LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w21 April tsa. 30-tsa. 31 pala. 5
  • Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Zimene Tingaphunzile pa Mawu Othela a Yesu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mvelani Mawu a Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kodi Yesu Khiristu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
w21 April tsa. 30-tsa. 31 pala. 5
Yesu wapacikidwa pamtengo wozunzikilapo pakati pa apandu aŵili kutacita mdima.

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

N’Cifukwa ciani Yesu atangotsala pang’ono kufa anagwila mawu a Davide opezeka pa Salimo 22:1?

Ena mwa mawu othela amene Yesu anakamba atatsala pang’ono kufa apezeka pa Mateyu 27:46: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyilanji ine?” Pokamba mawu amenewa, Yesu anakwanilitsa mawu a wa Masalimo Davide a pa Salimo 22:1. (Maliko 15:34) Kungakhale kulakwa kuganiza kuti Yesu anagwila mawu amenewa cifukwa cakuti anakhumudwa kapena cifukwa cakuti anataya cikhulupililo kwa kanthawi. Yesu anali kudziŵa bwino cifukwa cake anayenela kufa, ndipo analidi wokonzeka kufa. (Mat. 16:21; 20:28) Anadziŵanso kuti panthawi ya imfa yake, Yehova sadzafunika ‘kum’chinga’ kapena kuti kum’teteza. (Yobu 1:10) Mwakutelo, Yehova analola Yesu kuonetsa kuti adzakhalabe wokhulupilika mosasamala kanthu zovuta zimene adzakumana nazo kufikila imfa yake.—Maliko 14:35, 36.

Nanga n’cifukwa ciani Yesu anakamba mawu a m’Salimo limeneli? Ngakhale kuti sitingakambe motsimikiza, tiyeni tione zina zothekela kukhala zifukwa zake.a

Mwa kukamba mawu amenewa, mwina Yesu anali kugogomeza mfundo yakuti Yehova sadzalowelelapo kuti amuteteze pa imfa yake. Yesu anafunika kulipila dipo popanda thandizo la Yehova. Iye anali munthu weni-weni, ndipo anafunika kufa kuti “alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.”—Aheb. 2:9.

Pogwila mawu ocepa cabe m’salimo limenelo, mwina Yesu anali kufuna kuthandiza anthu kuganizila mawu a m’salimo lonselo. Zinali zofala m’masiku amenewo Ayuda kuloŵeza pamtima mawu a masalimo ambili. Mwa kukumbutsidwa vesi limodzi la m’salimo, iwo anakumbukila mawu a m’salimo lonselo. Ngati izi n’zimene Yesu anali nazo m’maganizo, ndiye kuti anathandiza otsatila ake Aciyuda kukumbukila maulosi ambili a m’salimo limeneli okhudza zocitika za panthawi ya imfa yake. (Sal. 22:7, 8, 15, 16, 18, 24) Cina, mavesi othela a m’salimo limeneli, akufotokoza kuti citamando ca Yehova monga mfumu cimafika ku malekezelo a dziko lapansi.—Sal. 22:27-31.

Pogwila mawu a Davide amenewa, mwina Yesu anali kuonetsa kuti anali wosalakwa. Yesu asanafe, anazengedwa mlandu mopanda cilungamo wakuti anali kunyoza Mulungu. (Mat. 26:65, 66) Mlanduwo unaweluzidwa mmangu-mmangu usiku kwambili, ndipo unaweluzidwa mosemphana na miyezo ya kaweluzidwe ka milandu. (Mat. 26:59; Maliko 14:56-59) Pamene Yesu anafunsa funso lakuti “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyilanji ine,” ayenela kuti anali kufuna kuthandiza anthu kudziŵa kuti sanalakwe ciliconse coyenela cilango ca mtundu umenewo.

Mwina Yesu anali kukumbutsanso ena kuti ngakhale kuti Davide wolemba salimo limeneli analoledwa kuvutika, izi sizinatanthauze kuti Yehova analeka kumuyanja Davide. Funso la Davide silinaonetse kuti analibe cikhulupililo. Atafunsa funso limeneli, anapitiliza kukamba mawu oonetsa kuti anali kudalila mphamvu zopulumutsa za Yehova, ndipo Yehova anapitiliza kum’dalitsa. (Sal. 22:23, 24, 27) Mofananamo, ngakhale kuti Yesu, “Mwana wa Davide,” anavutika pamtengo wonzunzikilapo, sizinatanthauze kuti Yehova analeka kum’yanja Yesu.—Mat. 21:9.

Mwina Yesu anali kuonetsa cisoni cacikulu cimene anali naco podziŵa kuti Yehova anafunika kucotsa citetezo cake n’colinga cakuti iye aonetse kukhulupilika kwake. Sicinali colinga ca Yehova poyamba kuti akatumize Mwana wake kuti adzavutike na kufa ayi. Izi zinangokhala zofunikila pambuyo pakuti Adamu na Hava apanduka. Yesu sanalakwe ciliconse. Koma anafunika kuvutika na kufa kuti ayankhe mafunso amene Satana anabutsa, ndiponso kuti apeleke malipilo a dipo ogulila zimene munthu anataya. (Maliko 8:31; 1 Pet. 2:21-24) Izi zikanatheka kokha ngati Yehova kwa kanthawi akanacotsa citetezo cake pa Yesu kwa nthawi yoyamba mu umoyo wake.

Mwina Yesu anali kuyesa kuthandiza otsatila ake kusumika maganizo pa cifukwa cimene Yehova analolela kuti iye afe mwa njila imeneyi.b Yesu anadziŵa kuti kufa kwake monga munthu wocita zoipa pamtengo wonzunzikilapo kudzakhumudwitsa anthu ambili. (1 Akor. 1:23) Kuganizila pa cifukwa ceni-ceni cimene Yesu anafela, kuyenela kuti kunathandiza otsatila ake kumvetsetsa kufunika kwa imfa yake. (Agal. 3:13, 14) Ziyenela kuti zinawathandiza kumuona kukhala Mpulumutsi, osati mpandu.

Kaya Yesu anagwila mawu amenewa pa zifukwa zotani, iye anazindikila kuti zimene zinali kum’citikila zinali mbali ya cifunilo ca Yehova. Patapita nthawi yocepa Yesu atagwila mawu a salimo limeneli, iye anati: “Ndakwanilitsa cifunilo canu!” (Yoh. 19:30; Luka 22:37) Inde, kucotsa citetezo cake Yehova kwa kanthawi kunalola Yesu kukwanilitsa zonse zimene anatumidwa kudzacita padziko lapansi. Kunam’patsanso mwayi wokwanilitsa zolembedwa zonse zokhudza iye za “m’cilamulo ca Mose, m’Zolemba za aneneli ndi m’Masalimo.”—Luka 24:44.

a Onaninso ndime 9 na 10 m’nkhani yakuti “Zimene Tingaphunzile pa Mawu Othela a Yesu” m’magazini ino.

b Pa utumiki wake, Yesu nthawi zina anali kukamba zinthu kapena kufunsa mafunso amene sanali kuonetsa mmene iye anali kumvelela. Anali kucita izi na colinga cakuti ayambitse makambilano na otsatila ake.—Maliko 7:24-27; Yoh. 6:1-5; onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2010, tsamba. 4-5.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani