LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 19
  • Kodi Mboni za Yehova ni Akhristu Enieni?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mboni za Yehova ni Akhristu Enieni?
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Mmene Akhristu Enieni Tingawadziŵile
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Mulungu Woona Ndani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Ni Cifukwa Ciani Timachedwa Mboni za Yehova?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Kodi Uthenga Wabwino Umalalikidwa Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 19
Phunzilo 19. A Mboni za Yehova akuceza panja pa Nyumba ya Ufumu.

PHUNZILO 19

Kodi Mboni za Yehova ni Akhristu Enieni?

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Ife monga Mboni za Yehova timakhulupililadi kuti ndife Akhristu enieni. Cifukwa ciyani? Tiyeni tikambilane maziko a zimene timakhulupilila, dzina limene limatipatula padela, komanso cikondi cathu kwa wina na munthu mnzake.

1. Kodi zimene a Mboni za Yehova amakhulupilila zimatsamila pa ciyani?

Yesu anati: “Mawu [a Mulungu] ndiwo coonadi.” (Yohane 17:17) Mofanana na Yesu, nthawi zonse zimene a Mboni za Yehova amakhulupilila zimatsamila pa Mawu a Mulungu. Mwacitsanzo, onani mmene acitila zimenezi kucokela kumayambililo kwa mbili yawo yamakono. M’ma 1870, kagulu ka ophunzila Baibo kanayamba kuiphunzila mozama Baibo. Iwo anakhulupililabe mfundo za m’Baibo ngakhale zinasiyana na zimene machalichi anali kuphunzitsa. Pambuyo pake, anayamba kuuzako anthu ena mfundo za m’Baibo zimenezo.a

2. N’cifukwa ciyani timanena kuti ndife Mboni za Yehova?

Yehova amacha anthu omulambila kuti ni mboni zake cifukwa iwo amakamba zoona ponena za iye. (Aheberi 11:4–12:1) Mwacitsanzo, m’nthawi zamakedzana, Mulungu anauza anthu ake kuti: “Inu ndinu mboni zanga.” (Ŵelengani Yesaya 43:10.) Yesu nayenso amachedwa “Mboni Yokhulupilika.” (Chivumbulutso 1:5) Ndiye cifukwa cake mu 1931, tinatenga dzina lakuti Mboni za Yehova. Ndipo timanyadila ngako kuchedwa na dzina limeneli.

3. Kodi Mboni za Yehova zimaonetsa bwanji cikondi potengela citsanzo ca Yesu?

Yesu anali kuwakonda kwambili ophunzila ake moti anakhala monga acibale ake. (Ŵelengani Maliko 3:35.) Mofananamo, Mboni za Yehova n’zogwilizana monga banja la padziko lonse. Ndiye cifukwa cake timachulana kuti m’bale kapena mlongo. (Filimoni 1, 2) Timamvelanso lamulo lakuti: “Kondani gulu lonse la abale.” (1 Petulo 2:17) Mboni za Yehova zimaonetsa cikondi cimeneci m’njila zambili, monga kuthandiza abale na alongo awo padziko lonse m’nthawi zovuta.

KUMBANI MOZAMILAPO

Phunzilani zambili zokhudza Mboni za Yehova zamakono kuti muone umboni wakuti tilidi Akhristu enieni.

Zithunzi: Mboni za Yehova zikulalikila. 1. Mlongo akuŵelenga malemba n’kuwakambilana na mzimayi winawake. 2. M’bale alalikila coonadi ca m’Baibo kwa munthu wina pa kasitandi ka ulaliki wapoyela.

Zimene Akhristu enieni amakhulupilila zimatsamila pa Baibo, ndipo iwo amauzakonso anthu ena

4. Zimene timakhulupilila zimacokela m’Baibo

Yehova ananenelatu kuti kumvetsetsa kwathu Baibo kudzawonjezeleka. Ŵelengani Danieli 12:4, na kukambilana funso ili:

  • Kodi anthu a Mulungu “adzadziŵa zinthu zambili” zotani pamene apitiliza kuphunzila Baibo?

Onani mmene kagulu ka ophunzila Baibo, kuphatikizapo Charles Russell, anafufuzila Mawu a Mulungu. Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

VIDIYO: Kupeza Coonadi ca m’Baibo (7:45)

  • Mu vidiyo iyi, kodi Charles Russell na ophunzila Baibo anzake anali kuiŵelenga motani Baibo?

Kodi mudziŵa?

