LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 6 nkhani 57-65
  • Kodi Akufa Ali Kuti?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Akufa Ali Kuti?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIANI CIMACITIKA KWENI-KWENI MUNTHU AKAFA?
  • ZIMENE YESU ANAKAMBA PA ZA IMFA
  • N’CIFUKWA CIANI ANTHU AMAFA?
  • KUDZIŴA ZENI-ZENI PONENA ZA IMFA KUNGAKHALE KOLIMBIKITSA
  • Kodi Munthu Akafa Amayenda Kuti?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • N’cifukwa Ciani Timakalamba Na Kufa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Yesu Kodi Zili ndi Tanthauzo Lotani kwa Inu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Anamvetsela kwa Satana—Nanga Cinacitika n’Ciani?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
Onaninso Zina
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 6 nkhani 57-65

NKHANI 6

Kodi Akufa Ali Kuti?

  • Kodi n’ciani cimacitika kwa ife tikafa?

  • N’cifukwa ciani timafa?

  • Kodi kudziŵa zeni-zeni ponena za imfa kungakhale kolimbikitsa?

1-3. Kodi anthu amafunsa mafunso anji ponena za imfa? Ndipo zipembedzo zimapeleka mayankho osiyana-siyana ati?

AWA ndi mafunso amene anthu akhala akuwaganizilapo kwa zaka zambili. Mafunso amenewa ndi ofunika kwambili, cifukwa kucokela tsiku limene tinabadwa mpaka pano, tonse timadziŵa kuti tsiku lina tidzafa ndipo timataya okondedwa athu mu imfa.

2 Mu Nkhani 5, tinaphunzila mmene nsembe ya dipo la Yesu Kristu inatsegulila mwai wodzakhala ndi moyo wosatha. Tinaphunzilanso zimene Baibo imalosela kuti “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) Koma pali pano, ife tonse timafa. Mfumu yanzelu Solomo inakamba kuti: “Amoyo amadziŵa kuti adzafa.” (Mlaliki 9:5) Timayesa-yesa kuti tikhale ndi moyo wotalikilapo. Ngakhale zili conco, sitimadziŵa zimene zidzacitika kwa ife tikafa.

3 Okondedwa athu akamwalila, timalila. Ndipo tingafunse kuti: ‘Kodi io apita kuti? Kodi akuvutika? Kodi akutiona? Kodi tingawathandize? Nanga tidzawaonanso?’ Zipembedzo zambili padziko zimapeleka mayankho osiyana-siyana pa mafunso amenewa. Ena amaphunzitsa kuti ngati umacita zinthu zabwino, ndiye kuti udzapita kumwamba, koma ngati umacita zoipa ndiye kuti udzapita kumalo acionongeko. Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti munthu akafa, amapita ku malo a mizimu kukakhala ndi makolo. Ndiponso zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti akufa amapita ku dziko lamdima kukaweluzidwa, ndiyeno amakabadwanso mwa munthu wina.

4. Kodi zipembedzo zambili zimagwilizana pa mfundo iti yokhudza imfa?

4 Zipembedzo zonsezi zimagwilizana pa mfundo imodzi yakuti, tikafa cinthu cina cimacoka m’thupi mwathu ndi kupitiliza kukhala ndi moyo kwinakwake. Pafupi-fupi zipembedzo zonse zimene zakhalapo, zimaphunzitsa kuti tikafa timapitilizabe kukhala ndi moyo m’njila inayake, ndipo timaona, kumva, ndi kuganiza. Koma kodi zimenezo zingacitike bwanji? Timamva, kuona, ndi kuganiza cifukwa cakuti ubongo wathu umagwila nchito. Tikafa, ubongo umaleka kugwila nchito. Conco, ubongo wathu ukasiya kugwila nchito, sitingakumbukile zinthu, kuzikhudza, kumva, kapena kuona ciliconse.

N’CIANI CIMACITIKA KWENI-KWENI MUNTHU AKAFA?

5, 6. Kodi Baibo imaphunzitsa kuti akufa ali mu mkhalidwe wotani?

5 Yehova amene analenga ubongo amadziŵa zimene zimacitika munthu akafa. Iye amadziŵa zeni-zeni, ndipo m’Mau ake, Baibo, amafotokoza mkhalidwe wa anthu akufa. Ciphunzitso comveka ca m’Baibo n’cakuti: Munthu akafa, sakhalaponso. Pali imfa palibe moyo. Akufa samaona, kumva, kapena kuganiza. Munthu akafa, palibe mzimu umene umacoka m’thupi mwake ndi kupitiliza kukakhala ndi moyo kwinakwake.a

A candle with the flame put out

Kodi laŵi lapita kuti?

6 Solomo atazindikila kuti amoyo amadziŵa kuti adzafa, analemba kuti: “Akufa sadziŵa ciliconse.” Ndiyeno anaonjezelapo kuti akufa sangakonde kapena kuzonda aliyense, ndi kutinso “kulibe kugwila nchito, kuganiza zocita, kudziŵa zinthu, kapena nzelu, ku Manda.” (Mlaliki 9:5, 6, 10) Mofananamo, Salimo 146:4 imakamba kuti, “zonse zimene anali kuganiza zimathelatu.” Anthufe timafa, ndipo tikafa palibe ciliconse cimene cimacoka m’thupi mwathu kukakhala ndi moyo kwinakwake. Moyo umene tili nao uli ngati laŵi la kandulo. Laŵi lija likazima, silipita kulikonse. Limangotha, silikhalaponso.

ZIMENE YESU ANAKAMBA PA ZA IMFA

7. Kodi Yesu anafotokoza kuti imfa ili ngati ciani?

7 Yesu Kristu anakambapo za mmene akufa alili. Panthawi ina, iye anamva zakuti munthu amene anali kum’dziŵa bwino, Lazaro, anamwalila. Pamenepo Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula.” Ophunzilawo anaganiza kuti Yesu anali kutanthauza kuti Lazaro anali m’tulo cabe, kuti anali kupumula cifukwa anali wodwala. Koma iye sanatanthauze zimenezo. Yesu anamveketsa bwino kuti: “Lazaro wamwalila.” (Yohane 11:11-14) Onani kuti Yesu anafanizila imfa ndi kugona tulo. Lazaro sanapite kumwamba kapena ku moto wa kuhelo. Sanali kwa angelo kapena ku mizimu ya makolo. Ndipo sanakabadwenso mwa munthu wina iyai. M’malo mwake, anali cigonele mu imfa, osamva kalikonse. Palinso malemba ena amene amafanizila imfa ndi kugona tulo. Mwacitsanzo, pamene wophunzila Sitefano anaponyedwa miyala, Baibo imakamba kuti “anagona tulo ta imfa.” (Machitidwe 7:60) Paulo nayenso analemba za anthu ena a m’nthawi yake amene “anagona mu imfa.”—1 Akorinto 15:6.

A husband and wife sitting in a garden, looking at a flower

Yehova anapanga anthu kuti akhale ndi moyo wamuyaya padziko lapansi

8. Kodi timadziŵa bwanji kuti sicinali cifunilo ca Mulungu kuti anthu azifa?

8 Kodi cinali cifunilo ca Mulungu kuti anthu azifa? Kutalitali! Yehova anapanga munthu kuti akhale ndi moyo kosatha padziko lapansi. Monga tinaphunzilila m’buku lino, Mulungu anaika anthu oyamba aŵili m’paladaiso wokongola. Anawapatsanso thanzi langwilo. Yehova anali kufunila anthu zinthu zabwino zokha-zokha. Kodi pali kholo lacikondi limene lingafune kuti ana ake akakalambe ndi kumwalila? Ndithudi ayi! Yehova anali kuwakonda kwambili ana ake amenewo, ndipo anali kufuna kuti akhale ndi moyo wacimwemwe padziko lapansi kwamuyaya. Ponena za anthu, Baibo imati: ‘[Yehova] anaika umuyaya m’mitima yao.’ (Mlaliki 3:11, Buku Lopatulika) Mulungu anatilenga ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo kosatha. Ndiye cifukwa cake anatumiza Mwana wake kuti tikapeze moyo wosatha.

N’CIFUKWA CIANI ANTHU AMAFA?

9. Kodi Yehova anapeleka lamulo lanji kwa Adamu? Ndipo n’cifukwa ciani linali losavuta kulitsatila?

9 Kuti tipeze yankho, tiyeni tione zimene zinacitika padziko lapansi pamene panali cabe mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi. Baibo imafotokoza kuti: “Yehova Mulungu anameletsa m’nthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya.” (Genesis 2:9) Koma panali cinthu cimodzi cabe cimene anawaletsa. Yehova anauza Adamu kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Lamulo limeneli silinali lovuta kulitsatila. Panali mitengo ina yambili imene Adamu ndi Hava anapatsidwa kuti azidya zipatso zake. Conco, lamulo limeneli linawapatsa mwai wakuti aonetse kuyamikila Mulungu amene anawapatsa zinthu zonse, kuphatikizapo moyo wangwilo. Akanamvela lamulo limeneli akanaonetsanso kuti anali kulemekeza Atate wao wakumwamba, ndi kuti anali kufuna kuti aziwatsogolela.

10, 11. (a) Kodi zinacitika bwanji kuti anthu aŵili oyambilila apandukile Mulungu? (b) Nanga n’cifukwa ciani kusamvela kwa Adamu ndi Hava kunali mlandu waukulu kwambili?

10 N’zomvetsa cisoni kuti anthu aŵili oyambilila anasankha kupandukila Yehova. Satana anafunsa Hava kupyolela mwa njoka kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Ndipo Hava anayankha kuti: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’”—Genesis 3:1-3.

11 Satana anati: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziŵa kuti tsiku limene mudzadye cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:4, 5) Cimene Satana anafuna n’cakuti Hava akhulupilile kuti akadya cipatso coletsedwa adzapindula. Maganizo a Satana anali akuti, Hava akanatha kumadzisankhila cabwino ndi coipa; kutanthauza kuti akanatha kumacita ciliconse cimene akanafuna. Satana anakambanso kuti Yehova ananama kuti Adamu ndi Hava akadya cipatso adzafa. Hava anakhulupilila zimenezo. Conco, anathyola cipatso ndi kudya. Pambuyo pake anapatsako mwamuna wake, nayenso anadya. Iwo sanacite zimenezi popanda kuzindikila bwino-bwino zimene anali kucita. Anadziŵa bwino kuti anali kucita zimene Mulungu anawaletsa. Mwa kudya cipatso, anacitila dala kusamvela lamulo lomveka bwino ndi losavuta kulitsatila. Ananyozela lamulo la Atate wao wakumwamba. Kupanda ulemu kumene anaonetsa kwa Mlengi wao wacikondi kwa mtundu umenewu, kunali kosakhululukika.

12. Kodi n’citsanzo citi cingatithandize kumvetsa mmene Yehova anamvelela pamene Adamu ndi Hava anam’pandukila?

12 Mwacitsanzo: Kodi mungamve bwanji ngati mwana amene mwalela ndi kum’kulitsa bwino wakupandukilani m’njila yoonetsa kuti sakulemekezani kapena kukukondani? Kunena zoona, zimenezi zingakukhumudwitseni kwambili. Ndiye ganizani cabe mmene Yehova anamvelela pamene Adamu ndi Hava anam’pandukila.

Adam at the time of creation, coming out of the dust

Adamu anacokela kufumbi, ndipo anabwelela kufumbi

13. Kodi Yehova anakamba kuti n’ciani cidzacitikila Adamu akamwalila? Ndipo zimenezi zitanthauza ciani?

13 Yehova analibe cifukwa cakuti asunge Adamu ndi Hava kosatha, anthu amene anali osamvela. Iwo anafa, monga mmene Yehova anakambila. Adamu ndi Hava sanakhaleponso. Sanapite ku malo a mizimu. Timadziŵa zimenezi cifukwa ca zimene Yehova anauza Adamu pambuyo pakuti wacimwa. Mulungu anati: ‘Udzabwelela kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwelela.’ (Genesis 3:19) Mulungu anapanga Adamu kucokela kudothi lapansi. (Genesis 2:7) Adamu asanapangidwe kunalibe. Conco, pamene Yehova anakamba kuti Adamu adzabwelela ku fumbi, anatanthauza kuti Adamu sadzakhalaponso. Adamu adzakhala wopanda moyo ngati dothi limene Mulungu anagwilitsila nchito pomupanga.

14. N’cifukwa ciani timafa?

14 Adamu ndi Hava akanakhala ndi moyo mpaka lelo, koma anafa cifukwa cakuti anacimwa pamene anasankha kusamvela Mulungu. Ife tonse monga ana a Adamu timafa cifukwa cakuti tinatengela ucimo ndi imfa kucokela kwa iye. (Aroma 5:12) Ucimo umenewo uli ngati nthenda yoopsa imene tinatengela kwa iye imene sitikanaipewa. Ndiyeno zotsatilapo zake ndi imfa, imene ili tembelelo. Imfa si bwenzi lathu koma mdani. (1 Akorinto 15:26) Conco, tiyenela kuyamikila kwambili Yehova amene anapeleka dipo kuti litipulumutse kwa mdani woipa ameneyu!

KUDZIŴA ZENI-ZENI PONENA ZA IMFA KUNGAKHALE KOLIMBIKITSA

15. N’cifukwa ciani kudziŵa zeni-zeni ponena za imfa kungakhale kolimbikitsa?

15 Zimene Baibo imaphunzitsa pa mkhalidwe wa akufa n’zolimbikitsa. Monga mmene taonela, akufa samva kupweteka ndipo sangakhumudwe. Sitiyenela kuwaopa cifukwa sangativulaze. Iwo safunikila thandizo lathu, ndipo naonso sangatithandize. Sitingakambe nao, naonso sangakambe nafe. Atsogoleli acipembedzo ambili amanena zabodza kuti angathandize anthu akufa, ndipo anthu amene amakhulupilila abusa amenewo amapeleka ndalama kwa io. Koma kudziŵa zeni-zeni ponena za imfa kumatiteteza kuti anthu amene amaphunzitsa mabodza amenewo asatiname.

16. Kodi ndani amene walimbikitsa ziphunzitso za zipembedzo zambili? Ndipo wacita zimenezi m’njila iti?

16 Kodi cipembedzo canu cimagwilizana ndi zimene Baibo imaphunzitsa za akufa? Zipembedzo zambili sizigwilizana ndi zimenezi. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Satana walimbikitsa ziphunzitso zao. Iye amagwilitsila nchito cipembedzo conama kupangitsa anthu kukhulupilila kuti munthu akafa, amapitiliza kukhala ndi moyo kumalo a mizimu. Satana amaligwilitsila nchito bodza limeneli pamodzi ndi mabodza ena kuti apatutse anthu kwa Yehova Mulungu. Amacita bwanji zimenezi?

17. N’cifukwa ciani ciphunzitso cakuti anthu amazunzidwa kosatha m’moto wa kuhelo sicimalemekeza Yehova?

17 Monga mmene taonela, zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti ngati munthu amacita zinthu zoipa, akafa amapita kumoto wa kuhelo kukazunzidwa kosatha. Ciphunzitso cimeneci sicimalemekeza Mulungu. Yehova ndi Mulungu wacikondi ndipo sangamavutitse anthu mwa njila imeneyi. (1 Yohane 4:8) Kodi mungamuone bwanji munthu amene angalange mwana wake wosamvela mwa kumuika manja pa moto? Kodi mungamulemekeze munthu ameneyu? Ndipo kodi mungafune ngakhale kum’dziŵa? Mwacionekele simungatelo! Ndipo munganene kuti anacita nkhanza kwambili. Koma Satana amafuna kuti tikhulupilile kuti Yehova amazunza anthu m’moto wa kuhelo kosatha, kapena kuti kwa zaka zosaŵelengeka.

18. Kodi kulambila anthu akufa n’kozikidwa pa ciphunzitso citi cabodza?

18 Satana amagwilitsilanso nchito zipembedzo zina kuphunzitsa kuti anthu akafa amakhala mizimu imene iyenela kulemekezedwa ndi anthu amoyo. Malinga ndi ciphunzitso cimeneci, mizimu ya akufa ingakhale mabwenzi a pamtima kapena adani oopsa. Anthu ambili amakhulupilila bodza limeneli. Amaopa akufa ndipo amawalemekeza ndi kuwalambila. Mosiyana ndi zimenezi, Baibo imaphunzitsa kuti akufa ali gone m’tulo. Imaphunzitsanso kuti tiyenela kulambila Yehova, Mulungu woona yekha, Mlengi wathu amene amatipatsa zinthu zonse.—Chivumbulutso 4:11.

19. Kodi kudziŵa zeni-zeni ponena za imfa kumatithandiza kumvetsetsa ciphunzitso cina citi ca m’Baibo?

19 Kudziŵa zeni-zeni ponena za anthu akufa kungakutetezeni kuti anthu asakunamizeni ndi mabodza a cipembedzo. Kungakuthandizeninso kuti mumvetsetse ziphunzitso zina za m’Baibo. Mwacitsanzo, mukadziŵa kuti anthu akafa samapita kumalo a mizimu, lonjezo la kukhala ndi moyo wosatha m’paladaiso padziko lapansi limakhala leni-leni kwa inu.

20. Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambitsilana funso liti?

20 Kale kwambili, munthu wolungama Yobu anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” (Yobu 14:14) Kodi zingatheke kuti munthu wopanda moyo amene ali gone mu imfa aukitsidwe kukhalanso ndi moyo? Zimene Baibo imaphunzitsa pankhani imeneyi n’zolimbikitsa kwambili, monga mmene tidzaonela m’nkhani yotsatila.

a Kuti mumve zambili pankhani ya “mzimu,” onani Zakumapeto pamapeji 208 mpaka 211.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Akufa samaona, kumva, kapena kuganiza.—Mlaliki 9:5.

  • Akufa ali cigonele m’tulo; ndipo samva kupweteka.—Yohane 11:11.

  • Timafa cifukwa tinatengela ucimo kwa Adamu.—Aroma 5:12.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani