) Lemba lina limati: “Munthu wowolowa manja adzadalitsidwa.” Linanso limati: “Wosangalala ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka.” (Miy. 22:9; Sal. 41:1) Conco, tiyenela kukhala opatsa cifukwa cakuti kuthandiza ena kumatikondweletsa.
17 Pa nthawi ina, mtumwi Paulo anagwila mawu a Yesu akuti “Kupatsa kumaticititsa kukhala osangalala kwambili kuposa kulandila.” Pa nthawiyo, iye sanali kukamba za kupatsa ena zinthu zakuthupi cabe, koma anali kukambanso za kupatsa ena cilimbikitso, malangizo, komanso thandizo kwa amene akufunikila zinthu zimenezi. (Mac. 20:31-35) Mwa mawu na citsanzo cake, mtumwiyu anatiphunzitsa kuti tiyenela kudzipeleka pothandiza ena mwa kuseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu, komanso kuŵalimbikitsa na kuŵaonetsa cikondi.
18 Akatswili a zacikhalidwe ca anthu nawonso azindikila kuti kupatsa kumathandiza anthu kukhala acimwemwe. Nkhani ina inati, “anthu amakhala acimwemwe kwambili akacitila ena zabwino.” Akatswiliwo amakamba kuti kuthandiza ena n’kofunika kuti munthu akhale na umoyo “waphindu komanso wokhutilitsa, cifukwa kumakwanilitsa zosoŵa zazikulu za anthu.” Ndiye cifukwa cake nthawi zambili akatswili amalimbikitsa anthu kuti azidzipeleka pa nchito zacitukuko kuti akhale na thanzi labwino komanso acimwemwe. Izi n’zosadabwitsa kwa ise amene timakhulupilila Baibo, imene ni Mawu a Mlengi wathu wacikondi, Yehova.—2 Tim. 3:16, 17.
Yehova Adzakuthandizani Pamene Mukudwala
7 Tikadwala, Mulungu angatilimbikitse, kutipatsa nzelu komanso kutithandiza ngati mmene anacitila na atumiki ake akale. Mfumu Davide analemba kuti: “Wosangalala ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka. Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa. Yehova adzamuteteza n’kusunga moyo wake.” (Sal. 41:1, 2) Davide sanali kutanthauza kuti anthu amene amacita zinthu moganizila ovutika, sangafe. M’malomwake, anali kungotanthauza kuti Mulungu amaŵathandiza anthu otelewa. Koma kodi amaŵathandiza bwanji? Davide anati, “Yehova adzathandiza munthu woganizila wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake. Mudzamusamalila bwino kwambili pa nthawi imene akudwala.” (Sal. 41:3) Munthu amene amacita zinthu moganizila ovutika ayenela kudziŵa kuti Mulungu amaona zabwino zimene amacitazo ndiponso kukhulupilika kwake. Komanso Mulungu amatithandiza cifukwa ni amene anapanga thupi lathu m’njila yakuti lizitha kucila.
Tengelani Khalidwe la Yehova la Cifundo
17 N’zoona kuti munthu amapindula ngati acitila ena cifundo. Koma cimeneci siciyenela kukhala cifukwa cacikulu cokhalila wacifundo. Tifunika kucitila ena cifundo maka-maka cifukwa cofuna kutengela Yehova Mulungu na kum’lemekeza monga Gwelo la cikondi na cifundo. (Miy. 14:31) Iye n’citsanzo cabwino kwambili kwa ise pankhani imeneyi. Conco, tiyeni ticite zilizonse zimene tingathe kuti titengele citsanzo cake mwa kucitila ena cifundo. Tikatelo, tidzakhala pa ubwenzi wabwino na Akhristu anzathu komanso anansi athu.—Agal. 6:10; 1 Yoh. 4:16
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 16
Yehova
Nkhani zonse za m’Baibo, zimaonetsa kuti Yehova ndiye woyenela kulamulila, ndipo zimaonetsa colinga cacikulu ca Yehova Mulungu cimene ni kuyeletsedwa kwa dzina lake. Kuyeletsedwa kumeneku kutanthauza kuyeletsa dzina la Mulungu ku zitonzo zonse. Koma kuposa pamenepa, zitanthauzanso kuti angelo na anthu onse, ayenela kulemekeza dzinalo na kuliona kukhala lopatulika. Cifukwa ca zimenezi, ayenela kuvomeleza na mtima wonse kuti Yehova ndiye wolamulila wapamwamba na kumulemekeza. Ayenelanso kumutumikila cifukwa comukonda na kukondwela kucita cifunilo cake. Pemphelo la Davide kwa Yehova pa Salimo 40:5-10 lionetsa bwino mzimu wodzipeleka umenewu komanso wofunadi kuyeletsa dzina la Yehova. (Onani mmene atumwi anaseŵenzetsela mbali za Salimoli pokamba za Khristu Yesu pa Aheberi 10:5-10.)
MAY 27–JUNE 2
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 42-44
Pindulani Kwathunthu na Maphunzilo Ocokela kwa Mulungu
w06 6/1 9 ¶4
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachiwiri cha Masalmo
42:4, 5, 11; 43:3-5. Ngati sitingathe kusonkhana limodzi na mpingo wa Cikhristu kwa kanthawi cifukwa ca zinthu zina zimene sitingazisinthe, tingalimbikitsidwe tikakumbukila cimwemwe cimene tinali kukhala naco pa nthawi imene tinali kusonkhana limodzi na mpingo. Ngakhale kuti poyamba zingakulitse ululu umene tingakhale nawo cifukwa ca kusungulumwa, zingatikumbutsenso kuti Mulungu ndiye pothaŵilapo pathu ndipo tiyenela kuyembekezela iye kuti atithandize.
w12 1/15 15 ¶2
Zomwe Mungacite Kuti Muzipindula Ndiponso Kusangalala Mukamaphunzila Baibo
1 KUPEMPHELA: Coyamba tiyenela kupemphela. (Sal 42:8) N’cifukwa ciyani tikutelo? Tiyenela kuona kuti kuphunzila Mawu a Mulungu ni mbali ya kulambila kwathu. Conco tiyenela kupempha Yehova kutithandiza kuti tikhale na maganizo oyenela ndiponso kuti atipatse mzimu wake woyela. (Luka 11:13) Kupemphela tisanayambe kuphunzila kumathandiza kuti titseguke maganizo ndiponso mtima n’colinga coti tipindule mokwanila na cakudya cauzimu ca mwanaalilenji cimene tikulandila.
“Manja Anu Asakhale Olefuka”
11 Mulungu amatilimbikitsa kupitila m’maphunzilo auzimu amene timalandila pa misonkhano ya mpingo, ya dela, ya cigawo, komanso m’masukulu osiyana-siyana. Maphunzilo amenewa amatilimbikitsa kucita zabwino, kukhala na zolinga zauzimu, na kukwanilitsa nchito zathu za Cikhiristu. (Sal. 119:32) Kodi inu mumacita kulakalaka kuti mulimbikitsidwe na maphunzilo amenewa?
12 Yehova anathandiza Aisiraeli kugonjetsa Aamaleki na Aitiyopiya. Anathandizanso Nehemiya na anzake mwa kuŵapatsa mphamvu pa nchito yawo yomanganso mpanda. Mofananamo, Mulungu adzatipatsa mphamvu kuti tikhale olimba tikakumana na anthu otsutsa kapena amene alibe cidwi mu ulaliki. Adzatithandizanso kulimbana na nkhawa kuti tikwanilitse nchito yathu yolalikila. (1 Pet. 5:10) Sitiyenela kuyembekezela kuti Yehova adzatithandiza mozizwitsa. M’malomwake, tiyenela kucita mbali yathu. Tiyenela kuŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, kukonzekela na kupezeka pa misonkhano mlungu uliwonse, kucita phunzilo laumwini na kulambila kwa pabanja komanso kupemphela kwa Yehova nthawi zonse. Conco, tisalole kuti zinthu zina zititsekele njila zimene Yehova amagwilitsila nchito kuti atilimbikitse. Ngati muona kuti dzanja lanu lalefuka pa zinthu zimenezi, pemphani Mulungu kuti akuthandizeni. Mukatelo, yembekezani kuti muone mmene mzimu wake udzakupatsilani “mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zocitila zinthuzo.”—Afil. 2:13
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 1242
Mimbulu
Kaŵili-kaŵili m’Malemba, mimbulu imachulidwa m’mafanizo. Pofotokoza mavuto amene anakumana nawo, Yobu anakamba kuti “ndakhala m’bale wake wa mimbulu.” (Yobu 30:29) Pokamba za kugonjetsedwa kocititsa manyazi kwa anthu a Mulungu, mwina wamasalimo anaganizila mmene mimbulu imasonkhanila kumalo a nkhondo kuti idye anthu amene aphedwa (Sal. 68:23), anati: “Mwatiphwanya kumalo amene mimbulu imakhala.” (Sal. 44:19) Pamene a Babulo anazungulila Yerusalemu mu 607 B.C.E. m’mzindawo munagwa njala yaikulu, zimene zinacititsa kuti amayi ayambe kucitila nkhanza ana awo. Conco Yeremiya anayelekezela nkhanza za anthu a Mulungu na mmene mimbulu yaikazi imasamalila ana.—Maliro 4:3, 10.