Nthawi zina, kwakhala kofunikila kuti tiwongolele zimene timakhulupilila. Cifukwa ciyani? Mwacitsanzo, dzuŵa likamatuluka zinthu zimayamba kuonekela bwino pang’ono-pang’ono. Mulungu nayenso amatithandiza pang’ono-pang’ono kumvetsa bwino Mawu ake. (Ŵelengani Miyambo 4:18.) Conco, ngakhale kuti Baibo siisintha, tikaimvetsetsa bwino timawongolela zimene timakhulupilila.

5. Timalalikila zoona ponena za Yehova

N’cifukwa ciyani tinatenga dzina lakuti Mboni za Yehova? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso ili.

VIDIYO: Dzina Lotiyenelela (2:40)

  • N’cifukwa ciyani dzina lakuti Mboni za Yehova n’lotiyenela?

N’cifukwa ciyani Yehova anasankha anthu kukhala mboni zake? Anatelo kuti athandize anthu kudziŵa za Mulungu woona, cifukwa pakukambidwa mabodza ambili onena za iye. Onan’koni aŵili okha a mabodza amenewo.

Zipembedzo zina zimaphunzitsa anthu awo zakuti Mulungu amafuna kuti iwo aziseŵenzetsa zifanizilo pomulambila. Kodi zimenezi n’zoona? Ŵelengani Levitiko 26:1, na kukambilana mafunso aya:

  • Malinga n’kunena kwa lemba ili, kodi Yehova amawaona bwanji mafano?

Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti Yesu ndiye Mulungu. Kodi zimenezi n’zoona? Ŵelengani Yohane 20:17, na kukambilana mafunso aya:

  • Malinga n’kunena kwa lemba ili, kodi Yesu ndiye Mulungu?

  • Kodi mukumva bwanji podziŵa kuti Yehova anatumiza Mboni zake kuti zilalikile coonadi ponena za iye na Mwana wake?

6. Timakondana wina na mnzake

Baibo imayelekezela Akhristu monga ziwalo zosiyana-siyana za thupi la munthu. Ŵelengani 1 Akorinto 12:25, 26, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Akhristu enieni ayenela kucita ciyani pamene Akhristu anzawo ali pamavuto?

  • Pa nkhani ya cikondi, kodi mwaona ciyani pakati pa Mboni za Yehova?

A Mboni za Yehova akakhala pamavuto kudela lina, a Mboni anzawo padziko lonse lapansi amagwapo mofulumila kuti athandize. Kuti muone citsanzo cimodzi, tambani VIDIYO. Pambuyo pake kambilanani funso lotsatila.

VIDIYO: Dziko la Haiti Lipilila Cimphepo Camkuntho Cochedwa Matthew (5:29)

  • Poonetsana cikondi, kodi Mboni za Yehova zinathandizana bwanji kutacitika cimphepo camkuntho?

Mboni za Yehova ziŵili zikuthandiza mzimayi na mwana wake amene akhudzidwa na ngozi imene yangocitika kumene. Akuwafunda bulangete yothuma na kuwapatsa madzi abwino akumwa.

Akhristu enieni amaonetsa cikondi pothandiza ena ofunikila thandizo

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Mboni za Yehova zimasokoneza ŵanthu.”

  • Kodi muganiza izi n’zoona kapena iyai?

CIDULE CAKE

Mboni za Yehova ndizo Akhristu enieni. Lathu ni banja la olambila a padziko lonse, amene ziphunzitso zawo zimatsamila pa Baibo, ndipo timathandiza anthu kumudziŵa bwino Yehova.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani tinatenga dzina lakuti Mboni za Yehova?

  • Timaonetsa bwanji kuti timakondana wina na mnzake?

  • Inu muganiza bwanji, kodi Mboni za Yehova ni Akhristu enieni?

Colinga

FUFUZANI

Phunzilani zambili zokhudza mbili yathu.

Mboni za Yehova Zinasonyeza Chikhulupiriro, Gawo 1: Kutuluka mu Mdima (1:00:53)

Onani citsanzo ca mmene Mboni za Yehova zavumbulila ziphunzitso zonyenga.

Anthu a Mulungu Amalemekeza Dzina Lake (7:08)

Pezani mayankho pa mafunso amene mungakhale nawo okhudza Mboni za Yehova.

“Mafunso Amene Amafunsidwa Kawili-kaŵili Ponena za Mboni za Yehova” (tsamba la pawebusaiti)

Stephen anatengako mbali m’zaciwawa cifukwa codana na mitundu ina. Pezani zomwe iye anaona pakati pa Mboni za Yehova zimene zinamuthandiza kusintha.

“Umoyo Wanga Unali Kuipilaipilabe” (Nsanja ya Mlonda, July 1, 2015)

a Magazini yathu yaikulu, Nsanja ya Mlonda, yakhala ikufalitsa coonadi ca m’Baibo mosasintha ciyambile m’caka ca 1879.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani