Kodi Mwasandulika?
“Sandulikani Mwa Kusintha Maganizo Anu.”—AROMA. 12:2.
KODI MUNGAFOTOKOZE BWANJI?
N’cifukwa ciani Akristu onse afunika kusandulika?
Kodi Mkristu aliyense afunika kusandulika motani?
N’ciani cingatithandize kusanduliza moyo wathu?
1, 2. Kodi mmene tinaleledwela ndiponso anthu amene timakhala nao zimatikhudza bwanji?
TONSEFE timacita zinthu mogwilizana ndi mmene tinaleledwela ndiponso anthu amene timakhala nao. Cifukwa ca zimenezi, timakonda zovala zina zake, zakudya zina zake ndi kucita zinthu m’njila ina yake.
2 Koma pali zinthu zina zofunika kwambili kupambana zakudya ndi zovala zimene timasankha. Mwacitsanzo, tinaphunzila kuona zinthu zina kukhala zabwino ndi zoyenela komanso kuona zinthu zina kukhala zoipa ndi zosayenela. Timaona zinthu zimenezi mosiyana ndi mmene ena amazionela. Zosankha zathu zimaonetsa mmene cikumbumtima cathu cilili. Potsimikizila mfundo imeneyi, Baibo imanena kuti nthawi zambili ‘anthu a mitundu amene alibe cilamulo amacita mwacibadwa zinthu za m’cilamulo.’ (Aroma 2:14) Kodi izi zitanthauza kuti ngati palibe lamulo lacindunji la Mulungu ndiye kuti tingacite zinthu mongotsatila zocita ndi miyezo ya anthu amene timakhala nao?
3. Kodi Akristu samacita zinthu mongotsatila zocita ndi miyezo ya anthu pa zifukwa ziŵili ziti?
3 Akristu samacita zinthu mongotsatila zocita ndi miyezo ya anthu amene amakhala nao. Pali zifukwa ziŵili zimene io sacitila zimenezi. Coyamba, Baibo imati: “Pali njila yooneka ngati yoongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.” (Miy. 16:25). Cifukwa copanda ungwilo, anthufe tilibe nzelu zokwanila ndipo sitingakwanitse kuongolela mapazi athu. (Miy. 28: 26; Yer. 10:23) Caciŵili, Baibo imanena kuti Satana “mulungu wa nthawi ino” ndi amene amacilikiza mfundo zimene anthu amayendela. (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Conco, ngati tifuna kuti Yehova atidalitse ndi kutiyanja, tiyenela kutsatila malangizo a pa Aroma 12:2.—Ŵelengani.
4. Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani?
4 Pa lemba la Aroma 12:2 pali mfundo zingapo zofunika kuziganizila. (1) N’cifukwa ciani tifunikila “kusandulika”? (2) Kodi kusandulika kumaphatikizapo kucita ciani? ndi (3) Kodi tingasandulike bwanji? Tiyeni tikambilane mafunso amenewa.
N’CIFUKWA CIANI TIFUNIKILA KUSANDULIKA?
5. Kodi ndani maka-maka amene Paulo analembela malangizo a pa Aroma 12:2?
5 Malangizo amene mtumwi Paulo analemba m’kalata yake yopita kwa Aroma, sanalembele anthu osakhulupilila, koma analembela Akristu anzake odzozedwa. (Aroma 1:7) Iye anawalimbikitsa kuti ‘asamatengele nzelu za nthawi ino.’ Zinthu zinali zovuta kwa Akristu a ku Roma amene anakhalako mu “nthawi” ya m’ma 56 C.E. Anthu anali kutengela mfundo ndi cikhalidwe ca Aroma. Mau a Paulo akuti “musamatengele” amaonetsa kuti Akristu ena anali kutsatila zocita za anthu a nthawi imeneyo. Kodi zimenezo zinakhudza bwanji abale ndi alongo athu?
6, 7. M’nthawi ya Paulo, kodi cikhalidwe ndi cipembedzo ca ku Roma cinakhudza bwanji Akristu?
6 Masiku ano, anthu amene amapita kukaona malo ku Roma kaŵili-kaŵili amaona mabwinja a makacisi, manda, zipilala, mabwalo a maseŵela, ndi zinthu zina. Zina mwa zinthu zimenezi zinamangidwa m’zaka 100 zoyambilila za nthawi yathu ino. Zinthu zimenezi zimatithandiza kudziŵa za cikhalidwe ndi cipembedzo ca anthu a mu mzinda wakale wa Roma. Tingaŵelengenso m’mabuku a mbili yakale za masewela omenyana, mpikisano wothamangitsa mahachi, masewelo, ndi nyimbo zosiyana-siyana kuphatikizapo zocititsa manyazi. Mzinda wa Roma unalinso likulu la zamalonda cakuti zinali zosavuta kupeza cuma.—Aroma 6:21; 1 Pet. 4:3, 4.
7 Ngakhale kuti Aroma anali ndi makacisi a milungu yambili, iwo sanali paubwenzi weni-weni ndi milungu imene anali kulambila. Kupembedza kwao kunaphatikizapo kucita miyambo yokhudza kubadwa kwa mwana, ukwati, ndi malilo, zimene anthu anali kucita malinga ndi cikhalidwe cao. Mwacionekele zimenezi zinakhudza Akristu a ku Roma. Ambili mwa io anali kucita zimenezi asanakhale Akristu, conco anafunika kusandulika kuti akhale Akristu oona. Iwo anafunika kupitiliza kusandulika pambuyo pa ubatizo.
8. Kodi dziko ndi loopsa bwanji kwa Akristu masiku ano?
8 Mofanana ndi nthawi ya Aroma, dziko masiku ano ndi loopsa kwa Akristu odzipatulila. N’cifukwa ciani? Cifukwa mzimu wa dziko umaonekela m’njila zambili. (Ŵelengani Aefeso 2:2, 3; 1 Yohane 2:16.) Tsiku lililonse timakhala paciyeso cotengela zikhumbo, nzelu, malingalilo, mfundo ndi khalidwe la dziko. Cifukwa ca zimenezi tiyenela kutsatila malangizo ouzilidwa akuti “musamatengele nzelu za nthawi ino” ndi akuti “sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” Kodi tingacite bwanji zimenezi?
KODI TIFUNIKILA KUSANDULIZA CIANI?
9. Kodi ambili amapanga masinthidwe ati asanabatizidwe?
9 Munthu akayamba kuphunzila coonadi ndi kucitsatila pa umoyo wake amapita patsogolo mwa kuuzimu. Iye amapanga masinthidwe kuti moyo wake ugwilizane ndi zimene waphunzila. Amaleka kucita miyambo ya cipembedzo conama ndi kusintha makhalidwe oipa ndipo amakulitsa makhalidwe acikristu. (Aef. 4:22-24) Timasangalala tikamaona anthu masauzande ambili akupita patsogolo caka ciliconse ndi kudzipeleka kwa Yehova Mulungu ndi kubatizidwa. Kunena zoona, Yehova amasangalala ndi zimenezi. (Miy. 27:11) Koma kodi zimenezi n’zokwanila?
10. Kodi kusandulika kumasiyana bwanji ndi kupita patsogolo?
10 Kusandulika kumaphatikizapo zambili kuposa kupita patsogolo kapena kuongolela zinthu zina pa umoyo wathu. Mwacitsanzo, kampani yopanga katundu winawake ingasinthe paketi ya katundu wao pofuna kukopa anthu. Kodi tinganene kuti katundu umenewo wasintha? Iyai, katunduwo udzakhalabe umodzi-modzi. Pofotokoza za liu lakuti “sandulikani,” buku lina lotanthauzila mau limati: “Lemba la Aroma 12:2 limasiyanitsa munthu amene amacita zinthu motengela nzelu za nthawi ino ndi amene amasanduliza mtima wake mwa kusintha maganizo kupyolela m’mphamvu ya Mzimu Woyela.” Conco, Mkristu amasandulika osati cabe mwa kuleka zizoloŵezi zoipa, kalankhulidwe koipa, ndi makhalidwe oipa. Anthu ena amene saphunzila Baibo amayesa-yesa kukhala ndi khalidwe labwino. Nanga kodi ife Akristu timafunika kucita ciani kuti tisandulike?
11. Kodi Paulo anaonetsa kuti kusandulika kumacitika bwanji?
11 Paulo analemba kuti: “Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” Liu lakuti “maganizo” limatanthauza mphamvu zathu za kulingalila. Koma kulingana ndi mmene limagwilitsidwila nchito m’Baibo, lingatanthauzenso mmene munthu amaonela zinthu, zimene amaganiza, ndi mphamvu ya maganizo ake. Kuciyambi kwa kalata yake yopita kwa Aroma, Paulo anakamba za anthu amene anali ndi ‘maganizo oipa.’ Anthu amenewo “anadzadzidwa ndi zosalungama zonse, kuipa konse, kusilila konse kwa nsanje, ndi ucimo wonse. Mtima wao unadzala kaduka, umbanda, ndewu, cinyengo” ndi zinthu zina zoipa. (Aroma 1:28-31) Tingaone cifukwa cake Paulo analimbikitsa atumiki a Mulungu amene anakulila ku Roma kuti ‘asandulike’ ndi ‘kusintha maganizo ao.’
12. Kodi mumaona kuti anthu m’dziko ali ndi maganizo otani? Nanga maganizo amenewa angakhudze bwanji Akristu?
12 N’zacisoni kuti ifenso tikukhala ndi anthu amene khalidwe lao ndi lofanana ndi la anthu amene Paulo anafotokoza. Iwo amaona kuti miyezo ndi mfundo za m’Malemba ndi zinthu zacikale. Aphunzitsi ndi makolo ambili amalimbikitsa ana kucita zinthu zimene anao afuna. Iwo amakamba kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha zilizonse zimene afuna. Ngakhale anthu ambili amene amanena kuti ndi opembedza amaona kuti ali ndi ufulu wocita zimene aona kuti ndi zabwino, ndipo samvela Mulungu kapena kutsatila malamulo ake. (Sal. 14:1) Akristu oona angatengele mosavuta maganizo amenewa. Akristu amene ali ndi malingalilo amenewa angamaone dongosolo la gulu m’njila yolakwika. Iwo angakane kutsatila malangizo a mumpingo ndi kuyamba kudandaula ndi zilizonse zimene sanakonde. Kapena angamakaikile malangizo a m’Baibo okhudza zosangulutsa, kugwilitsila nchito Intaneti, ndi kufuna-funa maphunzilo apamwamba.
13. N’cifukwa ciani tifunika kudzipenda moona mtima?
13 Kuti tisatengele maganizo a dziko, tiyenela kupenda moona mtima maganizo athu, zolinga zathu, ndi mfundo zimene timayendela. Anthu ena sangadziŵe zimene timaganiza ndipo angatiuze kuti timacita bwino. Ndife cabe amene timadziŵa ngati timalola kuti zinthu zimene timaphunzila m’Baibo zipitilize kusanduliza moyo wathu.—Ŵelengani Yakobo 1:23-25.
KODI TINGASANDULIKE BWANJI?
14. N’ciani cingatithandize kupanga masinthidwe oyenela?
14 Kusandulika kumaphatikizapo kusintha umunthu wathu wa m’kati. Conco, tiyenela kugwilitsila nchito cida cimene cingathe kufika m’kati mwa mtima wathu. Kodi n’ciani cingatithandize kucita zimenezi? Zimene timacita tikaphunzila m’Baibo zinthu zimene Yehova amafuna, zimavumbula mmene mtima wathu ulili. Ndiponso zimavumbula zimene tiyenela kusintha pa moyo wathu kuti zocita zathu zigwilizane ndi ‘cifunilo ca Mulungu, cangwilo.’—Aroma 12:2; Aheb. 4:12.
15. Kodi timasandulika bwanji pamene tiumbidwa ndi Yehova?
15 Ŵelengani Yesaya 64:8. Fanizo limene mneneli Yesaya ananena limatiphunzitsa mfundo yofunika kwambili. Kodi Yehova, amene ndi Wotiumba, amatiumba bwanji? Iye sasintha maonekedwe athu kuti tikhale okongola kwambili. Yehova amatiphunzitsa mwakuuzimu osati mwakuthupi. Tikalola kuti iye atiumbe, timasandulika mwakuuzimu kapena kuti umunthu wathu wonse umasintha. Zimenezi zimatithandiza kulimbana ndi zisonkhezelo zoipa za m’dziko. Kodi Mulungu amatiumba bwanji mwa kuuzimu?
16, 17. (a) Fotokozani zimene woumba mbiya amacita ndi dongo kuti aumbe mbiya. (b) Kodi Mau a Mulungu amatithandiza bwanji kuti tisandulike ndi kukhala ciwiya ca mtengo wapatali ca Yehova?
16 Kuti woumba mbiya aumbe mbiya yabwino, amagwilitsila nchito dongo labwino. Koma pali zinthu ziŵili zimene amacita. Coyamba, iye amacotsa zinyalala kapena zinthu zina zosafunikila ku dongo limenelo. Kenako, iye amalisakaniza ndi madzi ndi kulikanda kuti likhale labwino poligwilitsila nchito.
17 Onani kuti woumba mbiya amagwilitsila nchito madzi kuyeletsa dongo kuti likhale labwino poligwilitsila nchito popanga mbiya. Izi ndi zofanana ndi mmene Mau a Mulungu amagwilila nchito pa moyo wathu. Mau a Mulungu angatithandize kucotsa maganizo oipa amene tinali nao tisanadziŵe Mulungu ndi kusandulika kukhala ciwiya ca mtengo wapatali ca Mulungu. (Aef. 5:26) Nthawi zambili timalimbikitsidwa kuŵelenga Baibo tsiku ndi tsiku ndi kupezeka pa misonkhano nthawi zonse, kumene timaphunzila mau a Mulungu. N’cifukwa ciani timalimbikitsidwa kucita zimenezi? Cifukwa cakuti tikacita zimenezi, timalola Yehova kutiumba.—Sal. 1:2; Mac. 17:11; Aheb. 10:24, 25.
18. (a) N’cifukwa ciani kusinkha-sinkha ndi kofunika kuti Mau a Mulungu asandulize moyo wathu? (b) Kodi tifunika kudzifunsa mafunso ati?
18 Kuŵelenga ndi kuphunzila Baibo ndi ciyambi cabe kuti Mau a Mulungu atisandulize. Anthu ambili amaŵelenga Baibo nthawi ndi nthawi ndipo amadziŵa zimene iyo imanena. Mwina inuyo munakumanapo ndi anthu otelo mu ulaliki. Ena amakwanitsa kuchula pamtima zimene mavesi ena a m’Baibo amakamba.a Koma zimenezi sizisintha kweni-kweni maganizo ndi khalidwe lao. N’cifukwa ciani zili conco? Kuti Mau a Mulungu asandulize munthu, iye ayenela kuwalola kumufika pamtima. (Agal. 6:6) Conco, tifunika kupatula nthawi kuti tisinkhe-sinkhe zimene timaphunzila. Tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakhulupililadi kuti zimene ndimaphunzila ndi Mau a Mulungu? Kodi ndimakhulupilila kuti ici ndi coonadi? Kodi ndimayesetsa kugwilitsila nchito zimene ndimaphunzila osati kungouzako ena cabe? Ndikamaphunzila, kodi ndimamva kuti Yehova akamba ndi ine mwacindunji?’ Kuganizila ndi kusinkha-sinkha mafunso ngati amenewa kungathandize kukulitsa cikondi cathu pa Yehova. Ngati timakonda Mulungu kucokela pansi pa mtima, tidzapanga masinthidwe oyenela pa umoyo wathu.—Miy. 4:23; Luka 6:45.
19, 20. Kodi tiyenela kumvela malangizo ati a m’Baibo kuti tipindule?
19 Kuŵelenga ndi kusinkha-sinkha Mau a Mulungu nthawi zonse kudzatithandiza kupitiliza ‘kuvula umunthu wakale pamodzi ndi nchito zake, ndi kuvala umunthu watsopano umene Mulungu amapeleka, kutanthauza kuti mwa kudziŵa zinthu molondola, tidzacititsa umunthu wathu kukhala watsopano.’ (Akol. 3:9, 10) Ndithudi, tidzapindula kwamuyaya ngati timvetsetsa Mau a Mulungu ndi kucita zimene amanena. Kuvala umunthu watsopano kudzatithandiza kupewa misampha ya Satana.
20 Mtumwi Petulo anatipatsa malangizo akuti: “Monga ana omvela, lekani kukhala motsatila zilako-lako zimene munali nazo kale,” koma “khalani oyela m’makhalidwe anu onse.” (1 Pet. 1:14, 15) Ngati tiyesetsa kucotsa maganizo oipa ndi kusiya makhalidwe oipa akale kuti Mulungu atiumbe, tidzakhala ndi madalitso monga mmene tidzaonela m’nkhani yotsatila.
[Mau apansi]
a Onani citsanzo mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1994, tsamba 9, ndime 7.
[Zithunzi papeji 18, 19]
Anthu ambili afunika kucoka m’dziko la Satana ndi kusandulika (Onani ndime 9)
[Mau okopa papeji 19]
“Kupsa mtima mkwiyo, kulalata ndiponso mau acipongwe zicotsedwe mwa inu.”—Aef. 4:31
[Cithunzi papeji 21]
Kusandulika kudzakuthandizani kuthetsa mavuto mwanzelu kusiyana ndi kale (Onani ndime 18)