Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mlungu uno
July 28–August 3
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—2025 | July

JULY 28–AUGUST 3

MIYAMBO 24

Nyimbo Na. 38 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzikonzekera Mavuto

(10 min.)

Muziphunzira Baibulo kuti mupeze nzeru zokuthandizani kudziwa zinthu (Miy 24:5; w23.07 31:15)

Musamasiye kuchita zinthu zokhudza kulambira ngakhale pamene mwafooka (Miy 24:10; w09 12/15 2:12-13)

Kukhala olimba mwauzimu ndi komwe kungakuthandizeni kuthana ndi mavuto (Miy 24:16; w20.12 15)

Mlongo amene ali ndi matenda aakulu akulalikira khomo ndi khomo mosangalala ndi mlongo wina. Mlongoyu akuonetsa mwininyumba zinthu zina pa tabuleti yake.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Miy 24:27—Kodi ndi mfundo iti imene tikupeza palembali? (lvs 10:13-15)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Mat 2:9-16 (th phunziro 11)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Mwasiya kulankhula ndi munthu musanamulalikire. (lmd phunziro 2 mfundo 4)

5. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 3 mfundo 4)

6. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Muuzeni kuti timaphunzira Baibulo ndi anthu ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za phunziro la Baibulo. (lmd phunziro 4 mfundo 3)

7. Nkhani

(3 min.) lmd zakumapeto A mfundo 11—Mutu: Mulungu Anatipatsa Uthenga Wofunika. (th phunziro 6)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 99

8. Tizithandizana Tikakumana ndi Mavuto

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Miliri, ngozi zam’chilengedwe, zachiwawa, nkhondo kapena chizunzo zikhoza kuchitika mosayembekezereka. Zimenezi zikachitika, abale ndi alongo amene akhudzidwawo akhoza kuthandizana komanso kulimbikitsana. Komabe ngakhale kuti enafe sitinakhudzidwe mwachindunji, zimatiwawa ndipo timachita zonse zomwe tingathe kuti tiwathandize.—1Ak 12:25, 26.

Zithunzi zosonyeza abale ndi alongo akuthandiza Akhristu anzawo m’njira zosiyanasiyana: 1. Abale ndi alongo akumanganso Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongeka ndi ngozi ya m’chilengedwe. 2. Abale ndi alongo akulandira mosangalala mayi ndi mwana wake amene athawa m’dziko lawo. 3. Mlongo akuponya ndalama m’bokosi la zopereka ku Nyumba ya Ufumu. 4. Abale ndi alongo akupereka zinthu zofunika kwa Akhristu anzawo amene athawa kwawo pa Nyumba ya Ufumu. 5. Anthu ongodzipereka akugawa mabotolo a madzi. 6. M’bale akupemphera.

Werengani 1 Mafumu 13:6 ndi Yakobo 5:16b. Kenako funsani funso ili:

  • N’chifukwa chiyani mapemphero amene atumiki a Yehova amapereka m’malo mwa anzawo amakhala amphamvu?

Werengani Maliko 12:42-44 ndi 2 Akorinto 8:1-4. Kenako funsani funso ili:

  • Ngakhale titakhala kuti sitipeza ndalama zambiri moti timangokwanitsa kupereka zochepa pa ntchito yapadziko lonse, n’chifukwa chiyani tiyenera kumaperekabe?

Onerani VIDIYO yakuti Kulimbikitsa Abale Ntchito Yathu Ikaletsedwa. Kenako funsani funso awa:

  • Kodi abale anasonyeza bwanji chikondi chololera kuvutikira ena pothandiza Akhristu anzawo amene anali m’madera omwe ntchito yathu inali yoletsedwa ku Eastern Europe?

  • Pa nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa, kodi abale anasonyeza bwanji kumvera lamulo lakuti azisonkhana komanso kulimbikitsana?—Ahe 10:24, 25

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) lfb mutu 4-5

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 116 ndi Pemphero

Zimene Zili M’magaziniyi
Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2025 | May

Nkhani Yophunzira 21: July 28, 2025–August 3, 2025

14 Tiziyembekezera Mzinda Umene Sudzawonongeka

zinanso zimene mungawerenge

nkhani zowonjezera

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani