-
Deuteronomo 8:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Chifukwa Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino,+ dziko la mitsinje ya madzi,* akasupe ndi madzi ochuluka amene akuyenda mʼzigwa ndi mʼdera lamapiri, 8 dziko la tirigu, balere, mphesa, mitengo ya mkuyu ndi makangaza,*+ dziko la maolivi opangira mafuta ndiponso la uchi,+ 9 mʼdziko limene simudzasowa chakudya komanso simudzasowa chilichonse, dziko limene miyala yake amapangira zitsulo, limenenso mʼmapiri ake mudzakumbamo kopa.*
-
-
Yeremiya 14:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Kodi pa mafano opanda pake a mitundu ya anthu pali fano lililonse limene lingagwetse mvula?
Kapena kodi kumwamba pakokha kungagwetse mvula yamvumbi?
Kodi si inu nokha, Yehova Mulungu wathu, amene mumachititsa zimenezi?+
Chiyembekezo chathu chili mwa inu
Chifukwa inu nokha ndi amene mumachita zonsezi.
-