MFUNDO YOTHANDIZA PA KUWELENGA KWANU
Konzekeletsani Mtima Wanu
Pamene tiwelenga Baibo, timafuna kuti kaganizidwe ka Yehova kakhudze mtima komanso umunthu wathu wamkati. Ezara anapeleka citsanzo cabwino pamene “anakonzekeletsa mtima wake kuti aphunzile Cilamulo ca Yehova.” (Ezara 7:10) Kodi tingaukonzekeletse motani mtima wathu?
Pemphelani. Mukalibe kuyamba kuwelenga, muzipemphela. M’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa komanso kugwilitsa nchito zimene mufuna kuphunzila.—Sal. 119:18, 34.
Khalani wodzicepetsa. Mulungu amabisa coonadi cake kwa anthu amene modzikuza amadalila nzelu zawo. (Luka 10:21) Pamene tikuwelenga, colinga cathu cisamakhale kufuna kudzionetsela kwa ena kuti tidziwa zambili. Modzicepetsa, sinthani kaganizidwe kanu ngati sikagwilizana ndi kaganizidwe ka Mulungu.
Mvetselani nyimbo ya Ufumu. Nyimbo zili ndi mphamvu yokhudza mtima wathu. Conco kumvetsela nyimbo ya Ufumu tisanayambe kuwelenga kungatithandize kuika maganizo athu pa Yehova kuti zimene tidzaphunzila zitifike pamtima.