-
Deuteronomo 4:10-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pa tsiku limene munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebe, Yehova anandiuza kuti, ‘Sonkhanitsa anthu kwa ine kuti amve mawu anga,+ nʼcholinga choti aphunzire kundiopa+ masiku onse amene iwo adzakhale ndi moyo padzikoli komanso kuti aphunzitse ana awo.’+
11 Choncho anthu inu munayandikira nʼkuimirira mʼmunsi mwa phiri. Phirilo linkayaka moto umene unkafika kumwamba,* ndipo kunali mdima ndi mtambo wakuda.+ 12 Ndiyeno Yehova anayamba kukulankhulani kuchokera mʼmoto.+ Inu munamva mawu koma simunaone kalikonse.+ Munangomva mawu okha basi.+ 13 Iye anakuuzani pangano lake,+ kapena kuti Malamulo Khumi,*+ amene anakulamulani kuti muziwatsatira. Kenako analemba Malamulowo pamiyala iwiri yosema.+
-