LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr24 September masa. 1-13
  • Malifalensi a Kabuku ka “Umoyo na Utumiki”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka “Umoyo na Utumiki”
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2024
  • Tumitu
  • SEPTEMBER 2-8
  • SEPTEMBER 9-15
  • SEPTEMBER 16-22
  • SEPTEMBER 23-29
  • SEPTEMBER 30–OCTOBER 6
  • OCTOBER 7-13
  • OCTOBER 14-20
  • OCTOBER 21-27
  • OCTOBER 28–NOVEMBER 3
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2024
mwbr24 September masa. 1-13

Malifalensi a Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki

© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

SEPTEMBER 2-8

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 79-81

Onetsani Kuti Mumakonda Dzina la Yehova la Ulemelelo

w17.02 9 ¶5

Dipo​—‘Mphatso Yangwilo’ Yocokela kwa Atate

5 Nanga ise tingaonetse bwanji kuti timaikonda dzina la Yehova? Tingaonetse mwa zocita zathu. Yehova afuna kuti tizikhala oyela. (Ŵelengani 1 Petulo 1:15, 16.) Izi zitanthauza kuti tiyenela kulambila Yehova yekha cabe, ndi kumumvela na mtima wathu wonse. Ngakhale pamene tizunzidwa, timayesetsa mmene tingakwanitsile kukhala moyo mogwilizana ndi mfundo ndi malamulo ake olungama. Mwa zocita zathu zabwino, timaonetsa kuwala kwathu ndi kucititsa kuti dzina la Yehova lilemekezeke. (Mat. 5:14-16) Pokhala anthu oyela, timaonetsa mwa zocita zathu kuti malamulo a Yehova ni abwino, ndi kuti zokamba za Satana n’zabodza. Tikalakwa, timalapa moona mtima ndi kuleka kucita zinthu zosalemekeza Yehova.​—Sal. 79:9.

ijwbv 3 ¶4-5

Aroma 10:13​—“Adzaitana pa Dzina la Ambuye”

M’Baibo, mawu akuti ‘kuitana pa dzina la Yehova’ amatanthauza zambili osati cabe kudziŵa dzina la Mulungu na kuliseŵenzetsa pomulambila. (Salimo 116:12-14) Mawuwa amatanthauzanso kuti tiyenela kukhulupilila Mulungu na kumudalila kuti adzatithandiza.​—Salimo 20:7; 99:6.

Yesu Khristu anali kuona kuti dzina la Mulungu n’lofunika kwambili. Mawu ake oyamba m’pemphelo la citsanzo anali akuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.” (Mateyu 6:9) Yesu anaphunzitsanso kuti tiyenela kum’dziŵa Yehova, kumumvela, na kum’konda kuti tikapeze moyo wosatha.​—Yohane 17:3, 6, 26.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2-E 111

Yosefe

Dzina la Yosefe Ni Lolemekezeka. Popeza Yosefe anali na udindo wolemekezeka pakati pa ana a Yakobo, mpake kuti nthawi zina dzina lake linali kugwilitsidwa nchito pochula mtundu wonse wa Aisiraeli, (Sal. 80:1) kapena pochula aja amene anapanga ufumu wa kumpoto. (Sal. 78:67; Amosi 5:6, 15; 6:6) Dzina lake lilinso na malo olemekezeka m’maulosi a m’Baibo. M’masomphenya aulosi amene Ezekieli anaona, Yosefe anali kudzalandila zigawo ziŵili monga colowa. (Ezek. 47:13) Geti limodzi la mzinda wochedwa “Yehova Ali Kumeneko” limadziŵika na dzina lakuti Yosefe. (Ezek. 48:32, 35) Ulosi wokamba za kugwilizanitsanso anthu a Yehova, umaonetsa kuti Yosefe adzakhala mtsogoleli wa mbali imodzi ya mtunduwo, ndipo Yuda adzakhala mtsogoleli wa mbali inayo. (Ezek. 37:15-26) Obadiya analosela kuti “a m’banja la Yosefe” adzatengako mbali powononga “a m’banja la Esau.” (Obad. 18) Ndipo Zekariya ananenelatu kuti Yehova adzapulumutsa “nyumba ya Yosefe.” (Zek. 10:6) M’malo mwa Efuraimu, Yosefe ndiye akuchulidwa pa m’ndandanda wa mafuko a Isiraeli wauzimu.​—Chiv. 7:8

Kuchulidwa kwa Yosefe pa Chivumbulutso 7:8, kuonetsa kuti ulosi umene Yakobo anakamba asanamwalile unali kudzakwanilitsidwa pa Isiraeli wauzimu. Conco n’zocititsa cidwi kuti Wamphamvu wa Yakobo, Yehova Mulungu, anapeleka Khristu Yesu monga M’busa Wabwino amene anapeleka moyo wake cifukwa ca “nkhosa.” (Yoh. 10:11-16) Khristu Yesu ndiyenso mwala wapakona wa kacisi wa Mulungu amene ni Isiraeli wauzimu. (Aef. 2:20-22; 1 Pet. 2:4-6) Ndipo M’busa komanso Mwala ameneyu ali na Mulungu Wamphamvuzonse.​—Yoh. 1:1-3; Mac. 7:56; Aheb. 10:12; yelekezelani na Gen. 49:24, 25.

SEPTEMBER 9-15

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 82-84

Muziyamikila Mwayi wa Utumiki Umene Muli Nawo

wp16.6 8 ¶2-3

Phunzilani ku Mbalame za M’mlenga-lenga

Anthu okhala ku Yerusalemu anali kuzidziŵa bwino mbalame zochedwa namzeze (ena amati nyamkalema), zimene nthawi zambili zimamanga zisa munsi mwa mtenje wa nyumba. Zina mwa mbalame zimenezi zinali kumanga zisa m’kacisi amene Solomo anamanga. N’zosakayikitsa kuti mbalame zimene zinali kumanga zisa zawo pa kacisi caka ciliconse, zinali kukhala zotetezeka ndipo zinali kulela ana awo popanda cosokoneza.

Wolemba Salimo 84, amene ndi mmodzi wa ana a Kora, anali kutumikila pa kacisi wiki imodzi pa miyezi 6 iliyonse. Iye anali kuona zisa za anamzeze pa kacisi. Iye analaka-laka kukhala monga namzeze amene anali na malo okhalitsa pa nyumba ya Yehova. Anakamba kuti: “Inu Yehova wa makamu, ine ndimakondadi cihema canu cacikulu! Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookelatu cifukwa colakalaka mabwalowo . . . Ngakhale mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu. Namzeze wadzimangila cisa cake pamenepo, ndi kuikamo ana ake!” (Salimo 84:1-3) Kodi ife pamodzi ndi ana athu timalaka-laka kuti nthawi zonse tizisonkhana pamodzi na anthu a Mulungu monga anacitila wamasalimo?​—Salimo 26:8, 12

w08-CN 7/15 30 ¶3-4

Musadzipanikize, Ndipo Mudzakhala Achimwemwe

Tingakhale ndi malile pa zimene tingacite potumikila Yehova cifukwa ca ukalamba kapena matenda. Ngati ndinu kholo, mungaone ngati simukupindula ndi phunziro laumwini kapena misonkhano yacikhristu cifukwa mumathela nthawi ndi mphamvu zanu mukusamalila ana. Komabe kodi n’kutheka kuti nthawi zina mumalephela kuona zimene mungakwanitse cifukwa congoganizila kuti ndinu wolephela?

Kale, zaka zikwi zambili zapitazo, Mlevi wina anakhumba zinthu zomwe sizikanatheka. Iye anali ndi mwayi wotumikira pa kacisi milungu iŵili pacaka. Komabe, anafuna kuti azikhala pafupi ndi guwa la nsembe moyo wake wonse, ndipo zimenezo zinali zotamandika. (Sal. 84:1-3) Kodi n’ciyani cinathandiza munthu wokhulupilikayu kukhutila ndi mwayi umene anali nawo? Anazindikila kuti kukhala m’mabwalo a kacisi ngakhale tsiku limodzi ndi mwayi wapadela kwambili. (Sal. 84:4, 5, 10) Ifenso, m’malo mongoganizila zimene sitingathe kuchita, tizizindikila ndiponso kuyamikila zinthu zimene tingathe kucita.

w20.01 17 ¶12

Yehova Mulungu Wathu Amationa Kuti Ndife Ofunika!

12 Ngati mukudwala, dziŵani kuti Yehova amaona mavuto amene mukupitamo. Conco, m’pempheni kuti akuthandizeni kuona mavutowo m’njila yoyenela. Ndiyeno, ŵelengani Baibo kuti mupeze mawu abwino amene Yehova anaikamo kuti atilimbikitse. Ŵelengani mosamala mavesi amene amaonetsa kuti Yehova amakonda kwambili atumiki ake. Mukacita zimenezi, mudzaona kuti Yehova amakomela mtima atumiki ake onse amene amam’tumikila mokhulupilika.​—Sal. 84:11.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1-E 816

Mwana Wamasiye

Ana amasiye anali kukhala osatetezeka, ndipo cinali cosavuta anthu kungowanyalanyaza. Pa cifukwa cimeneci, Yehova anaseŵenzetsa mawu akuti “mwana wamasiye” pofotokoza mlingo wa kulungama kapena kupanduka kwa Aisiraeli. Mtunduwo ukamacita bwino kuuzimu, ana amasiye anali kusamalidwa. Koma kupanda cilungamo kukaculuka, ana amasiye anali kunyalanyazidwa. Izi zinali kuonetsa kuti mtunduwo wayamba kuloŵelela makhalidwe oipa. (Sal. 82:3; 94:6; Yes. 1:17, 23; Yer. 7:5-7; 22:3; Ezek. 22:7; Zek. 7:9-11; Mal. 3:5) Yehova anali kutembelela anthu opondeleza ana amasiye. (Deut. 27:19; Yes. 10:1, 2) Iye ananena kuti ni Mtetezi (Miy. 23:10, 11), Mthandizi (Sal. 10:14), komanso Tate (Sal. 68:5) wa ana otelowo. Iye ndiye amawaweluzila milandu (Deut. 10:17, 18), kuŵaonetsa cifundo (Hos. 14:3), kuŵathandiza (Sal. 146:9), na kuŵasamalila.​—Yer. 49:11.

Akhristu oona amadziŵika cifukwa coganizila akazi amasiye komanso ana amasiye. Yakobo analembela Akhristu anzake kuti: “Kulambila koyela komanso kosadetsedwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalila ana amasiye ndi akazi amasiye amene akukumana ndi mavuto komanso kupewa kuti dzikoli likucititseni kukhala ndi banga.”​—Yak 1:27.

SEPTEMBER 16-22

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 85-87

Pemphelo Limatithandiza Kupilila

w12-CN 5/15 25 ¶10

Kodi Mukuonetsa Ulemerero wa Yehova?

10 ‘Kulimbikila kupemphela’ kungatithandizenso kuonetsa ulemelelo wa Mulungu. (Aroma 12:12) Tifunika kupemphela kwa Yehova kuti atithandize kumutumikila m’njila yoyenela. Tiyenela kumupempha kuti atipatse mzimu woyela, atithandize kukhala ndi cikhulupililo camphamvu, kulimbana ndi mayeselo ndiponso kukhala ndi luso lotha “kufotokoza bwino mawu a coonadi.” (2 Tim. 2:15; Mat. 6:13; Luka 11:13; 17:5) Mofanana ndi mwana amene amadalila bambo wake, ifenso tiyenela kudalila Yehova yemwe ndi Atate wathu wakumwamba. Ngati titamupempha kuti atithandize kumutumikila bwino, tingakhulupilile kuti adzatithandizadi. Tisamaganize kuti mapemphelo athu amamuvutitsa. Tikamapemphela tiyenela kumutamanda, kumuthokoza ndiponso kumupempha kuti atithandize, makamaka tikakhala pa mayeselo. Tiyenelanso kumupempha kuti atithandize kumutumikila m’njila imene imalemekeza dzina lake loyela.​—Sal. 86:12; Yak. 1:5-7.

w23.05 13 ¶17-18

Mmene Yehova Amayankhila Mapemphelo Athu

17 Ŵelengani Salimo 86:6, 7. Wamasalimo Davide anali wotsimikiza kuti Yehova anamva komanso kuyankha mapemphelo ake. Inunso mungakhale na cidalilo cimeneco. Zitsanzo zimene takambilana m’nkhani ino, zatitsimikizila kuti Yehova adzatipatsa nzelu komanso mphamvu zofunikila kuti tipilile. Iye angaseŵenzetse banja lathu lauzimu, kapena aja amene sam’lambila kuti atithandize.

18 Ngakhale kuti si nthawi zonse pamene Yehova angayankhe mapemphelo athu mmene tifunila, tidziŵa kuti amayankhabe. Iye amatipatsa zimene tikufunikila komanso panthawi yake. Conco musaleke kupemphela, muli na cidalilo cakuti Yehova adzakusamalilani palipano, komanso kuti ‘adzakhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse’ m’dziko latsopano.​—Sal. 145:16.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1-E 1058 ¶5

Mtima

Kutumikila na “Mtima Wathunthu.” Mtima weniweni uyenela kukhala wathunthu kuti ugwile bwino nchito. Koma mtima wophiphilitsa ungakhale wogaŵanika. Davide anapemphela kuti: “Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu,” kuonetsa kuti mtima wa munthu ungakhale wogaŵanika pa zimene amakonda na kuopa. (Sal. 86:11) Munthu wotelo angakhale kuti mtima wake si wathunthu, kutanthauza kuti ni wofunda polambila Mulungu. (Sal. 119:113; Chiv. 3:16) Munthu angakhalenso na “mitima iŵili” (mawu ake eni-eni, kukhala na mtima na mtima winanso), kutanthauza kuti angamayese kutumikila ambuye aŵili kapena angamakambe zina uku akuganiza zina. (1 Mbiri 12:33; Sal. 12:2) Yesu anadzudzula mwamphamvu anthu a mitima iŵili otelo.​—Mat. 15:7, 8.

SEPTEMBER 23-29

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 88-89

Ulamulilo wa Yehova Ni Wabwino Koposa

w17.06 28 ¶5

Muzicilikiza Ulamulilo wa Yehova!

5 Palinso cifukwa cina cimene cipangitsa Yehova kukhala woyenela kulamulila. Iye amalamulila mwacilungamo. Mulungu anati: “Ine ndine Yehova, amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapeleka ziweluzo ndi kucita cilungamo padziko lapansi. Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa.” (Yer. 9:24) Mulungu sadalila buku lililonse la malamulo opangidwa ndi anthu opanda ungwilo kuti adziŵe cimene cili colungama ndi coyenela. Cilungamo ni mbali ya umunthu wake, ndipo malamulo amene iye anapatsa anthu ni ogwilizana ndi cilungamo cakeco. Wamasalimo anati: “Cilungamo ndi ciweluzo ndizo maziko a mpando [wake] wacifumu.” Conco, tili na cikhulupililo cakuti malamulo ake, mfundo zake, ndi zigamulo zake, zonse n’zolungama. (Sal. 89:14; 119:128) Ngakhale kuti Satana amakamba kuti ulamulilo wa Yehova ni wolephela, iye wakangiwa kukonza zinthu padziko kuti pakhale cilungamo.

w17.06 29 ¶10-11

Muzicilikiza Ulamulilo wa Yehova!

10 Ulamulilo wa Yehova si wopondeleza koma ni wololela. Umalimbikitsa anthu kukhala na umoyo waufulu ndi wacimwemwe. (2 Akor. 3:17) Davide anakamba kuti: “Ulemu ndi ulemelelo zili pamaso pake [pa Mulungu], pokhala pake pali mphamvu ndi cimwemwe.” (1 Mbiri 16:7, 27) Komanso wamasalimo wina, dzina lake Etani, analemba kuti: “Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala. Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova. Iwo amakondwela ndi dzina lanu tsiku lonse. Cilungamo canu cimawakweza.”​—Sal. 89:15, 16.

11 Kuganizila mozama za ubwino wa Yehova nthawi zonse, kungatithandize kukhulupilila kwambili kuti ulamulilo wake ndiwo wabwino koposa. Timafika pomvela monga mmene wamasalimo wina anamvelela. Iye anati: “Kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.” (Sal. 84:10) Izi n’zosadabwitsa cifukwa, monga Mlengi wathu wacikondi, Yehova amadziŵa bwino zimene timafunikila kuti tikhale na cimwemwe ceni-ceni, ndipo amatipatsa zonse zofunikila. Zilizonse zimene amatiuza kucita zimatipindulitsa ndi kutipatsa cimwemwe cosaneneka, ngakhale kuti nthawi zina tingafunike kudzimana zinthu zina.​—Ŵelengani Yesaya 48:17.

w14 10/15 10 ¶13

Khalani ndi Cikhulupililo Cosagwedela mu Ufumu

14 Ganizilani zimene Yehova analonjeza Davide, Mfumu ya Isiraeli wakale kupyolela mu pangano la Davide. (Ŵelengani 2 Samueli 7:12, 16.) Iye anacita pangano ndi Davide pamene anali Mfumu ku Yerusalemu. Ndipo anam’lonjeza kuti Mesiya adzacokela m’banja lake. (Luka 1:30-33) Yehova anapeleka malangizo acindunji onena za mzele wobadwila Mesiya. Iye anakamba kuti mbeu imeneyi ya Davide idzakhala ‘yoyenelela mwalamulo’ kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. (Ezek. 21:25-27) Kupyolela mwa Yesu Mesiya, ucifumu wa Davide ‘udzakhazikika mpaka kalekale.’ Ndithudi, mbeu ya Davide “idzakhala mpaka kalekale, ndipo mpando wake wacifumu udzakhala ngati dzuŵa.” (Sal. 89:34-37) Zoonadi, ulamulilo wa Mesiya sudzaipitsidwa, ndipo zimene udzacita zidzakhala kwamuyaya!

Kufufuza Cuma Cauzimu

cl-CN 281 ¶4-5

“Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika”

4 Mawu akuti “kukhulupilika” monga momwe agwilitsidwila nchito m’Malemba Acihebri, amafotokoza munthu wokoma mtima amene mwacikondi amadziphatika ku cinthu cina cake ndipo sacisiya cinthuco mpaka colinga cake pa cinthu cimenecho citakwanilitsidwa. Kukhulupiika kumeneku si kuja kongokhala munthu wodalirika. Zili conco cifukwa munthu wokhulupilika m’lingalilo lokhala wodalilika angamacite zimenezo popeza akudziŵa kuti ali ndi udindo umenewo. Mosiyana ndi lingalilo limeneli, kukhulupilika kumene tikulongosola m’nkhani ino kumazikidwa pa cikondi. Ndiponso, nazo zinthu zopanda moyo zikhoza kukhala zokhulupilika m’lingalilo la kukhala zodalilika. Mwacitsanzo, wamasalmo anati mwezi ndi “mboni yokhulupilika kuthambo” cifukwa cakuti umaoneka nthaŵi zonse usiku. (Salimo 89:37) Komatu sitinganene kuti mwezi ndi wokhulupilika m’lingalilo lofanana ndi mmene munthu angakhalile wokhulupilika. Cifukwa ciyani? Cifukwa cakuti kukhulupilika kwa munthu kungaonetse cikondi cimene munthuyo ali naco, pamene zinthu zopanda moyo zilibe cikondi.

5 M’lingalilo la m’Malemba, munthu wokhulupilika ndi waubwenzi. Mawu okhawo akuti kukhulupilika amasonyeza kuti pali ubale winawake pakati pa munthu wokhulupilikayo ndi munthu yemwe akumuonetsa kukhulupilikako. Kukhulupilika koteleku sikuti kumangocitika mwa apo ndi apo. Sikuli ngati mafunde a panyanja amene amakankhidwa ndi mphepo zosinthasintha. Koma munthu wokhulupilika, kapena kuti wacikondi cokhulupilika, amakhala wokhazikika ndi wolimba kotelo kuti amatha kugonjetsa mavuto aakulu kwambili.

SEPTEMBER 30–OCTOBER 6

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 90-91

Muzidalila Yehova Kuti Mukhale na Moyo Wautali

wp19.3 5 ¶3-5

Kufuna-funa Moyo Wautali

Olo kuti pali njila zambili zoletsela ukalamba, asayansi ambili amavomeleza kuti sitingakhale na moyo wautali kuposa pa zaka zimene timakhala na moyo masiku ano. N’zoona kuti kuyambila m’zaka za m’ma 1800, zaka zimene anthu amayembekezeledwa kukhala na moyo zawonjezekako. Koma kweni-kweni, izi zatheka cifukwa cakuti anthu amakhala aukhondo, komanso cifukwa ca njila zina zopewela matenda opatsilana, komanso akatemela ocinjiliza anthu ku matenda. Asayansi ena oona za majini, amati anthu sangakhale na moyo kupitilila pa zaka zimene amayembekezeledwa kukhala.

Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, wolemba Baibo Mose anakamba kuti: “Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70, ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadela amakwana zaka 80. Koma ngakhale zili conco, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka. Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timacoka mofulumila.” (Salimo 90:10) Ngakhale kuti anthu ayesa-yesa kutalikitsa moyo, kweni-kweni timakhala na moyo monga mmene Mose anafotokozela.

Koma zolengedwa zina monga fulu, komanso mtundu wina wa nkhono za m’madzi, zingakhale na moyo kupitilila zaka 200. Ndipo mitengo ina monga mtengo wa malambe, ingakhale na moyo kwa zaka masauzande. Tikaganizila kuculuka kwa zaka zimene zolengedwa izi zimakhala na moyo komanso zolengedwa zina, tingadzifunse kuti, ‘Kodi moyo ni uno cabe umene ulipo wokhala na moyo zaka 70 kapena 80?’

wp19.1 5, bokosi

Kodi Dzina La Mulungu N’ndani?

Ambili amadzifunsa funso limeneli. Mwina na imwe munadzifunsapo. Kapena tifunse kuti: Ngati zinthu zonse za m’cilengedwe zinacita kulengedwa, nanga analenga Mulungu n’ndani?

Asayansi ambili amakhulupilila kuti cilengedwe cinali na ciyambi. Izi zimagwilizana na zimene vesi yoyamba ya m’Baibo imakamba kuti: “Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”​—Genesis 1:1.

Zinthu za m’cilengedwe sizikanadzilenga zokha, zinali na ciyambi. Ngati kunalibe mlengi paciyambi, kodi zinthu zonse za m’cilengedwe zikanakhalako bwanji? Kukamba zoona, zinthu zonse zinalengedwa na Yehova Mulungu, wamphamvu zazikulu koposa komanso wanzelu.​—Yohane 4:24.

Ponena za Mulungu, Baibo imati: “Mapili asanabadwe, kapena musanakhazikitse dziko lapansi ndi malo okhalapo anthu, inu ndinu Mulungu kuyambila kalekale mpaka kalekale.” (Salimo 90:2) Conco, Mulungu sanacite kulengedwa. Iye wakhalapo nthawi zonse. Zoonadi, “pa ciyambi” analenga zonse za m’cilengedwe.​—Chivumbulutso 4:11.

w22.06 18 ¶16-17

Cikondi ca Yehova Cimatithandiza Kugonjetsa Mantha

16 Satana amadziŵa kuti moyo wathu timaukonda. Iye amakamba kuti tingalolele kutaya ciliconse​—ngakhale ubwenzi wathu na Yehova, cabe kuti tiuteteze. (Yobu 2:4, 5) Limeneli ni bodza lamkunkhuniza! Komabe, popeza kuti Satana “ali ndi njila yobweletsela imfa,” amagwilitsa nchito mantha athu acibadwa oopa imfa pofuna kutipangitsa kumusiya Yehova. (Aheb. 2:14, 15) Nthawi zina, anthu amene ali ku mbali ya Satana amaopseza anthu a Yehova kuti adzawapha ngati saleka kutumikila Mulungu. Nthawi zinanso, tikadwala matenda aakulu, iye angatengelepo mwayi wotipangitsa kuphwanya malamulo a Mulungu. Madokotala kapena acibale amene si Mboni angatikakamize kuti tilole kuikidwa magazi, kumene kungakhale kuphwanya lamulo la Mulungu. Kapena, wina angatinyengelele kuti tilandile cithandizo ca mankhwala cosemphana na mfundo za m’Malemba.

17 Olo kuti sitifuna kufa, tidziŵa kuti Yehova sadzaleka kutikonda ngakhale timwalile. (Ŵelengani Aroma 8:37-39.) Mabwenzi a Yehova akamwalila, iye amawakumbukilabe, ngati kuti akali moyo. (Luka 20:37, 38) Amacita kulakalaka kuwaukitsa. (Yobu 14:15) Yehova anapeleka malipilo apamwamba kwambili kuti ife ‘tikakhale na moyo wosatha.’ (Yoh. 3:16) Tidziŵa kuti Yehova amatikonda kwambili komanso amatisamalila. Conco tikadwala, kapena akatiopseza kuti adzatipha, tisamusiye Yehova. M’malo mwake, tiyenela kutembenukila kwa iye kuti atitonthoze, atipatse nzelu, ndiponso mphamvu. Izi n’zimene mlongo Valérie na mwamuna wake anacita.​—Sal. 41:3.

Kufufuza Cuma Cauzimu

wp17.5 5

Kodi Muli na Mngelo Wokutetezani?

Baibo siphunzitsa kuti munthu aliyense ali na mngelo amene amamuteteza. N’zoona kuti panthawi ina Yesu anati: “Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati [ophunzila a Khristu], cifukwa ndikukutsimikizilani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.” (Mateyu 18:10) Komabe, apa Yesu sanali kutanthauza kuti munthu aliyense ali na mngelo womuteteza, koma anali kungokamba kuti angelo amacita cidwi na wophunzila wake aliyense. Conco, alambili oona saika dala moyo wawo paciswe poganiza kuti angelo a Mulungu adzawateteza.

Kodi izi zitanthauza kuti angelo sathandiza anthu? Iyai. (Salimo 91:11) Anthu ena amakhulupilila kwambili kuti Mulungu amawateteza na kuwatsogolela kupitila mwa angelo. Kenneth, amene tam’chula m’nkhani yoyamba, nayenso amakhulupilila zimenezi. Koma sitingatsimikizile mfundo imeneyi, mwina akamba zoona. Nthawi zambili, a Mboni za Yehova amaona maumboni oonetsa kuti angelo amawathandiza pa nchito yawo yolalikila. Popeza angelo saoneka, sitingadziŵe kuti Mulungu amawaseŵenzetsa kufika pati pothandiza anthu pa zocitika zosiyana-siyana. Ngakhale n’conco, si kulakwa kuyamikila Wamphamvuyonse pa thandizo limene amapeleka.​—Akolose 3:15; Yakobo 1:17, 18.

OCTOBER 7-13

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 92-95

Kutumikila Yehova Ndiwo Umoyo Wabwino Koposa!

w18.04 26 ¶5

Acicepele, Kodi Mumaika Zolinga Zauzimu Patsogolo?

5 Cifukwa cacikulu cokhalila na zolinga zauzimu n’cakuti, timafuna kuonetsa kuti timamuyamikila Yehova kaamba ka cikondi cake, komanso cifukwa ca zimene amaticitila. Wamasalimo anati: “Ndi bwino kuyamika inu Yehova . . . Pakuti mwandicititsa kusangalala, inu Yehova, cifukwa ca zocita zanu. Ndimafuula mosangalala cifukwa ca nchito ya manja anu.” (Sal. 92:1, 4) Monga wacicepele, ganizilani zinthu zimene Yehova anakucitilani. Anakupatsani moyo, cikhulupililo, Baibo, mpingo, na ciyembekezo ca tsogolo labwino. Conco, kuika zinthu zauzimu patsogolo ni njila yoonetsela kuti mumamuyamikila Mulungu cifukwa ca madalitso amenewa. Ndipo kucita izi kudzakupangitsani kumuyandikila kwambili.

w18.11 20 ¶8

Kodi Mumayendela Maganizo a Ndani?

8 Molingana na kholo labwino, Yehova amafuna kuti ise ana ake tikhale na umoyo wacimwemwe kwambili. (Yes. 48:17, 18) Mwa ici, iye watiphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino. Yehova amafuna kuti tiziona zinthu mmene iye amazionela, komanso kuti tizitsatila mfundo zake za makhalidwe abwino. Kucita izi sikutilanda ufulu, koma kumatithandiza kukulitsa luso la kuganiza. (Sal. 92:5; Miy. 2:1-5; Yes. 55:9) Ngati titsatila mfundo za Yehova, timakhalabe na mwayi wocita zinthu malinga n’zokonda zathu. Ndipo timatha kupanga zosankha zimene zingatibweletsele cimwemwe. (Sal. 1:2, 3) Zoonadi, kutengela maganizo a Yehova n’kwabwino komanso n’kothandiza!

w20.01 19 ¶18

Yehova Mulungu Wathu Amationa Kuti Ndife Ofunika!

18 Ngati ndimwe wokalamba, dziŵani kuti Yehova akali na nchito imene afuna kuti mucite. (Sal. 92:12-15) Nthawi zina tingaone kuti mphamvu na maluso athu n’zocepa, kapenanso kuti zimene timacita n’zosafunika kweni-kweni. Koma Yesu anatiphunzitsa kuti Yehova amayamikila zilizonse zimene timacita pom’tumikila. (Luka 21:2-4) Conco, muzicita zimene mungakwanitse. Mwacitsanzo, muziuzako ena za Yehova, muzipemphelela abale na alongo anu, komanso muzilimbikitsa ena kuti akhalabe okhulupilika. Yehova amakuonani kuti ndimwe wa nchito mnzake, osati cifukwa ca zimene mumakwanitsa kucita, koma cifukwa cakuti mumamumvela na mtima wonse.​—1 Akor. 3:5-9.

Kufufuza Cuma Cauzimu

cl-CN 176 ¶18

“Ha! Kuya Kwake kwa Nzeru za Mulungu!”

18 Taonani mmene mtumwi Paulo analongosolela nzelu za Yehova kuti n’zapadela kwambili. Iye anati: “Ha! kuya kwake kwa kulemela ndi kwa nzelu ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweluzo ake, ndi njila zake n’zosalondoleka!” (Aroma 11:33) Mwa kuyamba vesili ndi mawu ofuula akuti “Ha!” Paulo anasonyeza malingalilo amphamvu amene anali nawo mumtima mwake, mantha limodzi ndi ulemu waukulu. Mawu acigiliki akuti “kuya” amene iye anagwilitsa nchito ndi ofanana kwambili ndi mawu otanthauza “phompho.” Motelo mawu ake amatipatsa cithunzithunzi ca m’maganizo cooneka bwino. Pamene tisinkhasinkha nzeru za Yehova, zimakhala ngati tikuyang’ana m’cidzenje cozama zedi, cimene pansi pake sipaoneka; cakuya komanso cacikulu kwambili moti sitingathe kudziŵa bwino kukula kwake, ndiponso ndi cokanika kucifotokoza kaya kucijambula mwatsatanetsatane. (Salmo 92:5) Kodi mfundo imeneyi siyenela kuticititsa kukhala odzicepetsa?

OCTOBER 14-20

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 96-99

“Muzilengeza Uthenga Wabwino”!

w11-CN 3/1 6 ¶1-2

Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?

AKHRISTU ayenela kumalalikila ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Ayenelanso kufotokozela ena kuti Ufumuwo ndi boma la m’tsogolo limene lidzalamulila dziko lonse lapansi mwacilungamo. Komabe m’Baibulo mawu akuti “uthenga wabwino” amagwilitsidwanso nchito m’njila zosiyanasiyana. Mwacitsanzo, m’Baibulo muli mawu ngati, “uthenga wabwino wa cipulumutso” (Salimo 96:2); “uthenga wabwino wa Mulungu” (Aroma 15:16); ndi “uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu.”​—Maliko 1:1.

Mwacidule, uthenga wabwino ndi mfundo zonse za coonadi zimene Yesu ananena ndiponso zimene ophunzira ake analemba. Yesu asanapite kumwamba anauza otsatila ake kuti: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.” (Mateyu 28:19, 20) Conco nchito ya Akhristu oona sikungouza anthu za Ufumu, koma ayenelanso kuyesetsa kuphunzitsa anthuwo kuti akhale ophunzila a Yesu.

w12 9/1 16 ¶1

Kodi pa Tsiku la Ciweluzo Padzacitika Zotani?

Monga tikuonela pacithunzi cili kumanjaci, anthu ambili amaganiza kuti pa Tsiku la Ciweluzo anthu onse adzaonekela pampando wacifumu wa Mulungu ndipo adzaweluzidwa malinga na nchito zimene anacita. Anthuwa amaganiza kuti ena adzalandila moyo kumwamba ndipo ena adzapita kukazunzidwa kumoto. Koma Baibo imasonyeza kuti colinga ca Tsiku la Ciweluzo ni kupulumutsa anthu ku zinthu zopanda cilungamo zimene zimacitika padzikoli. (Salimo 96:13) Mulungu wasankha Yesu kukhala Woweluza wake amene adzabweletsa cilungamo kwa anthu.​—Ŵelengani Yesaya 11:1-5; Machitidwe 17:31.

w12-CN 9/15 12 ¶18-19

Mtendele Udzayamba mu Ulamulilo wa Zaka 1,000!

18 Ubwenzi umenewu unasokonekela pamene Satana anacititsa anthu kupandukila ulamulilo wa Yehova. Koma kuyambila mu 1914, Ufumu wa Mesiya wakhala ukubwezeletsa mtendele ndi mgwilizano. (Aef. 1:9, 10) Mu Ulamulilo wa Zaka 1,000, zinthu zosangalatsa zimene tikuyembekezela zidzacitika. Ndiyeno n’ciyani cidzacitika “pa mapeto pake,” kapena kuti pa mapeto pa Ulamulilo wa Zaka 1,000? Ngakhale kuti Yesu anapatsidwa “ulamulilo wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi,” iye alibe mtima wofuna kulanda udindo wa Yehova. Yesu ndi wodzicepetsa ndipo “adzapeleka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake.” Iye adzagwilitsa nchito udindo wake kuti ‘alemekeze Mulungu.’​—Mat. 28:18; Afil. 2:9-11.

19 Pa nthawi imeneyo, anthu olamulidwa ndi Ufumu padziko lapansi adzakhala angwiro. Iwo adzatsatila citsanzo ca Yesu. Adzagonjela ulamuliro wa Yehova modzicepetsa ndiponso mofunitsitsa. Iwo akadzapambana mayeselo omaliza adzasonyeza kuti alidi ndi mtima wofuna kugonjera Yehova. (Chiv. 20:7-10) Pambuyo pake, adani onse a Mulungu, kungoyambila anthu, ziwanda komanso Satana weniweniyo, adzawonongedwa. Nthawi imeneyi idzakhala yosangalatsa kwambili. Onse a m’banja la Yehova adzamutamanda mosangalala ndipo iye adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”​—Ŵelengani Salimo 99:1-3.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2-E 994

Nyimbo

Mawu akuti “nyimbo yatsopano” amapezeka m’buku la Masalimo komanso m’zolemba za Yesaya na mtumwi Yohane. (Sal. 33:3; 40:3; 96:1; 98:1; 144:9; 149:1; Yes. 42:10; Chiv. 5:9; 14:3) Pambuyo posanthula nkhani za m’Baibo zimene mumapezeka mawu akuti “nyimbo yatsopano,” cioneka kuti nyimbozi zinali kuimbidwa Yehova akacita cina cake coonetsa kuti ni woyeneleladi kulamulila cilengedwe conse. Mwacitsanzo, pa Salimo 96:10 pamati: “Yehova wakhala mfumu.” “Nyimbo yatsopano imeneyi,” ifotokoza zimene Yehova wacita pokulitsa ucifumu wake, komanso mmene zinthu zimenezi zikhudzila kumwamba na dziko lapansi.​—Sal. 96:11-13; 98:9; Yes. 42:10, 13.

OCTOBER 21-27

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 100-102

Onetsani Kuti Mumayamikila Cikondi Cosasintha ca Yehova

w23.03 12 ¶18-19

Kodi Ubatizo Mungaukonzekele Motani?

18 Cikondi canu pa Yehova ndilo khalidwe lofunika kwambili limene muli nalo. (Ŵelengani Miyambo 3:3-6.) Kum’konda kwambili Mulungu kudzakuthandizani kuti mupambane polimbana na mavuto. Nthawi zambili, Baibo imakamba za cikondi cosasintha ca Yehova pa atumiki ake. Izi zitanthauza kuti iye sadzasiya atumiki ake ngakhale pang’ono, kapena kuleka kuwakonda. (Sal. 100:5) Kumbukilani kuti munalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu. (Gen. 1:26) Kodi mungaonetse bwanji cikondi cimeneci?

19 Coyamba, khalani woyamikila. (1 Ates. 5:18) Tsiku lililonse muzidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova waonetsa bwanji kuti amanikonda?’ Kenako, muyamikileni Yehova m’mapemphelo anu, na kuchula mwacindunji zimene wakucitilani. Muzitha kuona zabwino zimene Yehova amakucitilani inuyo panokha, na kuti amatelo cifukwa amakukondani. Izi n’zimene mtumwi Paulo anazindikila. (Ŵelengani Agalatiya 2:20.) Dzifunseni kuti, ‘Kodi inenso nimafuna kumuonetsa cikondi cimene iye amanionetsa?’ Cikondi canu pa Yehova cidzakuthandizani kupitiliza kukaniza mayeselo, komanso kupilila mavuto. Cidzakulimbikitsani kulambila Yehova nthawi zonse, poonetsa kuti mumam’konda Atate wanu wakumwamba.

w23.02 17 ¶10

“Khalanibe Oganiza Bwino Ndipo Khalani Maso!”

10 Zina mwa zoopsa zimene tiyenela kupewa ni kuceza mokopana, kumwa kwambili, kudya kwambili, mawu okhumudwitsa ena, kuonelela zaciwawa, zamalisece, na zina zotelo. (Sal. 101:3) Mdani wathu Mdyerekezi nthawi zonse amafunafuna mipata kuti awononge ubwenzi wathu na Yehova. (1 Pet. 5:8) Tikapanda kusamala, m’maganizo na mumtima mwathu Satana angabzalemo mbewu za kaduka, kusaona mtima, dyela, cidani, kudzikuza, komanso kusunga cakukhosi. (Agal. 5:19-21) Poyamba makhalidwe amenewa sangaoneke oopsa kwenikweni. Koma ngati siticitapo kanthu mwamsanga kuti tiwazule, adzapitiliza kukula monga comela cokhala na poizoni na kutibweletsela mavuto.​—Yak. 1:14, 15.

w11-CN 7/15 16 ¶7-8

Kodi Mukutsatira Machenjezo a Yehova Omveka Bwino?

7 Kodi tingapewe bwanji aphunzitsi onyenga? Sitiwalandila m’nyumba zathu kapena kuwapatsa moni. Timakananso kuŵelenga mabuku awo, kuwaonela pa TV ndiponso kuŵelenga kapena kuyankha zimene alemba pa Intaneti. N’cifukwa ciyani timawakana kwamtuwagalu? Cifukwa cakuti timakonda “Mulungu wacoonadi” ndipo timadana ndi ziphunzitso zopotoka zimene zimasemphana ndi Mawu ake a coonadi. (Sal. 31:5; Yoh. 17:17) Timakondanso gulu la Yehova limene latiphunzitsa mfundo zosangalatsa za coonadi. Mwacitsanzo, taphunzila za dzina lakuti Yehova ndi tanthauzo lake, colinga cimene Mulungu analengela dziko lapansi, zimene zimacitika munthu akamwalila ndiponso ciyembekezo cakuti akufa adzauka. Kodi mukukumbukila mmene munamvela mutangophunzila mfundo zamtengo wapatali ngati zimenezi? Musalole kuti mabodza amene aphunzitsi onyenga amanena akucititseni kupandukila gulu la Mulungu limene lakuphunzitsani mfundo za coonadi zimenezi.​—Yoh. 6:66-69.

8 Kaya aphunzitsi onyenga anene zotani, ife sitingawatsatile. Titati tiwatsatile tikhoza kukhumudwa kwambili cifukwa ali ngati zitsime zouma. M’malomwake, tiyenela kukhalabe okhulupilika kwa Yehova ndi gulu lake. Gulu limeneli silinatikhumudwitsepo ndipo kwa nthawi yaitali lakhala likutipatsa madzi oyela a coonadi ocokela m’Mawu a Mulungu.​—Yes. 55:1-3; Mat. 24:45-47.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2-E 596

Vuwo

Mbalame yochedwa vuwo ikakhuta kwambili, imauluka n’kupita kutali kwayokha. Kumeneko imakhala cete pamalo ena ake monga yokhumudwa, italowetsa mutu wake m’mapiko ake. Munthu akaiona alipatali, angaone monga ni mwala woyela. Mbalameyi imakhala conco kwa maola ambili. Izi n’zogwilizana kwambili na cisoni cacikulu cimene wamasalimo anali naco pamene analemba kuti: “Ndikufanana ndi mbalame yamʼcipululu yochedwa vuwo.” (Sal. 102:6) Pa lembali, mawu akuti “cipululu” satanthauza cipululu ceniceni, koma aimila malo akutali kumene sikukhala anthu, monga kumadambo.

Mbalameyi imakonda kukhala kuchile kumene anthu salimako kuti isasokonezedwe na anthu. Kumeneko imapanga zisa, kugonkhomola, komanso kupumula pambuyo pogwila nsomba. Cifukwa cokonda kukhala kwayokha, ku matongwe (mabwinja), mbalame imeneyi imagwilitsidwa nchito m’Baibo pokamba za ciwonongeko cothelatu. Pofotokoza za kuwonongedwa kwa Edomu, Yesaya anakambilatu kuti mbalame ya vuwo idzakhala kumeneko. (Yes. 34:11) Zefaniya analosela kuti mbalame za vuwo zidzakhala pa mitu ya zipilala za mzinda wa Nineve, kuonetsa kuti malowo adzawonongedwa kothelatu ndipo sikudzakhala anthu.​—Zef. 2:13, 14.

OCTOBER 28–NOVEMBER 3

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MASALIMO | 103-104

Iye Amakumbukila “Kuti Ndife Fumbi”

w23.07 21 ¶5

Khalani Ololela Potengela Yehova

5 Kudzicepetsa kwa Yehova na cifundo cake, zimamulimbikitsa kukhala wololela. Mwacitsanzo, kudzicepetsa kwa Yehova kuonaonekela bwino atatsala pang’ono kuwononga anthu oipa a mu Sodomu. Kupitila mwa angelo ake, Yehova anauza munthu wolungama Loti kuti athaŵile kumapili. Koma Loti anaopa kupita kumeneko. Conco, anacondelela Mulungu kuti amulole pamodzi na banja lake kuti athaŵile mu mzinda waung’ono wa Zowari, umene unayenelanso kuwonongedwa. Yehova akanafuna akanaumilila ndithu kuti Loti angotsatila malangizowo ndendende. Koma m’malo mwake, iye anamva pempho la Loti, ngakhale kuti izi zinatanthauza kusawononga mzinda wa Zowari. (Gen. 19:18-22) Patapita zaka mahandiledi, Yehova anaonetsa cifundo kwa anthu a ku Nineve. Anatuma mneneli Yona kukalengeza kuti mzindawo pamodzi na anthu oipa okhala mmenemo adzawonongedwa. Koma anthu a ku Nineve atalapa, Yehova anawamvela cisoni, ndipo sanauwononge mzindawo.​—Yona 3:1, 10; 4:10, 11.

w23.09 6-7 ¶16-18

Muzidalila Yehova Mmene Samisoni Anacitila

16 Ngakhale kuti Samisoni anakumana na mavuto aakulu cifukwa ca colakwa cake, iye sanaleke kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Nafenso tikalakwitsa zina zake, kenako n’kudzudzulidwa kapena kucotsedwa paudindo, sitiyenela kuleka kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Musaiŵale kuti Yehova ni okonzeka kutikhululukila. (Sal. 103:8-10) Monga zinalili kwa Samisoni, nafenso Yehova angadzapitilize kutigwilitsa nchito ngakhale titalakwitsa zina zake.

17 Onani zinacitikila m’bale wina wacinyamata dzina lake Michael. Anali wokangalika pa zinthu zauzimu, ndipo anali kutumikila monga mtumiki wothandiza komanso mpainiya wa nthawi zonse. N’zacisoni kuti analakwitsa zina zake zimene zinapangitsa kuti ataye mwayi wa mautumiki amenewo. Michael anati: “Kumbuyo konseku, zinthu zinali kuniyendela bwino kwambili mu utumiki wanga kwa Yehova. Koma mosayembekezela, ndinamva ngati zonse zaima. N’nadziŵa kuti Yehova sanganisiye, koma n’nali kudzifunsabe ngati ubwenzi wanga na iye ungadzakhalenso mmene unali poyamba, komanso ngati ningadzatumikilenso mu mpingo monga mmene n’nali kucitila kale.”

18 N’zokondweletsa kuti Michael sanabwelele m’mbuyo. Iye anawonjezele kuti: “N’naika maganizo anga pa kukonza ubwenzi wanga na Yehova mwa kupemphela mocokela pansi pa mtima, kucita phunzilo la munthu mwini, komanso kusinkhasinkha.” M’kupita kwa nthawi, Michael anakhalanso na kaimidwe kabwino mu mpingo. Ndipo lomba akutumikila monga mkulu komanso mpainiya wanthawi zonse. Ananenanso kuti: “Thandizo na cilimbikitso zimene n’nalandila makamaka kucokela kwa akulu, zinandithandiza kuona kuti Yehova anali kunikondabe. Pali pano nikutumikilanso mu mpingo na cikhumbumtima coyela. Cocitikaci caniphunzitsa kuti Yehova ni wokonzeka kukhululukila amene walapadi.” Tisakaikile zakuti Yehova angatigwilitsenso nchito na kutidalitsa ngakhale titalakwitsa zina zake, malinga ngati tiyesetsa kukonza zimene tinalakwitsazo, na kupitiliza kum’dalila.​—Sal. 86:5; Miy. 28:13.

w23.05 26 ¶2

N’zotheka Kuzikwanilitsa Zolinga Zanu Zauzimu

2 Ngati palipano simunakwanilitse colinga canu, dziŵani kuti sindinu wolephela. Ngakhale kukwanilitsa colinga cacing’ono kumafuna nthawi na kulimbika. Kuyesetsa kuti mukwanilitse colinga canu, kumaonetsa kuti mumaona ubale wanu na Yehova kukhala wofunika kwambili, komanso kuti mumafuna kum’patsa zabwino kopambana. Yehova amayamikila kuyesetsa kwanu. Komabe, iye sayembekezela kuti mucite zimene simungathe. (Sal. 103:14; Mika 6:8) Conco, dziikileni colinga cimene mungacikwanilitse, malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wanu. Mukadziikila colinga, kodi mungacite ciyani kuti mucikwanilitse? Tiyeni tikambilane malingalilo otsatilawa.

Kufufuza Cuma Cauzimu

cl-CN 55 ¶18

Mphamvu za Kulenga​—“Amene Analenga Zakumwamba ndi Dziko Lapansi”

18 Kodi tikuphunzilanji pa mmene Yehova amagwilitsila nchito mphamvu zake za kulenga? Timacita kakasi cifukwa ca kusiyanasiyana kwa cilengedwe. Wamasalmo wina anafuula kuti: “Nchito zanu ziculukadi, Yehova! . . . Dziko lapansi lidzala nacho cuma canu.” (Salimo 104:24) N’zoonadi zimenezo! Akatswili a sayansi ya zinthu zamoyo apeza mitundu ya zamoyo yopitilila wani miliyoni pa dziko lapansi; komatu zonena zawo zimasiyanasiyana kuti kaya pali mitundu yokwana 10 miliyoni, kaya 30 miliyoni, kapena yoposa pamenepo. Munthu waluso lojambula zithunzi ndi manja nthaŵi zina angaone kuti akusoŵa cojambula. Mosiyana ndi munthu waluso lotelolo, luso lopanga zinthu la Yehova, ndiko kuti mphamvu yake yolingalila za zinthu zosiyanasiyana zatsopano ndi kuzilenga, mwacionekele silitha.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani