NYIMBO 43
Pemphelo la Mayamiko
Yopulinta
(Salimo 95:2)
1. Yehova, Mulungu wamphamvuzonse,
Tikufikilani mu pemphelo.
Atate tagwada pamaso panu,
Conde mvelani pemphelo lathu.
Nthawi na nthawi ise timacimwa;
Tipempha mutikhululukile.
M’namutuma Yesu kudzatifela,
Tifuna tikutumikileni.
2. Mulungu wathu tikuyamikila,
Munatibweletsa m’gulu lanu.
Tithandizeni, ‘se tiphunzitseni,
Sitifuna kum’siyani imwe.
Cifukwa ca mzimu wanu woyela
Sitimayopa kulalikila.
Mwacimwemwe tidzakutamandani,
Ise tidzakutumikilani.
(Onaninso Sal. 65:2, 4, 11; Afil. 4:6.)