-
Levitiko 21:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Mkulu wa ansembe wokhala pakati pa abale ake ansembe, amene anamuthira mafuta odzozera unsembe pamutu pake,+ nʼkuikidwa kukhala wansembe* kuti azivala zovala zaunsembe,+ asalekerere tsitsi lake osalisamala ndipo asangʼambe zovala zake.+ 11 Iye asayandikire munthu aliyense wakufa+ ndipo asamadzidetse ngakhale amene wamwalirayo atakhala bambo ake kapena mayi ake. 12 Asamatuluke mʼmalo opatulika ndipo asamadetse malo opatulika a Mulungu wake,+ chifukwa pamutu pake pali chizindikiro cha kudzipereka, chomwe ndi mafuta odzozera a Mulungu wake.+ Ine ndine Yehova.
-