-
Numeri 25:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Dzina la mwamuna wa Chiisiraeli, amene anaphedwa limodzi ndi mkazi wa Chimidiyani uja linali Zimiri mwana wa Salu, ndipo anali mtsogoleri wa nyumba ya makolo a fuko la Simiyoni. 15 Dzina la mkazi wa Chimidiyani amene anaphedwayo linali Kozibi, mwana wa Zuri.+ Zuri anali mtsogoleri wa fuko la nyumba ina ya makolo ku Midiyani.+
-