LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • “Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi Yamapeto
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2020 | May
    • NKHANI YOPHUNZILA 19

      “Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi Yamapeto

      “M’nthawi ya mapeto mfumu ya kum’mwela idzayamba kukankhana nayo [mfumu ya kumpoto].”​—DAN. 11:40.

      NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

      ZIMENE TIKAMBILANEa

      1. Kodi maulosi a m’Baibo amatithandiza kudziŵa ciani?

      KODI n’ciani cidzacitikila anthu a Yehova posacedwapa? Si zovuta kudziŵa yankho lake. Maulosi a m’Baibo amafotokoza zocitika zikulu-zikulu zimene zicitike posacedwapa, zomwe zidzakhudza aliyense wa ife. M’Baibo muli ulosi wina umene umatithandiza kudziŵa zimene maboma ena amphamvu kwambili padzikoli adzacita. Ulosiwo uli pa Danieli caputa 11. Ndipo umafotokoza za mafumu aŵili olimbana, amene amachedwa mfumu ya kumpoto komanso mfumu ya kum’mwela. Mbali yaikulu ya ulosiwu inakwanilitsidwa kale. Conco, sitikayikila kuti mbali yotsala nayonso idzakwanilitsidwa.

      2. Kulingana na Genesis 3:15 komanso Chivumbulutso 11:7 na 12:17, ni mfundo zofunika ziti zimene tiyenela kukumbukila poŵelenga ulosi wa Danieli?

      2 Kuti timvetsetse ulosi wa pa Danieli caputa 11, tifunika kukumbukila kuti ulosiwu umakamba za olamulila na maboma okhawo amene zocita zawo zinakhudza anthu a Mulungu mwacindunji. Atumiki a Mulungu ni ocepa kwambili poyelekezela ndi anthu onse padzikoli. Nanga n’cifukwa ciani maboma amakonda kuwazunza? Cifukwa colinga cacikulu ca Satana na onse amene ali kumbali yake ni kuwononga anthu amene amatumikila Yehova na Yesu. (Ŵelengani Genesis 3:15 na Chivumbulutso 11:7; 12:17.) Kuti timvetsetse ulosi wa m’buku la Danieli, tifunikanso kuonetsetsa kuti ukugwilizana na maulosi ena a m’Mawu a Mulungu. Ndipo popanda kuyelekezela ulosi wa Danieli na mavesi ena a m’Baibo, sitingathe kuumvetsetsa.

      3. Tikambilana ciani m’nkhani ino komanso m’nkhani yotsatila?

      3 Tili na mfundo zimenezi m’maganizo, tiyeni lomba tikambilane lemba la Danieli 11:25-39. Pokambilana, tiona kuti ni maulamulilo ati amene anali mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela kucokela mu 1870 mpaka mu 1991. Tionanso cifukwa cake tiyenela kusintha kamvedwe kathu ka mbali inayake ya ulosi umenewu. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana Danieli 11:40–12:1. Tidzafotokoza lembali mogwilizana na kamvedwe kathu katsopano, ndipo tidzaona zimene mbali imeneyi ya ulosi imatiuza ponena za zocitika kuyambila m’ma 1990 mpaka pankhondo ya Aramagedo. Pamene muŵelenga nkhani ziŵilizi, mungacite bwino kuonanso chati yakuti “Mafumu Olimbana M’nthawi Yamapeto.” Koma coyamba, tifunika kudziŵa kuti mafumu aŵili okambidwa mu ulosiwu ni ati.

      MMENE TINGADZIŴILE MFUMU YA KUMPOTO NA MFUMU YA KUM’MWELA

      4. Ni zinthu zitatu ziti zimene zimatithandiza kudziŵa mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela?

      4 Maina akuti “mfumu ya kumpoto” komanso “mfumu ya kum’mwela,” kale anali kugwilitsidwa nchito pokamba za maulamulilo amphamvu andale amene anali kumpoto na kum’mwela kwa dziko la Isiraeli. N’cifukwa ciani takamba conco? Onani zimene mngelo amene anapeleka uthengawu kwa Danieli anakamba. Anati: “Ndabwela kudzakuthandiza kuzindikila zimene zidzagwela anthu a mtundu wako m’masiku otsiliza.” (Dan. 10:14) Kuyambila kale mpaka kudzafika pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Aisiraeli akuthupi ndiwo anali anthu a Mulungu. Koma kungocokela nthawiyo, Yehova anapeleka umboni woonekelatu wakuti anali kuona kuti ophunzila a Yesu okhulupilika ndiwo anthu ake. Conco, mbali yaikulu ya ulosi wa pa Danieli caputa 11, imakamba za otsatila a Khristu osati za Aisiraeli akuthupi. (Mac. 2:1-4; Aroma 9:6-8; Agal. 6:15, 16) M’kupita kwa nthawi, maulamulilo kapena kuti maboma oimila mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akusintha-sintha. Ngakhale n’telo, pali mbali zina zimene sizinasinthe. Coyamba, zocita za mafumu amenewa zinakhudza kwambili anthu Mulungu. Caciŵili, zimene mafumuwa anacitila anthu a Mulungu zinaonetsa kuti anali kuzonda Mulungu woona, Yehova. Cacitatu, mafumu aŵiliwa anali kulimbilana ulamulilo.

      5. Kodi padzikoli panali mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela kuyambila m’caka ca 100 C.E. mpaka mu 1870? N’cifukwa ciani mwayankha conco?

      5 Panthawi inayake m’zaka za m’ma 100 C.E., Akhristu ambili onyenga analoŵa mumpingo wacikhristu. Iwo anayamba kuphunzitsa ziphunzitso zabodza na kuphimba coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Kucokela nthawiyo mpaka kufika mu 1870, padziko lapansi panalibe gulu la atumiki a Mulungu. Akhristu onyenga anaculuka mumpingo wacikhristu monga namsongole, moti zinali zovuta kwambili kudziŵa Akhristu oona. (Mat. 13:36-43) N’cifukwa ciani kudziŵa zimenezi n’kofunika? Cifukwa zionetsa kuti mafumu kapena maboma amene analamulila kuyambila m’caka ca 100 C.E. mpaka mu 1870, sangakhale mfumu ya kumpoto kapena mfumu ya kum’mwela. Zili conco cifukwa panthawiyi panalibe gulu la anthu a Mulungu limene akanaliukila.b Koma pambuyo pa caka ca 1870, mafumu aŵili amenewa, ya kumpoto na ya kum’mwela, anaonekelanso. Tidziŵa bwanji zimenezi?

      6. Ni liti pamene anthu a Mulungu anayambanso kusonkhanitsidwa monga gulu? Fotokozani.

      6 Kuyambila mu 1870, anthu a Mulungu anayambanso kusonkhanitsidwa monga gulu. M’caka cimeneci, M’bale Charles T. Russell na anzake anapanga kagulu ka ophunzila Baibo. M’bale Russell na anzakewo ndiwo anali mthenga amene ananenedwelatu kuti ‘adzakonza njila’ Ufumu wa Mesiya usanakhazikitsidwe. (Mal. 3:1) Apa tsopano atumiki oona a Mulungu anaonekelanso. Kodi panthawiyo panali maulamulilo amphamvu padziko lonse amene zocita zawo zikanakhudza kwambili atumiki a Mulungu? Ganizilani mfundo zotsatilazi.

