11 Tsopano mʼchaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, pa tsiku la 20 la mweziwo,+ mtambo uja unanyamuka pamwamba pa chihema+ cha Umboni. 12 Choncho Aisiraeli ananyamuka mʼchipululu cha Sinai potsatira dongosolo lawo lonyamukira,+ ndipo mtambowo unakaima mʼchipululu cha Parana.+