- 
	                        
            
            Numeri 21:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
 - 
                            
- 
                                        
23 Koma Sihoni sanalole kuti Aisiraeli adutse mʼdziko lake. Mʼmalomwake, iye anasonkhanitsa anthu ake onse nʼkupita kukamenyana ndi Aisiraeli mʼchipululumo. Anakafika ku Yahazi ndipo anayamba kumenyana ndi Aisiraeli.+ 24 Koma Aisiraeli anapha anthuwo ndi lupanga+ nʼkuwalanda dziko lawo,+ kuyambira kuchigwa cha Arinoni+ mpaka kuchigwa cha Yaboki,+ pafupi ndi Aamoni, chifukwa Yazeri+ anachita malire ndi Aamoni.+
 
 - 
                                        
 
- 
	                        
            
            Oweruza 11:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
 - 
                            
- 
                                        
20 Koma Sihoni sanakhulupirire kuti Aisiraeli akufuna kungodutsa mʼdziko lake. Choncho Sihoni anasonkhanitsa anthu ake onse nʼkumanga misasa ku Yahazi ndipo anayamba kumenyana ndi Aisiraeliwo.+
 
 -