-
1 Samueli 14:47, 48Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 Sauli analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli ndipo anamenyana ndi adani ake mʼmadera onse. Anamenyana ndi Amowabu,+ Aamoni,+ Aedomu,+ mafumu a Zoba+ ndi Afilisiti.+ Kulikonse kumene ankapita ankagonjetsa adani akewo. 48 Iye ankamenya nkhondo molimba mtima ndipo anagonjetsa Aamaleki+ nʼkupulumutsa Aisiraeli kwa adani awowo.
-