JUNE 3-9
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 45-47
Nyimbo ya Ukwati wa Mfumu
Sangalalani Cifukwa ca Cikwati ca Mwanawankhosa!
8 Ŵelengani Salimo 45:13, 14a. Mkwatibwi akuonetsedwa kuti “ali pa ulemelelo waukulu” cifukwa ka cikwati ca mfumu. Pa Chivumbulutso 21:2, mkwatibwi akuyelekezeledwa na mzinda, Yerusalemu Watsopano, ndipo “wavala zokongola kuti akalandile mwamuna wake.” Mzinda wakumwamba umenewu uli na “ulemelelo wa Mulungu,” ndipo ukunyezimila “ngati mwala wamtengo wapatali kwambili, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.” (Chiv. 21:10, 11) Buku la Chivumbulutso limafotokoza za ulemelelo wa Yerusalemu Watsopano mocititsa cidwi. (Chiv. 21:18-21) N’cifukwa cake wamasalimo anafotokoza kuti mkwatibwi ameneyu ali na “ulemelelo waukulu.” Kuwonjezela pamenepo, cikwati cimeneci cidzacitikila kumwamba.
9 Mkwatibwi akumubweletsa kwa mwamuna wake, Mfumu Mesiya. Mwamunayu wakhala akukonzekeletsa mkwatibwi wake mwa ‘kumuyeletsa pomusambitsa m’madzi a mawu a Mulungu.’ Mkwatibwi ameneyu ni “woyela ndi wopanda cilema.” (Aef. 5:26, 27) Iye wavala bwino mogwilizana na cocitikaco. “Zovala zake ndi zagolide” ndipo “adzamubweletsa kwa mfumu atavala covala coluka.” Pa cikwati ca Mwanawankhosa, “iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimila ndi zoyela bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimila nchito zolungama za oyela.”—Chiv. 19:8.
Buku la Chivumbulutso—Mmene Likukhudzila Tsogolo Lanu
10 Kodi Yehova adzacita ciyani na kuukila koopsa kumeneku? Iye anatiuza kuti: “Ndidzakhala ndi mkwiyo waukulu.” (Ezek. 38:18, 21-23) Chivumbulutso caputala 19 imakamba zimene zidzatsatilapo. Yehova adzatumiza Mwana wake kuti akateteze anthu ake, na kuwononga adani awo. Yesu adzakhala pamodzi na “magulu ankhondo akumwamba,” omwe ni angelo okhulupilika komanso a 144,000. (Chiv. 17:14; 19:11-15) Kodi nkhondo imeneyi idzakhala na zotulukapo zotani? Anthu onse otsutsana na Yehova pamodzi na mabungwe awo adzawonongedwa kothelatu.—Ŵelengani Chivumbulutso 19:19-21.
11 Tangoganizilani mmene anthu okhulupilika padziko lapansi adzamvelela adani a Mulungu akadzawonongedwa. Idzakhala nthawi yokondweletsa ngako! Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, kumwamba kudzakhala mfuu yaikulu yacisangalalo. Koma palinso cina cidzabweletsa cimwemwe cacikulu. (Chiv. 19:1-3) Ni “ukwati wa Mwanawankhosa,” umene ni cocitika cokondweletsa kwambili cothela cochulidwa m’buku la Chivumbulutso.—Chiv. 19:6-9.
12 Kodi ukwati umenewo udzacitika liti? Nkhondo ya Aramagedo isanayambe, onse a 144,000 adzakhala kumwamba. Komabe, imeneyo sidzakhala nthawi ya ukwati wa Mwanawankhosa. (Ŵelengani Chivumbulutso 21:1, 2.) Ukwati wa Mwanawankhosa udzacitika pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, adani onse a Mulungu akadzawonongedwa.—Sal. 45:3, 4, 13-17.
