-
Deuteronomo 12:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mʼmalomwake, mudzafunefune Yehova Mulungu wanu pamalo alionse amene adzasankhe kuti aikepo dzina lake komanso malo amene azidzakhala pakati pa mafuko anu onse, ndipo muzidzapita kumeneko.+ 6 Nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu,+ nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo, nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzapita nazo kumalo amenewo.+
-
-
Oweruza 21:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Kenako anati: “Pajatu ku Silo+ kumachitika chikondwerero cha Yehova chaka chilichonse. Mzinda wa Silo uli kumpoto kwa Beteli, chakumʼmawa kwa msewu waukulu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kumʼmwera kwa Lebona.”
-