26 Kenako ndinatumiza amithenga kuchokera mʼchipululu cha Kademoti+ kupita kwa Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni, kuti akanene uthenga wamtendere kuti,+ 27 ‘Ndilole ndidutse mʼdziko lako. Ndidzangodutsa mumsewu ndipo sindidzakhotera kudzanja lamanja kapena lamanzere.+