it-2 1169
Nkhondo
Pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, dziko lapansi lidzakhala pa mtendele kwa zaka 1,000. Salimo limene limati “[Yehova] akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi. Wathyola uta ndi kupindapinda mkondo, ndipo wawocha pamoto magaleta ankhondo,” linakwanilitsidwa koyamba pamene Mulungu anabweletsa mtendele m’dziko la Aisiraeli mwa kuwononga zida zonse za nkhondo za adani awo. Pa Aramagedo, Khristu akadzagonjetsa anthu omwe amayambitsa nkhondo, anthu padziko lonse lapansi adzakondwela na mtendele weniweni. (Sal. 46:8-10) Anthu amene adzalandila moyo wosatha, ni anthu amene “adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndipo mikondo yawo adzaisula kuti ikhale zida zosadzila mitengo,” ndipo anthuwo “sadzaphunzilanso nkhondo.” “Cifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena zimenezi.”—Yes. 2:4; Mika 4:3, 4.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Kodi Cidzacokapo N’ciani Ufumu wa Mulungu Ukadzabwela?
9 N’ciyani cidzaloŵa m’malo mwa mabungwe acinyengo? Kodi padziko padzakhala dongosolo lililonse pambuyo pa Aramagedo? Baibo imatiuza kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezela mogwilizana na lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala cilungamo.” (2 Pet. 3:13) Kumwamba kwakale na dziko lakale zikutanthauza maboma oipa na anthu oipa amene amalamulidwa na mabomawo. Zonsezi sizidzakhalakonso. Nanga n’ciyani cidzakhalapo pambuyo pakuti zimenezi zawonongedwa? Mawu akuti “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” aonetsa kuti kudzakhala boma latsopano na anthu abwino amene adzalamulidwa na bomalo. Ufumu wa Mulungu, umene Mfumu yake ni Yesu Khristu, udzalamulila mogwilizana na cifunilo ca Yehova, Mulungu wadongosolo. (1 Akor. 14:33) Conco, “dziko lapansi latsopano” lidzakhala ladongosolo. Padzakhala anthu abwino otsogolela. (Sal. 45:16) Iwo azidzayang’anilidwa na Khristu na olamulila anzake okwana 144,000. Mabungwe onse oipa adzaloŵedwa m’malo na boma limodzi la Ufumu wa Mulungu, labwino komanso logwilizana. Nthawi imeneyo idzakhala yokondweletsa ngako!
JUNE 10-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 48-50
Makolo—Thandizani Banja Lanu Kudalila Kwambili Gulu la Yehova
Kulambila Koona Kudzawonjezela Cimwemwe Canu
11 Timalambila Yehova tikamaŵelenga Mawu ake, na kuphunzitsa ana athu za iye. Aisiraeli okhulupilika anali kuphunzitsa ana awo za Yehova na ubwino wake. Nafenso, tiyenela kupatula nthawi yoŵelenga Mawu a Mulungu. Iyi ni mbali ya kulambila Yehova, ndipo imatithandiza kumuyandikila. (Sal. 73:28) Tikamaphunzila pamodzi monga banja, tingathandize ana athu kukhala pa ubale wabwino na Atate wathu wacikondi wakumwamba.—Ŵelengani Salimo 48:13.
w11 3/15 19 ¶5-7
Zinthu Zimene Mungakondwele Nazo
“Gubani mozungulila Ziyoni. Zungulirani mzinda wonsewo, ŵelengani nsanja zake. Ganizilani mofatsa za mpanda wake wolimba. Yendelani nsanja zake zokhala ndi mpanda woliomba, kuti mudzafotokozele mibadwo yam’tsogolo.” (Sal. 48:12, 13) Pamenepa, wamasalimo analimbikitsa Aisiraeli kuti azikaona mzinda wa Yerusalemu. Kodi mukuganiza kuti mabanja a Ciisiraeli amene anapita kumzinda wopatulikawo kukacita nawo zikondwelelo za pacaka ndiponso kuona kacisi wokongola kwambili anali kumva bwanji akabwelela kwawo? Iwo ayenela kuti anali kulimbikitsidwa “[kufotokozela] mibadwo yam’tsogolo” zimene anaonazo.
Taganizilani za mfumukazi ya ku Sheba imene poyamba inali kukayikila zimene inamva zokhudza ulamulilo wapamwamba wa Solomo ndiponso nzelu zake zodabwitsa. Kodi n’ciyani cinathandiza mfumukaziyi kukhulupilila zimene inamvazo? Mfumukaziyi inati: “Sindinakhulupilile zimene ndinauzidwa mpaka pamene ndabwela n’kuona ndi maso anga.” (2 Mbiri 9:6) N’zoona kuti zimene timaona na ‘maso athu’ zimatikhudza kwambili.
