-
Deuteronomo 4:15-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Mukhale tcheru,* chifukwa pa tsiku limene Yehova analankhula nanu kuchokera pakati pa moto ku Horebe, simunaone kalikonse mʼmotowo. 16 Choncho musamale kuti musachite zinthu mosakhulupirika popanga chifaniziro chilichonse chosema, chifaniziro cha chinthu chilichonse chachimuna kapena chachikazi,+ 17 chifaniziro cha nyama iliyonse yapadziko lapansi kapena chifaniziro cha mbalame iliyonse youluka mumlengalenga,+ 18 chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene chimakwawa panthaka kapena chifaniziro cha nsomba iliyonse yamʼmadzi apansi pa dziko.+
-