LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso citundu cina: Betsileo
  • Lelo

Mande, October 27

Amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondela matupi awo.​—Aef. 5:28.

Yehova amayembekezela mwamuna kumukonda mkazi wake na kumusamalila kuthupi komanso kuuzimu. Kukhala oganiza bwino, kulemekeza akazi, komanso kukhala wodalilika, kungakuthandizeni mukadzakwatila. Mukakwatila, mungakhale tate. Mungaphunzile ciyani kwa Yehova pa nkhani yokhala tate wabwino? (Aef. 6:4) Yehova anauza mwana wake Yesu pa anthu kuti amamukonda komanso kuti amakondwela naye. (Mat. 3:17) Mukadzakhala tate muzikaonetsetsa kuti nthawi na nthawi mukuwatsimikizila ana anu kuti mumawakonda. Muzikawayamikila moona mtima pa zimene azikacita bwino. Atate amene amatengela citsanzo ca Yehova amathandiza ana awo kukhala Akhristu okhwima. Mungakonzekele pali pano udindo umenewu mwa kusamalila ena mwacikondi m’banja na mu mpingo komanso mwa kuwayamikila.​—Yoh. 15:9. w23.12 28-29 ¶17-18

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵili, October 28

Mʼmasiku anu, [Yehova] adzacititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.​—Yes. 33:6.

Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupilika a Yehova, nafenso timakumana na zovuta, komanso kudwala monga mmene zilili na anthu ena. Kuwonjezela apo, timafunikanso kupilila citsutso kapena mazunzo ocokela kwa anthu amene amadana na anthu a Mulungu. Ngakhale kuti Yehova satiteteza ku mavutowa, iye analonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Na thandizo lake, tingakhalebe acimwemwe, kupanga zisankho zanzelu, komanso kukhalabe okhulupilika kwa iye ngakhale pomwe tikukumana na zinthu zovuta. Yehova analonjeza kutipatsa cimene Baibo imacha “mtendele wa Mulungu.” (Afil. 4:6, 7) Mtendele umenewu umatithandiza kukhala odekha, komanso a bata mu mtima cifukwa cokhala pa ubale wa mtengo wapatali na iye. Mtendele umenewu “anthu sangathe kuumvetsa”; ndipo ni wapadela kwambili kuposa mmene tingaganizile. Kodi munakhalapo wodekha pambuyo popemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima? Munamva conco cifukwa iye anakupatsani “mtendele wa Mulungu.” w24.01 20 ¶2; 21 ¶4

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Citatu, October 29

Moyo wanga utamande Yehova. Ciliconse ca mkati mwanga, citamande dzina lake loyela.​—Sal. 103:1.

Kukonda Mulungu kumasonkhezela anthu okhulupilika kulemekeza dzina lake na mtima wonse. Mfumu Davide anadziŵa kuti kutamanda dzina la Yehova kunali kutamanda Yehova iye mwini. Dzina la Yehova limaphatikizapo mbili yake. Limatikumbutsa za makhalidwe ake abwino, komanso zocita zake zocititsa cidwi. Davide anaona dzina la Atate wake kukhala loyela, ndipo analitamanda. Anacita zimenezi na ‘ciliconse ca mkati mwake’​—kutanthauza kuti na mtima wake wonse. Mofananamo, Alevi anatsogolela pa nchito yotamanda Yehova. Iwo anavomeleza modzicepetsa kuti mawu awo sakanakwanitsa kupeleka citamando coyenela kupatulika kwa dzinalo. (Neh. 9:5) Mosakaikila, mawu odzicepetsa acitamando amenewa, anakondweletsa mtima wa Yehova. w24.02 9 ¶6

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani