-
Deuteronomo 12:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mʼmalomwake, mudzafunefune Yehova Mulungu wanu pamalo alionse amene adzasankhe kuti aikepo dzina lake komanso malo amene azidzakhala pakati pa mafuko anu onse, ndipo muzidzapita kumeneko.+
-
-
Deuteronomo 15:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Mwana aliyense wamphongo woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena wa nkhosa muzimupatula nʼkumupereka kwa Yehova Mulungu wanu.+ Musamagwiritse ntchito iliyonse mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe,* kapena kumeta ubweya wa mwana woyamba kubadwa wa nkhosa. 20 Chaka chilichonse inuyo ndi banja lanu muzidzadya mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena wa nkhosa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Yehova adzasankhe.+
-