-
Yoswa 5:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Aisiraeliwo anayenda mʼchipululu zaka 40,+ mpaka anthu onse amene anatuluka mu Iguputo, amene sanamvere mawu a Yehova+ atatha kuphatikizapo amuna onse otha kupita kunkhondo. Amenewo Yehova anawalumbirira kuti sadzawalola kuona dziko+ limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzalipereka kwa anthu ake,*+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+
-
-
Salimo 95:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kwa zaka 40, mʼbadwo umenewo unkandinyansa ndipo ndinati:
“Awa ndi anthu amene mitima yawo imasochera nthawi zonse,
Njira zanga sakuzidziwa.”
-