NKHANI 8
Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
Kodi Baibo imatiuza ciani za Ufumu wa Mulungu?
Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita ciani?
Kodi Ufumu umenewu udzakwanilitsa liti cifunilo ca Mulungu padziko lapansi?
1. Kodi tsopano tidzakambitsilana pemphelo lochuka liti?
ANTHU oculuka padziko lapansi amalidziŵa pemphelo limene ambili amalicha pemphelo la Atate Wathu Wakumwamba, kapena kuti Pemphelo la Ambuye. Maina onsewa amanena za pemphelo lochuka limene Yesu Kristu mwini wake anapeleka monga citsanzo. Pemphelo limeneli ndi latanthauzo kwambili. Kukambitsilana zopempha zitatu zoyambilila za m’pemphelo limeneli kudzakuthandizani kudziŵa zambili zimene Baibo imaphunzitsa m’ceni-ceni.
2. Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kupemphelela zinthu zitatu ziti?
2 Ku ciyambi kwa pemphelo lacitsanzo limeneli, Yesu analangiza omvela ake kuti: “Muzipemphela motele: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.’” (Mateyu 6:9-13) Kodi zopempha zitatu izi zimatanthauza ciani?
3. Kodi tiyenela kudziŵa ciani ponena za Ufumu wa Mulungu?
3 Taphunzila zambili za dzina la Mulungu lakuti Yehova. Ndipo takambitsilanako za cifunilo ca Mulungu—zimene wacita kale ndi zimene adzacitila mtundu wa anthu. Koma kodi Yesu anali kutanthauza ciani pamene anatiuza kupemphela kuti: “Ufumu wanu ubwele”? Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani? Kodi kubwela kwake kudzayeletsa bwanji dzina la Mulungu? Ndipo kodi kubwela kwa Ufumu umenewu kugwilizana bwanji ndi kucitika kwa cifunilo ca Mulungu?
KODI UFUMU WA MULUNGU N’CIANI?
4. Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani? Nanga Mfumu yake ndani?
4 Ufumu wa Mulungu ndi boma lokhazikitsidwa ndi Yehova Mulungu lokhala ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndani? Ndi Yesu Kristu. Yesu monga Mfumu ndi wamkulu kuposa olamulila onse padziko lapansi ndipo iye amachedwa Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. (1 Timoteyo 6:15) Iye ali ndi mphamvu yocita zinthu zabwino kwambili kuposa wolamulila aliyense, ngakhale wolamulila amene angaoneke kukhala wocita bwino zinthu.
5. Kodi Ufumu wa Mulungu udzalamulila kucokela kuti? Ndipo udzalamulila ndani?
5 Kodi Ufumu wa Mulungu udzakhala kuti polamulila? Kodi Yesu ali kuti? Kumbukilani zimene tinaphunzila kuti iye anaphedwa mwa kukokhomeledwa pamtengo wozunzikilapo, ndipo pambuyo pake anaukitsidwa. Patapita masiku 40, Yesu anabwelela kumwamba. (Machitidwe 2:33) Conco, kumeneko n’kumene kuli Ufumu wa Mulungu. Ndiye cifukwa cake Baibo imaucha kuti ‘ufumu wakumwamba.’ (2 Timoteyo 4:18) Ngakhale kuti Ufumu wa Mulungu uli kumwamba, udzalamulila dziko lonse lapansi.—Chivumbulutso 11:15.
6, 7. Kodi n’ciani cipangitsa Yesu kukhala Mfumu yapadela?
6 N’ciani cikupangitsa Yesu kukhala Mfumu yapadela? Cifukwa cimodzi n’cakuti, iye sadzafa. Poyelekezela Yesu ndi mafumu a padziko lapansi, Baibo imafotokoza kuti “Iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa, amene amakhala m’kuwala kosafikilika.” (1 Timoteyo 6:16) Izi zimatanthauza kuti zabwino zonse zimene Yesu adzacita sizidzatha, zidzapitiliza kukhalapo. Ndipo adzacita zinthu zikulu-zikulu komanso zabwino kwambili.
7 Tiyeni tione ulosi uwu wa m’Baibo wonena za Yesu wakuti: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzelu, womvetsa zinthu, wolangiza, wamphamvu, wodziŵa zinthu ndi woopa Yehova. Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova. Sadzaweluza potengela zimene wangoona ndi maso, kapena kudzudzula potengela zimene wangomva ndi makutu. Adzaweluza mwacilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.” (Yesaya 11:2-4) Mau amenewa amaonetsa kuti Yesu adzakhala Mfumu yacilungamo ndi yacifundo polamulila anthu padziko lapansi. Kodi simungakonde kukhala ndi wolamulila ngati ameneyu?
8. Kodi ndani adzalamulila pamodzi ndi Yesu?
8 Mfundo ina yoona yonena za Ufumu wa Mulungu ndi yakuti: Yesu adzalamulila pamodzi ndi anthu ena. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti: “Tikapitiliza kupilila, tidzalamulilanso limodzi ndi iye monga mafumu.” (2 Timoteyo 2:12) Inde, Paulo, Timoteyo, ndi anthu ena okhulupilika amene asankhidwa ndi Mulungu adzalamulila pamodzi ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. Kodi ndi anthu angati amene adzakhala ndi mwai umenewu?
9. Kodi ndi angati amene adzalamulila pamodzi ndi Yesu? Ndipo Mulungu anayamba liti kuwasankha?
9 Monga mmene tinaonela m’Nkhani yapita, mtumwi Yohane anapatsidwa masomphenya mmene anaona “Mwanawankhosa [Yesu Kristu] ataimilila paphili la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pao.” Kodi a 144,000 ndani? Yohane akutiuza kuti: “Amenewa ndiwo amatsatila Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita. Iwowa anagulidwa kucokela mwa anthu, monga zipatso zoyambilila.” (Chivumbulutso 14:1, 4) Inde, ndi otsatila okhulupilika a Yesu Kristu amene anasankhidwa mwapadela kuti akalamulile pamodzi naye kumwamba. Pambuyo pakuti aukitsidwa mu imfa ndi kukakhala ndi moyo kumwamba, “adzakhala mafumu olamulila dziko lapansi” pamodzi ndi Yesu. (Chivumbulutso 5:10) Kucokela m’nthawi ya atumwi, Mulungu wakhala akusankha Akristu okhulupilika kuti akwanilitse nambala ya 144,000.
10. N’cifukwa ciani ndi makonzedwe acikondi kuti Yesu pamodzi ndi a 144,000 akalamulile mtundu wa anthu?
10 Makonzedwe akuti Yesu pamodzi ndi a 144,000 akalamulile mtundu wa anthu amaonetsa cikondi cacikulu. Yesu anakhalapo munthu ndipo amadziŵa mmene kuvutika kumamvekela. Paulo anakamba kuti Yesu “si mkulu wa ansembe amene sangatimvele cisoni pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda ucimo.” (Aheberi 4:15; 5:8) Anthu amene adzalamulila naye naonso avutitsidwapo ndi kupilila mavuto monga anthu. Kuonjezela pamenepo, io alimbana ndi kupanda ungwilo ndi matenda ambili-mbili. Kukamba zoona, io adzamvetsetsa mavuto amene anthu amakumana nao!
KODI UFUMU WA MULUNGU UDZACITA CIANI?
11. N’cifukwa ciani Yesu ananena kuti ophunzila ake ayenela kupemphelela cifunilo ca Mulungu kuti cicitike kumwamba?
11 Pamene Yesu anakamba kuti ophunzila ake ayenela kupemphelela Ufumu wa Mulungu kuti ubwele, anakambanso kuti ayenela kupemphelela cifunilo ca Mulungu kuti cicitike “monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.” Mulungu ali kumwamba, ndipo cifunilo cake cakhala cikucitika nthawi zonse kumwamba ndi angelo okhulupilika. Koma mu Nkhani 3 m’buku lino, tinaphunzila kuti mngelo woipa analeka kucita cifunilo ca Mulungu ndipo anapangitsa Adamu ndi Hava kucimwa. mu Nkhani 10, tidzaphunzila zambili zimene Baibo imaphunzitsa pankhani ya mngelo woipa ameneyu, amene amachedwa Satana Mdyelekezi. Satana ndi angelo amene anasankha kum’tsatila, ochedwa ziŵanda, analoledwa kukhala kumwamba kwakanthawi. Conco, si onse amene anali kucita cifunilo ca Mulungu kumwamba panthawi imeneyo. Zimenezo zinayenela kusintha pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila. Mfumu yatsopano, Yesu Kristu, inali kudzacita nkhondo ndi Satana.—Chivumbulutso 12:7-9.
12. Kodi n’zocitika ziŵili ziti zapadela zimene zafotokozedwa pa Chivumbulutso 12:10?
12 Mau aulosi otsatilawa afotokoza zimene zinali kudzacitika: “Ndinamva mau ofuula kumwamba, akuti: ‘Tsopano cipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamulilo wa Kristu wake zafika, cifukwa woneneza abale athu [Satana] waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu!’” (Chivumbulutso 12:10) Kodi mwaziona zocitika ziŵili zapadela zimene zafotokozedwa mu vesi imeneyi? Coyamba, Ufumu wa Mulungu wolamulilidwa ndi Yesu Kristu uyamba kulamulila. Caciŵili, Satana acotsedwa kumwamba ndi kuponyedwa padziko lapansi.
13. Kodi pakhala zotsatilapo zanji pamene Satana anacotsedwa kumwamba?
13 Kodi pakhala zotsatilapo zanji cifukwa ca zocitika ziŵili zimenezi? Ponena za zimene zinacitika kumwamba, Baibo imati: “Pa cifukwa cimeneci, kondwelani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!” (Chivumbulutso 12:12) Inde, angelo okhulupilika kumwamba amakondwela cifukwa, Satana ndi ziŵanda zake anacotsedwako. Conco, aliyense kumwamba akutumikila Yehova Mulungu mokhulupilika. Kuli mtendele ndi mgwilizano wosatha. Inde, cifunilo ca Mulungu cikucitika kumwamba.
Kucotsedwa kwa Satana kumwamba pamodzi ndi ziŵanda zake kunabweletsa masoka padziko lapansi. Mavuto amenewa adzatha posacedwa
14. Kodi kuponyedwa kwa Satana padziko lapansi kwakhala ndi zotsatilapo zanji?
14 Nanga bwanji za dziko lapansi? Baibo imati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, cifukwa Mdyelekezi watsikila kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.” (Chivumbulutso 12:12) Satana ndi wokwiya cifukwa cakuti anacotsedwa kumwamba ndi kuti kam’tsalila kanthawi kocepa. Cifukwa cakuti ndi wokwiya, akucititsa mavuto kapena kuti ‘masoka’ padziko lapansi. Tidzaphunzila zambili za ‘masoka’ amenewa m’nkhani yotsatila. Poganizila zimenezo, tingafunse kuti, Kodi Ufumu udzakwanilitsa bwanji cifunilo ca Mulungu padziko lapansi?
15. Kodi cifunilo ca Mulungu cokhudza dziko lapansi n’ciani?
15 Kumbukilani kuti cifunilo ca Mulungu ca dziko lapansi n’ciani. Tinaphunzila zimenezi m’Nkhani 3. Zimene Mulungu anacita mu Edeni, zinaonetsa kuti cifunilo cake n’cakuti dziko lapansi likhale paladaiso, ndi kuti lidzale ndi anthu olungama, okhala ndi moyo wosatha. Satana anapangitsa Adamu ndi Hava kucimwa. Conco, zimenezo zinakhudza kukwanilitsidwa kwa cifunilo ca Mulungu ca dziko lapansi. Koma ngakhale zinali conco, sizinasinthe cifunilo ca Mulungu cimeneco. Yehova akali ndi colinga cakuti “olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Ufumu wa Mulungu udzacita zimenezi. Mwa njila yanji?
16, 17. Kodi lemba la Danieli 2:44 limatiuza ciani za Ufumu wa Mulungu?
16 Onani ulosi wa pa Danieli 2:44. Pamenepo pamati: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” Kodi lemba limeneli limatiuza ciani pa za Ufumu wa Mulungu?
17 Coyamba, limatiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsidwa “m’masiku a mafumu amenewo,” kapena kuti pamene maufumu ena adzakhala akulamulila. Caciŵili, limatiuzanso kuti Ufumu udzakhalapo kosatha. Ufumu umenewu sudzaonongedwa kapena kuloŵedwa m’malo ndi boma lina lililonse. Cacitatu n’cakuti Ufumu wa Mulungu udzacita nkhondo ndi mafumu a padziko lapansi, ndipo udzapambana. Potsilizila pake, Ufumu umenewu udzakhala boma lokha limene lidzalamulila mtundu wa anthu. Pamenepo, anthu adzakhala ndi ulamulilo wabwino kuposa wina uliwonse.
18. Kodi nkhondo yotsilizila imene idzacitika pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maboma a padziko lapansi imachedwa ciani?
18 Baibo imatiuza zambili zokhudza nkhondo yotsilizila imene idzacitika pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maboma a padziko lapansi. Mwacitsanzo, imatiphunzitsa kuti pamene nthawi ya nkhondo imeneyo iyandikila, mizimu yoipa idzafalitsa mabodza kuti inamize “mafumu a dziko lonse lapansi.” N’cifukwa ciani idzacita zimenezi? ‘Kuti iwasonkhanitsile [mafumu] pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ Mafumu a padziko lapansi adzasonkhanitsidwa pamodzi “kumalo amene m’Cihebeli amachedwa Haramagedo.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Cifukwa ca zimene zakambidwa m’mavesi aŵili amenewa, nkhondo yotsilizila ya pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maboma a padziko lapansi imachedwa nkhondo ya Haramagedo, kapena kuti Aramagedo.
19, 20. Kodi n’ciani cimalepheletsa cifunilo ca Mulungu kucitika padziko lapansi panthawi ino?
19 Kodi Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa ciani kupitila m’nkhondo ya Aramagedo? Ganizaninso za cifunilo ca Mulungu cokhudza dziko lapansi. Colinga ca Yehova Mulungu cinali cakuti dziko lapansi lidzale ndi anthu olungama ndi angwilo, komanso kuti azimutumikila m’Paladaiso. Kodi n’ciani cikulepheletsa zimenezo kucitika panthawi ino? Coyamba n’cakuti, tili ocimwa ndipo timadwala ndi kufa. Tinaphunzila mu Nkhani 5, kuti Yesu anatifela kuti tikhale ndi moyo wosatha. Mwina mukumbukila mau a Yohane akuti: “Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
20 Vuto lina n’lakuti anthu ambili amacita zinthu zoipa. Amakamba mabodza, amacita zacinyengo ndi zaciwelewele. Iwo safuna kucita cifunilo ca Mulungu. Anthu amene amacita zinthu zoipa adzaonongedwa pankhondo ya Mulungu ya Aramagedo. (Salimo 37:10) Cifukwa cinanso cimene cifunilo ca Mulungu sicikucitika padziko lapansi n’cakuti maboma salimbikitsa anthu kucita cifunilo ca Mulungu cimeneci. Maboma ambili amalephela kulamulila anthu, amacita nkhanza ndi zacinyengo. Baibo imakamba mosapita m’mbali kuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.”—Mlaliki 8:9.
21. Kodi Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa bwanji cifunilo cake padziko lapansi?
21 Pambuyo pa Aramagedo, mtundu wa anthu udzalamulilidwa ndi boma limodzi cabe, Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewo udzacita cifunilo ca Mulungu ndi kubweletsa madalitso. Mwacitsanzo, udzaponya Satana ndi ziŵanda zake m’phompho kwa zaka 1,000. (Chivumbulutso 20:1-3) Nsembe ya Yesu idzagwila nchito kuti anthu okhulupilika asakadwalenso ndi kufa. M’malo mwake, mu ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu io adzakhala ndi moyo kosatha. (Chivumbulutso 22:1-3) Dziko lapansi lidzakhala paladaiso. Conco Ufumu umenewo udzakwanilitsa cifunilo ca Mulungu padziko lapansi, ndi kuyeletsa dzina lake. Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Zitanthauza kuti m’kupita kwanthawi, munthu aliyense mu Ufumu wa Mulungu adzalemekeza dzina la Yehova.
KODI NDI LITI PAMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACITAPO KANTHU?
22. Timadziŵa bwanji kuti Ufumu wa Mulungu sunabwele pamene Yesu anali padziko lapansi, kapena pambuyo pakuti wangoukitsidwa?
22 Pamene Yesu anauza otsatila ake kupemphela kuti, “Ufumu wanu ubwele,” zinali zoonekelatu kuti Ufumuwo unali ukalibe kubwela panthawiyo. Kodi unabwela pamene Yesu anapita kumwamba? Iyai, cifukwa onse aŵili Petulo ndi Paulo anakamba kuti pambuyo pakuti Yesu waukitsidwa, ulosi wa pa Salimo 110:1 unakwanilitsika mwa iye, ndipo umati: “Yehova wauza Ambuye wanga kuti: ‘Khala kudzanja langa lamanja kufikila nditaika adani ako monga copondapo mapazi ako.’” (Machitidwe 2:32-34; Aheberi 10:12, 13) Kodi panafunika kuyembekeza kwanthawi yaitali bwanji kuti Ufumu wa Mulungu uyambe kulamulila?
Mu ulamulilo wa Ufumu umenewu, cifunilo ca Mulungu cidzacitika padziko lapansi monga kumwamba
23. (a) Kodi Ufumu wa Mulungu unayamba liti kulamulila? (b) Nanga tidzakambitsilana ciani m’nkhani yotsatila?
23 Kodi nthawi imeneyi inafunika kukhala yaitali bwanji? Kumapeto kwa zaka za m’ma 1800 ndi kuciyambi kwa zaka za m’ma 1900, ophunzila Baibo oona mtima anaŵelengela kuti nthawi imeneyi inali kudzatha m’caka ca 1914. (Kuti mudziŵe zambili za deti limeneli, onani Zakumapeto, pamapeji 215 mpaka 218.) Zocitika za padziko lapansi zimene zinayamba m’caka ca 1914 zimatsimikizila kuti kamvedwe ka ophunzila Baibo oona mtima amenewa kanali kolongosoka. Kukwanilitsika kwa ulosi wa m’Baibo kumaonetsa kuti m’caka ca 1914, Kristu anakhala Mfumu ndipo Ufumu wa Mulungu wa kumwamba unayamba kulamulila. Conco, tikukhala mu “kanthawi kocepa” kamene kam’tsalila Satana. (Chivumbulutso 12:12; Salimo 110:2) Ifenso tingakambe motsimikiza kuti posacedwa Ufumu wa Mulungu udzacitapo kanthu kuti cifunilo ca Mulungu cicitike padziko lapansi. Kodi uwu si uthenga wokondweletsa? Kodi mukhulupilila kuti zimenezi n’zoona? Nkhani yotsatila idzakuthandizani kuona kuti Baibo imaphunzitsadi zinthu zimenezi.