Kodi mungathandize bwanji ana anu kuona na ‘maso awo’ zinthu zocititsa cidwi m’gulu la Yehova? Ngati pali ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova pafupi na kwanu, mungacite bwino kukaiona. Mwacitsanzo, Mandy na Bethany ni atsikana amene anakulila m’dela lomwe lili pa mtunda wa makilomita 1,500 kucokela ku Beteli ya m’dziko lawo. Koma makolo awo anali kukonza zoti azikaona malowo maka-maka pamene anawa anali kukula. Atsikanawo anati: “Tisanapite ku Beteli tinali kuganiza kuti ni malo osasangalatsa a anthu okalamba okha-okha. Koma tinakumana na acinyamata amene anali kutumikila Yehova mwakhama komanso mosangalala. Tinaona kuti gulu la Yehova silinali kungopezeka m’dela lathu lokha ndipo ulendo uliwonse umene tinali kupita ku Beteli tinali kulimbikitsidwa kwambili mwauzimu.” Mandy na Bethany ataona bwino-bwino gulu la Mulungu analimbikitsidwa kucita upainiya ndipo kenako anaitanidwa kukatumikila ku Beteli kwa kanthawi.
w12 8/15 12 ¶5
Muzicita Zinthu Monga Nzika za Ufumu
5 Ayenela kuphunzila mbili ya dzikolo. Munthu amene akufuna kukhala nzika ya dziko linalake angafunike kudziŵa zinthu zina zokhudza mbili ya dzikolo. Nawonso anthu ofuna kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu ayenela kuphunzila zambili zokhudza mbili yake. Ana a Kora, amene anali kutumikila mu Isiraeli, anapeleka citsanzo cabwino pa nkhaniyi. Iwo anali kukonda kwambili mzinda wa Yerusalemu na malo ake olambilila ndipo anali kukonda kuuza ena mbili ya mzindawu. Cimene cinali kuŵacititsa cidwi si kukongola kwa mzindawu koma zimene mzindawo komanso malo ake olambilila zinali kuimila. Yerusalemu anali “mzinda wa Mfumu Yaikulu” cifukwa cakuti anthu anali kulambila Yehova ndiponso kuphunzila Cilamulo cake kumeneko. Komanso Yehova anali kukomela mtima anthu olamulidwa na Mfumu ya ku Yerusalemu. (Ŵelengani Salimo 48:1, 2, 9, 12, 13.) Kodi nanunso mumakonda kuphunzila na kuuzako ena mbili ya anthu a Yehova? Mudzayamba kuyamikila kwambili Ufumu wa Mulungu mukamaphunzila zambili zokhudza anthu a Mulungu ndiponso mmene Yehova amaŵathandizila. Izi zidzakuthandizani kukhala na mtima wofuna kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu.—Yer. 9:24; Luka 4:43
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2 805
Cuma
Pokhala mtundu wotukuka, Aisiraeli anali kusangalala kudya komanso kumwa (1 Maf. 4:20; Mlal. 5:18, 19), ndipo cuma cawo cinawateteza ku mavuto obwela cifukwa ca umphamwi. (Miy. 10:15; Mlal. 7:12) Komabe, ngakhale kuti Yehova anali kufuna kuti Aisiraeli azikondwela na cuma cimene anali naco cifukwa cogwila nchito molimbika (yelekezelani na Miy. 6:6-11; 20:13; 24:33, 34), iye anaŵacenjeza za kuopsa komuiwala monga Gwelo la cuma cawo na kuyamba kudalila cuma cimeneco. (Deut. 8:7-17; Sal. 49:6-9; Miy. 11:4; 18:10, 11; Yer. 9:23, 24) Iwo anakumbutsidwa kuti cuma n’cosakhalitsa (Miy. 23:4, 5), sicingapelekedwe mong dipo kwa Mulungu kuwombola munthu ku imfa (Sal. 49:6, 7), ndipo sicingathandize akufa (Sal. 49:16, 17; Mlal. 5:15). Anaonetsedwa kuti akamakondesetsa cuma angamacite zinthu zacinyengo na kutaya ciyanjo ca Yehova. (Miy. 28:20; Yer. 5:26-28; 17:9-11.) Analimbikitsidwanso kuti azilemekeza “Yehova ndi zinthu [zawo] zamtengo wapatali.”—Miy. 3:9.
JUNE 17-23
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 51-53
Zimene Mungacite Kuti Mupewe Macimo Akulu-akulu
Kodi Tingauteteze Bwanji Mtima Wathu?
4 Pa Miyambo 4:23, liwu lakuti “mtima” litanthauza ‘umunthu wamkati.’ (Ŵelengani Salimo 51:6, mawu a m’munsi.) M’mawu ena, “mtima” uphatikizapo zimene timaganiza, mmene timamvelela, zolinga zathu, komanso zimene timalakalaka. “Mtima” ni umunthu wathu weniweni wamkati, osati cabe maonekedwe akunja.
5 Umunthu wamkati timafunika kuusamalila. Kuti timvetsetse kufunika kocita zimenezi, tiyeni tiyelekezele na thanzi lathu. Coyamba, kuti tikhalebe na thanzi labwino timafunika kudya zakudya zopatsa thanzi, komanso kucita maseŵela olimbitsa thupi kaŵilikaŵili. Mofananamo, kuti tikhalebe athanzi mwauzimu, timafunika kudya cakudya cauzimu. Cinanso, nthawi zonse timafunika kucita zinthu zoonetsa kuti tili na cikhulupililo mwa Yehova. Ndipo tingaonetse kuti tili na cikhulupililo mwa kuseŵenzetsa zimene timaphunzila, komanso kuuzako ena zimene timakhulupilila. (Aroma 10:8-10; Yak. 2:26) Caciŵili, nthawi zina tingapusitsike na maonekedwe akunja a munthu, n’kuganiza kuti ni wathanzi, pamene m’thupi mwake muli matenda. Mofananamo, tingakhale na pulogilamu yocita zauzimu, n’kumaganiza kuti tili na cikhulupililo colimba. Koma pa nthawi imodzimodzi, zilakolako zoipa zingakhale kuti zikukula mu mtima mwathu. (1 Akor. 10:12; Yak. 1:14, 15) Tizikumbukila kuti Satana amafuna kuipitsa mtima wathu mwa kutipangitsa kutengela maganizo ake.
Tingathe Kupewa Ciwelewele
5 Tiyenela kupemphela kwa Yehova kuti atithandize kucotsa maganizo oipa. Kucita zimenezi kumaonetsa kuti timamudalila kwambili. Tikamayandikila Yehova m’pemphelo, nayenso amatiyandikila. Iye amatipatsa mzimu woyela moolowa manja, umene umatithandiza kukaniza maganizo oipa kuti tikhalebe oyela. Conco, tiyenela kuuza Mulungu m’pemphelo kuti timafunitsitsa kusinkhasinkha zinthu zimene zimamukondweletsa. (Sal. 19:14) Kodi timamupempha modzicepetsa kuti atifufuze na kuona ngati tili na zilakolako zoipa zimene ‘zingaticititse kuyenda m’njila yoipa’ na kucita chimo? (Sal. 139:23, 24) Kodi timamupempha nthawi zonse kuti atithandize kukhalabe okhulupilika pamene takumana na ciyeso?—Mat. 6:13.
6 Tikalibe kuphunzila za Yehova, mwina tinali kucita zinthu zimene iye amadana nazo, ndipo mwina tikali kulimbana na zilakolako zoipa. Yehova angatithandize kusintha na kuyamba kumutumikila m’njila imene amavomeleza. Mwa citsanzo, Mfumu Davide atacita cigololo na Batiseba, anapempha Yehova kuti: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo sinthani mmene ndimaganizila kuti ndikhale wokhulupilika.” (Sal. 51:10, 12) Conco, ngati tikali kulimbana na zilakolako zoipa, Yehova angatithandize kukhala na mtima wofunitsitsa kumvela malamulo ake na kucita zinthu zoyenela. Iye angatithandizenso kulamulila maganizo athu opanda ungwilo.—Sal. 119:133.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 644
Doegi
Anali Mwedomu ndipo anali mkulu wa abusa a Mfumu Sauli. (1 Sam. 21:7; 22:9) Doegi ayenela kuti anasintha n’kukhala Mwiisiraeli. Doegi anali kuona pamene Mkulu wa Ansembe Ahimeleki anapatsa Davide mkate wacionetselo komanso lupanga la Goliyati. Patapita nthawi, pamene Sauli anali kuuza atumiki ake za ciwembu cimene anakonzela Davide, Doegi anaulula zimene anaona ku Nobu. Pambuyo poitanitsa mkulu wa ansembe na ansembe ena ku Nobu, komanso atafunsa mafunso Ahimeleki, Sauli analamula asilikali othamanga kuti aphe ansembe onse. Asilikaliwo atakana kumvela lamuloli la Sauli, Doegi sanazengeleze kupha ansembe okwanila 85. Kuwonjezela pa cinthu coipa cimeneci, Doegi anaseselatu mzinda wonse wa Nobu, anapha anthu onse a mmenemo kuyambila ana mpaka okalamba, anapha ngakhale ziweto zonse.—1Sa 22:6-20.
