42 Kenako Yonatani anauza Davide kuti: “Pita mwamtendere, chifukwa tonse talumbira+ mʼdzina la Yehova kuti, ‘Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndiponso pakati pa mbadwa zako ndi mbadwa zanga mpaka kalekale.’”+
Kenako Davide ananyamuka nʼkumapita ndipo Yonatani anabwerera kwawo.