      KODI MFUMU YA KUM’MWELA NDANI?

      7. Ndani anali mfumu ya kum’mwela kucokela mu 1870 mpaka mkati mwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse?

      7 Pofika m’caka ca 1870, dziko la Britain linali kulamulila dela lalikulu kwambili kuposa dziko lina lililonse, ndiponso linali na gulu la asilikali lamphamvu kwambili pa dziko lonse. Mu ulosi wa Danieli, dzikoli likuimilidwa na nyanga yaing’ono imene inagonjetsa nyanga zina zitatu. Nyanga zitatuzo ziimila dziko la France, Spain, na Netherlands. (Dan. 7:7, 8) Dziko la Britain ndilo linali mfumu ya kum’mwela kuyambila mu 1870 mpaka mkati mwa Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse. Panthawi imodzi-modziyo, dziko la America linakhala lolemela kwambili padziko lonse, ndipo linayamba kupanga mgwilizano wamphamvu na dziko la Britain.

      8. M’masiku otsiliza ano, ni maiko ati amene akhala akulamulila monga mfumu ya kum’mwela?

      8 Panthawi ya Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse, Britain na America anamenya nkhondo mogwilizana, cakuti ulamulilo wawo unakhala wamphamvu kwambili. Panthawiyo, maikowa anagwilizana kwambili, ndipo anapanga ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America. Monga mmene ulosi wa Danieli unakambila, mfumuyi inasonkhanitsa “gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.” (Dan. 11:25) M’nthawi yonse ya masiku otsiliza, maiko a Britain na America ndiwo akhala akulamulila monga mfumu ya kum’mwela.c Nanga ni boma liti limene linali kulamulila monga mfumu ya kumpoto?

      Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America m’Maulosi a m’Baibo

      Masiku ano, Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America ndiwo mfumu ya kum’mwela. Mfumu imeneyi imafotokozedwa m’njila zosiyana-siyana m’maulosi a m’Baibo. Imafotokozedwa monga . . .

      • Mapazi acitsulo cosakanizika na dongo.

        mapazi acitsulo cosakanizika na dongo (Dan. 2:41-43

      • Mutu wa cilombo wokhala na nyanga. Pakati pa nyangazo pamela nyanga yaing’ono yokhala na maso na pakamwa.

        nyanga imene inamela pa mutu wa cilombo coopsa kwambili (Dan. 7:7, 8)

      • Cilombo cokhala na nyanga 10 komanso mitu 7.

        mutu wa 7 wa cilombo (Chiv. 13:1)

      • Cilombo ca nyanga ziŵili.

        cilombo ca nyanga ziŵili (Chiv. 13:11-15)

      • Nyumba za boma zoimila ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America.

        “mneneli wonyenga” (Chiv. 19:20)

      MFUMU YA KUMPOTO IONEKELANSO

      9. Kodi mfumu ya kumpoto inaonekelanso liti? Nanga lemba la Danieli 11:25 linakwanilitsidwa bwanji?

      9 Mu 1871, mfumu ina ya kumpoto inaonekela. Apa n’kuti papita caka cimodzi kucokela pamene m’bale Russell na anzake anapanga kagulu ka ophunzila Baibo. M’caka cimeneco, Otto von Bismarck anathandiza kwambili pokhazikitsa ulamulilo wamphamvu wa Germany. Wilhelm Woyamba ndiye anakhala mfumu yoyamba ya Germany, ndipo anasankha Bismarck kukhala nduna yaikulu yoyamba.d M’kupita kwa zaka, dziko la Germany linayamba kulamulila maiko ena a mu Africa komanso a ku nyanja ya Pacific. Germany anakula mphamvu kwambili moti anayamba kupikisana na dziko la Britain. (Ŵelengani Danieli 11:25) Dziko la Germany linakhazikitsa gulu lankhondo lalikulu kwambili komanso lamphamvu lotsala pang’ono kulingana na la Britain. Pankhondo yoyamba ya padziko lonse, Germany anaseŵenzetsa gulu limeneli la asilikali polimbana na adani ake.

      10. Kodi ulosi wa pa Danieli 11:25b, 26 unakwanilitsidwa bwanji?

      10 Ndiyeno, Danieli anakambilatu zimene zinali kudzacitikila Ulamulilo wa Germany na gulu lake la asilikali. Ulosiwo unakamba kuti mfumu ya kumpoto ‘sidzalimba.’ Cifukwa ciani? “Cifukwa adzamukonzela ciwembu. Anthu amene amadya zakudya zake zokoma ndi amene adzacititsa kuti iye athyoke.” (Dan. 11:25b, 26a) M’masiku a Danieli, anthu amene anali ‘kudya zakudya zokoma za mfumu’ anali akulu-akulu ‘otumikila mfumu.’ (Dan. 1:5) Kodi pamenepa ulosiwu ukamba za ndani? Ukamba za anthu a udindo wapamwamba mu Ufumu wa Germany, monga akulu-akulu a asilikali komanso alangizi a zankhondo. M’kupita kwa nthawi, amenewa anacititsa kuti ufumu wa Germany uthe mphamvu.e Ulosi wa Danieli sunakambe cabe za kutha mphamvu kwa ulamulilo wa Germany, koma unakambanso za mmene nkhondo ya pakati pa Germany na mfumu ya kum’mwela idzayendela. Pokamba za mfumu ya kumpoto, ulosiwo unati: “Pamenepo gulu lake lankhondo lidzagonja ngati kuti latengedwa ndi madzi osefukila, ndipo anthu ambili adzaphedwa.” (Dan. 11:26b) Monga mmene ulosiwo unakambila, pankhondo yoyamba ya padziko lonse, gulu la asilikali a Germany ‘linagonja ngati kuti latengedwa ndi madzi osefukila,’ moti ‘anthu ambili anaphedwa.’ Pankhondoyo panaphedwa anthu ambili kuposa amene anaphedwa pankhondo ina iliyonse kumbuyoko.

      11. Kodi mafumu aŵili, ya kumpoto komanso ya kum’mwela, anacita ciani?

      11 Pofotokoza zimene zinacitika Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse ili pafupi kuyamba, Danieli 11:27, 28 imakamba kuti mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela “azidzalankhula bodza patebulo limodzi.” Izi n’zimenedi zinacitika. Maiko a Germany na Britain anali kukambilana zakuti afuna mtendele, koma nkhondo imene inayamba mu 1914 inaonetselatu kuti zokamba zawozo zinali zabodza. Ulosi wa Danieli umakambanso kuti mfumu ya kumpoto idzadziunjikila “katundu woculuka.” Mogwilizana na ulosi umenewu, podzafika m’caka ca 1914, dziko la Germany linali litakhala dziko laciŵili lolemela kwambili padziko lonse. Ndiyeno, pokwanilitsa ulosi wa pa Danieli 11:29, na mbali yoyamba ya vesi 30, dziko la Germany linamenya nkhondo na mfumu ya kum’mwela, koma linagonjetsedwa.

      MAFUMU AŴILIWA AKHALA AKUZUNZA ANTHU A MULUNGU

      12. Kodi mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela anacita ciani pankhondo yoyamba ya padziko lonse?

      12 Kucokela mu 1914, mafumu aŵiliwa, ya kumpoto na ya kum’mwela, akhala akulimbana kwambili komanso kuzunza anthu a Mulungu. Mwacitsanzo, pankhondo yoyamba ya padziko lonse, maboma a Germany na Britain anazunza atumiki a Mulungu amene anakana kumenya nawo nkhondo. Boma la America linaponya m’ndende abale amene anali kutsogolela pa nchito yolalikila. Cizunzo cimeneci cinakwanilitsa ulosi wa pa Chivumbulutso 11:7-10.

      13. N’ciani cimene mfumu ya kumpoto inacita m’zaka za m’ma 1930 komanso pankhondo yaciŵili ya padziko lonse?

      13 M’zaka za m’ma 1930 komanso maka-maka pankhondo yaciŵili ya padziko lonse, mfumu ya kumpoto inazunza anthu a Mulungu mwankhanza kwambili. Cipani ca Nazi citayamba kulamulila Germany, Hitler na otsatila ake analetsa nchito ya anthu a Mulungu. Anthu otsutsawo anapha atumiki a Yehova pafupi-fupi 1,500, ndipo ena ofika m’masauzande anawatsekela m’ndende zacibalo. Ulosi wa Danieli unakambilatu kuti zimenezi zidzacitika. Mfumu ya kumpoto inaika ziletso pa atumiki a Mulungu kuti asakhale na ufulu wotamanda dzina la Yehova poyela. Mwa kucita izi, ‘inaipitsa malo opatulika’ ndiponso ‘inacotsa nsembe zoyenela kupelekedwa nthawi zonse.’ (Dan. 11:30b, 31a) Mtsogoleli wa dzikolo, dzina lake Hitler, anacita kulumbila kuti adzafafanizilatu Mboni za Yehova mu Germany.

      MFUMU YATSOPANO YA KUMPOTO IONEKELA

      14. Ndani anakhala mfumu ya kumpoto pambuyo pankhondo yaciŵili ya padziko lonse? Fotokozani.

      14 Pambuyo pankhondo yaciŵili ya padziko lonse, boma la cikomyunizimu la Soviet Union linayamba kulamulila maiko amene linalanda kwa Germany. Boma la Soviet Union na maiko ogwilizana naye ndiwo anakhala mfumu ya kumpoto. Mofanana na ulamulilo wopondeleza wa Nazi, boma la Soviet Union linali kuzunza mwankhanza aliyense amene anali kulambila Mulungu woona mokhulupilika m’malo momvela zilizonse zimene boma lalamula.

      15. Kodi mfumu ya kumpoto inacita ciani Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha?

      15 Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha, posapita nthawi mfumu yatsopano ya kumpoto, kutanthauza Soviet Union na maiko ogwilizana naye, inayamba kuzunza anthu a Mulungu. Mogwilizana na ulosi wa pa Chivumbulutso 12:15-17, mfumu ya kumpoto imeneyi inaletsa nchito yolalikila komanso inathamangitsila ku Siberia anthu a Yehova ofika m’masauzande. M’nthawi yonse ya masiku otsiliza ano, mfumu ya kumpoto yakhala ‘ikulavula madzi ngati mtsinje’ kapena kuti kuzunza anthu a Mulungu pofuna kuletsa nchito yawo, koma yalephela.f

      16. Kodi boma la Soviet Union linakwanilitsa bwanji ulosi wa pa Danieli 11:37-39?

      16 Ŵelengani Danieli 11:37-39. Pokwanilitsa ulosi wa pa lembali, mfumu ya kumpoto inacita zinthu ‘mosaganizila Mulungu wa makolo ake.’ Kodi inacita bwanji zimenezi? Pofuna kuthetsa zipembedzo, boma la Soviet Union linapanga pulani inayake yomwe colinga cake cinali kulanda mphamvu zipembedzo. Kuyambila mu 1918, bomalo linakhazikitsa lamulo limene linapangitsa kuti m’kupita kwa nthawi, kumasukulu ana aziphunzitsidwa zakuti kulibe Mulungu. Nanga kodi mfumu ya kumpoto inapeleka bwanji “ulemu kwa mulungu wa m’malo okhala ndi mipanda yolimba kwambili”? Boma la Soviet Union linawononga ndalama zambili-mbili popanga gulu la nkhondo lalikulu ndi la mphamvu kwambili, komanso popanga zida za nyukiliya masauzande oculuka kuti ulamulilo wake ukhale wamphamvu. M’kupita kwa nthawi, mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela, onse anakwanitsa kupanga zida zankhondo zambili zamphamvu zotha kupha anthu mabiliyoni!

      MAFUMU OLIMBANAWO ANACITILA ZINTHU PAMODZI

      17. Kodi “cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko” n’ciani?

      17 Mfumu ya kumpoto inacilikiza mfumu ya kum’mwela m’njila inayake yapadela. Iwo ‘anaika pamalowo cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko.’ (Dan. 11:31) “Cinthu conyansa” cimeneco ni bungwe la United Nations.

      18. N’cifukwa ciani Bungwe la United Nations limachulidwa kuti “cinthu conyansa”?

      18 N’cifukwa ciani Bungwe la United Nations likuchulidwa kuti “cinthu conyansa”? Cifukwa bungweli limakamba kuti lingakwanitse kubweletsa mtendele padziko lonse, pamene m’ceni-ceni Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo ungakwanitse kucita zimenezi. Ulosiwu umakambanso kuti cinthu conyansa cimeneci ni “cobweletsa ciwonongeko,” cifukwa cakuti bungwe la United Nations ndilo lidzaukila zipembedzo zonama na kuziwononga.—Onani chati yakuti, “Mafumu Olimbana M’nthawi Yamapeto.”

      N’CIFUKWA CIANI KUDZIŴA MBILI IMENEYI N’KOFUNIKA?

      19-20. (a) N’cifukwa ciani mbili imene takambilanayi ni yofunika kuidziŵa bwino? (b) Tidzakambilana funso liti m’nkhani yotsatila?

      19 Kudziŵa mbili imeneyi n’kofunika cifukwa ipeleka umboni wakuti kucokela mu 1870 mpaka mu 1991, ulosi wa Danieli wokamba za mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela unakwanilitsidwa. Conco, sitikayika konse kuti mbali yothela ya ulosiwu nayonso idzakwanilitsidwa.

      20 Mu 1991, ulamulilo wa Soviet Union unatha. Nanga n’ndani amene akulamulila monga mfumu ya kumpoto masiku ano? Nkhani yotsatila idzayankha funso limeneli.

      KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

      • Ni zinthu zitatu ziti zimene zimatithandiza kudziŵa “mfumu ya kumpoto” na “mfumu ya kum’mwela”?

      • Ni maiko ati amene analamulila monga mfumu ya kumpoto komanso mfumu ya kum’mwela kucokela m’ma 1870 mpaka mu 1991?

      • N’cifukwa ciani mbili imene takambilanayi ni yofunika kuidziŵa bwino?

      NYIMBO 128 Pilila Mpaka Mapeto

      a Tikuona umboni woonetsa kuti ulosi wa Danieli wokamba za “mfumu ya kumpoto” na “mfumu ya kum’mwela” ukupitiliza kukwanilitsidwa. N’cifukwa ciani sitikukayikila zimenezi? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kuumvetsetsa ulosiwu?

      b Pa cifukwa cimeneci, sitingakambenso kuti Mfumu Yaikulu ya Roma, Uleliya (wolamulila kuyambila mu 270-275 C.E.) anali “mfumu ya kumpoto.” Komanso, sitingakambe kuti Mfumukazi Zenobia (wolamulila kuyambila mu 267-272 C.E.) anali “mfumu ya kum’mwela.” Izi zasintha mfundo zimene zili m’buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! macaputa 13 na 14.

      c Onani bokosi yakuti, “Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America mu Ulosi wa m’Baibo.”

      d Mu 1890, Mfumu ya Germany Wilhelm II inacotsa Bismarck paudindo.

      e Anthu a udindo wapamwamba anacita zambili zimene zinapangitsa kuti boma la Germany lithe mphamvu. Mwacitsanzo, analeka kucilikiza mfumu, anali kuulula zinsinsi zokhudza nkhondo, komanso anakakamiza mfumu kuti itule pansi udindo.

      f Malinga na zimene Danieli 11:34 imakamba, kwa kanthawi mfumu ya kumpoto inaleka kuzunza Akhristu. Mwacitsanzo, izi zinacitika pamene ulamulilo wa Soviet Union unatha mu 1991.

  • Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndani Masiku Ano?
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2020 | May
    • NKHANI YOPHUNZILA 20

      Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndani Masiku Ano?

      “Iyo idzafika kumapeto a moyo wake ndipo sipadzapezeka woithandiza.”​—DANIELI 11:45.

      NYIMBO 95 Kuwala Kuwonjezeleka

      ZIMENE TIKAMBILANEa

      1-2. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

      LELOLINO kuposa kale lonse, tili na umboni woculuka wakuti tikukhala ku mapeto kwa masiku otsiliza a dzikoli. Posacedwa, Yehova na Yesu Khristu adzawononga maboma onse amene amatsutsa Ufumu wa Mulungu. Koma izi zisanacitike, mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela adzapitiliza kulimbana okha-okha komanso kulimbana ndi anthu a Mulungu.

      2 M’nkhani ino, tikambilana ulosi wa pa Danieli 11:40 mpaka Danieli 12:1. Pokambilana, tiona kuti mfumu ya kumpoto ndani masiku ano. Tionanso cifukwa cake sitiyenela kuda nkhawa na mavuto amene tidzakumana nawo kutsogoloku.

      MFUMU YATSOPANO YA KUMPOTO IONEKELA

      3-4. Kodi mfumu ya kumpoto ndani masiku ano? Fotokozani.

      3 Ulamulilo wa Soviet Union utatha mu 1991, anthu a Mulungu m’maiko amene anali kulamulidwa na bomalo analandila “thandizo locepa,” kutanthauza kuti anakhala na ufulu kwa kanthawi. (Dan. 11:34) Pa cifukwa cimeneci, iwo anayamba kulalikila mwaufulu, ndipo posapita nthawi anthu masauzande ambili m’maikowo anakhala Mboni. M’kupita kwa nthawi, Russia na maiko ogwilizana naye anakhala mfumu ya kumpoto. Monga tinakambila m’nkhani yapita, boma limakhala mfumu ya kumpoto kapena ya kum’mwela ngati: (1) zocita zake zimakhudza mwacindunji anthu a Mulungu, (2) limacita zinthu zoonetsa kuti limazonda Yehova ndi anthu ake, komanso (3) limalimbana na mfumu inzake yamphamvu.

      4 N’cifukwa ciani takamba kuti Russia na maiko ogwilizana naye ndiwo mfumu ya kumpoto masiku ano? Onani zifukwa izi: (1) Zocita zawo zakhudza mwacindunji anthu a Mulungu. Analetsa nchito yolalikila, ndiponso azunza abale na alongo athu masauzande ambili amene amakhala m’maikowo. (2) Zimene acitazi zaonetsa kuti amazonda Yehova komanso anthu ake. (3) Maiko amenewa akhala akulimbana na mfumu ya kum’mwela, imene ni Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America. Tsopano tiyeni tione zimene Russia na maiko ogwilizana naye acita, zoonetsa kuti iwo ni mfumu ya kumpoto.

      MFUMU YA KUMPOTO NA MFUMU YA KUM’MWELA AKUPITILIZA KUKANKHANA

      5. Kodi Danieli 11:40-43 inakambilatu zocitika za pa nthawi iti? Nanga inati n’ciani cidzacitika pa nthawiyo?

      5 Ŵelengani Danieli 11:40-43. Mbali imeneyi ya ulosi wa Danieli ikamba za zocitika za m’nthawi ya mapeto. Mavesiwa akamba za kulimbana pakati pa mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela. Danieli anakambilatu kuti m’nthawi ya mapeto, mfumu ya kum’mwela idzayamba “kukankhana nayo” mfumu ya kumpoto.—Dan. 11:40.

      6. Kodi pali umboni wotani woonetsa kuti mfumu ya kumpoto yakhala ikukankhana na mfumu ya kum’mwela?

      6 Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akulimbilana ulamulilo wa dziko lonse. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha. Pambuyo pa nkhondoyo, Boma la Soviet Union linayamba kulamulila madela ambili ku Europe. Izi zinakakamiza mfumu ya kum’mwela kupanga mgwilizano wa zankhondo na maiko ena. Mgwilizano umenewo umachedwa NATO (North Atlantic Treaty Organization). Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akupikisana pofuna kupanga gulu lankhondo lamphamvu kwambili padziko lonse. Iwo amawononga ndalama zambili pocita zimenezi. Kuwonjezela apo, mfumu ya kumpoto inalimbana na mfumu ya kum’mwela mwa kuthandiza maiko kapena magulu odana na mfumu ya kum’mwelayo mu Africa, ku Asia, na ku Latin America. M’zaka zaposacedwa, Russia na maiko ogwilizana naye akhala amphamvu kwambili padzikoli. Iwo amalimbana na mfumu ya kum’mwela poseŵenzetsa makompyuta. Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela amaimbana milandu yakuti akuwonongelana mapulogilamu a pa kompyuta, pofuna kusokoneza cuma ca mfumu inzake kapena kugwetsa boma. Ndiponso monga mmene Danieli anakambila, mfumu ya kumpoto ikupitiliza kuzunza anthu a Mulungu.—Dan. 11:41.

      MFUMU YA KUMPOTO ILOŴA “M’DZIKO LOKONGOLA”

      7. Kodi “dziko lokongola” n’ciani?

      7 Lemba la Danieli 11:41 limakamba kuti mfumu ya kumpoto idzaloŵa “m’Dziko Lokongola.” Kodi dziko limeneli n’ciani? Kale, dziko la Isiraeli n’limene linali kuonedwa kuti ni “dziko lokongola kwambili kuposa maiko onse.” (Ezek. 20:6) Dziko limenelo linali kuonedwa lokongola kwambili cifukwa cakuti n’kumene anthu anali kulambila Yehova. Koma kucokela pa Pentekosite wa mu 33 C.E., “dziko lokongola” si dela leni-leni padzikoli. Takamba telo cifukwa tsopano anthu a Yehova ali kulikonse padziko lapansi. Conco, masiku ano, “dziko lokongola” ni paradaiso wauzimu wa anthu a Yehova. Paradaiso ameneyu aphatikizapo zimene anthu a Yehova amacita pom’lambila, monga kusonkhana pamodzi na kulalikila.

      8. Kodi mfumu ya kumpoto inaloŵa bwanji “m’Dziko Lokongola”?

      8 M’masiku otsiliza ano, mfumu ya kumpoto yaloŵa mobweleza-bweleza “m’Dziko Lokongola.” Mwacitsanzo, pamene boma la Nazi ku Germany linali mfumu ya kumpoto, linaloŵa “m’Dziko Lokongola” mwa kuzunza na kupha anthu a Mulungu. Izi zinacitika kwambili pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse. Pambuyo pa nkhondoyo, boma la Soviet Union n’limene linakhala mfumu ya kumpoto. Bomali nalonso linaloŵa “m’Dziko Lokongola” mwa kuzunza anthu a Mulungu na kuwathamangitsila ku Siberia, dela lakutali kwambili na kwawo.

      9. Kodi Russia na maiko ogwilizana naye aloŵa bwanji “m’Dziko Lokongola” m’zaka zaposacedwapa?

      9 M’zaka zaposacedwa, nalonso boma la Russia na maiko ogwilizana nalo aloŵa “m’Dziko Lokongola.” Motani? Mu 2017, mfumu ya kumpoto yatsopano imeneyi inaletsa nchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo, ndiponso inaponya m’ndende ena mwa abale na alongo athu. Bomali linaletsanso mabuku athu, kuphatikizapo Baibulo la Dziko Latsopano. Kuwonjezela apo, linalanda ofesi yathu ya nthambi ya m’dzikolo, Nyumba zina za Ufumu, na Mabwalo ena a Misonkhano. Izi zitacitika, mu 2018 Bungwe Lolamulila linaona kuti Russia na maiko ogwilizana naye ndiwo mfumu ya kumpoto. Koma ngakhale anthu a Yehova azunzidwe bwanji na boma, iwo salimbana nalo kapena kuyesa kusintha ulamulilo. M’malomwake, amatsatila malangizo a m’Baibo akuti tiyenela kupemphelela “anthu onse apamwamba,” maka-maka ngati akupanga zosankha zimene zingakhudze ufulu wa kulambila.—1 Tim. 2:1, 2.

      KODI MFUMU YA KUMPOTO IDZAGONJETSA MFUMU YA KUM’MWELA?

      10. Kodi mfumu ya kumpoto idzagonjetsa mfumu ya kum’mwela? Fotokozani.

      10 Ulosi wa pa Danieli 11:40-45 umakamba kwambili za mfumu ya kumpoto. Kodi izi zitanthauza kuti mfumuyi idzagonjetsa mfumu ya kum’mwela? Iyai. Mfumu ya kum’mwela idzakhala ikali ‘yamoyo’ pamene Yehova na Yesu azidzawononga maboma onse a anthu pa Aramagedo. (Chiv. 19:20) Tidziŵa bwanji zimenezi? Onani zimene maulosi a m’buku la Danieli komanso a m’buku la Chivumbulutso amakamba.

      Mwala wocokela m’phili wagunda mapazi acifanizilo cacikulu.

      Pa Aramagedo, Ufumu wa Mulungu umene umayelekezedwa na mwala, udzaphwanya maboma a anthu, amene akuimilidwa na cifanizilo cacikulu. (Onani ndime 11)

      11. Kodi lemba la Danieli 2:43-45 limaonetsa ciani? (Onani cithunzi pacikuto.)

      11 Ŵelengani Danieli 2:43-45. Mneneli Danieli anafotokoza za maboma osiyana-siyana a anthu amene zocita zawo zinakhudza mwacindunji anthu a Mulungu. Maboma amenewa anawayelekezela na mbali zosiyana-siyana za cifanizilo cacikulu. Boma lotsiliza pa maboma amenewo likuyelekezedwa na mapazi a cifaniziloco, amene ni acitsulo cosakanizika na dongo. Mapaziwo aimila Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America. Ulosi umenewu uonetsa kuti ulamulilowu udzakhalabe ukulamulila pamene Ufumu wa Mulungu udzaphwanya na kuwononga maboma onse a anthu.

      12. Kodi mutu wa 7 wa cilombo uimila ciani? Nanga n’cifukwa ciani kudziŵa zimenezi n’kofunika?

      12 Nayenso mtumwi Yohane anakamba za maboma amphamvu padziko lonse amene zocita zawo zinakhudza anthu a Yehova. Mu ulosi wa Yohane, maboma amenewa anawayelekezela na cilombo ca mitu 7. Mutu wa 7 wa cilombo cimeneci uimila Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America. Kudziŵa mfundo imeneyi n’kofunika cifukwa Baibo imaonetsa kuti cilomboci sicidzakhalanso na mutu wina. Mutu wa 7 umenewu udzakhalabe ukulamulila pamene Khristu na magulu ake ankhondo akumwamba adzawononga mutuwo pamodzi na cilombo.b—Chiv. 13:1, 2; 17:13, 14.

      KODI MFUMU YA KUMPOTO IDZACITA CIANI POSACEDWA?

      13-14. Kodi “Gogi wa kudziko la Magogi” ndani? Nanga zioneka kuti n’ciani cidzamusonkhezela kuukila anthu a Mulungu?

      13 Ulosi wina m’buku la Ezekieli umatithandiza kudziŵa zimene zingadzacitike pamene mafumu aŵili amenewa, ya kumpoto na ya kum’mwela, ali pafupi kuwonongedwa. Cioneka kuti maulosi a pa Ezekieli 38:10-23; Danieli 2:43-45; Danieli 11:44 mpaka caputa 12:1; komanso Chivumbulutso 16:13-16, 21 amafotokoza zocitika zimodzi-modzi. Ngati zilidi conco, ndiye kuti zinthu zotsatilazi n’zimene zidzacitika kutsogolo.

      14 Pa nthawi inayake mkati mwa cisautso cacikulu, “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzapanga mgwilizano wa mitundu. (Chiv. 16:13, 14; 19:19) M’Baibo, mgwilizano umenewo umachedwa “Gogi wa kudziko la Magogi.” (Ezek. 38:2) Mgwilizano wa mitundu umenewu udzaukila anthu a Mulungu komaliza kuti uwafafanize kothelatu. Kodi n’ciani cidzakwiyitsa Gogi kuti acite zimenezi? M’masomphenya aulosi okhudza nthawiyi, mtumwi Yohane anaona matalala akulu-akulu kwambili akugwela adani a Mulungu. Zioneka kuti matalala amenewa akuimila uthenga woŵaŵa waciweluzo, umene anthu a Yehova azikalengeza. N’kutheka kuti uthenga umenewu ndiwo udzakwiyitsa Gogi wa Magogi kuti aukile anthu a Mulungu n’colinga cakuti awafafaniziletu padziko lapansi.—Chiv. 16:21.

      15-16. (a) Kodi zioneka kuti lemba la Danieli 11:44, 45 limakamba za ciani? (b) N’ciani cidzacitikila mfumu ya kumpoto na mitundu ina yonse imene idzakhala Gogi wa Magogi?

      15 Ŵelengani Danieli 11:44, 45. Cioneka kuti lemba limeneli nalonso limakamba za uthenga woŵaŵa waciweluzo komanso za kuukilidwa komaliza kwa anthu a Mulungu. Pa lembali, Danieli anakamba kuti “kotulukila dzuwa ndi kumpoto kudzacokela mauthenga” amene adzasokoneza mfumu ya kumpoto. Ndipo iyo idzapita na “ukali waukulu” kuti ‘ikawononge ambili.’ Zioneka kuti “ambili” amene achulidwa pa lembali ni anthu a Yehova.c Conco, Danieli ayenela kuti anali kukamba za adani amene adzaukila anthu a Mulungu komaliza, n’colinga cakuti awawononge kothelatu.

      16 Mfumu ya kumpoto na maboma ena padzikoli akadzaukila anthu a Mulungu, adzaputa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuzonse, ndipo izi zidzayambitsa nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Panthawiyo, mfumu ya kumpoto pamodzi na mitundu ina yonse imene idzakhala Gogi wa Magogi, idzawonongedwa kothelatu, ndipo “sipadzapezeka woithandiza.”—Dan. 11:45.

      Yesu wakwela pa hosi yoyela ndipo wakonzeka kuponya muvi. Komanso angelo akwela pa mahosi oyela ndipo anyamula malupanga.

      Pa nkhondo ya Aramagedo, Yesu Khristu na magulu ake ankhondo a kumwamba adzawononga dziko loipa la Satana na kupulumutsa anthu a Mulungu (Onani ndime 17)

      17. Kodi “Mikayeli, kalonga wamkulu” wochulidwa pa Danieli 12:1 ndani? Kodi acita ciani palipano, nanga adzacita ciani kutsogolo?

      17 Vesi yoyamba m’caputa 12 ca buku la Danieli, imafotokoza mmene mfumu ya kumpoto na maboma ogwilizana nayo adzawonongedwela. Imafotokozanso mmene Yehova adzatipulumutsila. (Ŵelengani Danieli 12:1.) Kodi vesiyi imatanthauza ciani? Mikayeli ni dzina lina la Mfumu yathu, Khristu Yesu. Kuyambila mu 1914 pamene Ufumu unakhazikitsidwa kumwamba, Khristu ‘anaimilila kuti azithandiza’ anthu a Mulungu. Koma posacedwapa, iye “adzaimilila,” kutanthauza kuti adzawononga adani ake pankhondo ya Aramagedo. Nkhondo imeneyo ndiyo idzakhala cocitika cothela pa “nthawi ya masautso” aakulu kwambili amene Danieli anakamba kuti sanacitikepo. Mu ulosi wa Yohane wolembedwa m’buku la Chivumbulutso, nthawi yovuta imeneyo yomwe idzathela pa Aramagedo, imachedwa “cisautso cacikulu.”—Chiv. 6:2; 7:14.

      KODI DZINA LANU ‘LIDZALEMBEDWA M’BUKU’?

      18. N’cifukwa ciani sitiyenela kukhala na nkhawa tikaganizila zimene zidzacitika kutsogolo?

      18 Onse aŵili, Danieli na Yohane anakamba kuti Yehova na Yesu adzapulumutsa atumiki awo pa “cisautso cacikulu.” Conco, sitiyenela kukhala na nkhawa tikaganizila zimene zidzacitika kutsogolo. Danieli anakamba kuti anthu amene maina awo ‘adzalembedwa m’buku’ ndiwo adzapulumuka. (Dan. 12:1) Tingacite ciani kuti maina athu alembedwe m’buku limenelo? Tifunika kucita zinthu zoonetsa kuti tili na cikhulupililo mwa Yesu, “Mwanawankhosa wa Mulungu.” (Yoh. 1:29) Tifunikanso kudzipatulila kwa Mulungu na kubatizika. (1 Pet. 3:21) Kuwonjezela apo, tifunika kucilikiza Ufumu wa Mulungu mwa kucita zonse zimene tingathe pophunzitsa ena za Yehova.

      19. Kodi tiyenela kucita ciani panthawi ino? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kucita zimenezo?

      19 Ino ndiyo nthawi yofunika kuphunzila kudalila kwambili Yehova na gulu la atumiki ake okhulupilika. Ino ndiyo nthawi yofunika kucilikiza Ufumu wa Mulungu. Tikatelo, tidzapulumuka pamene Ufumu wa Mulungu udzawononga mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela.

      KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

      • Kodi “mfumu ya kumpoto” ndani masiku ano?

      • Kodi mfumu ya kumpoto yaloŵa bwanji “m’Dziko Lokongola”?

      • N’ciani cidzacitikila mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela?

      NYIMBO 149 Nyimbo ya Cipambano

      a Kodi “mfumu ya kumpoto” ndani masiku ano? Nanga idzawonongedwa bwanji? Kudziŵa mayankho pa mafunso amenewa kungalimbitse cikhulupililo cathu, komanso kungatithandize kukonzekela mayeselo amene tidzakumana nawo posacedwa.

      b Kuti mumve mafotokozedwe atsatane-tsatane a Danieli 2:36-45 na Chivumbulutso 13:1, 2, onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012, peji 7-11,12,13-17,18-19.

      c Kuti mumve zambili, onani Nsanja ya Mlonda ya May 15, 2015, peji 29-30.

  • Mafumu Aŵili Olimbana M’nthawi Yamapeto
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2020 | May
    • Mafumu Aŵili Olimbana M’nthawi Yamapeto

      Maulosi ena m’chati ino akamba zinthu zimene zinacitika panthawi yofanana. Maulosi onsewa amatsimikizila kuti tikukhala ‘m’nthawi yamapeto.’​—Dan. 12:4.

      Chati ya maulosi okamba za mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela. Chatiyi ionetsanso maboma amene anali kuimila mafumu aŵiliwa kuyambila mu 1870 mpaka masiku ano.
      • Chati yoyamba pa machati 4, ionetsa maulosi osiyana-siyana ofotokoza za masiku otsiliza ano. Maulosiwa afotokoza zocitika kuyambila m’caka ca 1870 mpaka 1918, ndipo zina mwa zocitikazo zinacitika pa nthawi imodzi. Zaka zoyambila mu 1914 mpaka kutsogolo, zafotokozedwa kukhala masiku otsiliza. Ulosi 1: Cilombo ca mitu 7 cimene cinawonekela kale-kale caka ca 1870 cisanakwane. Mkati mwa Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse mutu wa 7 wa cilomboci unavulazidwa. Kuyambila mu 1917, mutu wa 7 umenewo unacila, ndipo cilombo cinakhalanso ca mphamvu. Ulosi 2: Mfumu ya kumpoto inaonekelanso mu 1871, ndipo mfumu ya kumwela inaonekelanso mu 1870. Mfumu ya kumpoto inali boma la Germany. Mfumu ya kum’mwela poyamba inali Great Britain. Koma mu 1917, Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America ndiwo unakhala mfumu ya kumwela. Ulosi 3: Kuyambila m’zaka za m’ma 1870, M’bale Charles T. Russell na anzake ndiwo anali ‘mthenga.’ Kuciyambi kwa zaka za m’ma 1880, magazini ya Zion’s Watch Tower inalimbikitsa oŵelenga magaziniyi kuti azilalikila uthenga wabwino. Ulosi 4: Kuyambila mu 1914 kupita mtsogolo, nyengo yokolola. Namsongole akumucotsa pakati pa tiligu. Ulosi 5: Kuyambila mu 1917, mapazi acitsulo cosakanizika na dongo anaonekela. Chati ionetsanso izi: Zocitika za padzikoli kuyambila mu 1914 mpaka mu 1918, Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse. Zocitika zokhudza anthu a Yehova: Kuyambila mu 1914 mpaka 1918, Ophunzila Baibo anaponyedwa m’ndende ku Britain na ku Germany. Mu 1918, abale kulikulu lathu anaponyedwa m’ndende ku America.
        Ulosi 1.

