LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g18 na. 2 tsa. 5
  • 2 Kugwilizana

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 2 Kugwilizana
  • Galamuka!—2018
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE KUMATANTHAUZA
  • CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA
  • ZIMENE MUNGACITE
  • KAMBILANANI NA MNZANU WA M’CIKWATI
  • MUNGACITENSO IZI
  • ‘Cikwati Cikhale Colemekezeka’
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • 3 Kulemekezana
    Galamuka!—2018
  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Cikwati Canu?
    Galamuka!—2021
  • 1 Kukhulupilika
    Galamuka!—2018
Onaninso Zina
Galamuka!—2018
g18 na. 2 tsa. 5
Okwatilana acitila zinthu pamodzi monga woyendetsa ndeke na wom’thandiza wake

Kugwilizana kumatanthauza kucita zinthu monga woyendetsa ndeke na wom’thandiza wake amene onse ali na colinga copita ku malo amodzi

KWA OKWATILANA

2 Kugwilizana

ZIMENE KUMATANTHAUZA

Ngati mwamuna na mkazi amagwilizana amakhala monga woyendetsa ndeke na wom’thandiza wake amene onse ali na colinga copita ku malo amodzi. Ngakhale pamene akumana na mavuto, aliyense amakhala na maganizo akuti, “tidzacita ciani” osati “nidzacita ciani.”

MFUNDO YA M’BAIBO: “Salinso aŵili, koma thupi limodzi.”—Mateyu 19:6.

“Ukwati sudalila pa munthu mmodzi. Onse mwamuna na mkazi afunika kucitila zinthu pamodzi kuti banja lawo liyende bwino.”—Christopher.

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA

Ngati mwamuna na mkazi ni osagwilizana, akasemphana maganizo amayamba kupezana zifukwa m’malo mothetsa vutolo. Nkhani zing’ono-zing’ono zimakula kukhala mavuto aakulu.

“Kugwilizana n’kofunika kwambili m’cikwati. Ine na mwamuna wanga tikanakhala kuti sitinali kucita zinthu mogwilizana, sembe tili monga anthu aŵili amene akhala cabe m’nyumba imodzi, ndipo sakambilana popanga zosankha zikulu-zikulu.”—Alexandra.

ZIMENE MUNGACITE

DZIFUFUZENI

  • Kodi nimaona kuti ndalama zimene nimapeza “zonse n’zanga cabe”?

  • Kodi nimakondwela maningi nikakhala kuti sinili pamodzi na mwamuna kapena mkazi wanga?

  • Kodi nimaipidwa ndi acibululu a mwamuna kapena a mkazi wanga, olo kuti iye amawakonda kwambili?

KAMBILANANI NA MNZANU WA M’CIKWATI

  • Kodi ni zinthu ziti zimene timakonda kucitila pamodzi mogwilizana m’cikwati cathu?

  • Kodi ni mbali ziti zimene tingafunike kuongolela?

  • Kodi tingacite ciani kuti tikulitse mgwilizano wathu?

MUNGACITENSO IZI

  • Yelekezelani kuti muchaya nsolo ndipo mnzanu wa m’cikwati ali ku timu ina. Kodi mungacite ciani kuti mukhale timu imodzi na mnzanu wa m’cikwati?

  • M’malo moganiza kuti, ‘Ningacite ciani kuti niwine?’ muziganiza kuti, ‘Tingacite ciani kuti tiwine?’

“Musamakonda kuganizila zakuti wolakwa n’ndani nanga wosalakwa n’ndani. Zimenezo zilibe phindu kweni-kweni. Cofunika kwambili ni mtendele komanso mgwilizano m’cikwati.”—Ethan.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.”—Afilipi 2:3, 4.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani