Mukadzidziŵa bwino, simungagonje mukakumana ndi ziyeso zimene zili monga cimphepo camphamvu
KWA ACICEPELE
9 Umunthu Wanu
ZIMENE UMATANTHAUZA
Umunthu wanu umaposa dzina lanu kapena maonekedwe anu. Umaphatikizapo makhalidwe anu, zimene mumakhulupilila, komanso zocita zanu. Inde, umunthu wanu umaphatikizapo zonse zokhudza imwe.
CIFUKWA CAKE NI WOFUNIKA
Ngati umunthu wanu muudziŵa bwino, mudzakwanitsa kukhalila kumbuyo zimene mumakhulupilila, komanso kupewa kumangotengela zocita za anzanu.
“Anthu ambili ali monga akadoli otsatsila malonda a zovala mu shopu. Iwo samadzisankhila okha zovala zimene ayenela kuvala, koma ena ndi amene amawasankhila.”—Adrian.
“Naphunzila kusagwedezeka pocita coyenela olo pamene kuli kovuta kutelo. Nimakwanitsa kudziŵa kuti anzanga eni-eni ni ati, mwa kuona mmene iwo amacitila zinthu komanso mmene ine nimamasukila nikakhala pakati pawo.”—Courtney.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.”—Aroma 12:2.
ZIMENE MUNGACITE
Dzifufuzeni kuti mudziŵe mmene umunthu wanu ulili tsopano komanso mtundu wa munthu amene mufuna kukhala, mwa kuona zimene mumacita bwino, zimene simucita bwino, komanso zimene m’makhulupilila. Kuti muyambe kucita zimenezi, mungacite bwino kuyankha mafunso otsatilawa.
Zimene mumacita bwino: Kodi nili na maluso ati? Kodi nimacita bwino mbali ziti? (Mwacitsanzo: Kodi nimasunga nthawi? Kodi ndine wodziletsa? wolimbikila nchito? wopatsa?) Nanga n’zinthu zabwino ziti zimene nimacita?
CINANSO CIMENE MUNGACITE: Kodi zikukuvutani kudziŵa zimene mumacita bwino? Funsani kholo lanu kapena mnzanu wodalilika kuti akuuzeni zimene mumacita bwino komanso cifukwa cake wakuuzani zimenezo.
MFUNDO YA M’BAIBO: “Aliyense payekha ayese nchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatelo adzakhala ndi cifukwa cosangalalila ndi nchito yake, osati modziyelekezela ndi munthu wina.”—Agalatiya 6:4.
Zimene simucita bwino: Kodi ni makhalidwe ati amene nifunika kuongolela? Ni panthawi iti maka-maka pamene nimalephela kupilila ciyeso? Nanga nifunika kuonetsa kwambili kudziletsa pa mbali ziti?
MFUNDO YA M’BAIBO: “Tikanena kuti: ‘Tilibe ucimo,’ ndiye kuti tikudzinamiza.”—1 Yohane 1:8.
Zimene mumakhulupilila: Kodi ni mfundo ziti za makhalidwe abwino zimene nimayendela? Ndipo n’cifukwa ciani? Kodi nimakhulupilila kuti Mulungu aliko? Kodi n’ciani cimanipangitsa kukhulupilila kuti iye aliko zoona? Kodi n’zinthu ziti zimene nimaona kuti n’zopanda cilungamo? Ndipo n’cifukwa ciani? Nanga n’zinthu ziti zimene nimakhulupilila kuti zidzacitika m’tsogolo?
MFUNDO YA M’BAIBO: “Kuganiza bwino kudzakuyang’anila, ndipo kuzindikila kudzakuteteza.”—Miyambo 2:11.