NYIMBO 12
Mulungu Wamkulu, Yehova
Yopulinta
(Ekisodo 34:6, 7)
1. M’lungu Wamkulu
ndimwe Yehova,
Atate wacikondi tidzakutamandani.
Ndimwe wabwino mu zinthu zonse.
Ndimwe M’lungu kosatha.
2. Atate wathu
mumatikonda.
Olo ndise ocimwa mumatisamalila.
Tiyamikila mumatiyankha,
Ise tikapemphela.
3. Mokweza mau za
padzikoli
Na zonse za kumwamba zimakuimbilani.
Na mtima wonse tidzatamanda
Imwe Yehova M’lungu.
(Onaninso Deut. 32:4; Miy. 16:12; Mat. 6:10; Chiv. 4:11.)