Monga mmene mawu apamwamba a Salimo 52 aonetsela, pokamba za Doegi, Davide analemba kuti: “Lilime lako limene ndi lakuthwa ngati lezala, limakonza ciwembu komanso kucita zacinyengo. Umakonda kwambili zinthu zoipa kuposa zabwino, umakonda kwambili kunama kuposa kulankhula zoona. Umakonda mawu onse opweteka ena, iwe amene lilime lako limalankhula zacinyengo.”—Sal. 52:2-4.
JUNE 24-30
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO 54-56
Mulungu Ali Kumbali Yanu
w06 8/1 22 ¶10-11
Khalani Anzeru mwa Kuopa Mulungu
10 Panthawi ina, Davide anapita kwa Akisi, mfumu ya mzinda wa Afilisti wa Gati, kwawo kwa Goliyati. (1 Samueli 21:10-15) Atumiki a mfumuyo ananena kuti Davide ni mdani wa mtundu wawo. Kodi Davide anatani zinthu zitafika poopsa conci? Iye anapemphela kwa Yehova na mtima wonse. (Salimo 56:1-4, 11-13) Ngakhale kuti anacita kufika ponamizila misala, Davide anali kudziŵa kuti kwenikweni Yehova ndiye anamuwombola podalitsa nzelu imeneyi. Davide anadalila Yehova na mtima wonse, kusonyeza kuti analidi munthu woopa Mulungu.—Salimo 34:4-6, 9-11.
11 Monga Davide, ifenso tingaonetse kuti timaopa Mulungu podalila lonjezo lake lakuti atithandiza kuthana na mavuto athu. Davide anati: “Lola kuti Yehova akutsogolele panjila yako, uzimudalila ndipo iye adzakuthandiza.” (Salimo 37:5) Zimenezi sizikutanthauza kuti mavuto athuwo timangomusiyila Yehova kuti iyeyo ndiye athane nawo ifeyo n’kungopinda manja basi, osacitapo ciliconse. Davide sanangopemphela kuti Mulungu amuthandize n’kulekela pomwepo basi. Koma anagwilitsa nchito mphamvu ndiponso nzelu zimene Yehova anam’patsa n’kuthana na vuto lakelo. Komatu Davide anali kudziŵa kuti zocita za munthu payekha sizingakhale zodalilika. Ifenso tizidziŵa zimenezi. Tikacita mbali yathu na mphamvu zathu zonse, tiyenela kusiya zonse m’manja mwa Yehova. Kwenikweni, nthawi zambili sipakhala ciliconse coti tingacite kupatulapo kudalila Yehova basi. Imeneyi ndiyo nthawi yakuti ifeyo patokha tionetse kuti timaopadi Mulungu. Tingalimbikitsidwe na mawu amene Davide ananena mocoka pansi pa mtima akuti: “Anthu amene amaopa Yehova ndi amene amakhala naye pa ubwenzi wolimba.”—Salimo 25:14.
cl 243 ¶9
Palibe Cikhoza “Kutisiyanitsa Ife ndi Cikondi ca Mulungu”
9 Yehova amayamikila kupilila kwathu. (Mateyu 24:13) Kumbukilani kuti Satana amafuna mutam’kana Yehova. Tsiku lililonse limene mumakhulupilikabe kwa Yehova mumathandiza kuyankha zotonza za Satana. (Miyambo 27:11) Nthawi zina kupilila kumakhala kovuta kwambili. Matenda, mavuto a zacuma, kuvutika maganizo, ndiponso mavuto ena zingakhale ziyeso za tsiku na tsiku. Tingalefukenso cifukwa cakuti zimene tikuyembekezela zikucedwa kucitika. (Miyambo 13:12) Kupilila pamene tikumana na mavuto otelowo n’kwamtengo wapatali kwambili kwa Yehova. Ndico cifukwa cake Mfumu Davide anapempha Yehova kuti amusungile misozi yake “m’thumba . . . lacikopa.” Ali na cidalilo anawonjezela kuti: “Kodi misozi yanga sinalembedwe m’buku lanu?” (Salimo 56:8) Inde, Yehova amasunga ndiponso amakumbukila misozi yonse na kuvutika konse kumene timapilila nako pokhalabe okhulupilika kwa iye. Misoziyo limodzi na kuvutikako ni zamtengo wapatali m’maso mwake.
Cikondi ca Yehova Cimatithandiza Kugonjetsa Mantha
16 Satana amadziŵa kuti moyo wathu timaukonda. Iye amakamba kuti tingalolele kutaya ciliconse—ngakhale ubwenzi wathu na Yehova—cabe kuti titeteze moyo wathu. (Yobu 2:4, 5) Limeneli ni bodza lamkunkhuniza! Komabe, popeza kuti Satana “ali ndi njila yobweletsela imfa,” amagwilitsa nchito mantha athu acibadwa oopa imfa pofuna kutipangitsa kumusiya Yehova. (Aheb. 2:14, 15) Nthawi zina, anthu amene ali ku mbali ya Satana amaopseza anthu a Yehova kuti adzawapha ngati saleka kutumikila Mulungu. Nthawi zinanso, tikadwala matenda aakulu, iye angatengelepo mwayi wotipangitsa kuphwanya malamulo a Mulungu. Madokotala kapena acibale amene si Mboni angatikakamize kuti tilole kuikidwa magazi, kumene kungakhale kuphwanya lamulo la Mulungu. Kapena, wina angatinyengelele kuti tilandile cithandizo ca mankhwala cosemphana na mfundo za m’Malemba.
17 Olo kuti sitifuna kufa, tidziŵa kuti Yehova sadzaleka kutikonda ngakhale timwalile. (Ŵelengani Aroma 8:37-39.) Mabwenzi a Yehova akamwalila, iye amaŵakumbukilabe, ngati kuti akali moyo. (Luka 20:37, 38) Amacita kulakalaka kuŵaukitsa. (Yobu 14:15) Yehova anapeleka malipilo apamwamba kwambili kuti ife ‘tikakhale na moyo wosatha.’ (Yoh. 3:16) Tidziŵa kuti Yehova amatikonda kwambili komanso amatisamalila. Conco tikadwala, kapena akatiopseza kuti adzatipha, tisamusiye Yehova. M’malo mwake, tiyenela kutembenukila kwa iye kuti atitonthoze, atipatse nzelu, ndiponso mphamvu.—Sal. 41:3.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1 857-858
Kudziŵilatu Zamtsogolo
Kupanduka kwa Yudasi Isikariyoti kunakwanilitsa ulosi wa m’malemba komanso kunaonetsa kuti Yehova na Mwana wake amakwanitsa kudziŵilatu zamtsogolo. (Sal. 41:9; 55:12, 13; 109:8; Mac. 1:16-20) Ngakhale n’telo sitinganene kuti Mulungu anakonzelatu zakuti Yudasi adzapanduka. Maulosi anakambilatu kuti bwenzi lokondeka la Yesu ni limene lidzamupeleka, koma sanakambiletu kuti bwenzilo lidzakhala ndani. Cina, mfundo za m’Baibo sizigwilizana na zakuti Mulungu anakonzelatu zocita za Yudasi. Mouzilidwa na Mulungu, mtumwi Paulo anaika lamulo ili: “Usafulumile kuika munthu aliyense pa udindo, kapena kugaŵana ndi anthu ena macimo awo. Pitiliza kukhala ndi khalidwe loyela.” (1 Tim. 5:22; yelekezelani na 3:6.) Poonetsa nkhawa imene anali nayo kuti asankhe atumwi 12 mwanzelu komanso moyenela, Yesu anapemphela usiku wonse kwa Atate wake asanapange cisankho. (Luka 6:12-16) Ngati Yudasi anasankhidwilatu kuti ndiye adzapeleke Yesu, pakanakhala kusiyana pakati pa malangizo a Mulungu na citsogozo cake poyankha pempho la Yesu. Ndipo malinga na lamulo, ndiye kuti Mulungu akanacimwila naye limodzi Yudasi.
Conco, n’zoonekelatu kuti pamene Yudasi anali kusankhidwa kukhala mtumwi, mtima wake sunaonetse khalidwe lililonse la kupanduka. Iye analola kuti mumtima mwake ‘mutuluke muzu wapoizoni’ umene unamuwononga. Iye anapanduka na kuleka kucita cifunilo ca Mulungu. Anayamba kucita zofuna za Mdyelekezi, zimene zinamupangitsa kukhala wakuba komanso wacinyengo. (Aheb. 12:14, 15; Yoh. 13:2; Mac. 1:24, 25; Yak. 1:14, 15) Maganizo oipa amenewa atakula, Yesu anatha kuona za mumtima wa Yudasi na kukambilatu kuti adzamupeleka.—Yoh. 13:10, 11.