Kulamanzele: Mlongo amene ndi kopotala akulalikila ku Korea mu 1931; kulamanja: Alongo akulalikila m’cinenelo ca manja ku Korea
CIGAWO 2
Kulalikila za Ufumu—Kufalitsa Uthenga Wabwino Padziko Lonse
YELEKEZELANI kuti mukukonzekela kupita muulaliki m’mamawa patsiku limene simukupita kunchito. Koma mukukaikila zopita muulaliki cifukwa cakuti mukumva kutopa, ndipo mukuona kuti ndi bwino mutapuma. Komabe pambuyo popemphelela nkhaniyo mukusankha kupita muulaliki. Pamene mukulalikila ndi mlongo wacikulile wokhulupilika, mukulimbikitsidwa poona kupilila ndi kukoma mtima kwake. Ndipo pamene mukulalikila uthenga wa coonadi kunyumba ndi nyumba, mukukumbukila kuti abale ndi alongo anu padziko lonse naonso akulengeza uthenga wofananawo mwa kugwilitsila nchito zofalitsa zofanana ndi zimene inu mukugwilitsila nchito ndiponso maphunzilo amodzimodzi amene munaphunzitsidwa. Pamene mukufika kunyumba, mukudzimva kuti mwalimbikitsidwa, ndipo ndinu wosangalala kuti simunangokhala panyumba.
Nchito yaikulu imene Ufumu wa Mulungu ukucilikiza masiku ano ndi yolalikila. Yesu ananenelatu kuti nchito yolalikila idzafalikila padziko lonse m’masiku otsiliza. (Mat. 24:14) Kodi ulosi wa Yesu umenewu wakwanilitsidwa bwanji? M’cigawo cino, tikambilana za anthu amene amagwila nchitoyi, njila zimene amagwilitsila nchito, ndi zida zimene zathandiza kwambili kuti nchito yolalikila ipite patsogolo. Nchito imeneyi ikuthandiza anthu mamiliyoni ambili padziko lonse lapansi kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni.