-
Deuteronomo 28:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Koma mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu poonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mudzatembereredwa ndipo zinthu zoipa zotsatirazi zidzakuchitikirani:+
-
-
2 Mbiri 7:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndikatseka kumwamba ndipo mvula sinagwe, ndikalamula dzombe kuti lidye zomera zamʼdzikoli, ndikatumiza mliri pakati pa anthu anga, 14 anthu anga otchedwa ndi dzina langa+ akadzichepetsa,+ kupemphera, kundifunafuna komanso kusiya njira zawo zoipa,+ ine ndidzamva ndili kumwamba nʼkuwakhululukira tchimo lawo ndipo ndidzachiritsa dziko lawo.+
-