LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 10/15 masa. 13-17
  • Mudzakhala “Ufumu wa Ansembe”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mudzakhala “Ufumu wa Ansembe”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • PANGANO LIMENE LIMATETEZA MBEU
  • MTUNDU WATSOPANO UBADWA
  • PANGANO LATSOPANO LIYAMBA KUGWILA NCHITO
  • PANGANO LIMENE LILOLA ENA KULAMULILA NDI KRISTU
  • KHALANI NDI CIKHULUPILILO COSAGWEDELA MU UFUMU WA MULUNGU
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 10/15 masa. 13-17

Mudzakhala “Ufumu wa Ansembe”

“Mudzakhala ufumu wanga wa ansembe ndi mtundu wanga woyela.”—EKS. 19:6.

KODI MUNGAFOTOKOZE BWANJI?

Mwa kugwilitsila nchito zimene zili pa kamutu kakuti “Mmene Mulungu Adzakwanilitsila Cifunilo Cake,” mu nkhani yapita, fotokozani . . .

  • pangano la Cilamulo.

  • pangano latsopano.

  • pangano la Ufumu.

1, 2. N’cifukwa ciani mbeu ya mkazi inafunikila kutetezedwa?

ULOSI woyamba kulembedwa m’Baibulo ndi wofunika kwambili pa kukwanilitsidwa kwa colinga ca Yehova. Popeleka lonjezo la mu Edeni, Mulungu woona anati: “Ndidzaika cidani pakati pa iwe [Satana] ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake.” Kodi udani umenewu unali kudzakhala waukulu motani? Yehova anati: “Mbeu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako [Satana], ndipo iwe udzaivulaza cidendene.” (Gen. 3:15) Udani pakati pa njoka ndi mkazi udzakhala waukulu cakuti Satana adzayesetsa kuononga mbeu ya mkazi.

2 Ndiye cifukwa cake wamasalimo anapemphela ponena za anthu a Mulungu osankhidwa kuti: “Taonani! Adani anu akucita phokoso. Anthu odana nanu kwambili atukula mitu yao. Iwo amakumana mwacinsinsi kuti akambilane zocitila ciwembu anthu anu. Iwo anena kuti: ‘Bwelani tiwafafanize kuti asakhalenso mtundu.’” (Sal. 83:2-4) Mzele wobadwila mbeu ya mkazi unafunikila kutetezedwa, kuti usaonongedwe ndi kuipitsidwa. Kuti Yehova akwanilitse zimenezi, anapanga mapangano ena kuti cifunilo cake cikwanilitsidwe.

PANGANO LIMENE LIMATETEZA MBEU

3, 4. (a) Pangano la Cilamulo linayamba liti kugwila nchito? Ndipo mtundu wa Isiraeli unavomeleza kucita ciani? (b) Nanga pangano la Cilamulo linali kudzateteza ciani?

3 Pamene mbadwa za Abulahamu, Isaki, ndi Yakobo zinaculuka kufika mamiliyoni, Yehova anapanga mtundu wa Isiraeli wakale kucokela ku mbadwa zimenezi. Kupyolela mwa Mose, Yehova anacita pangano lapadela ndi mtundu umenewu mwa kuwapatsa Cilamulo. Ndipo mtundu wa Isiraeli unavomeleza zonse zokhudza pangano limenelo. Baibulo limakamba kuti: “[Mose] anatenga buku la pangano ndi kuŵelengela anthuwo kuti amve. Zitatelo anthuwo anati: ‘Zonse zimene Yehova wanena tidzacita zomwezo ndipo tidzamumvela.’ Pamenepo Mose anatenga magaziwo [a ng’ombe zazimuna] ndi kuwaza anthuwo, ndipo anati: ‘Awa ndiwo magazi okhazikitsila pangano limene Yehova wapangana nanu mwa mau onsewa.’”—Eks. 24:3-8.

4 Pangano la Cilamulo linayamba kugwila nchito pa Phili la Sinai mu 1513 B.C.E. Kupyolela mu pangano limenelo, mtundu wakale wa Isiraeli unakhala mtundu wa Mulungu wosankhidwa. Pamenepo Yehova anakhala ‘Woweluza wao, Wowapatsa Malamulo, ndi Mfumu yao.’ (Yes. 33:22) Mbili ya Isiraeli ionetsa zimene zimacitika ngati malamulo olungama a Mulungu atsatilidwa kapena ngati satsatilidwa. Popeza kuti Cilamulo cinaletsa Aisiraeli kukwatilana ndi mitundu ya cikunja ndi kulambila konama, colinga cake cinali kuteteza mzele wobadwila wa mbadwa za Abulahamu kuti usaipitsidwe.—Eks. 20:4-6; 34:12-16.

5. (a) Pangano la Cilamulo linapeleka mwai wotani kwa Aisiraeli? (b) N’cifukwa ciani Mulungu anakana Aisiraeli?

5 Pamene pangano la Cilamulo linali kugwila nchito, ansembe anaikidwa kuti azitumikila mu Isiraeli. Ansembewo anali kuimila gulu lina la ansembe amene anali kudzatumikila anthu mtsogolo. (Aheb. 7:11; 10:1) Ndipo kupyolela m’pangano limenelo, Aisiraeli anali ndi mwai wapadela wodzakhala “ufumu wa ansembe,” malinga ngati io akanamvela malamulo a Yehova. (Ŵelengani Ekisodo 19:5, 6.) Komabe, Aisiraeli analephela kumvela malamulo amenewo. M’malo moyamikila kubwela kwa Mesiya, amene ndi mbali yoyamba ya mbeu ya Abulahamu, Aisiraeli anamukana. Conco, Mulungu nayenso anawakana.

6. Kodi Cilamulo cinakwanilitsa ciani?

6 Cifukwa ca kusakhulupilika kwao, Aisiraeli sanakhale ufumu wa ansembe. Koma zimenezo sizinacititse Cilamulo kulephela kugwila nchito yake. Cilamulo cinateteza mbeu ndi kuthandiza anthu kudziŵa Mesiya. Cilamulo cinakwanilitsidwa pamene Kristu anabwela padziko lapansi. Baibulo limati: “Kristu ndiye kutha kwa Cilamulo.” (Aroma 10:4) Conco, funso lingakhale lakuti: Ndani amene anali ndi mwai wodzakhala ufumu wa ansembe? Yehova Mulungu anapanga makonzedwe ena oyenelela okhazikitsa mtundu watsopano.

MTUNDU WATSOPANO UBADWA

7. Kupyolela mwa Yeremiya, kodi Yehova anakambilatu ciani ponena za pangano latsopano?

7 Kale kwambili Cilamulo cisanaleke kugwila nchito, Yehova anakambilatu kupyolela mwa mneneli wake Yeremiya kuti, adzacita “pangano latsopano” ndi mtundu wa Isiraeli. (Ŵelengani Yeremiya 31:31-33.) Pangano limenelo linali losiyana ndi pangano la Cilamulo, cifukwa linacititsa kuti macimo akhululukidwe popanda kupeleka nsembe za nyama. Nanga zimenezo zikanatheka bwanji?

8, 9. (a) Magazi okhetsedwa a Yesu anakwanilitsa ciani? (b) Aja amene ali m’pangano la tsopano ali ndi mwai wotani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

8 Zaka mahandiledi pambuyo pake, Yesu anakhazikitsa Mgonelo wa Ambuye pa Nisani 14, 33 C.E. Ponena za kapu ya vinyo, Yesu anauza ophunzila ake okhulupilika 11 kuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa cifukwa ca inu.” (Luka 22:20) Nkhani ya pa Mateyu imagwila mau a Yesu ponena za vinyo kuti: “Vinyoyu akuimila ‘magazi anga a pangano,’ amene adzakhetsedwa cifukwa ca anthu ambili kuti macimo akhululukidwe.”—Mat. 26:27, 28.

9 Magazi amene Yesu anakhetsa ndiwo umboni wa pangano latsopano. Magazi amenewo anacititsanso kuti macimo akhululukidwe kosatha. Koma Yesu sali mbali ya pangano latsopano. Popeza iye ndi wangwilo sanafunikile kukhululukidwa macimo. Mulungu anagwilitsila nchito nsembe yake kuti mbadwa za Adamu zipindule. Iye anasankha anthu ena odzipeleka kuti akhale “ana” mwa kuwadzoza ndi mzimu woyela. (Ŵelengani Aroma 8:14-17.) Mulungu amawaona kuti alibe ucimo monga mmene amaonela Mwana wake Yesu, amene ndi wangwilo. Odzozedwa amenewa adzakhala “olandila coloŵa anzake a Kristu,” ndipo adzakhala ndi mwai wokhala “ufumu wa ansembe.” Uwu unali mwai umene Aisiraeli akanakhala nao pamene anali kutsogoleledwa ndi Cilamulo. Ponena za “olandila coloŵa anzake a Kristu,” mtumwi Petulo anati: “Inu ndinu ‘fuko losankhidwa mwapadela, ansembe acifumu, mtundu woyela, anthu odzakhala cuma capadela, kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambili’ a amene anakuitanani kucoka mu mdima kuloŵa m’kuwala kwake kodabwitsa.” (1 Pet. 2:9) Ndithudi, pangano latsopano n’lofunikadi! Linathandiza ophunzila a Yesu kukhala mbali yaciŵili ya mbeu ya Abulahamu.

PANGANO LATSOPANO LIYAMBA KUGWILA NCHITO

10. Pangano latsopano linayamba liti kugwila nchito? Nanga n’cifukwa ciani silinayambe kugwila nchito nthawi imeneyo?

10 Ndi liti pamene pangano latsopano linayamba kugwila nchito? Pangano limeneli silinayambe kugwila nchito pamene Yesu analichula usiku wake wotsiliza ali padziko lapansi. Kuti liyambe kugwila nchito, coyamba Yesu anafunikila kukhetsa magazi ake. Ndiyeno, mtengo wansembe yake unafunikila kupelekedwa kwa Yehova kumwamba. Mzimu woyela unayenelanso kutsanulidwa pa aja amene anali kudzakhala “olandila coloŵa anzake a Kristu.” Conco, pangano latsopano linayamba kugwila nchito pa Pentekosite wa mu  33 C.E., pamene ophunzila a Yesu okhulupilika anadzozedwa ndi mzimu woyela.

11. Kodi pangano latsopano linathandiza motani Ayuda ndi anthu Akunja kukhala mbali ya Isiraeli wa kuuzimu? Ndipo ndi angati amene adzakhala m’pangano latsopano?

11 Pamene Yehova kupyolela mwa Yeremiya analengeza kuti adzacita pangano ndi Isiraeli, zimenezi zinaonetsa kuti pangano la Cilamulo silidzagwilanso nchito. Cilamulo cinatha nchito pamene pangano latsopano linayamba kugwila nchito. (Aheb. 8:13) Zimenezo zitacitika, Mulungu anayamba kuona Ayuda ndi anthu Akunja osadulidwa mofanana, cifukwa cakuti ‘mdulidwe wao ndi wa mumtima wocitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.’ (Aroma 2:29) Pocita nao pangano latsopano, Mulungu anali kudzaika ‘malamulo ake m’maganizo mwao ndi kuwalemba m’mitima yao.’ (Aheb. 8:10) Ciŵelengelo conse ca anthu a m’pangano latsopano ndi 144,000. Ndipo anthu amenewa amapanga mtundu watsopano umene ndi “Isiraeli wa Mulungu,” kapena kuti Isiraeli wa kuuzimu.—Agal. 6:16; Chiv. 14:1, 4.

12. Pali kufanana kotani pakati pa pangano la Cilamulo ndi pangano latsopano?

12 Nanga pangano la Cilamulo limafanana bwanji ndi pangano latsopano? Pangano la Cilamulo linali pakati pa Yehova ndi Isiraeli wakuthupi, ndipo pangano latsopano lili pakati pa Yehova ndi Isiraeli wa kuuzimu. Mose anali mkhalapakati wa pangano la Cilamulo, koma Yesu ndiye Mkhalapakati wa pangano latsopano. Magazi a nyama anali umboni wa pangano la Cilamulo, pamene magazi okhetsedwa a Yesu ndi umboni wa pangano latsopano. Pamene pangano la Cilamulo linali kugwila nchito, Mose ndiye anali kutsogolela mtundu wa Isiraeli. Mofananamo, Yesu, Mutu wa mpingo, ndiye mtsogoleli wa anthu amene ali m’pangano latsopano.—Aef. 1:22.

13, 14. (a) Pangano latsopano ndi logwilizana motani ndi Ufumu? (b) N’ciani cinali kufunikila kuti Isiraeli wa kuuzimu akalamulile ndi Kristu kumwamba?

13 Pangano latsopano ndi logwilizana ndi Ufumu mwanjila yakuti limapanga mtundu woyela, umene uli ndi mwai wodzakhala mafumu ndi ansembe mu Ufumu wakumwamba. Mbali yaciŵili ya mbeu ya Abulahamu ndiyo imapanga mtundu umenewo. (Agal. 3:29) Conco, pangano latsopano limacilikiza pangano la Abulahamu.

14 Koma palinso mbali ina ya Ufumu imene iyenela kukhazikitsidwa. Pangano latsopano limayala maziko a anthu amene adzakhala “olandila coloŵa anzake a Kristu.” Komabe, panali kufunikila makonzedwe oyenelela kuti io akalamulile ndi Yesu mu Ufumu wake monga mafumu ndi ansembe.

PANGANO LIMENE LILOLA ENA KULAMULILA NDI KRISTU

15. Ndi pangano lotani limene Yesu anapanga ndi ophunzila ake okhulupilika?

15 Yesu atayambitsa Mgonelo wa Ambuye, anakhazikitsa pangano ndi ophunzila ake okhulupilika. Pangano limeneli limachedwa pangano la Ufumu. (Ŵelengani Luka 22:28-30.) Mosiyana ndi mapangano ena, Yehova alibe mbali m’pangano limeneli. M’malo mwake, pangano limeneli lili pakati pa Yesu ndi odzozedwa. Pamene Yesu anati, “mmene Atate wanga wacitila pangano la ufumu ndi ine,” mwacionekele anali kukamba za pangano limene Yehova anapanga ndi iye kuti akhale “wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”—Aheb. 5:5, 6.

16. Pangano la Ufumu limapeleka mwai wotani kwa Akristu odzozedwa?

16 Ophunzila a Yesu okhulupilika 11, ‘anakhalabe ndi Yesu m’mayeselo ake.’ Pangano la Ufumu linawatsimikizila kuti adzakhala pamipando yacifumu, ndi kulamulila monga mafumu ndi kutumikila monga ansembe. Komabe, mwai umenewu sunapelekedwe kwa atumwi 11 okha. Yesu mu ulemelelo wake anaonekela kwa mtumwi Yohane m’masomphenya ndi kukamba kuti: “Wopambana pa nkhondo ndidzamulola kukhala nane pampando wanga wacifumu, monga mmene ine ndinakhalila ndi Atate wanga pampando wao wacifumu.” (Chiv. 3:21) Motelo, pangano la Ufumu linacitidwa ndi Akristu odzozedwa okwanila 144,000. (Chiv. 5:9, 10; 7:4) Pangano limeneli limawalola kulamulila ndi Yesu kumwamba. Zimenezi n’zofanana ndi mkazi amene wakwatiwa ndi mfumu. Iye akakwatiwa, amalamulila ndi mfumuyo. Ndipo Malemba amakamba za Akristu odzozedwa kuti ndi “mkazi” wa Kristu, “namwali woyela” amene walonjezedwa kukwatiwa ndi Kristu.—Chiv. 19:7, 8; 21:9; 2 Akor. 11:2.

KHALANI NDI CIKHULUPILILO COSAGWEDELA MU UFUMU WA MULUNGU

17, 18. (a) Fotokozani mwacidule mapangano 6 amene takambilana amene amagwilizana ndi Ufumu. (b) N’cifukwa ciani tiyenela kukhala ndi cikhulupililo cosagwedela mu Ufumu?

17 M’nkhani ziŵilizi, takambilana mmene mapangano amenewo amagwilizanilana ndi mbali zofunika zokhudza Ufumu. (Onani kamutu kakuti, “Mmene Mulungu Adzakwanilitsila Cifunilo Cake.”) Malinga ndi mapangano oona amenewa, sitikaikila kuti Ufumu umenewu udzapambana. Tili ndi cikhulupililo cosagwedela cakuti Ufumu wa Mesiya ndiwo njila yokha imene Mulungu adzagwilitsila nchito kukwanilitsa cifunilo cake ca dziko lapansi ndi ca mtundu wa anthu.—Chiv. 11:15.

18 Sitikaikila kuti Ufumuwo udzathetsa mavuto a mtundu wa anthu. Motelo, tili ndi cidalilo cakuti Ufumu Mulungu udzabweletsa madalitso osatha kwa anthu onse. Conco, tiziuzako ena coonadi ca Ufumu cimeneci mwacangu.—Mat. 24:14.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani