-
Numeri 16:47Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 Nthawi yomweyo Aroni anatenga chofukiziracho mogwirizana ndi zimene Mose anamuuza, nʼkuthamanga kukalowa pakati pa mpingowo. Koma mliri unali utayamba kale pakati pawo. Choncho Aroni anaika nsembe yofukiza ija pachofukiziracho nʼkuyamba kuphimbira anthuwo machimo.
-
-
Deuteronomo 9:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Zitatero ndinkadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova kwa masiku 40, masana ndi usiku, ngati mmene ndinachitira poyamba. Sindinkadya chakudya kapena kumwa madzi+ chifukwa cha machimo anu onse amene munachita pochita zinthu zoipa pamaso pa Yehova nʼkumukhumudwitsa.
-