- 
	                        
            
            Oweruza 1:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
- 
                            - 
                                        21 Anthu a fuko la Benjamini sanathamangitse Ayebusi a ku Yerusalemu, moti Ayebusiwo akukhalabe ndi anthu a fuko la Benjamini ku Yerusalemu mpaka lero.+ 
 
- 
                                        
- 
	                        
            
            2 Samueli 5:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
- 
                            - 
                                        6 Ndiyeno mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene ankakhala kumeneko. Ayebusi anayamba kunyoza Davide kuti: “Sudzalowa mumzinda uno, chifukwa ngakhale anthu osaona ndi olumala adzakuthamangitsa.” Iwo ankaganiza kuti: ‘Davide sadzalowa mumzinda muno.’+ 7 Koma Davide analanda malo amene anali mumpanda wolimba kwambiri mu Ziyoni, umene panopa ndi Mzinda wa Davide.+ 
 
-