Kodi Ndileke Kuyendetsa Galimoto?
Tinene kuti mwakhala mukuyendetsa galimoto kwa zaka zambili. Mumamva bwino kukhala ndi galimoto yanu-yanu, ndipo mungapite kulikonse kumene mufuna. Ngakhale n’telo, acibale komanso mabwenzi anu akukudelani nkhawa ndipo akufuna kuti muganizilenso cisankho canu ca kupitiliza kuyendetsa galimoto. Koma inu simukumvetsa cifukwa cake ali ndi nkhawa.
Kodi umu ndi mmene zilili kwa inu? Ngati n’telo, n’ciani cingakuthandizeni kudziwa ngati mufunika kuleka kuyendetsa galimoto?
M’maiko ena, munthu akafika pa msinkhu winawake, amafunika cilolezo ca dokotala kuti apitilize kuyendetsa galimoto. Akhristu omwe amakhala m’maiko amenewa, ayenela kumvela malamulo a boma. (Aroma 13:1) Koma kaya mumakhala kuti, pali mfundo zimene zingakuthandizeni kudziwa ngati mumayendetsabe bwino galimoto.
ONANINSO MMENE MUMAYENDETSELA GALIMOTO
Bungwe lina lothandiza acikulile linati okalamba ayenela kudzifunsa mafunso awa:
Kodi zimandibvuta kuwelenga zizindikilo za pa mseu kapena kuona usiku?
Kodi ndimakwanitsabe kutembenuka kuti ndiyang’ane pamagilasi oonetsa za kumbuyo komanso mbali zina zonse?
Kodi ndimakwanitsa kucita zinthu msanga-msanga, monga kubweza magiya mofulumila n’kuponda pabuleki?
Kodi ndimayendetsa pang’ono-pang’ono kwambili moti n’kusokoneza magalimoto ena?
Kodi zandicitikilapo kangapo kuti ndatsala pang’ono kucita ngozi, kapena kodi galimoto yanga ndi yokwesheka-kwesheka cifukwa cogunda zinthu?
Kodi apolisi anandiimikapo cifukwa ca kayendetsedwe kanga?
Kodi ndinaodzelapo ndikuyendetsa galimoto?
Kodi ndimamwa mankhwala omwe angandisokoneze poyendetsa galimoto?
Kodi a m’banja mwanga kapena mabwenzi anga anandiuzapo kuti akundidela nkhawa cifukwa ca mmene ndimayendetsela galimoto?
Ngati mwayankha kuti inde pa funso limodzi kapena awili ali pamwambapa, zingakhale bwino kuganizila zopanga masinthidwe. Mwacitsanzo, mungacepetseko kuyendetsa galimoto, maka-maka usiku. Nthawi ndi nthawi, muziona mmene mumayendetsela galimoto. Mungauze wacibale kapena bwenzi lanu kuti akuuzeni mmene aonela kayendetsedwe kanu ka galimoto. Mwinanso mungaciteko kosi yophunzitsa anthu kuyendetsa galimoto mosamala. Komabe, ngati mwayankha kuti inde pa mafunso atatu kapena kuposelapo ali pamwambapa, zingakhale bwino kuleka kuyendetsa galimoto.a
LOLANI MFUNDO ZA M’BAIBO KUKUTSOGOLELANI
Nthawi zina, sitingazindikile kuti sitikuthanso kuyendetsa bwino galimoto. Ndipo nkhani yakuti muleke kuyendetsa galimoto ingakhale yobvuta kwa inu kuikambilana. Conco, ndi mfundo ziti za m’Baibo zimene zingakuthandizeni kuiona bwino-bwino nkhaniyi ndi kupanga cisankho canzelu? Nazi mfundo ziwili.
Khalanibe odzicepetsa. (Miy. 11:2) Tikamakalamba, mphamvu yathu yoona, ya kumva, ndi yocita zinthu mwamsanga imacepela-cepela. Nayonso minofu imatha mphamvu. Pa cifukwa cimeneci, anthu ambili amaleka kucita masewela olimbitsa thupi akamakalamba cifukwa amadziwa kuti zimakhala zosabvuta kubvulala. N’cimodzi-modzi ndi nkhani yoyendetsa galimoto. Munthu wodzicepetsa amasiya kuyendetsa galimoto akazindikila kuti angacititse ngozi akapitiliza kutelo. (Miy. 22:3) Ndipo amamvetsela ena akakambapo pa kayendetsedwe kake.—Yelekezelani ndi 2 Samueli 21:15-17.
Pewani mlandu wa magazi. (Deut. 22:8) Ngati munthu sayendetsa bwino galimoto angabvulaze anthu kapena kuwapha kumene. Ngati munthu sakuthanso kuyendetsa galimoto bwino-bwino koma akupitiliza, amaika moyo wake ndi wa anthu ena pa ciopsezo. Ndipo ngati ngozi ingacitike, angakhale ndi mlandu wa magazi.
Musaganize kuti anthu adzasiya kukulemekezani mukaleka kuyendetsa galimoto. Yehova amakukondani cifukwa ca kudzicepetsa kwanu komanso cifukwa ca mtima wanu woganizila ena. Ndipo akulonjeza kuti sadzakusiyani ngakhale pang’ono. (Yes. 46:4) Conco, m’pempheni kuti akupatseni nzelu ndi luso la kuzindikila pomwe mukusankha kaya kuleka kapena kupitiliza kuyendetsa galimoto.
a Kuti mudziwe zambili, welengani nkhani yakuti “Kodi Ngozi Zapamsewu Sizingakuchitikireni?” mu Galamukani! ya Chichewa ya September 8, 2002.