-
Deuteronomo 31:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu kuti akutsogolereni. Iye adzawononga mitundu imeneyi pamaso panu ndipo inu mudzaithamangitsa.+ Yoswa ndi amene akutsogolereni nʼkukuwolotsani,+ mogwirizana ndi zimene Yehova wanena. 4 Yehova adzachitira mitundu imeneyi zimene anachitira Sihoni+ ndi Ogi,+ mafumu a Aamori, ndiponso zimene anachitira dziko lawo pamene anawawononga.+
-