        (Ma)lemba Chiv. 11:7; 12:13, 17; 13:1-8, 12

        Ulosi “Cilombo” cakhala cikulamulila padzikoli kwa zaka zoposa 3,000. M’nthawi ya mapeto, mutu wa 7 wa cilomboco unavulazidwa. Pambuyo pake, mutuwo unacila ndipo “dziko lonse” lapansi linatsatila cilomboco. Satana amaseŵenzetsa cilomboci ‘pocita nkhondo ndi otsala.’

        Kukwanilitsidwa kwake Cigumula citapita, maboma a anthu otsutsana na Yehova anayamba kulamulila padzikoli. Patapita zaka zoposa 3,000, padzikoli panacitika Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse. Pa nthawi ya nkhondoyo, limodzi mwa maboma amphamvu lochedwa Britain linacepa mphamvu kwambili. Boma la Britain linakhalanso lamphamvu litagwilizana na boma la America. Maka-maka m’nthawi ya mapeto ino, Satana wakhala akuseŵenzetsa maboma onse a anthu pozunza atumiki a Mulungu.

      • Ulosi 2.

        (Ma)lemba Dan. 11:25-45

        Ulosi Kulimbana kwa mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela m’nthawi yamapeto.

        Kukwanilitsidwa kwake Dziko la Germany linacita nkhondo na Britain na America. Mu 1945, boma la Soviet Union na maiko ogwilizana nalo anakhala mfumu ya kumpoto. Mu 1991, boma la Soviet Union linatha, ndipo m’kupita kwa nthawi dziko la Russia na maiko ogwilizana nalo ndiwo anakhala mfumu ya kumpoto.

      •  Ulosi 3.

        (Ma)lemba Yes. 61:1; Mal. 3:1; Luka 4:18

        Ulosi Yehova adzatumiza “mthenga” wake kuti ‘akonze njila’ Ufumu wa Mesiya usanakhazikitsidwe. Mthengayo adzalengeza “uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.”

        Kukwanilitsidwa kwake Kuyambila m’ma 1870, M’bale C. T. Russell na anzake anali kuphunzila Baibo mwakhama kuti amvetsetse coonadi na kuuzako ena. M’zaka za m’ma 1880, iwo anayamba kulimbikitsa atumiki a Mulungu kuti azilalikila. Anafalitsa nkhani monga yakuti, “Alaliki 1,000 Akufunika,” komanso yakuti “Anadzozedwa Kuti Azilalikila.”

      •  Ulosi 4.

        (Ma)lemba Mat. 13:24-30, 36-43

        Ulosi Munthu anafesa tiligu m’munda. Mdani anabwela na kufesamo namsongole. Namsongoleyo analoledwa kukula mpaka kuphimba tiligu. Panthawi yokolola, namsongoleyo akumucotsa pakati pa tiligu.

        Kukwanilitsidwa kwake Kuyambila mu 1870, kusiyana pakati pa Akhristu oona na Akhristu onama kunayamba kuonekela kwambili. M’nthawi ya mapeto, Akhristu oona akusonkhanitsidwa na kulekanitsidwa na Akhristu onama.

      •  Ulosi 5.

        (Ma)lemba Dan. 2:31-33, 41-43

        Ulosi Mapazi a fano lopangidwa na zinthu zosiyana-siyana. Mapaziwo ni acitsulo cosakanizika na dongo.

        Kukwanilitsidwa kwake Dongo ni anthu wamba olamulidwa na Britain na America amene amatsutsa maboma amenewa. Anthu amenewa amapangitsa kuti ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America uzilephela kucita zinthu mwamphamvu mmene ungathele.

      • Chati yaciŵili pa machati 4, yoonetsa maulosi osiyana-siyana ofotokoza za masiku otsiliza ano. Maulosiwa afotokoza zocitika kuyambila m’caka ca 1919 mpaka 1945, ndipo zina mwa zocitikazo zinacitika pa nthawi imodzi. Boma la Germany ndilo linali mfumu ya kumpoto mpaka kudzafika mu 1945. Ulamulilo wa Mphamvu Padziko Lonse wa Britain na America ndiwo unakhala mfumu ya kum’mwela. Ulosi 6: Mu 1919, Akhristu odzozedwa anayamba kusonkhanitsidwa mumpingo wobwezeletsedwa. Kuyambila mu 1919, nchito yolalikila yapitilizabe ndipo ikupita patsogolo. Ulosi 7: Mu 1920, bungwe la League of Nations linakhazikitsidwa, ndipo linagwila nchito mpaka kuciyambi kwa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Chati ionetsanso izi: Ulosi 1, cilombo ca mitu 7 cikalipo. Ulosi 5, mapazi acitsulo cosakanizika na dongo akalipo. Zocitika padzikoli kuyambila mu 1939 mpaka 1945, Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Zocitika zokhudza anthu a Yehova: Kuyambila mu 1933 mpaka mu 1945, Mboni za Yehova zoposa 11,000 zinaponyedwa m’ndende ku Germany. Kuyambila mu 1939 mpaka mu 1945, Mboni pafupi-fupi 1,600 zinaponyedwa m’ndende ku Britain. Kuyambila mu 1940 mpaka mu 1944, Mboni zinacitidwa cipongwe na magulu aciwawa nthawi zoposa 2,500.
        Ulosi 6.

        (Ma)lemba Mat. 13:30; 24:14, 45; 28:19, 20

        Ulosi “Tiligu” akumusonkhanitsa na kumuika “m’nkhokwe,” ndipo “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” anaikidwa kuti aziyang’anila anchito apakhomo. “Uthenga wabwino uwu wa ufumu” unayamba kulalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”

        Kukwanilitsidwa kwake Mu 1919, kapolo wokhulupilika anaikidwa kuti aziyang’anila anthu a Mulungu. Kuyambila pa nthawiyo, Ophunzila Baibo anawonjezela cangu cawo pa nchito yolalikila. Masiku ano, Mboni za Yehova zimalalikila m’maiko oposa 200, ndiponso zimafalitsa mabuku ophunzilila Baibo m’vitundu voposa 1,000.

      •  Ulosi 7.

        (Ma)lemba Dan. 12:11; Chiv. 13:11, 14, 15

        Ulosi Cilombo ca nyanga ziŵili cinauza anthu “kupanga cifanizilo ca cilombo” ca mitu 7 komanso cinapeleka ‘mpweya ku cifaniziloco.’

        Kukwanilitsidwa kwake Ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America unayambitsa bungwe la League of Nations. Maiko enanso anayamba kucilikiza bungweli. M’kupita kwa nthawi, mfumu ya kumpoto nayonso inaloŵa m’bungweli. Koma inangokhalamo kuyambila mu 1926 mpaka mu 1933. Anthu anali kukhulupilila kuti bungwe la League of Nations lidzabweletsa mtendele padziko lonse, pamene m’ceni-ceni ni Ufumu wa Mulungu wokha ungacite zimenezi. Masiku ano, anthu amakhulupililanso kuti United Nations idzabweletsa mtendele padziko lonse.

      • Chati yacitatu pa machati 4, yoonetsa maulosi osiyana-siyana ofotokoza za masiku otsiliza ano. Maulosiwa afotokoza zocitika kuyambila m’caka ca 1945 mpaka 1991, ndipo zina mwa zocitikazo zinacitika pa nthawi imodzi. Boma la Soviet Union na maiko ogwilizana nalo ndiwo anali mfumu ya kumpoto mpaka mu 1991. Pambuyo pake Russia na maiko ogwilizana naye ndiwo anakhala mfumu ya kumpoto. Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America ndiwo unali Mfumu ya kum’mwela. Ulosi 8: Ciusi ca bomba la nyukiliya, comwe cionetsa kuti Ulamulilo Mphamvu Padziko Lonse wa Britain na America wapha anthu ambili na kuwononga zinthu zambili. Ulosi 9: Bungwe la United Nations linakhazikitsa mu 1945, kulowa m’malo bungwe la League of Nations. Chati ionetsanso izi: Ulosi 1, cilombo ca mitu 7 cokalipo. Ulosi 5, mapazi acitsulo cosakanizika na dongo akalipo. Ulosi 6, mu 1945, panali ofalitsa oposa 156,000. Mu 1991, panali ofalitsa oposa 4,278,000. Zocitika zokhudza anthu a Yehova: Kuyambila mu 1945 mpaka m’zaka za m’ma 1950, boma la Soviet Union linathamangitsila ku Siberia Mboni masausande ambili.
        Ulosi 8.

        Lemba Dan. 8:​23, 24

        Ulosi Mfumu ya maonekedwe oopsa “idzawononga zinthu zambili.”

        Kukwanilitsidwa kwake Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America unapha anthu ambili komanso unawononga zinthu zambili. Mwacitsanzo, pa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse, dziko la America linaponya mabomba aŵili a nyukiliya m’dziko lodana na Britain na America. Mabombawo anapha anthu ambili komanso anawononga zinthu zoculuka kuposa cida cina ciliconse.

      • Ulosi 9.

        (Ma)lemba Dan. 11:31; Chiv. 17:​3, 7-11

        Ulosi ‘Cilombo cofiila kwambili’ cokhala na nyanga 10 cinatuluka m’phompho, ndipo ndico mfumu ya 8. Buku la Danieli limachula mfumu imeneyi kuti “cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko.”

        Kukwanilitsidwa kwake Mkati mwa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse Bungwe la League of Nations linaleka kugwila nchito. Nkhondoyo itatha, bungwe la United Nations ‘linaikidwa pamalowo,’ kapena kuti linakhazikitsidwa. Mofanana na League of Nations, bungwe la United Nations limapatsidwa ulemelelo woyenela kupelekedwa ku Ufumu wa Mulungu. Bungweli lidzaukila zipembedzo zonama.

      •  Chati yothela pa machati 4, yoonetsa maulosi osiyana-siyana ofotokoza za masiku otsiliza. Maulosiwa afotokoza zocitika za masiku ano mpaka kukadutsa nkhondo Aramagedo. Russia na maiko ogwilizana naye ndiwo mfumu ya kumpoto. Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America ndiwo mfumu ya kum’mwela. Ulosi 10: Atsogoleli a maiko adzalengeza ‘bata ndi mtendele.’ Kenako, cisautso cacikulu cidzayamba. Ulosi 11: Maboma adzaukila zipembedzo zonama. Ulosi 12: Maboma a dziko adzaukila anthu a Mulungu. Otsalila odzozedwa adzasonkhanitsidwa kupita kumwamba. Ulosi 13: Aramagedo. Wokwela pa hosi yoyela adzatsiliza kugonjetsa adani ake. Cilombo ca mitu 7 cidzawonongedwa; mapazi acitsulo cosakanizika na dongo acifanizilo cacikulu adzapwanyidwa. Chati ionetsanso izi: Ulosi 1, cilombo ca mitu 7 cidzakhalapobe mpaka pa Aramagedo. Ulosi 5, mapazi acitsulo cosakanizika na dongo adzapitiliza adzakhalapobe mpaka pa Aramagedo. Ulosi 6, tsopano pali ofalitsa oposa 8,580,000. Zocitika zokhudza anthu a Yehova: Mu 2017, boma la Russia linaponya m’ndende Mboni na kulanda ofesi yanthambi.
        Ulosi wa 10 komanso wa 11.

        (Ma)lemba 1 Ates. 5:3; Chiv. 17:16

        Ulosi Atsogoleli a maiko adzalengeza “Bata ndi mtendele!” Kenako “nyanga 10” komanso “cilombo,” zidzaukila “hulelo” na kuliwononga. Pambuyo pake, mitundu ya anthu idzawonongedwa.

        Kukwanilitsidwa kwake Atsogoleli a maiko adzalengeza kuti akwanitsa kubweletsa bata na mtendele padzikoli. Ndiyeno, maiko amene amacilikiza bungwe la United Nations adzawononga zipembedzo zonama. Ici cidzakhala ciyambi ca cisautso cacikulu. Cisautso cacikulu cidzatha pamene Yesu adzawononga mbali yotsala ya dziko la Satana pa Aramagedo.

      • Ulosi 12.

        (Ma)lemba Ezek. 38:11, 14-17; Mat. 24:31

        Ulosi Gogi adzaukila dziko la anthu a Mulungu. Ndiyeno, angelo adzasonkhanitsa anthu “osankhidwa.”

        Kukwanilitsidwa kwake Mfumu ya kumpoto pamodzi na maboma ena onse adzaukila anthu a Mulungu. Panthawi inayake kuukilako kuli mkati, otsalila odzozedwa adzatengedwa kupita kumwamba.

      • Ulosi 13.

        (Ma)lemba Ezek. 38:18-23; Dan. 2:34, 35, 44, 45; Chiv. 6:2; 16:14, 16; 17:14; 19:20

        Ulosi ‘Wokwela’ pa “hachi yoyela” adzatsiliza ‘kugonjetsa adani ake’ mwa kuwononga Gogi na gulu lake la nkhondo. “Cilombo” ‘cidzaponyedwa m’nyanja ya moto,’ komanso cifanizilo cacikulu cidzaphwanyidwa-phwanyidwa.

        Kukwanilitsidwa kwake Yesu, Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzabwela kudzapulumutsa anthu a Mulungu. Iye pamodzi na olamulila anzake 144,000, komanso magulu ankhondo a angelo, adzawononga mitundu yonse ya anthu oukila anthu a Mulungu. Uku ndiye kudzakhala kutha kwa dziko la Satana.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani