LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 221-nkhani 222 pala. 2
  • Kodi Yesu Anabadwa M’mwezi wa December?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Yesu Anabadwa M’mwezi wa December?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Nkhani Zofanana
  • Angelo Alengeza za Kubadwa kwa Yesu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 221-nkhani 222 pala. 2

ZAKUMAPETO

Kodi Yesu Anabadwa M’mwezi wa December?

BAIBO siikamba kuti Yesu anabadwa liti. Komabe, imatipatsa zifukwa zomveka zoonela kuti sanabadwe m’mwezi wa December.

Ganizilani mmene nyengo inali kukhalila m’mwezi umenewu ku Betelehemu, kumene Yesu anabadwila. Mwezi waciyuda wa Kisilevi (umene umakhala mu November/December) unali mwezi wozizila ndi wamvula. Mwezi wotsatila unali wa Tebeth (December/January). M’mwezi umenewu kunali kuzizila kwambili, ndipo kumalo amapili kunali kugwa cipale cofewa. Tiyeni tione zimene Baibo imatiuza ponena za nyengo ya dela limeneli.

Wolemba Baibo Ezara anaonetsa kuti Kisilevi unali kudziŵika kukhala mwezi wozizila ndi wamvula. Ezara atanena kuti gulu la anthu linasonkhana mu Yerusalemu “m’mwezi wa 9, pa tsiku la 20 la mweziwo,” iye anati anthu anali ‘kunjenjemela . . . cifukwa kunali kugwa mvula.” Ponena za mmene nyengo inalili m’mwezi umenewo, anthu amene anasonkhana anati: “Ino ndi nyengo ya mvula yamvumbi, conco n’zosatheka kuima panja.” (Ezara 10:9, 13; Yeremiya 36:22) Ndiye cifukwa cake abusa amene anali kukhala m’madela apafupi ndi Yerusalemu sanali kukhala panja usiku ndi ziŵeto zao m’mwezi wa December.

Komabe, Baibo imakamba kuti usiku pamene Yesu anabadwa, abusa anali kuthengo kudyetsa nkhosa zao. Wolemba Baibo Luka anaonetsa kuti panthawi imeneyo, abusa anali “kugonela kubusa akuyang’anila nkhosa zao.” (Luka 2:8-12) Onani kuti abusa anali kukhala kunja, osati cabe kuyenda-yenda nthawi ya masana. Iwo anali ndi nkhosa zao ku ubusa usiku. Ndi mmene Baibo imafotokozela kuti abusa anali kucoma ndi kugona kunja osati m’nyumba zao, kodi zingamveke kunena kuti zinali kucitika m’nyengo yozizila ndi ya mvula? Iyai. Conco, zocitika panthawi ya kubadwa kwa Yesu zimaonetsa kuti sanabadwe mu December iyai.a

Zakuti Yesu anamwalila liti, Mau a Mulungu amatiuza bwino-bwino. Koma za kubadwa kwake, Baibo siichula kweni-kweni. Zimenezi zimatikumbutsa mau a Mfumu Solomo akuti: “Mbili yabwino imaposa mafuta onunkhila, ndipo tsiku lomwalila limaposa tsiku lobadwa.” (Mlaliki 7:1) Conco, m’posadabwitsa kuti Baibo imatiuza zambili za utumiki wa Yesu ndi imfa yake, koma zakuti anabadwa liti siikamba zambili.

Shepherds in the fields with their flocks at night near Bethlehem

Pamene Yesu anabadwa, abusa anali kuthengo usiku ndi nkhosa zao

a Kuti mudziŵe zambili, onani buku lakuti Kukambitsirana za m’Malemba, mapeji 239 mpaka 246, lolembedwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani