7
Ningacite Bwanji Ngati Wina Aninyengelela kuti Nigone Naye?
KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?
Ganizila cocitika ici: Ngakhale kuti Heather wakhala akuceza na Mike kwa miyezi iŵili cabe, amvela monga anadziŵana naye kalekale. Iwo amatumizilana mameseji na kuceza nthawi itali pafoni, cakuti afika pokondana kwambili! Koma manje, Mike afuna zipitilile pa kuceza cabe.
M’miyezi iŵili imeneyi, Mike na Heather akhalanso akugwilana manja na kukising’ana pang’ono. Ngakhale kuti Heather safuna kuti zipitilile apa, safunanso kuti cibwenzi cawo cisile. Ndipo amakamba mumtima mwake kuti ‘Koma Mike na ine tikondana . . . ’
Kukhala Heather, kodi ungacite bwanji?
YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!
Kugonana ni mphatso yocokela kwa Mulungu kwa anthu ali m’cikwati. Koma kugonana mukalibe kungena m’cikwati, kumakhala monga kutenga cinthu ca mtengo wapatali n’kuciviika m’zinthu zonyansa. Cilinso monga kutenga covala cokongola cimene wina anakugulila n’kuyamba kucipukutila.
Ngati upitilila dala maloboti akayaka redi, umadzibweletsela mavuto. Ndiye mmene zimakhalila ukaphwanya yamulo ya m’Baibo monga yakuti: ‘Pewani dama.’—1 Atesalonika 4:3.
Ni mavuto anji amene amabwela ukaphwanya lamulo imeneyi? Baibo imati: “Amene amacita dama amacimwila thupi lake.” (1 Akorinto 6:18) Nanga zimacitika bwanji?
Ofufuza apeza kuti acicepele ambili amene anagona na munthu wina akalibe kungena m’banja amakumana na mavuto aya.
KUVUTIKA MAGANIZO. Acicepele ambili amene amagona na munthu wina akalibe kungena m’banja amadziimba mlandu pambuyo pake.
KUSAKHULUPILILANA. Pambuyo pakuti anthu aŵili agonana, onse aŵili amayamba kuda nkhawa na kudzifunsa kuti, ‘kodi ameneyu wagonapo na ine cabe?’
KUDZIGONG’A. Pansi pamtima, atsikana ambili amafuna mnyamata amene angawateteze, osati amene amafuna kuwaseŵenzetsa cabe. Ndipo anyamata ambili sapitiliza kukonda mtsikana amene anavomela kucita nawo ciwelewele.
Zimene ufunika kudziŵa: Ukagona na munthu ukalibe kungena m’cikwati, udziŵe kuti wadzichipitsa mwa kupangitsa thupi yako kukhala conyansa. (Aroma 1:24) Thupi yako ni yamtengo wapatali kwambili. Si cinthu coseŵeletsa!
Onetsa kuti munthu sangakuchipitse. Ungacite zimenezi mwa “kupewa dama.” (1 Atesalonika 4:3) Koma pamene udzangena m’cikwati, kugonana kudzakhala mphatso yokondweletsa kwambili. Mudzayamba kugonana popanda nkhawa iliyonse, kudziimba mlandu, kapena zotulukapo zoipa zimene zimabwela cifukwa cogonana mukalibe kuloŵa m’cikwati.—Miyambo 7:22, 23; 1 Akorinto 7:3.
UGANIZA BWANJI?
Kodi munthu amene amakukonda zoona, angakupangitse kucita cinthu cimene cingakubweletsele mavuto pambuyo pake?
Kodi munthu amene amakukonda zoona, angafune kukuwonongela unansi wako na Mulungu?—Aheberi 13:4.