-
Levitiko 21:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Munthu akakhala ndi chilema chilichonse, asayandikire malo opatulika. Kaya akhale ndi vuto losaona, wolumala, wankhope yopotoka,* wamkono kapena mwendo wautali kwambiri kuposa unzake,
-
-
Yesaya 56:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Izi nʼzimene Yehova wanena kwa anthu ofulidwa amene amasunga sabata langa. Amene asankha kuchita zimene ndimasangalala nazo komanso amene amatsatira pangano langa:
5 “Mʼnyumba mwanga ndiponso mkati mwa mpanda wanga ndidzawapatsa chipilala chachikumbutso ndiponso dzina,
Zomwe ndi zabwino kwambiri kuposa ana aamuna ndi aakazi.
Ndidzawapatsa dzina limene lidzakhalapo mpaka kalekale,
Dzina limene silidzatha.
-